Miyambo 2:3-6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Komanso ukapempha kuti ukhale womvetsa zinthu+Ndi kuchonderera kuti ukhale wozindikira,+ 4 Ukapitiriza kuzifunafuna ngati siliva,+Ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+ 5 Udzamvetsa tanthauzo la kuopa Yehova+Ndipo udzamudziwadi Mulungu.+ 6 Chifukwa Yehova ndi amene amapereka nzeru.+Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka mʼkamwa mwake. Yohane 15:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Mukapitiriza kukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+ 1 Yohane 5:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndipotu ife sitikayikira*+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.+
3 Komanso ukapempha kuti ukhale womvetsa zinthu+Ndi kuchonderera kuti ukhale wozindikira,+ 4 Ukapitiriza kuzifunafuna ngati siliva,+Ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+ 5 Udzamvetsa tanthauzo la kuopa Yehova+Ndipo udzamudziwadi Mulungu.+ 6 Chifukwa Yehova ndi amene amapereka nzeru.+Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka mʼkamwa mwake.
7 Mukapitiriza kukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+
14 Ndipotu ife sitikayikira*+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.+