Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 3/8 tsamba 3
  • Pamene Kunalibe Upandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Kunalibe Upandu
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Upandu Unayambira Kuti?
  • Nchifukwa Ninji Pali Upandu Wochulukira Chotero?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kulimbana ndi Upandu Kukulephereka
    Galamukani!—1998
  • Mapeto a Upandu Ali Pafupi Tsopano!
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kuyesayesa Kuthetsa Upandu
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 3/8 tsamba 3

Pamene Kunalibe Upandu

KODI mungalingalire dziko lopanda upandu? Mwinamwake simungatero ngati mwaŵerengapo nkhani za m’manyuzipepala zonga imene inatuluka m’nyuzipepala yofalitsidwa tsiku ndi tsiku ya ku Germany yotchedwa Süddeutsche Zeitung imene inati: “Akatswiri a zaupandu akunena za kufalikira kwatsopano kwa upandu. Amakamba za malodza ndipo amapereka chithunzi chakuti tsoka layandikira.”

Mogwirizana ndi zimene ananena anthu zikwizikwi a ku Ulaya omwe anafunsidwa mu 1995, pafupifupi aliyense amaopa kuchitiridwa mwaupandu. Ku Germany, Netherlands, Poland, Russia, ndi ku United Kingdom, upandu ndiwo chinthu chachikulu chomwe anthu amaopa kwambiri. Kuopa upandu kunali pamalo achiŵiri ku Denmark, Finland, ndi Switzerland ndipo pamalo achitatu ku France, Greece, ndi Italy. Mwa maiko 12 amene anafufuzidwa, ndi dziko la Spain lokha limene silinanene za upandu kukhala chimodzi cha zinthu zikuluzikulu zitatu zochititsa mantha.

Upandu wakula kwambiri ku Eastern Europe m’zaka zisanu ndi ziŵiri zapitazi. M’maiko angapo a amenewa, kuwonjezerekako kwakhala pakati pa 50 ndi 100 peresenti, pamene m’maiko ena kumatha kuchokera pa 193 kufika pa 401 peresenti!

Komatu, panthaŵi ina panalibe upandu padziko. Kodi ndi liti limenelo, ndipo kodi dziko limenelo linawonongeka bwanji?

Kodi Upandu Unayambira Kuti?

Upandu, wotanthauzidwa kukhala “kuswa lamulo kodziŵikiratu,” unayambira m’dziko la mizimu. Anthu oyambawo, Adamu ndi Hava, sanalengedwe ndi malingaliro opandukira, ndiponso sanali oyambitsa enieni a upanda pakati pa anthu. Mwana wangwiro wauzimu wa Mulungu analola maganizo oipa kuzika mizu mumtima mwake, pamene anawakulitsa, anabala upandu. Ameneyo ndiye amene anaipitsa dziko lopanda upandu loyambalo. Mwa kuswa lamulo la Mulungu, iye anadzipanga kukhala mpandu, ndipo m’Baibulo amadziŵika kuti Satana Mdyerekezi.—Yakobo 1:13-15; Chivumbulutso 12:9.

Atayamba kutsutsa Mulungu m’miyamba mosaonekamo, Satana anatsimikiza kukafalitsa njira zake zaupandu kwa anthu padziko. Nkhani ya m’Baibulo ya m’mene Mdyerekezi anachitira zimenezi njaifupi ndi yosavuta, koma yomveka bwino. (Genesis, machaputala 2-4) Adamu ndi Hava, atasokeretsedwa ndi wopanduka wauzimu wamachenjerayu, anakana kutsatira malamulo a Mulungu. Mwa kusamvera Mulungu iwo anakhala opanduka. Pambuyo pake, mosakayikira iwo anadzidzimuka ndi mantha pamene mwana wawo woyamba, Kaini, anafikira polanda mbale wake Abele chinthu chake cha mtengo wapatali kwambiri, moyo weniweniwo!

Choncho, mwa anthu anayi oyamba kukhala padziko, atatu anapanduka. Motero Adamu, Hava, ndi Kaini anataya mwaŵi wawo wakukhala m’dziko lopanda upandu. Pambuyo panthaŵi yonseyi, kodi nchifukwa chiyani tsopano tingatsimikizire kuti dziko lotero lili pafupi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena