-
Numeri 10:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Tsopano mʼchaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20 la mweziwo,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni. 12 Choncho Aisiraeli ananyamuka mʼchipululu cha Sinai potsatira dongosolo lawo lonyamukira,+ ndipo mtambowo unakaima mʼchipululu cha Parana.+ 13 Kameneka kanali koyamba kuti iwo asamuke motsatira malangizo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose.+
-