Kodi Mukufuna Kuchita Zochuluka?
1 Yesu anayerekezera Ufumu ndi chuma chamtengo wapatali. (Mat. 13:44-46) Ntchito yofalitsa uthenga wa Ufumu ilinso chuma chamtengo wapatali. Utumiki umenewu n’ngofunika kukhala patsogolo m’moyo wathu, ngakhale kuti kuchita mokwanira ntchito imeneyi kungafune kudzilanga. (Mat. 6:19-21) Kodi mukufuna kuchita zochuluka mu utumiki wa Ufumu?
2 Onani Zinthu Zofunika Izi: Kuti tiwonjezere zimene timachita mu utumiki pakufunika zinthu zingapo: (1) kutsimikiza mtima kuika zinthu za Ufumu patsogolo m’moyo wathu (Mat. 6:33); (2) chikhulupiriro ndiponso kudalira Yehova (2 Akor. 4:1, 7); (3) kupempha thandizo kwa Mulungu mwa kupemphera mochokera pansi pamtima ndiponso mobwerezabwereza (Luka 11:8-10); (4) kutsatira malangizo ndiponso kuchita mogwirizana ndi mapemphero athu.—Yak. 2:14, 17.
3 Njira Zimene Tingakulitsire Utumiki Wathu: Tonse tingakhale ndi cholinga chofunika kwambiri chakuti mwezi uliwonse nthaŵi ina tizikhala mu utumiki. Koma kodi mwalingaliranso kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kulalikira mwamwayi, kupanga ulaliki wanu kukhala watanthauzo kwambiri, kuyesetsa kuti maulendo anu obwereza akhale ogwira mtima, ndiponso kuyesetsa kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba opita patsogolo? Kodi mungathe kuchita upainiya wothandiza kapena wokhazikika kapena kukatumikira kumene kuli kosoŵa kwambiri? Ngati ndinu mbale wobatizidwa, kodi mungalimbikire kuti muyenerere kukhala mtumiki wotumikira kapena mkulu? (1 Tim. 3:1, 10) Kodi mungawonjezere utumiki wanu mwa kufunsira Sukulu Yophunzitsa Utumiki?—Luka 10:2.
4 Mbale amene tsiku lonse ankagwira ntchito yolembedwa ndi kuthera nthaŵi yambiri kuchita maseŵero olimbitsa thupi analimbikitsidwa kuti akhale mpainiya wokhazikika. Anayamba upainiya wothandiza ndipo anasintha zimene ankachita kuti akhale mu utumiki wa nthaŵi zonse. Kenako anapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, imene inam’thandiza kukonzekera ntchito imene akugwira panopa yoyang’anira dera. Akusangalala kwambiri kuti anagwiritsa ntchito zimene analimbikitsidwa, ndipo akukhulupirira kuti akusangalala chifukwa chakuti anasankha kuchita zochuluka mu utumiki wa Ufumu.
5 Yehova amadalitsa odzipereka. (Yes. 6:8) Musalole chilichonse kukulepheretsani kuwonjezera utumiki wanu ndipo mapeto ake mudzakhutira ndi kusangalala kwambiri.