Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 13:6-9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Mchimwene wanu, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi anu, kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mkazi wanu wokondedwa kapena mnzanu wapamtima, akayesa kukukopani mwachinsinsi pokuuzani kuti, ‘Tiyeni tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene inuyo kapena makolo anu sankaidziwa, 7 kaya ndi milungu ya anthu amene akuzungulirani, amene akukhala pafupi ndi inu kapena amene akukhala kutali ndi inu, kuchokera kumalekezero ena a dziko kukafika kumalekezero ena, 8 musavomere kuchita zimene akufunazo kapena kumumvera.+ Musamumvere chisoni kapena kumuchitira chifundo kapenanso kumuteteza. 9 Koma muzimupha ndithu.+ Dzanja lanu lizikhala loyamba kumʼponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+

  • Deuteronomo 32:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Iwo ankapereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+

      Anapereka nsembe kwa milungu imene sankaidziwa,

      Kwa milungu yatsopano yongobwera kumene,

      Komanso kwa milungu imene makolo anu sankaidziwa.

  • Yeremiya 19:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndidzachita zimenezi chifukwa iwo andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Pamalo ano iwo akupereka nsembe kwa milungu ina, imene iwowo, makolo awo komanso mafumu a Yuda sankaidziwa ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena