-
1 Mbiri 19:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Kenako Nahasi, mfumu ya Aamoni, anamwalira ndipo mwana wake anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+ 2 Zitatero, Davide anati: “Ndimusonyeza Hanuni mwana wa Nahasi chikondi chokhulupirika+ chifukwa bambo ake anandisonyeza chikondi chokhulupirika.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamutonthoze chifukwa cha imfa ya bambo ake. Koma atumiki a Davidewo atafika mʼdziko la Aamoni+ kuti atonthoze Hanuni, 3 akalonga a Aamoni anauza Hanuni kuti: “Kodi mukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthozani chifukwa cholemekeza bambo anu? Kodi iye sanatumize atumiki akewa kuti adzafufuze zokhudza mzindawu nʼcholinga choti adzaulande?” 4 Choncho Hanuni anatenga atumiki a Davide aja nʼkuwameta ndevu,+ kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza mʼmatako nʼkuwauza kuti azipita. 5 Davide atamva zomwe zinachitikira atumiki akewo, nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane nawo chifukwa atumiki akewo anali atachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ mpaka ndevu zanu zitakula, kenako mudzabwere.”
-