-
2 Samueli 10:1-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako mfumu ya Aamoni+ inamwalira, ndipo mwana wake Hanuni anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+ 2 Zitatero, Davide anati: “Ndimusonyeza Hanuni mwana wa Nahasi chikondi chokhulupirika ngati mmene bambo ake anandisonyezera chikondi chokhulupirika.” Choncho Davide anatumiza atumiki ake kuti akamutonthoze chifukwa cha imfa ya bambo ake. Koma atumiki a Davidewo atangofika mʼdziko la Aamoni, 3 akalonga a Aamoni anauza Hanuni mbuye wawo kuti: “Kodi mukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthozani chifukwa cholemekeza bambo anu? Kodi iye sanatumize atumiki akewa kuti adzafufuze zokhudza mzindawu nʼcholinga choti adzaulande?” 4 Choncho Hanuni anatenga atumiki a Davide aja nʼkuwameta ndevu mbali imodzi,+ kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza mʼmatako nʼkuwauza kuti azipita. 5 Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane nawo chifukwa atumiki akewo anali atachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ mpaka ndevu zanu zitakula, kenako mudzabwere.”
-