Mphamvu ya Nyimbo
“Nyimbo pazokha, chifukwa cha chikoka chake, zingathe kukhazika pansi mtima wosakhazikika, ndiponso kutonthoza maganizo ovutika.”
ANALEMBA motero William Congreve pafupifupi zaka 300 zapitazo m’buku lake lotchedwa Hymn to Harmony. Zaka mazana ambiri m’mbuyo mwake, mabuku akale a Agiriki ankanena kuti “kuphunzitsa mwakugwiritsa ntchito nyimbo ili njira yamphamvu koposa zonse, chifukwa chakuti chuni komanso mavume zimakhudza mtima kwambiri.”
Makolo ena aona kuti zimenezi n’zoona poona achinyamata awo akuyamba kukhala osakondwa ndi osagwirizanika akakhala kuti amamvetsera kaŵirikaŵiri nyimbo zamtundu wa heavy metal. Zinalinso chimodzimodzi m’ma 1930 ndi 1940 ku Germany pamene anthu a Chipani cha Nazi anagwiritsa ntchito nyimbo zokoka mtima zoimbidwa poguba kuti zithandize kukonzekeretsa makamu kuti amvetsere zoyankhula zachikoka za Adolf Hitler.
Mosakayikira, nyimbo zingakhudze maganizo ndi mitima ndipo zingagwiritsidwe ntchito kuti zikhudze anthu m’njira yabwino kapena yoipa. Mwachitsanzo, ana akamamvetsera nyimbo za mitundu ina yake akuti zimawachititsa kuti akhale anzeru ndiponso amaganizo abwino. Ngakhale achibwibwi nthaŵi zina angaimbe nyimbo imene mawu ake sangathe kuwatchula.
Nthaŵi zina, mmene nyimbo zimakhudzira odwala matenda a ubongo amene amaumitsa ziwalo m’modabwitsa kwabasi, anatero Anthony Storr m’buku lake lotchedwa Music and the Mind. Storr akupereka chitsanzo cha wodwala wina wamkazi: “Atauma miyendo chifukwa cha matenda a Parkinson, ankalephera ngakhale kusuntha mpaka atakumbukira nyimbo zimene anali kuimba ali wamng’ono. Nyimbozo zimam’patsa mphamvu zotha kuyendanso nthaŵi yomweyo.”
Chifukwa Chodera Nkhaŵa
Choncho zikuoneka kuti mphamvu ya nyimbo ili ndi mapindu ake. Komabe, choopsa n’chakuti anthu oipa kapena aumbombo angathe kugwiritsa ntchito mphamvu ya nyimbo kukhala chida choopsa. Kufufuza kwina kwasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa khalidwe loipa ndi mitundu ina ya nyimbo.
Povomereza zimenezi, magazini ya Psychology of Women Quarterly inati: “Pali umboni wosonyeza kuti kuonerera mafilimu a nyimbo za rock n’chimodzimodzi ndi kuonerera zamaliseche chifukwa chakuti amuna amene anasonyezedwa mafilimu a chiwawa a nyimbo za rock anaonetsa kusamva chisoni ndiponso kudana ndi akazi pamene amuna omwe anaonetsedwa mafilimu a nyimbo za rock zopanda chiwawa sanatero.”
Si amuna okha amene amatero. Ngakhalenso akazi zingawakhudze. Nkhani yomweyo ikuwonjezera kuti: “Amuna ndi akazi omwe, angayambe kuvomereza uthenga wonyoza umene nyimbozi zimapereka wonena kuti akazi ngopanda ntchito.”
Nyuzipepala yotchedwa Sex Roles povomereza mfundo imeneyi, ikuti: “Kufufuza kwaposachedwapa . . .kwasonyeza kuti kukulira m’banja losalongosoka ndiponso kuonera mavidiyo a nyimbo kumachititsa atsikana ambiri kukhala ndi khalidwe losaopa kuchita zachiwerewere.” Mawu a chiwawa choopsa a m’nyimbo zina za rap komanso mawu ake olaula zinachititsa woweruza wina wa ku United States kunena kuti nyimbo za rap zomwe zili pachimbale chinachake “n’zolaula malingana ndi chikhalidwe cha anthu.”
Kodi woweruzayo ananyanya? Kutalitali! Nyuzipepala yotchedwa Adolescence inafikira ponena kuti “ana komanso makolo asimba za kusokonezeka kwakukulu kumene achinyamata omwe amamvera nyimbo za heavy metal ndi za rap amakhala nako m’moyo.” Kusokonezeka kumeneku kumayendera limodzi ndi “khalidwe lachiwawa ndi kuwononga zinthu” komanso kulephera sukulu.
N’zoonadi kuti kugwirizana kwa mitundu inayake ya nyimbo ndi chiwerewere, kudzipha, ndi khalidwe loipa, n’kotsimikizika. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti nyimbo zonse n’zoipa motero? Ŵerengani nkhani zotsatirazi kuti mumve yankho pa nkhaniyi.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Nyimbo zingathe kukhudza mitima ndi maganizo m’njira yabwino kapenanso yoipa