Mawu a Mulungu Amapereka Chitsogozo
1 “Tikukhala ndi moyo m’dziko lokhala ndi zovuta zochulukitsitsa ndi mayankho oŵerengeka kwambiri. Mamiliyoni ochuluka nthaŵi ndi nthaŵi amakhala ndi njala. Ziŵerengero zomawonjezereka zikukhala zomwerekera ndi mankhwala oledzeretsa. Mabanja owonjezerekawonjezereka akusweka. Chiwawa cha kugonana kwapachibale ndi m’banja zili zakaŵirikaŵiri m’nkhani. Mpweya umene timapuma ndi madzi amene timamwa zikuipitsidwa pang’onopang’ono. Patsopano lino, owonjezerekawonjezereka a ife akukhala mikhole yaupandu.”
2 Limayamba motero buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Mawu ake oyamba ngoyenerera kwambiri lerolino kuposa ndi mmene analili pamene bukulo linafalitsidwa zaka zisanu ndi ziŵiri zapitazo. Anthu afunikira kudziŵa kuti Mawu a Mulungu amapereka chitsogozo ndipo amapereka njira zothetsera mavuto onse amene akuwavutitsa. Tidzayesetsa kuthandiza anthu mu December mwa kuwagaŵira New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Komabe, kungosiyira munthu mabuku sikupereka chitsimikiziro chakuti adzalandira chitsogozo cha Mulungu. Tiyenera kupanga maulendo obwereza ndi chifuno cha kuyambitsa phunziro la Baibulo. Tidzathandizidwadi ngati tiyesetsa motero. (Mat. 28:19, 20) Nawa maulaliki ena amene mungagwiritsire ntchito:
3 Ngati mwakumana ndi wachikulire, mungayese mafikidwe awa:
◼ “Kodi ndingafunse: Pamene munali wachichepere, kodi anthu m’chitaganya ankachitirana motani? [Yembekezerani yankho.] Zinthu zasintha kwambiri tsopano, si choncho kodi? Kodi muganiza kuti chachititsa kusinthaku nchiyani? [Yembekezerani yankho.] Kwenikweni zimene tikuonazi zikukwaniritsa ulosi wina wa m’Baibulo. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:1-5.] Kusiyapo kufotokoza dziko molongosoka monga momwe lilili lerolino, Baibulo limalonjeza dziko labwino kwambiri lomwe layandikira patsogolopa. Pachifukwa chimenecho tikulimbikitsa aliyense kuŵerenga Baibulo. Chinenero chimene chili mu New World Translation nchosavuta kumva.” Fotokozani kuti lalembedwa m’Chingelezi chamakono, chomwe chapangitsa Baibulo kukhala lomvetsetseka. Sonyezani buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, ndi kusonyeza mutu 10, umene umafotokoza ulosi winanso umene taona ukukwaniritsidwa. Gaŵirani Baibulolo ndi buku.
4 Pamene mubwerera kwa wachikulire amene munagaŵira Baibulo ndi buku, munganene kuti:
◼ “Pamene tinakambitsirana poyamba, tinavomerezana kuti m’njira zambiri chitaganya chamakono chasintha kukhala choipa kwambiri poyerekezera ndi mmene moyo unalili zaka zingapo zapitazo. Komabe, ndabweranso kudzakusonyezani kuti Baibulo limafotokoza zinthu zimene tingayembekeze m’dziko labwino kwambiri la mtsogolo. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Kudziŵa kuti awa ndi Mawu a Mulungu kuyenera kutilimbikitsa kuona zinanso zimene Baibulo limanena.” Tsegulani buku la Mawu a Mulungu pa mutu 14, ndi kuŵerenga ndime 3-4. Pemphani kuchititsa phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.
5 Ngati mwayambitsa makambitsirano ndi wachichepere, munganene kuti:
◼ “Ndikufuna kukufunsa funso: Monga wachichepere, kodi uona kuti uli ndi chifukwa chimene ungakhalire ndi chiyembekezo chabwino ponena za mtsogolo? Kodi kwa iwe mtsogolo mukuoneka bwanji? [Yembekezerani yankho.] Mwamwaŵi, pali chifukwa chabwino chokhalira ndi chiyembekezo chabwino ponena za mtsogolo. [Ŵerengani Salmo 37:10, 11.] Popeza kuti anthu ali ndi malingaliro osiyanasiyana ponena za Baibulo ndi zimene limanena, tafalitsa buku ili, Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Ona zifukwa zoŵerengera Baibulo zimene limapereka. [Ŵerengani ndime 16-17 pamasamba 10-11.] Titatsimikizira kuti zimene Baibulo limanena nzoona, timakhala ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha mtsogolo.” Gaŵirani bukulo pachopereka chamasiku onse.
6 Pamene mwabwerera kukaona wachichepere amene analandira buku la “Mawu a Mulungu,” mungayambe mwa kunena kuti:
◼ “Ndinayamikira kudziŵa nkhaŵa yako ponena za mtsogolo. Kumbukira kuti ndinakusonyeza lemba la m’Baibulo limene limatilonjeza mtsogolo mwachimwemwe ndi mosungika. Nali linanso. [Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.] Buku limene ndinakusiyira limapereka umboni wokhutiritsa wakuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, osati a munthu ayi. Choonadi chimenecho chimatanthauza zochuluka. Taona zimenezo pano. [Ŵerengani ndime 1-2 pamasamba 184-5.] Ngati ukufuna, ndingakonde kuphunzira nawe Baibulo kwaulere.” Ngati wavomera phunziro, mfunseni munthuyo ngati ali ndi kope la Baibulo. Ngati alibe, gaŵirani New World Translation.
7 Munthu amene sadziŵa koyang’ana kaamba ka chitsogozo cholimbana ndi mavuto a moyo angamvetsere ndi kafikidwe aka:
◼ “Tikukhala panthaŵi imene pafupifupi aliyense ali ndi mavuto aakulu. Ambiri amapita kwa aphungu amitundu yonse kaamba ka chitsogozo. Ena amapita ku maula kuti awathandize. Kodi mukuganiza kuti ndi kuti kumene tingapeze uphungu wabwino umene udzatithandizadi? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limatchula choonadi chofunika chimene tonsefe tiyenera kuchidziŵa.” Ŵerengani Yeremiya 10:23. Tsegulani Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? patsamba 187, ndi kuŵerenga ndime 9. “Bukuli lidzakuthandizani kuona mmene mavuto athu onse adzachotsedwerapo mu Ufumu wa Mulungu. Kodi mungakonde kuliŵerenga?” Gaŵirani bukulo.
8 Ngati paulendo woyamba munalankhula za kusoŵa chitsogozo kwa anthu, mungapitirize makambitsiranowo paulendo wobwereza mwa kunena kuti:
◼ “Pamene tinakumana poyamba, tinavomerezana kuti tifunikira chitsogozo cha Mulungu ngati tikufuna kulimbana mwachipambano ndi mavuto a moyo. Ponena za zimenezo, ndiyesa mudzakondwera ndi mawu omaliza a m’buku limene ndinakusiyirani. [Ŵerengani ndime 12-13 patsamba 189 m’buku la Mawu a Mulungu.] Ndili wachimwemwe kukugaŵirani kosi yaulere yapanyumba yophunzira Baibulo, ndipo ndili wokonzeka kukusonyezani tsopano lino.”
9 Yehova adzadalitsa zoyesayesa zathu pamene tithandiza achikulire ndi achichepere omwe kuti adziŵe kufunika kwa Mawu a Mulungu ndi chitsogozo chake m’moyo wathu.—Sal. 119:105.