Nanunso Mungakhale ndi Zokumana Nazo Zabwino!
Ofalitsa ena nthaŵi zonse amaoneka kukhala ali ndi zokumana nazo zokondweretsa ndi zolimbikitsa zoti asimbe ponena za munthu wina wabwino amene anamfikira kapena ulendo wobwereza umene wawapatsa chimwemwe chambiri. Kaŵirikaŵiri zokumana nazo zabwino sizimangodza zokha. Zambiri zimachitika chifukwa cha kuyesayesa kwakhama kosalekeza. Sizimangochitikira ofalitsa amene ali osadodoma kapena okhoza kwambiri okha.
Nazi zina za zinthu zimene zaonedwa mwa awo amene amapambana kwambiri pa zimenezi: (1) Amakhala ndi phande mu utumiki wakumunda nthaŵi zonse, kaŵirikaŵiri kangapo mlungu uliwonse, kumene kumawapatsa mipata yambiri ya kuonana ndi anthu okondwerera; (2) amasunga mkhalidwe wabwino wamaganizo kulinga kwa eninyumba, samawaganizira kuti iwo sadzamva; (3) ali okonda kucheza ndi ena, akumasonyeza chikondi chenicheni kwa amene amamvetsera; (4) iwo ali akhama ndi osatopa pa kubwerera kwa anthu amene anawafikira ndiponso pa nyumba zimene panalibe anthu; ndipo (5) ali ndi chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
Mutapenda zochita zanu, mwinamwake inu mungathe kuona mmene mungakhalire ndi zokumana nazo zambiri zokondweretsa zimenezo zimene zimachititsa utumiki kukhala wobala zipatso ndi wokhutiritsa kwambiri.