Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
DZIŴANI IZI: Monga mwa nthaŵi zonse, m’nthaŵi yamisonkhano Utumiki Wathu wa Ufumu udzakhala ndi ndandanda ya Msonkhano wa Utumiki wa mlungu uliwonse. Choncho mipingo ingasinthe mofunikira kuti ipangiretu msonkhano wa mlungu umene ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Aphunzitsi a Mawu a Mulungu.” M’mwezi wa October, Msonkhano wina wa Utumiki udzakhala wokambirana mfundo zazikulu zokhazokha za kumsonkhano wachigawo. Pokonzekera kukambirana kumeneko, tonse tikalembe notsi zogwira mtima kumsonkhano wachigawo, komanso mfundo zimene tikufuna kuzigwiritsira ntchito m’moyo wathu ndiponso mu utumiki wakumunda. Tikatero tidzakhala okonzeka kufotokoza mmene tagwiritsira ntchito malingalirowo titachokera kumsonkhano wachigawo. Tidzalimbikitsana kumva ena akunena momwe akupindulira ndi malangizo abwino amene tinalandira.
Mlungu Woyambira August 13
Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Kambiranani “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ukudzawo, ndiponso limbikitsani anthu onse kudzapezeka pa pulogalamu yonse. Limbikitsani ofalitsa kuitanira anthu amene achita chidwi posachedwapa ndiponso anthu amene akuphunzira nawo Baibulo.
Mph. 17: “Kodi Mukufuna Kuchita Zochuluka?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Thirirani ndemanga mwachidule kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1997, masamba 26-9.
Mph. 15: “Kusangalala Kuzikhala ndi Nthaŵi Yake.” Wochititsa phunziro la buku akambirane ndi mwamuna ndi mkazi wake pambuyo pa phunzirolo. Mkuluyo anene mwachikondi kuti masiku apitawo sanalione banjali mu utumiki wakumunda kapena pa misonkhano yakumapeto kwa mlungu. Banjalo lifotokoze kuti tchuti ndiponso zochita zina zinawatangwanitsa. Mkuluyo apende mfundo zazikulu m’nkhaniyi, kuthandiza banjalo kuona kuti zinthu zauzimu zizikhala patsogolo nthaŵi zonse. Banjalo lithokoze mkuluyo chifukwa cha malangizo abwinowa. Banjalo livomereze kuti nthaŵi ina lidzaika zinthu zofunika patsogolo.—Onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 2000, tsamba 19-20.
Nyimbo Na. 68 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 20
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Ndinu ‘Choonetsedwa’!” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani zochitika zina za kumaloko zimene zinapangitsa anthu kuyamikira ntchito ndi khalidwe la Mboni za Yehova.—Onani Nsanja ya Olonda ya March 15, 1998, tsamba 10, ndi January 15, 1999, tsamba 32.
Mph. 22: “Khalidwe Labwino Lili Chizindikiro Chapadera cha Anthu a Mulungu.” Mkulu akambe nkhani mphindi zisanu kuchokera pa ndime 1-5. Ndiyeno akambirane ndime zotsalazo ndi mkulu mnzake ndiponso mtumiki wotumikira papulatifomu. Akambirane momwe angathetsere khalidwe losalingalira ena lomwe lingadodometse misonkhano yathu ndiponso limene lingachepetse mapindu amene timapeza pamisonkhanopo. Agogomezere momwe kucheza ndi ena kulili kolimbikitsa zedi ngati tisonyeza kudera nkhaŵa ndi kukonda abale athu.—Afil. 2:4.
Nyimbo Na. 72 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 27
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wakumunda a August. Tchulani mwachidule zimene tinganene pogaŵira buku lililonse la masamba 192 mu utumiki m’mwezi wa September.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: “Mwambo Wapadera m’Malaŵi.” Ngati n’kotheka nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu amene anapita ku mwambo wopatulira nthambi ya Malaŵi. Funsani anthu a mu mpingomo amene anapezeka pa mwambowu mmene akumvera.
Nyimbo Na. 74 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 3
Mph. 8: Zilengezo za pampingo.
Mph. 17: “Kodi Mayanjano Achikristu ndi Ofunika Motani?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1996, tsamba 22 pamutu wakuti “Kupyolera Mumpingo.”
Mph. 20: Ngati Wina Anena Kuti. Nkhani yochokera m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba ndiponso yokhala ndi zitsanzo. Mu utumiki, anthu akanena zina kapena akafunsa mafunso amene sitinawayembekezere, tiziyesetsa kuyankha m’malo mosintha mutu wankhani kapena kuthetsa kukambiranako. Nthaŵi zambiri buku la Kukambitsirana lidzakuthandizani kuchita zimenezi. Tchulani mawu angapo amene ali otchuka m’deralo, ndipo ofalitsa achite chitsanzo cha momwe angayankhire mwa kugwiritsa ntchito ndemanga za m’buku la Kukambitsirana. Mwachitsanzo: ‘Sindimakhulupirira Mulungu.’ (tsamba 311-2) ‘Kodi n’chifukwa chiyani simugwira nawo ntchito yokonza dera lanu?’ (tsamba 278-9) ‘Zilibe kanthu kwenikweni ndi tchalitchi chomwe muli.’ (tsamba 332) Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito mbali zimenezi mu buku la Kukambitsirana akafunsidwa mafunso amene sanawayembekezere mu utumiki.
Nyimbo Na. 121 ndi pemphero lomaliza.