-
Mateyu 28:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nʼkunena kuti: “Moni azimayi!” Kenako iwo anafika pafupi nʼkugwira mapazi ake ndipo anamuweramira mpaka nkhope zawo pansi.
-
-
1 Akorinto 15:4-7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiponso kuti anaikidwa mʼmanda,+ kenako anaukitsidwa+ pa tsiku lachitatu,+ mogwirizana ndi Malemba.+ 5 Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa,*+ kenako kwa atumwi 12 aja.+ 6 Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi,+ ndipo ambiri a iwo tidakali nawo, koma ena anagona mu imfa. 7 Atatero anaonekera kwa Yakobo,+ kenako kwa atumwi onse.+
-