Kulitsani Chikondwerero m’Buku La Kukhala Ndi Moyo Kosatha
1 Pamene tifika pa nyumba zawo, kaŵirikaŵiri timapeza kuti anthu ngotanganitsidwa ndi “malabadiro a dziko lapansi.” (Marko 4:19) Timayang’anizana ndi chitokoso cha kuwakopa ndi ulaliki wosonkhezera maganizo. Poyamba, anthu ochuluka angakhale ndi chikondwerero chaching’ono pa zimene titi tinene. Ngati tingathe kunena kanthu kena kamene kadzakhudza miyoyo yawo, tingakhale okhoza kusonkhezera chikondwerero chokulirapo cha uthenga wa Ufumu. Mfungulo ya kuyambitsa makambitsirano ndiyo kusankha mfundo zokopa zokambitsirana za m’buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha. Kodi munganenenji?
2 Mungagwiritsire ntchito kafikidwe aka:
◼ “Ngati mukanakhala ndi mphamvu, kodi ndi mavuto osautsa a m’tsiku lathu ati amene mukanathetsa? [Yembekezerani yankho, ndipo ngati nkoyenera, vomerezani kuti anthu ambiri amalingalira mofananamo.] Kufikira pano, atsogoleri adziko akuonekera kukhala atachita zochepa m’kupeza zothetsera mavuto osautsa a lerolino. Koma pali Uyo amene angathe kutero ndi amene adzathetsa mavuto onse amene akukantha mtundu wa anthu. Chonde onani zimene zanenedwa pa Salmo 145:16. [Ŵerengani lembalo, ndipo tembenukirani pa zithunzithunzi zimene zili patsamba 11-13.] Ndime 14 patsamba 14 imabutsa funso limene tangokambitsirana kumeneli ndipo imapitiriza kufunsa kuti: ‘Koma kodi zimenezi zidzachitika liti?’” Fotokozani kuti bukulo lidzayankha funso limenelo ndipo gaŵirani bukulo.
3 Kapena munganene motere:
◼ “Inu mwinamwake mumadziŵa mkhalidwe wa kupanda pake umene umadza pa kutayikiridwa ndi wokondedwa mu imfa. Mwachionekere munali wachisoni ndi wosoŵeratu chochita. Mungakhale mutasinkhasinkha mafunso awa: [Ŵerengani mafunso a m’ndime 1 patsamba 76.] Kodi sikungakhale kotonthoza kukhala ndi mayankho a mafunso ameneŵa? Kungakulimbikitseni kudziŵa kuti Baibulo limapereka chiyembekezo chotsimikizirika kaamba ka awo amene afa. [Ŵerengani Yohane 5:28, 29.] Buku ili limatithandiza kuzindikira mkhalidwe wa akufa ndi chiyembekezo chimene chilipo kaamba ka mtsogolo.” Kambani naye mwachidule pa mitu 8 ndi 20.
4 Pali kuthekera kwabwino kwakuti mudzakhala ndi mipata ya kuchitira umboni mwamwaŵi. Ngati ndi choncho, inu munganene motere m’mawu a inu mwini:
◼ “Masiku ano dziko nlodzala ndi mavuto, ndipo mosakayikira nanunso mumakhudzidwa nawo. Mwachisoni, kukuonekera kuti anthu opanda chifukwa ndiwo amene amavutika koposa. Kodi muganiza kuti Mulungu adzathetsadi kuvutika konseku? [Yembekezerani yankho.] Ndiloleni ndikusonyezeni zimene Mulungu akulonjeza kuchitira awo amene amamtumikira. [Ŵerengani Salmo 37:40 ndiyeno tsegulani buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha patsamba 99.] Buku ili limafotokoza chifukwa chake Mulungu walolera kuipa ndi mmene adzakuthetsera.”
5 Ngati ndinu wofalitsa wachichepere, mungagwiritsire ntchito ulaliki wozikidwa pa zithunzithunzi zopezeka pamasamba 156-8. Mungayambe mwa kufunsa kuti:
◼ “Kodi mungakonde kukhala ndi moyo m’dziko longa ili? [Yembekezerani yankho.] Chilichonse cha zithunzithunzi zokongola zimenezi nchozikidwa pa lonjezo lonenedwa m’Mawu a Mulungu, Baibulo. [Sonyezani mavesi a Malemba.] Buku limeneli lingakuthandizeni kuphunzira zambiri ponena za lonjezo la Mulungu la kupanga dziko lapansi lonse kukhala paradaiso. Lili ndi chidziŵitso chopulumutsa moyo ndipo nkoyenera kupatula nthaŵi ya kuliŵerenga.”—Yoh. 17:3.
6 Pogaŵira bukulo, yalani maziko a ulendo wobwereza mwa kufunsa mafunso odzakambitsirana mtsogolo.