-
Aheberi 8:8-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Chifukwa Mulungu akuona kuti anthu akulakwitsa zinazake choncho iye akunena kuti: “‘Taonani! Masiku akubwera pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso ndi nyumba ya Yuda,’ akutero Yehova.* 9 ‘Koma silidzakhala pangano lofanana ndi limene ndinachita ndi makolo awo pa tsiku limene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse mʼdziko la Iguputo.+ Popeza sanapitirize kusunga pangano langalo, ndinasiya kuwasamalira,’ akutero Yehova.”*
10 “‘Pangano limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmaganizo mwawo ndiponso kuwalemba mʼmitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ akutero Yehova.*
11 ‘Munthu sadzaphunzitsanso nzika inzake kapena mʼbale wake kuti, “Mumʼdziwe Yehova!”* Chifukwa aliyense adzandidziwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. 12 Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+
-