Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 3/1 tsamba 5-7
  • Kodi Zolinganiza za Chisungiko cha Padziko Lonse Zidzapambana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Zolinganiza za Chisungiko cha Padziko Lonse Zidzapambana?
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Limanenanji?
  • Chisungiko Chenicheni pa Dziko Lapansi
  • Mtendere Weniweni ndi Chisungiko Zayandikira!
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kuyang’ana Kuposa pa “Mtendere ndi Chisungiko” Zaumunthu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Lingaliro Labaibulo la mtendere ndi Chisungiko
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 3/1 tsamba 5-7

Kodi Zolinganiza za Chisungiko cha Padziko Lonse Zidzapambana?

“NKHONDO Yoputana ndi Mawu, imene yavutitsa dziko lonse kwa zoposa zaka 40, ikuwoneka ngati yatha mwachithandizo cha Mulungu,” anatero magazini a One World a WCC (World Council of Churches). “Zochitika zazikulu Kum’maŵa kwa Yuropu ndi Pakati pake . . . zikuwoneka ngati zikupereka chizindikiro chabwino cha mtendere ndi chisungiko mu Yuropu ndi padziko lonse,” anawonjezera tero John Pobee, wolemba nkhani za tchalitchi cha Angilikani, wa Programme on Theological Education ya WCC.

Oimira a WCC sindiwo okha amene amaloŵetsa Mulungu m’zolinganiza za munthu za chisungiko cha padziko lonse. Mu April 1991, nkhondo ya ku Persian Gulf itangotha, Papa John Paul anatumiza uthenga kwa Javier Pérez de Cuéllar, amene anali mlembi wamkulu wa UN panthaŵiyo, m’mene ananena kuti: “Abishopu a Matchalitchi a Katolika a ku Middle East ndi Kumadzulo ali ndi chidaliro m’ntchito ya Mitundu Yogwirizana . . . Akhulupirira kuti, kupyolera mwa Mitundu Yogwirizana ndi ziungwe zake za akatswiri, anthu amene nkhondo yaposachedwapa yawaloŵetsa muumphaŵi wadzawoneni adzapeza chithandizo cha padziko lonse ndi chigwirizano.”

Ndiponso, Vatican linali limodzi la Maiko 35 amene analinganiza ndi kusaina zonse ziŵiri pangano la Helsinki Agreement la mu 1975 ndi Stockholm Document ya mu 1986. Mitundu Yogwirizana italengeza 1986 kukhala “Chaka cha Mtendere wa Padziko Lonse,” papa analabadira mwakuitanira oimira zipembedzo zazikulu za dziko kuchikondwerero cha “Tsiku la Mapemphero a Mtendere wa Dziko Lonse.” Mu October 1986, oimira zipembedzo za Chibuda, Chihindu, Chisilamu, Chishinto, Angilikani, Lutheran, Greek Orthodox, Chiyuda ndi zipembedzo zina anasonkhana ku Assisi, Italiya, namasinthana kumapempherera mtendere wa dziko lonse.

Zaka zingapo pambuyo pake, muulaliki umene anapereka ku Roma, Akibishopu wa Canterbury wa Angilikani anakumbukira chochitika chotchulidwa pamwambapa. Iye anati: “Ku Assisi, tinawona kuti Bishopu wa Roma [papa] anaitanitsa Matchalitchi Achikristu. Tinapempherera pamodzi, kulankhulana ndi kuchitira zinthu pamodzi kaamba ka mtendere ndi ubwino wa anthu . . . Pachochitikacho chopempherera mtendere wa dziko lonse ndinadzimva kuti ndinali pamaso pa Mulungu amene anati ‘Tawonani ndikupanga chinthu chatsopano.’”

Zipembedzo zina nazonso, ngakhale kuti sizinaliko ku Assisi, nzotsimikiza kuti zolinganiza za munthu za chisungiko cha padziko lonse zidzapambana. Nkhani yolembedwa ndi mkonzi wa Die Kerkbode, magazini alamulo a Dutch Reformed Church ya South Africa, inati: “Tikuwona kusintha kuloŵa m’dongosolo ladziko latsopano. Zimene zinawoneka ngati zosatheka zaka zingapo zapitazo zikuchitika m’maso mwathu. Kuyanjana kumene kukuchitika pamlingo waukulu padziko pakati pa Soviet Union ndi maiko a Kumadzulo kuli ndi tanthauzo lalikulu m’zigawozo. Kumbali yathu ino ya dziko, zipani zotsutsana nthaŵi zonse ndi adani osayanjanitsika akulankhuzana, ndipo chikhumbo cha ‘mtendere’ chikuwoneka kulikonse . . . Malinga ndi lingaliro Lachikristu, zoyesayesa zonse zodzetsera mtendere pakati pa anthu ziyenera kulandiridwa. Tingapempherere mtendere m’nthaŵi yathu.”

Kodi Mulungu akawadalitsa makonzedwe a munthu a chisungiko cha mitundu yonse?

Kodi Baibulo Limanenanji?

Ponena za kudalira pazoyesayesa za anthu, Baibulo limapereka chenjezo lachindunji lakuti: ‘Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitaika.’ (Salmo 146:3, 4) Zochitika zamakono zolinga kumtendere zingawoneke kukhala zolimbikitsa. Koma tifunikira kuwona zinthu mmene ziliridi. Mphamvu za anthu nzochepa. Kaŵirikaŵiri, zochitika nzazikulu kuwaposa. Sakhoza kuzindikira kwenikweni zisonkhezero zobisika, mphamvu zosawoneka, zimene zimadodometsa zolinganiza zawo zabwino.

Zaka mazana asanu ndi aŵiri nthaŵi ya Yesu isanafike, m’masiku a mneneri Yesaya, atsogoleri Achiyuda ankalinganiza chisungiko kupyolera mwa mapangano amitundu yonse ndi maiko apafupi mwanjira yofanana ndi zimene zikuchitika lerolino. M’masikuwo nawonso, atsogoleri achipembedzo anachirikiza zimene atsogoleri andale ankachita. Koma Yesaya anachenjeza kuti: ‘Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mawu, koma sadzachitika.’ (Yesaya 8:10) Upo wawo unalephera momvetsa chisoni. Kodi chinthu chofananacho chingachitike lerolino?

Inde, chingaterodi, pakuti kupyolera mwa mneneri mmodzimodziyo, Mulungu analengeza kuti Ali ndi njira Yake yodzetsera chisungiko padziko lapansi. Sichidzapyolera m’gulu lirilonse la anthu, koma mwa mbadwa ya mfumu Davide wa Israyeli. (Yesaya 9:6, 7) Woloŵa wa Mfumu Davide ameneyo ndiye Yesu Kristu, amene, pofunsidwa ndi Pontiyo Pilato, anavomera kuti anali Mfumu koma nati: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi.” (Yohane 18:36; Luka 1:32) Zowona, Ufumu wa Yesu ukakhala wakumwamba. Ndipo uwo wokha​—osati Mitundu Yogwirizana kapena boma lirilonse landale padziko lapansi​—ukadzetsa chisungiko chodalirika, ndi chachikhalire padziko lapansi.​—Danieli 2:44.

Yesu Kristu ananeneratu kuti Ufumu wake ukayamba kulamulira kumwamba panthaŵi imene kudzakhala “nkhondo ndi mbiri za nkhondo,” ndi ‘mtundu umodzi wa anthu ukaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.’ Kukwaniritsidwa kwa ulosiwo kumasonyeza 1914 kukhala nthaŵi pamene zochitikazo zinayamba ndipo kumadziŵikitsa zaka zoyambira panthaŵiyo kukhala “mapeto a dongosolo la zinthu.”(NW).​—Mateyu 24:3, 6-8.

Kodi zimenezi zitanthauzanji? Zitanthauza kuti nthaŵi yotsalako ya dongosolo ladziko lamakono njochepa, ndipo idzatha posachedwapa. Kodi zimenezo nzodetsa nkhaŵa kapena nzomvetsa chisoni? Ndithudi ayi, makamaka titakumbukira nkhanza, chisalungamo, chitsenderezo, nkhondo, ndi mavuto onse amene afalikira m’dongosolo ili la zinthu. Kudzakhaladi kodzetsa mpumulo kulamuliridwa ndi wolamulira amene Mawu a Mulungu, Baibulo, amamfotokoza kuti: ‘Mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziŵa ndi wakuwopa Yehova.’​—Yesaya 11:2.

Chisungiko Chenicheni pa Dziko Lapansi

Kunena zowona, sipadzakhala chisungiko chenicheni padziko lapansi, kufikira pamene ulosi wotsatira wa Yesaya udzakwaniritsidwa padziko lonse mu Ufumu wa Mulungu: “Ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima.” (Yesaya 65:17) Mosasamala kanthu ndi unyinji wa mapemphero operekedwa ndi atsogoleri achipembedzo kupempherera dzikoli, zolinganiza za anthu za chisungiko cha padziko lonse sizingatenge malo a njira ya Mulungu yodzetsera mtendere ndi chisungiko.

Chisungiko chachikhalire cha padziko lonse chimene Ufumu wa Mulungu udzadzetsa chidzakhala chaulemerero. Naŵa ena a malongosoledwe opezeka m’Baibulo: ‘Ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake; ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.’​—Mika 4:3, 4.

Chisungiko cholonjezedwa ndi Mulungu chokha ndicho chachikhalire ndi chodalirika. Chifukwa chake, mmalo moika chidaliro chanu mwa zinduna, bwanji osangoika chidaliro chanu mwa iye? Mutatero mudzazindikira chowonadi cha mawu a wamasalmo akuti: ‘Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chiri pa Yehova, Mulungu wake, amene Analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m’mwemo; ndiye wakusunga chowonadi kosatha.’​—Salmo 146:5, 6.

[Bokosi patsamba 7]

Tchalitchi cha Katolika ndi Ndale Zadziko Lonse

“Ngakhale kuti Yesu ananena kuti ufumu wake ‘sunali wa dziko lino lapansi,’ atsogoleri achipembedzo m’malo apamwamba ndi apapa monga chiungwe akhala ndi phande lokulira m’kulimbana kwa zandale kwa padziko lonse ndi kwa mtundu wawo kuyambira nthaŵi ya Constantine.” ​—The Catholic Church in World Politics, lolembedwa ndi Profesa Eric Hanson wa pa Yunivesiti ya Jesuit Santa Clara.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena