1 Akorinto 4:11, 12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Mpaka pano tikadali anjala,+ aludzu+ ndiponso ausiwa. Tikumenyedwabe,+ tikusowabe pokhala 12 ndipo tikugwirabe ntchito mwakhama ndi manja athu.+ Akamatinenera zachipongwe, timadalitsa+ ndipo akamatizunza, timapirira moleza mtima.+ Aefeso 4:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwira ntchito molimbikira. Azigwira ntchito yabwino ndi manja ake+ kuti azitha kupeza zinthu zimene angathe kugawana ndi munthu wosowa.+ 2 Atesalonika 3:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Ndipotu pamene tinali ndi inu, tinkakupatsani lamulo lakuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+ 1 Timoteyo 5:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a mʼbanja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.+
11 Mpaka pano tikadali anjala,+ aludzu+ ndiponso ausiwa. Tikumenyedwabe,+ tikusowabe pokhala 12 ndipo tikugwirabe ntchito mwakhama ndi manja athu.+ Akamatinenera zachipongwe, timadalitsa+ ndipo akamatizunza, timapirira moleza mtima.+
28 Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwira ntchito molimbikira. Azigwira ntchito yabwino ndi manja ake+ kuti azitha kupeza zinthu zimene angathe kugawana ndi munthu wosowa.+
10 Ndipotu pamene tinali ndi inu, tinkakupatsani lamulo lakuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.”+
8 Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a mʼbanja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.+