Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/95 tsamba 4
  • Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Maulaliki a Utumiki wa Kumunda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Mmene Mungagawire Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Tsatirani Okondwerera Onse kuti Mupindulitse Ena
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Chidziŵitso Chochokera kwa Mulungu Chimayankha Mafunso Ambiri
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 2/95 tsamba 4

Bwererani Kumene Munapeza Wokondwerera

1 Pogwira ntchito ku nyumba ndi nyumba, kaŵirikaŵiri nthaŵi yocheza ndi munthu wokondwerera imachepa. Nthaŵi zambiri ntchito yeniyeni yophunzitsa imachitidwa pamene tipanga maulendo obwereza ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. (Mateyu 28:19, 20) Kuti tiphunzitse mogwira mtima paulendo wobwereza, timafunikira kupendanso zimene tinakambitsirana paulendo woyamba ndiyeno kukonzekera makambitsirano enanso.

2 Ngati munakambitsirana za kusakhazikika kwa makonzedwe a banja, mungagwiritsire ntchito mfundo za m’mutu 29 wa buku la “Kukhala ndi Moyo Kosatha.” Munganene kuti:

◼ “Tsiku lija tinakambitsirana za nzeru ya kulondola uphungu wa Baibulo kotero kuti tikhale ndi moyo wa banja wachimwemwe. Kodi muganiza kuti nchiyani chimene chili njira yogwirizanitsira mabanja lerolino?” Yembekezerani yankho. Tembenukirani pa ndime 27 patsamba 247, ndi kuŵerenga Akolose 3:12-14. Nenani mawu owonjezera osonyeza mmene chikondi chenicheni chingagwirizanitsire mabanja pamodzi. Fotokozani mmene kuphunzira buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha mwa njira yadongosolo kungathandizire kuthetsa mavuto.

3 Ngati paulendo wanu woyamba munakambitsirana za mikhalidwe ya dziko yomaipiraipira, mungapitirize zimenezo mwa kunena kuti:

◼ “Ndikhulupirira mudzavomereza kuti pakufunikira kusintha kwakukulu ngati titi tikhale pamtendere. Baibulo limasonyeza kuti Satana ndiye wochitisa mavuto athu wamkulu. Ambiri amadabwa chifukwa chake Mulungu wamlola iye kupitiriza kwa nthaŵi yaitali yotero. Kodi muganiza bwanji?” Yembekezerani yankho. Tsegulani patsamba 20, ndime 14 ndi 15, m’buku lakuti Kukhala ndi Moyo Kosatha, ndipo fotokozani chifukwa chake Satana sanawonongedwebe. Ndiyeno ŵerengani pa Aroma 16:20, pamene pakusonyeza zimene tingayembekezere mtsogolo posachedwapa.

4 Ngati munakambitsirana za madalitso amene adzakhalapo mu ulamuliro wa Ufumu, paulendo wanu wobwereza, munganene kuti:

◼ “Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso odabwitsa padziko lapansi ndi kwa mtundu wa anthu. Madalitso ameneŵa akusonyezedwa bwino pano pa chithunzithunzi pamasamba 12 ndi 13. Kodi mukuonapo chiyani chimene chakukondweretsani? [Yembekezerani yankho.] Tangolingalirani mmene kudzakhalira kukhala m’dziko longa ili.” Ŵerengani ndime 12. Ngati akukondwera nazo, funsani funso la pandime 13, ndipo kambitsiranani yankho. Tchulani kuti mutu umenewu umayankha mafunso owonjezereka onena za madalitso a Ufumu ndi kuti mudzakhala wokondwa kukambitsirana zimenezo mukadzabweranso.

5 Mungathe kuyambitsa phunziro mwa kunena kuti:

◼ “Anthu ambiri apeza mayankho a mafunso awo pa Baibulo mwa kugwiritsira ntchito buku ili.” Tsegulani pa mpambo wa zamkatimu, ndipo funsani kuti: “Kodi ndi nkhani iti pano imene mungakonde kwambiri kumva?” Yembekezerani yankho, tsegulani pa mutu umene angakondewo, ndi kuŵerenga ndime yoyamba. Fotokozani mmene mafunsowo m’munsi mwa tsamba lililonse amasonyezera mfundo zazikulu m’ndime iliyonse. Perekani chitsanzo mwa kukambitsirana ndime ina imodzi kapena ziŵiri, ndiyeno pangani makonzedwe akudzafikanso.

6 Kubwerera kwa amene anakondwera ndi buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha kumasonyeza chikhumbo chathu cha kutsiriza utumiki wathu mokwanira. (2 Tim. 4:5) Tingathe kuthandiza otimvetsera kuti akalimirire moyo wosatha.—Yohane 17:3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena