Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Babulo, amene ndi waulemerero kwambiri* kuposa maufumu onse,+

      Chinthu chokongola chimene Akasidi amachinyadira,+

      Adzakhala ngati Sodomu ndi Gomora pa nthawi imene Mulungu anawononga mizindayi.+

  • Yesaya 14:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 mudzanena mwambi uwu wonyoza mfumu ya Babulo:

      “Amene ankagwiritsa ntchito anzake mokakamiza uja wawonongedwa!

      Kuponderezedwa kuja kwatha ndithu!+

  • Yesaya 45:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Izi ndi zimene Yehova akunena kwa wodzozedwa wake, kwa Koresi,+

      Amene wamugwira dzanja lake lamanja+

      Kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+

      Kuti alande zida zankhondo za mafumu,*

      Kuti amutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri,

      Kuti mageti adzakhale osatseka. Iye wamuuza kuti:

  • Yeremiya 51:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Babulo wagwa mwadzidzidzi ndipo wasweka.+

      Mulirireni mofuula.+

      Mʼpatseni mafuta a basamu kuti ululu wake uthe, mwina angachire.”

  • Danieli 5:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 PERESI, ufumu wanu wagawidwa ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+

  • Danieli 5:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa.+

  • Chivumbulutso 14:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kenako mngelo wachiwiri anamutsatira ndipo anati: “Wagwa! Babulo Wamkulu+ wagwa,+ amene anachititsa kuti mitundu yonse ya anthu imwe vinyo wa chilakolako cha* chiwerewere* chake!”+

  • Chivumbulutso 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo amene ziwanda zimakhala. Wakhalanso malo amene mzimu uliwonse wonyansa* komanso mbalame iliyonse yonyansa ndi imene imadedwa zimabisala.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena