Simudzagwiritsidwa Mwala
OKWATIRANA ena ku Philippines anayenda masiku aŵiri kuti akafikeko. Anakwera matola kwa mtunda wa makilomita 70, atanyamula ana aang’ono aŵiri kudutsa nkhalango zodzaza ndi misundu ndi mitsinje yosefukira ndi mvula yamkuntho. Koma analimba mtima.
Akazi aŵiri a ku Zaire anayenda kwa mtunda woposa makilomita 500, akumathera masiku 14 pamsewu, kotero kuti akapezekeko. Ndiponso ku Zaire komweko, mwamuna wokalamba wa zaka 70 anatchova njinga yake kwa mtunda wa makilomita 260 kuti akapezekeko. Sanaletsedwe ndi mtundawo kapena zopinga. Chinthu chofunika chinali kusaphonya.
Kodi onsewo amapita kuti? Ku umodzi wa misonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova yolinganizidwa m’maiko awo. Ndipo mosasamala kanthu za kuvuta kwa kayendedwe, onse analingalira kuti zoyesayesa zawo zinali zopindulitsa.
Kodi mwapanga kale makonzedwe akukapezekapo pa Msonkhano Wachigawo wa 1992 wa “Onyamula Kuunika”? Mwinamwake, simudzafunikira kupanga kuyesayesa kwakukulu konga kumene kunapangidwa ndi anthu okhulupirikawo kuti mukapezekepo. Koma ngakhale ngati pakakhala zopinga zina, tikufulumizani kusauphonya.
Programu yabwino koposa ndi yothandiza yakonzedwa. Ngati mumasangalala ndi mayanjano Achikristu ndipo mumafuna kudziŵa mmene mungapezere mtendere weniweni, zimene ziri kutsogolo, kapena mmene mungachitire bwino chifuniro cha Mulungu, tikulonjezani kuti simudzagwiritsidwa mwala. Mboni iriyonse m’dera lanu ingakuuzeni malo ndi nthaŵi imene msonkhano wakufupi kwambiri ndi kwanu udzachitidwa.