-
Aheberi 10:19-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Choncho abale, timalimba mtima kulowa mʼmalo oyera+ chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye ndi amene anatitsegulira njira imeneyi yomwe ndi yatsopano komanso yamoyo ndipo imadutsa katani yotchingira,+ imene ndi thupi lake. 21 Popeza tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyangʼanira nyumba ya Mulungu,+ 22 tiyeni tifike kwa Mulungu ndi mtima wonse komanso tili ndi chikhulupiriro chonse, chifukwa mitima yathu yayeretsedwa* kuti tisakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa mʼmadzi oyera.+
-