10 Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha,” akutero Yehova,
“Ndipo iwe Isiraeli usaope.+
Chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera kutali
Ndidzapulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza.
Sipadzakhala wowaopseza.+
11 Chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,” akutero Yehova.
“Ndidzawononga anthu a mitundu yonse yakumene ndinakubalalitsirani.+
Koma iweyo sindidzakuwononga.+
Ndidzakulanga pamlingo woyenera,
Ndipo sindidzakusiya osakupatsa chilango.”+