Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa Septemer 1 kufikira December 22, 1997. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Sipakanakhala kuipa Mulungu akanapanda kupatsa zolengedwa zaluntha ufulu wa kudzisankhira. [rs-CN tsa. 185 ndime 1]
2. Pa Luka 22:30, “mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli” akutanthauza zomwezonso zotchulidwa pa Mateyu 19:28, pamene akutanthauza kuti si ansembe aang’ono a Yesu obadwa ndi mzimu okha komanso anthu ena onse. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w87-CN 3/1 tsa. 30 ndime 10; tsa. 31 ndime 12.]
3. Chifukwa chimene ophunzira a Yesu anadabwira pomuona akulankhula ndi mkazi wachisamariya chinali chakuti anali wachisembwere. (Yohane 4:27) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 7/15 tsa. 15 ndime 1-2.]
4. Mawu akuti “poyamba” pa Yohane 6:64 akusonyeza kuti Yesu anadziŵa panthaŵi imene anasankha Yudasi kukhala mtumwi kuti ndi yemweyo anali wodzampereka. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani it-2 tsa. 129 ndime 4-6.]
5. Kukhala ndi moyo wabanja lachikristu ndiko chabe kungosiya chisembwere ndi kulembetsa ukwati mwalamulo. [uw-CN tsa. 139 ndime 1]
6. Petro woyamba 3:3, 4 samaletsa kugwiritsira ntchito moyenera majuwelo ndi mafuta osalalitsa khungu monga momwedi samaletsera kuvala zovala. [rs-CN tsa. 31 ndime 1]
7. Eksodo 21:22, 23 amatithandiza kuzindikira kuti Mulungu amaona mwana wa munthu wa m’mimba monga moyo wamtengo wapatali. [kl-CN tsa. 128 ndime 21]
8. Ngati wolambira mnzathu watikhumudwitsa, kungakhale kulakwa kusafuna kumuonanso wokhumudwitsayo m’moyo wathu, kupeŵa kulankhula naye. [uw-CN tsa. 134 ndime 7]
9. Tonsefe timafunikira uphungu ndi mwambo. [uw-CN tsa. 130 ndime 12]
10. Kaya maboma aonedwe ngati olungama kapena osalungama, Akristu oona ayenera kulembetsa ukwati wawo kwa iwo. [kl-CN tsa. 122 ndime 11]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi umutu wachikristu uyenera kuchitidwa motani? [uw-CN tsa. 142 ndime 7]
12. Fotokozani chifukwa chake liwu lakuti “womthangatira” pa Genesis 2:18 silochepetsa akazi. [rs-CN tsa. 27 ndime 3]
13. Kodi nchifukwa ninji Yesu anakana kuloŵerera pamkangano wa choloŵa? (Luka 12:13, 14) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w97-CN 4/1 tsa. 28.]
14. Kodi ophunzira aja sanazindikire chiyani pamene anafunsa Yesu zobwezera Ufumu kwa Israyeli, monga kwalembedwa pa Machitidwe 1:6? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 6/1 tsa. 11 ndime 4.]
15. Tchulani zinthu ziŵiri zimene zingathandizire kulimbitsa ukwati. [uw-CN tsa. 140 ndime 4]
16. Kodi nchifukwa ninji mkazi wachikristu amavala chophimba kumutu pazochitika zina? [rs-CN tsa. 29 ndime 1]
17. Kodi nchifukwa ninji New World Translation imati “Mawu anali mulungu” osati “Mawu anali Mulungu,” monga mmene ma Baibulo ena amanenera pa Yohane 1:1? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani rs-CN tsa. 426 ndime 4.]
18. Kodi Chilamulo cha Mose ‘chinapangitsa motani zolakwa kuonekera’? (Agal. 3:19, NW) [uw-CN tsa. 147 ndime 4]
19. Popeza Yesu anali munthu wangwiro ndipo anavomera kuti anali Mphunzitsi, kodi nchifukwa ninji anakana kutchedwa kuti “Mphunzitsi Wabwino”? (Luka 18:18, 19) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 3/1 tsa. 15 ndime 7.]
20. Kodi chinali chatsopano nchiyani palamulo la pa Yohane 13:34? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 2/1 tsa. 21 ndime 5-6.]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Ngati tadziŵa kuti mbale wathu ali nafe chifukwa, zimafuna ․․․․․․․․ ndi ․․․․․․․․ kuti ifeyo tiyambe kuyesa kubwezeretsa ․․․․․․․․. [uw-CN tsa. 135 ndime 10]
22. “Matalente” khumi anaimira ․․․․․․․․ chimene ophunzira obadwa ndi mzimu akanatha kugwiritsira ntchito kupezera ․․․․․․․․ a Ufumu wakumwamba. (Luka 19:13) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 10/1 tsa. 8.]
23. Milandu itatu imene Ayuda anamneneza Yesu kwa Pilato, bwanamkubwa wachiroma wa ku Yudeya, inaphatikizapo kupandutsa ․․․․․․․․, kuletsa kupereka ․․․․․․․․, ndi kudzinenera yekha kuti Iyeyo anali ․․․․․․․․. (Luka 23:2) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w90-CN 12/1 tsa. 9 ndime 1.]
24. Kukonda kwathu abale athu kungakule ngati tiyesayesa kukwirira ․․․․․․․․ zawo zilizonse zazing’ono, ndi kuyamikira ․․․․․․․․ yawo yabwino, kuona mmene ․․․․․․․․ akuwagwiritsirira ntchito. [uw-CN tsa. 137 ndime 15]
25. Monga ophunzira Baibulo, tiyenera kuphunzira kugwiritsira ntchito maindekisi amene alipo pofufuza nkhani, sitiyenera kuyembekeza ․․․․․․․․ kapena ․․․․․․․․ pafunso lililonse, ndipo tiyenera ․․․․․․․․ zochita mosonyeza kukonda kwathu ․․․․․․․․ ndiponso apabanja lathu. [uw-CN tsa. 144 ndime 13]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Malinga ndi mtumwi Petro, (chifundo cha; chikondi cha; kuleza mtima kwa) Yehova kwapitirizabe mpaka tsiku lathu kuti atipatse mpata wosonyeza (kulapa; kukhulupirika; kumvera). (2 Pet. 3:9) [rs-CN tsa. 185 ndime 4]
27. Choonadi chimene chimamasula anthu ndicho choonadi chonena za (sayansi; chipembedzo chonyenga; Yesu Kristu) chifukwa kupyolera mwa chokhacho tingamasulidwe pa (ziphunzitso zonyenga; malingaliro a dziko; tchimo lakupha). (Yoh. 8:12-36) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 5/1 tsa. 9 ndime 5.]
28. “Nkhosa zina” zotchulidwa pa Yohane 10:16 ndizo (Akristu akunja; Akristu Achiyuda; onse amene ali ndi chiyembekezo cha moyo m’Paradaiso padziko lapansi). [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 4/15 tsa. 31 ndime 4.]
29. Pamene Yesu anafunsa mtumwi Petro kuti, “Kodi undikonda Ine koposa [izi?, NW],” anali kufunsa Petro ngati anakonda Yesu koposa (mmene anakondera ophunzira enawa; mmene ophunzira enawa anakondera Yesu; mmene anakondera zinthu izi; monga nsomba). (Yoh. 21:15) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w88-CN 11/1 tsa. 31 ndime 9.]
30. Kukhala ndi moyo waumulungu kumatitsimikizira kuti (nthaŵi zonse ena azitichitira zabwino; tidzakhala ndi chuma chakuthupi chochuluka tsopano; Mulungu adzatiyanja chifukwa tikuchita choyenera). [kl-CN tsa. 118 ndime 2]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Eks. 31:12, 13; Miy. 3:9, 10; Mat. 5:14-16; Luka 13:4, 5; Aroma 7:6, 7
31. Yesu anatsutsa anthu oganiza kuti moyo umakhala ndi zoikidwiratu, natchula za tsoka limene omvetsera akewo anadziŵa bwino ndipo anati limenelo linagwa panthaŵi yosadziŵika. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 9/1 tsa. 5 ndime 5.]
32. Chilamulo cha Mose sichinali kugwira ntchito kwa anthu onse. [uw-CN tsa. 147 ndime 5]
33. Yehova adzatidalitsa ngati tigwiritsira ntchito nthaŵi yathu, nyonga yathu, ndi zinthu zina, kuphatikizapo ndalama zathu, kuti tichirikize kulambira koona. [kl-CN tsa. 120 ndime 8]
34. Pamene Chilamulo cha Mose chinathetsedwa, nawonso Malamulo Khumi anathetsedwa. [uw-CN tsa. 147 ndime 5]
35. Amene ali Akristu ayenera kukhala mboni zokangalika kudziko ponena za dzina la Mulungu ndi zifuno zake. [rs-CN tsa. 130 ndime 5]
S-97-CN Zam, Mal & Moz #293b 12/97