38 Mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema masana ndipo usiku pankakhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inkaona zimenezi mʼzigawo zonse za ulendo wawo.+
15 Pa tsiku limene anamanga chihema,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho. Koma kuyambira madzulo mpaka mʼmamawa, moto unkaoneka pamwamba pa chihemacho.+