Kusonyeza Mogwira Mtima Buku la Kukhala Ndi Moyo Kosatha
1 Yesu anali katswiri pa kugwiritsira ntchito kwake mawu oyamba. Iye anadziŵa chonena kuti adzutse chikondwerero. Nthaŵi ina anayambitsa makambitsirano ndi mkazi Wachisamariya mwa kungompempha madzi akumwa. Zimenezi mwamsanga zinachititsa chidwi mkaziyo chifukwa chakuti ‘Ayuda sanayenderane ndi Asamariya.’ Makambitsirano omwe anatsatirapo potsirizira pake anathandiza iye ndi ena ambiri kukhala okhulupirira. (Yohane 4:7-9, 41) Tingatengepo phunziro pa chitsanzo chimenechi.
2 Pokonzekera kugaŵira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, dzifunseni kuti, ‘Kodi nchiyani chimene chili nkhaŵa za anthu zimene zilipo m’gawo lathu? Kodi nchiyani chimene chidzakondweretsa wachinyamata, munthu wachikulire, mwamuna, kapena mkazi?’ Mungakonzekere mawu oyamba angapo ndi kulinganiza kugwiritsira ntchito amene akuoneka kukhala oyenerera kwambiri mkhalidwewo.
3 Popeza kuti kuwonongeka kwa moyo wa banja kumadetsa nkhaŵa ambiri, munganene kuti:
◼ “Zovuta za tsiku ndi tsiku zaika mavuto aakulu pa mabanja lerolino. Kodi iwo angapeze kuti chithandizo? [Yembekezerani yankho.] Baibulo lingakhale chithandizo chenicheni kwa ife. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16, 17.] Malemba amapereka zitsogozo zopindulitsa zimene zingathandize mabanja kukhalapobe. Onani zimene zanenedwa m’ndime 3 patsamba 238 la bukuli lakuti, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.” Ŵerengani ndime 3, ndi kuligaŵira.
4 Ngati mukugwiritsira ntchito nkhani ya panyuzi ya kumaloko, munganene kuti:
◼ “Kodi mwamva nkhani ya panyuzi yakuti [tchulani nkhani yokhudza anthu akumaloko]? Kodi munaganiza chiyani pankhaniyi? [Yembekezerani yankho.] Zimenezi zimachititsa munthu kudabwa kuti kodi dzikoli lidzafika kuti, sichoncho kodi? Baibulo linaneneratu zinthu zoterozo kukhala umboni wakuti tikukhala m’masiku otsiriza.” Ndiyeno kambitsiranani mfundo za m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha, masamba 150-3.
5 Ambiri akudera nkhaŵa za kukula kwa vuto la upandu. Mugagwiritsire ntchito mawu oyamba oyambirira pansi pa mutu wakuti “Upandu/Chisungiko” patsamba 14 la buku la “Kukambitsirana.”
◼ “Tikukambitsirana ndi anthu za chisungiko cha munthu. Muno mwathu muli upandu wambiri, ndipo umayambukira miyoyo yathu. Kodi muganiza kuti chimene chingachitidwe nchiyani kuti anthu monga inu ndi ine tisamawope m’misewu usiku?” Mungaŵerenge Salmo 37:10, 11 ndi kusonyeza madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretsa, mwa kugwiritsira ntchito masamba 156-8 a buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.
6 Ngati mungafune kafikidwe kosavuta, mungagwiritsire ntchito mawu oyamba ofanana ndi achinayi patsamba 12 m’buku la “Kukambitsirana”:
◼ “Tikulimbikitsa anansi athu kulingalira za lonjezo la mtsogolo mwaulemerero limene Baibulo limatipatsa. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Kodi zimenezi zikumveka kukhala zabwino kwa inu? [Yembekezerani yankho.] Mutu 19 wa buku limeneli umasonyeza madalitso ena amene anthu omvera adzakhala nawo mu Ufumu wa Mulungu.” Gaŵirani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha.
7 Kukonzekera mawu oyamba ogwira mtima kungakuthandizeni kufika pamitima ya awo akumva njala ya chilungamo.—Mat. 5:6.