18 Ndiye palinso mbewu zina zimene zimafesedwa paminga. Amenewa ndi anthu amene amamva mawu,+ 19 koma nkhawa za moyo+ wamʼnthawi ino, chinyengo champhamvu cha chuma+ komanso kulakalaka zinthu+ zina zonse, zimalowa mʼmitima yawo nʼkulepheretsa mawuwo kukula ndipo sabereka zipatso.