Kupindula ndi Nkhani Zapoyera Zokonzedwanso
1 Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova yafotokozedwa molondola m’mawu a Miyambo 4:18 kuti: “Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kucha, kunkabe kuŵala kufikira usana woti mbe.”
2 Mogwirizana ndi zimenezi, mpingo Wachikristu ukupitirizabe kulandira kumveketsedwa bwino kwa zinthu kwa panthaŵi yake ndi chidziŵitso chatsopano pa ziphunzitso za Baibulo. (Mat. 24:45-47) Inu mosakayikira mungasimbe zitsanzo za zimenezi zimene mwaona chiyambire pamene munayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova. Misonkhano ya mpingo, kuphatikizapo nkhani zapoyera, zimatithandiza kuyendera limodzi ndi kuunika kowonjezereka kwa choonadi.
3 Maautilaini Okonzedwanso: Posachedwapa, Sosaite yakonzanso maautilaini ambiri a nkhani zapoyera. Mfundo zatsopano zaloŵetsedwamo, ndipo mfundo zina zofunika zamveketsedwa bwino. Ngati mpingo uti ulandire phindu lokwanira la chidziŵitso chatsopano chimenechi, abale amene amapereka nkhani ayenera kugwiritsira ntchito maautilaini atsopano ameneŵa okha.
4 Polingalira za kupindula koposa ndi nkhani zapoyerazi, sinkhasinkhani pa mitu ya nkhani zoti ziperekedwezo. Musanafike pa Msonkhano Wapoyera, yesayesani kukumbukira chidziŵitso chaposachedwapa chateokrase pankhaniyo. Ndiyeno, pamene mukumvetsera, yembekezerani kufotokozedwa kwa chidziŵitso chimenechi. Khalani watcheru ndi njira zilizonse zatsopano zoperekera choonadi chimenechi mtsogolo. Zimenezi zidzatsimikizira kuti mudzapeza phindu lalikulu koposa kuchokera m’nkhani zokonzedwanso zimenezi.
5 Nkhani Zapoyera Ziyenera Kukhala Zopatsa Chidziŵitso Ndiponso Zosonkhezera Omvetsera: Pamene Yesu analankhula mawu, anafika mitima ya omvetsera ake. Pamapeto a Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu, nkhani yapoyera yotchuka kwambiriyo imene inaperekedwapo, monga momwe Mateyu 7:28 akusimbira: “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.”
6 Pokumbukira chitsanzo cha Yesu, mabungwe a akulu ayenera kugwiritsira ntchito luntha povomereza okamba nkhani zapoyera atsopano, akumagaŵira nkhanizo kokha kwa abale amene ali aphunzitsi abwino, amene adzamamatira mosamalitsa pa autilaini ya Sosaite, ndi amene ali okhoza kuchititsa omvetsera kutchera khutu. Abale amene amagaŵiridwa mwaŵi wa kupereka nkhani zapoyera ayenera kupitirizabe kuyesayesa kuwongolera luso lawo la kulankhula, akumalandira uphungu ndi malingaliro alionse operekedwa ndi akulu.
7 Monga momwe kunanenedweratu pa Yesaya 65:13, 14, kulemera kwauzimu kwa anthu a Mulungu kukupitirizabe kukhala koonekera kwambiri. Makonzedwe a nkhani zapoyera ali imodzi ya njira zambiri zimene ‘Yehova akutiphunzitsira.’—Yes. 54:13.