Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 4/1 tsamba 5-6
  • Mkazi Wachigololo ndi “Mafumu a Dziko Lapansi”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkazi Wachigololo ndi “Mafumu a Dziko Lapansi”
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mkazi Wachigololo wa Umbombo
  • Chipembedzo Chonyenga Chikupita ku Chiwonongeko Chake!
    Galamukani!—1996
  • Chifukwa Chake Chipembedzo cha Dziko Chidzatha
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kuweruza Hule la Makhalidwe Oipa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Kulamulira kwa Atsogoleri Achipembedzo—Kodi Iko Kuli Yankho?
    Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1989
w89 4/1 tsamba 5-6

Mkazi Wachigololo ndi “Mafumu a Dziko Lapansi”

MBIRI yakale ya Chikristu cha Dziko iri yodzala ndi zitsanzo za chisonkhezero cha kugulitsa ndi kuloŵerera m’mabwalo a mphamvu. Tiyeni tilingalire zoŵerengeka za izo. Charlemagne (724-814 C.E.) anali wolamulira yemwe anawona mapindu a kugwirizana ndi chipembedzo ndi kukhala ndi dalitso la mtsogoleri wa chipembedzo wa Tchalitchi cha Chikatolika.

The New Encyclopædia Britannica ikulongosola kuti papa anadzoza Charlemagne, atate wake, ndi mbale wake, m’kukhazikitsa ufumu watsopano pambuyo pakuti banja lolamulira lakale linali ‘linakankhidwira kumbali.’ Kenaka iyo ikuwonjezera kuti: “Kugwirizana kwa ndale zadziko pakati pa maFrank [anthu a Charlemagne] ndi Papa molimbana ndi a Lombard kunatsimikiziridwa pa chochitika chimodzimodzicho. . . . Charles [yemwe anadzakhala Charlemagne] kumayambiriroka anadziŵitsa kugwirizana kwathithithi pakati pa mphamvu ya dziko ndi tchalitchi.”

M’chaka cha 800 C.E., Papa Leo III, “anagamulapo kupanga Charles wolamulira” wa Ufumu wa Chiroma wa Kumadzulo, kumuveka iye chisoti chachifumu pa Misa ya Krisimasi mu St. Peter’s, Roma.

Mkazi Wachigololo wa Umbombo

Koma mkazi wachigololo amafunikira malipiro. Nchiyani chomwe Charlemagne akanalipira oimira a Babulo, Roma? “Charles . . . anabwereza, mu St. Peter’s Basilica, lonjezo la atate wake la kusamutsira ku ulamuliro wa papa mbali zazikulu za Italy.” Magwero amodzimodziwo akuwonjezera kuti: “M’chipembedzo chake cholinganizidwa mwa ndale zadziko, ufumuwo ndi tchalitchicho zinakula kukhala gawo la maphunziro ndi uzimu.”

Chitsanzo china cha chisonkhezero champhamvu cha chipembedzo m’kulamulira chiri Cardinal Wolsey wa ku England (1475-1530). Britannica ikulongosola kuti iye anali “cardinal ndi mwamuna wa boma yemwe analamulira boma la Mfumu Henry VIII wa ku England. . . . Mu December 1515 Wolsey anakhala mbuye wolamulira wa England. . . . Wolsey anagwiritsira ntchito mphamvu zake zokulira za kudziko ndi za ulaliki kuwunjika chuma chachiŵiri kokha ku chija cha Mfumu.” Kugwiritsira ntchito kalankhulidwe kophiphiritsira ka Chivumbulutso, kuchita chigololo kwapamwamba kumafunanso kulipiridwa kwapamwamba.

Chitsanzo china choipitsitsa cha chisonkhezero cha chipembedzo m’nkhani za Boma chinali cardinal ndi wolamulira wa ku Richelieu (1585-1642), yemwe anasonyeza mphamvu zazikulu mu France ndiponso anasonkhanitsa chuma chomwe chinali “chopambanitsa ngakhale pa miyezo ya msinkhu,” inalongosola tero Britannica.

Richelieu analoŵedwa m’malo ndi cardinal wina, Jules Mazarin (1602-61), yemwe anatumikira monga mtumiki woyamba wa France mkati mwa kulamulira kwa Mfumu Louis XIV. Ngakhale kuti sanali wansembe woikidwa, iye anapangidwa kukhala cardinal mu 1641 ndi Papa Urban VIII. Cardinal Mazarin nayenso anali wokhumbira chuma. Bukhu la nazonselo likulongosola kuti: “Adani a Mazarin anamutonza iye chifukwa cha umbombo wake. Iye anali atasonkhanitsa ndalama za boma ndi ndalama za tchalitchi ndipo nthaŵi zina anasokoneza ndalama zobwera zachifumu ndi ndalama zake.”

Mu nthaŵi zamakono chipembedzo chonyenga chidakawunjikabe chuma ndi kuyesera kusonkhezera ndipo, ngati nkotheka, kulamulira mbale za ndale zadziko. Chitsanzo chimodzi chowonekera chiri gulu lachinsinsi la Chikatolika la Opus Dei (Latin, Ntchito ya Mulungu), limene pa nthaŵi ino likusangalala ndi chiyanjo cha papa ndipo, mogwirizana ndi mkonzi Lawrence Lader, liri “kotheratu lodzipereka ku kutsutsa chikomyunizimu ndi magulu a ndale zadziko oukira ulamuliro.” Ilo liri ndi lamulo la kutenga ophunzira apamwamba achichepere Achikatolika kupyolera mu masukulu ake apamwamba ndi mayuniversiti ndipo kenaka kupangitsa anthu ake kuikidwa m’malo apamwamba a chisonkhezero ndi kulamulira m’boma, chuma, ndi olemba nkhani. Mu Spain anali ndi nyengo ya kusonyeza kutchuka kokulira pansi pa wolamulira wotsendereza ufulu wa Chikatolika wa chiFascist Franco pamene, mkati mwa nyengo ina, 10 za ziwalo za bungwe lolangiza lake 19 anali oyanjana ndi gulu lotchuka la Opus Dei.a

Mu United States, alengezi a pa TV amadziŵidwa kaamba ka chiwonetsero chawo cha chuma ndi kakhalidwe ka moyo kolemera. Atsogoleri ena a chipembedzo a Chiprotesitanti modzikuza aloŵa m’bwalo la ndale zadziko ndipo afikira ngakhale pa kupikisana ku uprezidenti. Mosakaikira ponena za icho, ngakhale kuti ali mu mkhalidwe wakugwa, mkazi wachigololo wamkuluyo, pansi pa kudzisanduliza kumodzi kapena kunzake, akusangalalabe ndi misampha ndi chikondwerero cha mphamvu ndipo amayesera kulamulira chirombocho.​—Chibvumbulutso 17:4.

Koma bwanji ponena za dzina la mkazi wachigololoyo, Babulo Wamkulu? Ndimotani mmene chimenecho chimathandizira kutsimikizira chizindikiritso cha mkazi wophiphiritsiridwa mu Chibvumbulutso?

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka pa Opus Dei ndi kudziloŵetsamo kwa tchalitchi m’ndale zadziko, onani mabukhu akuti Hot Money and the Politics of Debt, lolembedwa ndi R. T. Naylor, ndi Politics, Power, and the Church, lolembedwa ndi L. Lader.

[Zithunzi patsamba 6]

Cardinals Wolsey, Mazarin, ndi Richelieu anawunjika chuma pamene anali kutumikira Boma

[Mawu a Chithunzi]

Zithunzi: Culver Pictures

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena