Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 10/8 tsamba 31
  • Mtengo wa Kusawona Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtengo wa Kusawona Mtima
  • Galamukani!—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Sitili Amatsenga Kapena Milungu
    Galamukani!—1994
  • Yehova Anadalitsa Kaimidwe Kawo Kolimba Kaamba ka Lamulo Lake
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kutetezera Ana Anu ku Mwazi
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Kodi Muli Wokonzekera Kuyang’anizana ndi Vuto la Kuchipatala Loyesa Chikhulupiriro?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 10/8 tsamba 31

Mtengo wa Kusawona Mtima

IMSO za Casey Lunsford zinali kulephera kugwira ntchito. Adokotala anayerekeza kuti mnyamata wa zaka zitatu ndi theka zakubadwa ameneyu angapulumuke kwa miyezi ina itatu kapena inayi yokha kusiyapo kokha ngati anadzalidwa imso. Makolo ake, omwe ndi Mboni za Yehova, anasankha moyanja kuchitidwa opareshoniyo; kwenikweni, atate ake a Casey anafunikira kupereka imso yawo imodzi kwa mnyamatayo.a Lamulo lokha limene iwo anapereka linali lakuti asagwiritsire ntchito mwazi—Mboni za Yehova zimakana kuthiridwa mwazi pamaziko a Malemba.—Onani Machitidwe 15:20.

Banja la Lunsford linakonzekera kuti maopareshoniwo akachitikire ku chipatala cha ku Texas chimene chinali ndi mbiri yabwino ya kudzala imso mwachipambano popanda kuthira mwazi. Koma chipatala chomwe chinali pamtunda wochepa kuchokera kunyumba ya a Lunsford mu California chinavomereza kudzala chiŵalocho popanda kuthira mwazi. Banja la Lunsford linasankha chipatala chapafupichi.

Mlungu umodzi opareshoniyo isanachitike, ogwira ntchito pachipatalapo ndi dokotala wopanga opareshoni yodzala ziŵaloyo anatsimikizira makolowo mobwerezabwereza kuti sipakafunikira kuthira mwazi kapena lamulo la ku khoti lovomereza winawake motsutsana ndi chitsutso cha makolowo. Komabe, makolowo atangovomereza kutumbulako, dokotala wotumbulayo anayamba kupanga makonzedwe opeza lamulo la khoti lokakamiza kuthira mwazi Casey. Iye anafikira pa kusintha wogwira ntchito yamayanjano amene anaumirira kuti makolowo anali ndi kuyenera kodziŵa ponena za lamulo la khoti la kuthira mwazi. Pa m’mawa wa opareshoniwo, akuluakulu a chipatalacho anatumiza chikalata chopempha lamulo la khoti kuthira mwazi Casey. Chikalatacho chinamveka ngati kuti Casey anali gone pa gome lotumbulira akukha mwazi, pamene, kwenikweni opareshoniyo inali isanayambe nkomwe! Ola limodzi pambuyo pa opareshoniyo, yomwe inachitidwa mwachipambano popanda kuthira mwazi, Casey anathiridwa mwazi.

Banja la Lunsford linazengetsa mlandu dokotala wotumbulayo ndi chipatalacho chifukwa cholakwira kuyenera kwawo kwalamulo ndi kunyenga, kufwamba, ndi kutsendereza maganizo kwadala, ndi kulakwira chidaliro. Pambuyo pa milungu inayi ya kuzenga mlanduwo, abwalowo anakambitsirana kwa masiku aŵiri ndi theka ndipo mlanduwo unagwera dokotala wotumbulayo ndi chipatalacho. Iwo analamulidwa kulipira a Lunsford chiwonkhetso cha $500,000.

Ngakhale kuti woweruza wozenga mlanduyo tsopano wachotsapo chiweruzo cha kulakwira kuyenera kwalamulo ndikulamula kuzenga mlandu kwatsopano kaamba ka chinyengo ndi milandu ina, abwalo 12 amenewo anakhutiritsidwa kuti kunama kwa chipatalacho ndi dokotalayo kunalungamitsidwa ndi mphotho ya $500,000. Aloya a banjalo asonyeza kuti adzafuna kuchilikiza chigamulo cha bwalolo mwakuchita apilu.

[Mawu a M’munsi]

a Mboni zimalingalira opareshoni yodzalidwa ziŵalo kukhala nkhani ya chosankha chaumwini mogwirizana ndi chikumbumtima cha munthuyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena