Zamkatimu
December 15, 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
MAGAZINI YOPHUNZIRA
FEBRUARY 3-9, 2014
“Musafulumire Kugwedezeka pa Maganizo Anu”
TSAMBA 6 • NYIMBO: 65, 59
FEBRUARY 10-16, 2014
Kodi Mungapereke Chiyani pa Ntchito ya Ufumu?
TSAMBA 11 • NYIMBO: 40, 75
FEBRUARY 17-23, 2014
‘Tsikuli Lidzakhala Chikumbutso Chanu’
TSAMBA 17 • NYIMBO: 109, 18
FEBRUARY 24, 2014–MARCH 2, 2014
“Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
TSAMBA 22 • NYIMBO: 99, 8
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ “Musafulumire Kugwedezeka pa Maganizo Anu”
Sitiyenera kukhulupirira zinthu zabodza kapena zimene sizinafotokozedwe m’Baibulo. Mabuku a 1 ndi 2 Atesalonika amapereka machenjezo a pa nthawi yake.
▪ Kodi Mungapereke Chiyani pa Ntchito ya Ufumu?
Tiyenera kudzipereka kwambiri kuti tithandize pa ntchito ya Ufumu. M’nkhaniyi tiona zimene tingaphunzire pa nsembe zimene Aisiraeli ankapereka. Tionanso zitsanzo za anthu ambiri masiku ano amene akudzipereka kwambiri kuti athandize pa ntchito ya Ufumu.
▪ ‘Tsikuli Lidzakhala Chikumbutso Chanu’
▪ “Muzichita Zimenezi Pondikumbukira”
Akhristu oona amachita Chikumbutso cha imfa ya Yesu pa nyengo yofanana ndi imene Ayuda amachita Pasika. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa za Pasika? Kodi timadziwa bwanji deti la Chikumbutso? Nanga mwambowu ndi wofunika bwanji kwa ife?
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI
3 Yehova Anawateteza Pamene Ankazemba M’mapiri
PATSAMBA LOYAMBA: Akulalikira kumapiri a Matobo. Kumalo ena m’derali kumakhala miyala yosanjikizana. Zimakhala zovuta kuti abale ndi alongo akalalikire kumeneko. Koma iwo amayesetsa kulalikira kumapiriwa, omwe ali m’chigawo cha Matabeleland ku Zimbabwe
ZIMBABWE
KULI ANTHU OKWANA:
12,759,565
KULI OFALITSA OKWANA:
40,034
MAPHUNZIRO A BAIBULO:
90,894
Anthu a ku Zimbabwe amakonda kuwerenga mabuku athu. Pa avereji, Mkhristu aliyense amagawira magazini 16 pa mwezi