Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira June 9
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 17: “Utumiki Wachikristu Ndiyo Ntchito Yathu Yaikulu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Limbikitsani achinyamata kuganizira phindu limene angapeze mwa kuyamba utumiki wanthaŵi zonse. Phatikizanipo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2000, masamba 19-20, pa kamutu kakuti “Pamene Chikhalidwe ndi Chikumbumtima Zisemphana.”
Mph. 20: “Kodi Nthaŵi Yopuma Pantchito Ingakhale Nthaŵi Yowonjezera Zochita?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati n’kotheka, funsani mwachidule wofalitsa amene wagwiritsa ntchito nthaŵi yopuma pantchito kuchita zochuluka potumikira Yehova. Mufunseni zimene wasintha pamoyo wake kuti awonjezere utumiki ndiponso zimene wapindula chifukwa chochita zimenezo.
Nyimbo Na. 190 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 16
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 12: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: “Khalani Akhama ‘Pochitira Umboni Mokwanira’” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Mukakambirana ndime 5 ndi 6, sonyezani chitsanzo chachidule cholalikira mwamwayi kwa wogulitsa m’sitolo ndi kugaŵira thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Musanakambirane ndime 7 ndi 8, ziŵerengeni kaye mokweza. Pomaliza, ŵerengani ndi kukambirana bokosi lakuti “Musawaiwale!”
Nyimbo Na. 131 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 23
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya June 15 ndi Galamukani! ya June 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsira ntchito magazini imodzi pokambirana. Phatikizanipo lemba m’zitsanzo ziŵiri zonsezo.
Mph. 20: Kodi Tingachitenji Ngati Tikufooka? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 1999, masamba 28 ndi 29, kulekeza pamene pathera mutu wakuti “Kukhalabe ndi Maganizo Abwino.” Pendani mfundo zothandiza ndiponso malangizo a m’Malemba amene ali m’nkhaniyi. Konzeranitu zoti wofalitsa mmodzi kapena aŵiri ochita bwino afotokoze zimene zimawathandiza kukhalabe achimwemwe ndi utumiki wawo.
Mph. 15: “Kulalikira M’dziko Losinthasinthali.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 2 ndi 3, funsani omvera nkhani zimene zachitika posachedwapa zimene zingagwiritsidwe ntchito kuyambitsira kukambirana m’gawolo. Pokambirana ndime 4, sonyezani chitsanzo chachidule, pogwiritsa ntchito ulaliki umodzi umene unaperekedwa m’zofalitsa zimene zatchulidwa m’ndimeyi.
Nyimbo Na. 15 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 30
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a mu utumiki wa kumunda a June. Phatikizanipo ndemanga za m’nkhani yoti “Lipoti Labwino Limalimbikitsa.”
Mph. 15: “Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Ena Kupeza Njira ya ku Moyo Wosatha?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 3, sonyezani chitsanzo cha ulaliki wachidule. Pemphani onse kuchita zotheka poyambitsa maphunziro a Baibulo atsopano.
Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Mawu a Mulungu Mogwira Mtima Polalikira Ufumu. Kukambirana ndi omvetsera. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Timayesetsa kumuuza munthu aliyense amene takumana naye mu utumiki, mfundo ya m’Malemba yogwira mtima yonena za Ufumu. Komabe, sitiyenera kungoŵerenga malemba m’Baibulo basi. Tiyenera kuwafotokoza, kupereka fanizo, ndiponso kufotokoza mmene angawagwiritsire ntchito. Sonyezani momwe tingachitire zimenezi, gwiritsani ntchito monga chitsanzo malemba ena amene ali m’buku la Kukambitsirana patsamba 65, pa kamutu ka mawu olembedwa mopendekeka kakuti “Olamulira aumunthu sakupereka zimene mtundu wa anthu ukufuna mofulumira.” Mukatha kukambiranako, wofalitsa wokonzekera bwino achite chitsanzo cha momwe tingagwiritse ntchito lemba limodzi mogwira mtima paulendo wobwereza, kulifotokoza momveka bwino, kunena fanizo losavuta, ndiponso kufotokoza mwachidule momwe angagwiritsire ntchito lembalo zimene zingasonyeze mwininyumba momwe iye adzapindulire ndi ulamuliro wa Ufumu. Wofalitsa ayambe chitsanzocho ndi kuŵerenga lemba. Chikatha chitsanzocho, kambiranani momwe lembalo analifotokozera, kupereka fanizo, ndiponso mmene angaligwiritsire ntchito. Limbikitsani onse kukulitsa luso logwiritsa ntchito Mawu a Mulungu mogwira mtima.
Nyimbo Na. 171 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 7
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo ziŵiri momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya July 1 ndi Galamukani! ya July 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezi, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsira ntchito magazini imodzi pokambirana. Chitsanzo chimodzi chikhale cha wofalitsa akuchita ulaliki wa mu msewu.
Mph. 10: Zokumana nazo. Simbani kapena chitani chitsanzo cha zokumana nazo zimene ofalitsa pampingopo anapeza polalikira mwa njira zina osati ku nyumba ndi nyumba ndi mu msewu.
Mph. 25: “Kudziŵikitsa Dzina la Mulungu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Wofalitsa waluso achite chitsanzo cha ulendo wobwereza. Gwiritsani ntchito malemba aŵiri kapena atatu a m’buku la Kukambitsirana patsamba 420 ndi 421, kusonyeza chifukwa chake n’kofunika kudziŵa ndi kugwiritsira ntchito dzina lenileni la Mulungu.
Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.