Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 45:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mulungu ndi mpando wako wachifumu mpaka kalekale.+

      Ndodo ya ufumu wako ndi ndodo yachilungamo.+

  • Yesaya 9:6, 7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Chifukwa kwa ife kwabadwa mwana,+

      Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,

      Ndipo ulamuliro* udzakhala paphewa pake.+

      Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wamuyaya, Kalonga Wamtendere.

       7 Ulamuliro* wake udzafika kutali

      Ndipo mtendere sudzatha,+

      Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake

      Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba

      Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+

      Kuyambira panopa mpaka kalekale.

      Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.

  • Danieli 2:44
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 44 Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+

  • Luka 1:32, 33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wamʼmwambamwamba.+ Yehova* Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.+ 33 Iye adzalamulira monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya ndipo Ufumu wake sudzatha.”+

  • Chivumbulutso 11:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mngelo wa 7 analiza lipenga lake.+ Ndiyeno kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana akunena mokweza kuti: “Ufumu wa dziko wakhala Ufumu wa Ambuye wathu+ ndi wa Khristu wake+ ndipo iye adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena