Ngati Mungakhoze Kukhala ndi Moyo Kosatha Kodi Mungasankhe Kutero?
Mungathedi kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi, monga momwe broshali likusonyezera bwino lomwe. Chifuno cha Mulungu cha mikhalidwe imeneyo chidzakwaniritsidwadi! Koma muyenera kusankha kukhala ndi moyo kosatha.
Yesu Kristu anaphunzitsa kuti chosankha chimenecho chiyenera kuzikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu. Broshali laperekedwa kuti likuthandizeni kupeza chidziŵitso chimenecho. Chithandizo chowonjezereka chingalandiridwe kuchokera kwa Mboni za Yehova. Izo zidzakondwa kukuchezerani pa nthaŵi ndi malo oyenera kwa inu. Ndipo ngati mungakonde kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere, mungatidziŵitse zimenezi mwa kulembera ku Watch Tower, ku keyala yoyenera pansipa.