Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Lirani mofuula, chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi.

      Lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.+

  • Yeremiya 25:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Pa tsiku limenelo anthu amene adzaphedwe ndi Yehova adzachokera kumalekezero a dziko lapansi kukafika kumalekezero ena a dziko lapansi. Maliro awo sadzaliridwa, sadzawasonkhanitsa pamodzi kapena kuwaika mʼmanda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’

  • Ezekieli 30:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Tsikulo lili pafupi, inde tsiku la Yehova lili pafupi.+

      Tsikulo lidzakhala la mitambo+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+

  • Yoweli 1:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Tsikulo lidzakhala lochititsa mantha.

      Tsiku la Yehova lili pafupi.+

      Lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.

  • Yoweli 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Lizani lipenga mu Ziyoni.+

      Lengezani mʼphiri langa loyera kuti kukubwera nkhondo.

      Anthu onse okhala mʼdzikoli anjenjemere,

      Chifukwa tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi.

  • Yoweli 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova adzawalankhula asilikali ake mokweza+ chifukwa anthu amumsasa wake ndi ambiri.+

      Amene akukwaniritsa mawu ake ndi wamphamvu.

      Tsiku la Yehova ndi lalikulu komanso lochititsa mantha.+

      Ndani angalimbe pa tsiku limeneli?”+

  • Zefaniya 1:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Tsiku limenelo ndi tsiku la mkwiyo,+

      Tsiku la masautso ndi zowawa,+

      Tsiku lowononga ndi la mphepo yamkuntho,

      Tsiku la mdima wochititsa mantha,+

      Tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani,+

  • 2 Petulo 3:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka chonchi, ganizirani za mtundu wa anthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. 12 Muzichita zimenezi pamene mukuyembekezera komanso kukumbukira nthawi zonse* kubwera kwa tsiku la Yehova.*+ Pa tsikuli kumwamba kudzapsa ndi moto nʼkuwonongekeratu+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena