Zamkatimu
June 15, 2015
© 2015 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI YOPHUNZIRA
JULY 27, 2015–AUGUST 2, 2015
Khristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu
TSAMBA 3 • NYIMBO: 14, 109
AUGUST 3-9, 2015
TSAMBA 8 • NYIMBO: 84, 99
AUGUST 10-16, 2015
TSAMBA 13 • NYIMBO: 83, 57
AUGUST 17-23, 2015
Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo I
TSAMBA 20 • NYIMBO: 138 (nyimbo yatsopano yakuti Inu Ndinu Yehova), 89
AUGUST 24-30, 2015
Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo 2
TSAMBA 25 • NYIMBO: 22, 68
NKHANI ZOPHUNZIRA
▪ Khristu Ndiye Mphamvu ya Mulungu
▪ Yesu Amakonda Anthu
Nkhanizi zikufotokoza zozizwitsa za Yesu ndipo zikusonyeza zimene tingachite potsanzira mtima wake wopatsa komanso wachifundo. Zikufotokozanso makhalidwe ena abwino a Yesu. Nkhanizi zitithandizanso kudziwa kuti posachedwapa tidzaona zozizwitsa zikuchitika padziko lonse.
▪ N’zotheka Kukhalabe Oyera
M’dzikoli, kukhala oyera si chinthu chapafupi. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zimene zingatithandize kupewa maganizo oipa n’kumatsatira mfundo zapamwamba za Yehova. Zinthu zake ndi kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova, kutsatira malangizo a m’Baibulo ndiponso kulola kuti Akhristu anzathu atithandize.
▪ Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo I
▪ Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo 2
Akhristu saloweza pemphero la Ambuye kuti azilinena mobwerezabwereza. Koma tikhoza kuphunzira zambiri pa mfundo za m’pempheroli. Nkhanizi zitithandiza kuti tizichita zinthu mogwirizana ndi pemphero limeneli.
M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI
PATSAMBA LOYAMBA: A Mboni akwera maboti kuti akalalikire pazilumba za kumpoto chakumadzulo kwa Panama. Ayenera kulalikira anthu ena m’chilankhulo cha Chinobele
PANAMA
KULI ANTHU
3,931,000
KULI OFALITSA
16,217
KULI APAINIYA OKHAZIKIKA
2,534
Ku Panama kuli mipingo 309 ndiponso apainiya apadera oposa 180. Kuli ofalitsa pafupifupi 1,100 m’mipingo 35 yachinobele ndiponso timagulu 15. Kulinso ofalitsa pafupifupi 600 m’mipingo 16 yachinenero chamanja cha ku Panama ndiponso timagulu 6