Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Nyimbo za Alternative Rock—Kodi Nzondiyenerera?
“Ndingathe kugwirizanitsa nyimbozo ndi mavuto osiyanasiyana ndi zochitika zimene achicheperefe timakumana nazo.”—George wazaka zakubadwa 15.a
“Zili pakati mpakati pa nyimbo za pop ndi za heavy metal.”—Dan wazaka zakubadwa 19.
“Nzatsopano. Nzamtundu wina. Si nyimbo zofala zimene zimatulutsidwa mu unyinji.”—Maria wazaka zakubadwa 17.
NYIMBO za alternative rock. Achichepere ambiri amakonda kuzimvetsera. Anthu ena achikulire zimawanyansa. Ndipo makolo ochuluka samazidziŵa nyimbozo.
Zoonadi, nkovuta kulongosola bwinobwino chimene chimatchedwa nyimbo za alternative rock. Poyamba, zinali nyimbo za achichepere amene anali kufuna kanthu ka mtundu wina, kosiyana ndi nyimbo zotchuka zofala zimene zimamvedwa pa wailesi. Ena amanena kuti zinayamba pamene nyumba za wailesi za m’makoleji zinayamba kuimba nyimbo za magulu ena osadziŵika—magulu oimba nyimbo amene anadzitama posagulitsa nyimbo zawo m’malonda a nyimbo. Mbadwo watsopano wa oimba unaipidwa ndi makampani aakulu ojambula nyimbo ndi njira zazikulu zamalonda, monga mavidiyo anyimbo. Ndiponso, analemba nkhani zimene sizimakhudzidwa kaŵirikaŵiri m’nyimbo za mu Top 40.
Mosiyana ndi nyimbo za heavy metal kapena za rap, nkovuta nthaŵi zina kudziŵa nyimbo za alternative rock kapena kuziika m’gulu lake. Ngakhale akatswiri a malonda a nyimbo samavomerezana pa nyimbo zimene kwenikweni zili za alternative rock. Nchifukwa chakuti, monga momwe dzina lakelo limasonyezera, zili ndi maliridwe, mkhalidwe, ndi malingaliro osiyanasiyana kwambiri. Mnyamata wina anati: “Nkovuta kwambiri kulongosola gulu lake. Zimaphatikizapo nyimbo zamakono zamitundumitundu.” Mnyamata wina anayesayesa kufotokoza motere: “Sizimakhala nthaŵi zonse nyimbo zaphokoso kapena zofeŵa, zothamanga kapena zosathamanga, zokwera kapena zotsika.” Wachichepere wina anavomerezadi kuti: “Sindikudziŵa bwino ngati ndinganene kuti ndimakonda nyimbo za alternative rock chifukwa chakuti sindikudziŵa bwino mtundu wake.”
Mulimonse mmene zilili, kutchuka kwa nyimbo za alternative rock kwakula kwakuti ambiri a akatswiri ake otchuka kwambiri tsopano akulingaliridwa kukhala mbali ya oimba nyimbo ofala. Ndiponso, makolo akuoneka kukhala osafunitsitsa kuziletsa monga momwe amachitira ndi heavy metal kapena mitundu ina ya rock yogonthetsa m’kutu. Ndithudi, makolo oŵerengeka ndiwo achita ngati amadziŵa za gulu kapena mitu ya maalabamu imene imatchedwa kuti alternative. Ngakhale zili choncho, inu mufunikira kusamala pa nyimbo zimenezi.
Kodi Nchiyani Chimene Chimakopa?
Mwachitsanzo, lingalirani chifukwa chimene achichepere ambiri amakopekera ndi nyimbo zimenezi. Kwa ambiri imeneyi yangokhala nkhani ya kuchita mogwirizana ndi mabwenzi awo. Zimaperekanso maziko ogwirizaniranapo a kukambitsirana kapena a machitachita, onga kusinthana matepi ndi ma CD.
Komabe, kwa achichepere ambiri, chimene chimawakopa ndicho maliridwe ndi uthenga wa nyimbo za alternative rock. Makamaka, achichepere ambiri amapeza kuti zochitika ndi malingaliro a olemba nyimbozo zimagwirizana ndi zimene zimawachitikira. Nkhani ya pachikuto ya m’magazini a Time pa nkhaniyi inafotokoza kuti: “Pamene kuli kwakuti nyimbo zotchuka kaŵirikaŵiri zimanena za chikondi, mawu a nyimbo za alternative nthaŵi zambiri amanena za kulimba mtima: kuthedwa nzeru, chilakolako cha kugonana, kusokonezeka. . . . Ngati muli m’zaka zanu za kusinkhuka kapena za m’ma 20, mwinamwake banja lanu limakhala litapyola m’chisudzulo. Nyimbo za alternative zakhala zamamvekedwe okhudza mtima, zikumatchula mwachindunji nkhani zimene zili zosathetsedwa za kusiyidwa ndi chisalungamo.” Chotero, disc jockey wa pakoleji wazaka zakubadwa 21 akunena kuti: “Ine ndi mabwenzi anga tinakopeka chifukwa chakuti mbadwo wathu susamala ndi zimene zikuchitika m’dziko. Palibe chimene tingayembekezere pamene timaliza sukulu.”
Achichepere ena achikristu nawonso akonda nyimbo za alternative rock. Mwanzeru, ochuluka apeŵa nyimbo zoipa, zachipanduko chachikulu, zachiwawa, kapena zachisembwere. Ngakhale zili choncho, ena a Akristu achichepere ameneŵa akayikira ponena za nyimbo zimene zimamveka ngati zabwinopo. Dan wachichepere anati: “Ena a oimba ndi amathanyula achimuna ndi achikazi odziŵika kapena ogwiritsira ntchito anamgoneka, ndipo mawu a nyimbo zawo amasonyeza moyo wawo.” Wachichepere wina wotchedwa Jack, anati: “Magulu ena ali ndi lingaliro lakuti palibe amene amasamala za iwo, za mavuto awo, kapena za mtsogolo mwa achichepere amakono, chotero amatchula zimenezi m’nyimbo zawo. Ambiri alibe chisonkhezero kapena chiyembekezo.”
Mawu a Chenjezo
Baibulo limatiuza kuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Pamenepo, simuyenera kudabwa kuti nyimbo zili imodzi ya njira zimene Satana amasokeretsera nazo achichepere. Nkhani zakumbuyoku m’magazini ano ndi anzakewo, Nsanja ya Olonda, mobwerezabwereza zasonyeza mfundo imeneyi.b Machenjezo amene aperekedwa ponena za nyimbo za heavy metal ndi za rap alinso oyenerera pa nyimbo za alternative rock. Monga momwe Baibulo limanenera, “wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.
Kwenikweni, si kwanzeru kutsata khamu pankhani ya nyimbo zimene mumakonda. Onani pulinsipulo ili la Baibulo, limene lingagwire ntchito pa kulola ena kukusankhirani: “Kodi simudziŵa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye?” (Aroma 6:16) Kwa Mkristu wachichepere, si nkhani ya chimene mabwenzi ake amavomereza koma chimene chili “chokondweretsa Ambuye.” (Aefeso 5:10) Ndiponso, kodi ndi achichepere otani amene amakopeka ndi nyimbo za alternative rock? Kodi ndiwo achichepere amene amaoneka ngati okondwa, anzeru, ndi okonda zinthu zauzimu? Kapena kodi zimaoneka kuti amene amazikonda makamaka ndiwo achichepere amene ali osakhutira, opanda chimwemwe, kapena ngakhale okwiya?
Zoonadi, achichepere ena amaumunthu ansangala ndi otsimikiza angakopekebe ndi nyimbo za alternative rock. Koma lingalirani izi: Akristu, achichepere ndi achikulire, ali ndi mtsogolo mwabwino kwambiri mmene mukuwayembekezera. (2 Petro 3:13) Mtumwi Paulo amatikumbutsa za chitsimikizo chakuti malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa, akumati: “Mulungu sakhoza kunama.” (Ahebri 6:18) Nangano, kodi mumapindulaponji ngati mwalola lingaliro losakondweretsa lonena zamtsogolo limene nyimbo zina za alternative rock zimatchula? Kodi kumwerekera m’nyimbo zimene zimafotokoza mantha, kuthedwa nzeru, ndi kupanda chiyembekezo kungafoole chikhulupiriro chanu? Ndiponso, kodi ndi chiyambukiro chotani chimene kuloŵetsa nyimbo zimenezo m’maganizo kosalekeza kungakhale nacho pa malingaliro a mtima wanu?
Muzisankha
Uku si kunena kuti nyimbo zonse zolembedwa kuti “alternative” zili zovulaza kapena zonyansa. Komano tiyeni tinene kuti mwazindikira kuti munthu wina anali kufuna kukupatsani poizoni. Ngakhale kuti simungaleke kudya, inu ndithudi mudzafuna kupenda mosamala chakudya chanu, sichoncho kodi? Kudziŵa kuti Satana akuyesa kuika poizoni m’maganizo mwanu ndi mtima kuyeneranso kukupangitsani kusamala ponena za nyimbo zimene mukusankha. Monga momwe Baibulo limanenera, “khutu liyesa mawu, monga m’kamwa mulaŵa chakudya.” (Yobu 34:3) M’malo mwa kutsatira khamu chimbulimbuli, yesani nyimbo zimene mumakonda.
Kodi mungachite zimenezo motani? Bokosi lotchedwa “Chitsogozo Chosankhira Nyimbo” lili ndi malingaliro ena othandiza amene mungayese. Ndiponso, yesani kufunsa makolo anu Achikristu zimene amaganiza ponena za nyimbo zanu. (Miyambo 4:1) Mungadabwe ndi mayankho awo! Zoonadi, makolo anu ngaakulu kwa inu. Motero, sangakonde nyimbo zanu. Koma ngati sakonda nyimbo zanu kufikira pa kuziona kukhala zonyansa, zoluluza, kapena zangozi, kodi muyenera kunyalanyaza zimene anganene? Baibulo limati: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kulandira malangizo ambiri.”—Miyambo 1:5, NW.
Talingalirani za mmene nyimbozo zimakuyambukirirani. Kodi zimakupangitsani kukwiya, kufuna kupanduka, kapena kupsinjika mtima? Ngati ndi choncho, zimenezi zili zizindikiro zimene simuyenera kuzinyalanyaza! Bwanji osapeza nyimbo zimene zimakumasulani thupi kapena kukutonthozani kapena kukusangalatsani?
Mikhalidwe ya nyimbo ikusintha nthaŵi zonse. Posapita nthaŵi, mtundu wina wa nyimbo umadzakhala nyimbo zatsopano zotchuka. Komano musapitire limodzi ndi funde limeneli la kusintha. Khalani waluntha ndi wosankha pankhani ya nyimbo. Tsimikizirani kuti zimene mukumvetsera zili zabwino ndi zomangirira. (Afilipi 4:8) Pamenepo nyimbo zidzakhala mbali yopindulitsa ndi yosangalatsa ya moyo wanu!
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa.
b Onani nkhani zakuti “Achichepere Akufunsa Kuti . . . ” zotuluka mu makope a Galamukani! a February 8, March 8, ndi April 8, 1993. Ndiponso onani nkhani yakuti “Chenjerani ndi Nyimbo Zosayenera!,” m’kope la Nsanja ya Olonda la April 15, 1993.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
“Pamene kuli kwakuti nyimbo zotchuka kaŵirikaŵiri zimanena za chikondi, mawu a nyimbo za alternative nthaŵi zambiri amanena za kulimba mtima: kuthedwa nzeru, chilakolako cha kugonana, kusokonezeka.”—magazini a Time
[Bokosi patsamba 30]
Chitsogozo Chosankhira Nyimbo
◆ Pendani chikuto cha alabamu. Kaŵirikaŵiri chimenechi chimakudziŵitsani zambiri ponena za nyimbo ndi oziimba ake. Samalani ndi zikuto za alabamu zimene zikusonyeza chiwawa, zizindikiro zauchiŵanda, mavalidwe ndi makonzedwe a tsitsi achilendo, kapena umaliseche.
◆ Lingalirani za uthenga wa m’mawu a nyimbo. Zimenezi zimadziŵikitsa malingaliro ndi moyo wa oziimba. Kodi akufuna kuti mulandire malingaliro otani?
◆ Maliridwe a nyimbo yonse amasonyeza mkhalidwe ndi malingaliro amene oziimba ake akufuna kuti mukhale nawo—chisoni, chimwemwe, chipongwe, kudzutsa chilakolako cha kugonana, bata, kapena kuthedwa nzeru.
◆ Lingalirani za anthu ake onse amene amakopeka ndi gulu la nyimbozo. Kodi mungakonde kudziŵika pamodzi ndi gulu la anthu limenelo ndi maganizo awo?
[Chithunzi patsamba 30]
Achichepere ambiri amaganiza kuti mawu a m’nyimbo zamakono amawakhudza