-
Oweruza 9:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Kodi mukuona kuti mwachita bwino kuika Abimeleki kukhala mfumu?+ Kodi mwachita zimenezi kuchokera pansi pa mtima? Nanga Yerubaala ndi banja lake mwamuchitira zabwino? Kodi zimene mwamuchitira ndi zogwirizana ndi zimene iye anachita? 17 Pamene bambo anga anakumenyerani nkhondo,+ anaika moyo wawo pangozi kuti akulanditseni kwa Amidiyani.+ 18 Koma inu lero mwaukira banja la bambo anga ndipo mwapha ana awo aamuna 70 pamwala umodzi.+ Kenako mwaika Abimeleki, mwana wa kapolo wake wamkazi,+ kukhala mfumu ya atsogoleri a ku Sekemu chifukwa chongoti ndi mchimwene wanu.
-