Zamkatimu
Mboni Za Yehova
ANTHU AKE
Mutu 1 mpaka 4
A Mboni za Yehova akupezeka m’mayiko oposa 240 ndipo anthu amenewa akuchokera m’mitundu yonse ndiponso ndi a zikhalidwe zosiyanasiyana. N’chiyani chachititsa kuti anthu osiyanasiyanawo azigwirizana? Kodi a Mboni za Yehova ndi anthu otani?
ZIMENE TIMACHITA
Mutu 5 mpaka 14
Timadziwika kwambiri chifukwa cha ntchito yathu yolalikira. Komanso timasonkhana m’Nyumba za Ufumu kuti tiphunzire Baibulo ndi kulambira Mulungu. Kodi misonkhanoyo imachitika bwanji, ndipo ndani amene amaloledwa kubwera ku Nyumba ya Ufumu?
GULU LATHU
Mutu 15 mpaka 28
Gulu lathu ndi gulu lachipembedzo limene likupezeka m’mayiko osiyanasiyana, ndipo cholinga chake si kupeza ndalama. Anthu a m’gululi amatumikira Mulungu modzipereka kwambiri. Kodi gululi limayenda bwanji, amalitsogolera ndani, ndipo limapeza bwanji ndalama zake? Kodi gulu limeneli likuchitadi chifuniro cha Yehova masiku ano?