Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Aug. 1
“Kodi mukuvomereza kuti kutsatira lamulo la Yesu ili kungathandize anthu kusangalala m’banja? [Werengani Yohane 13:34. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikusonyeza kuti zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso chitsanzo chake zingathandize aliyense m’banja.” Asonyezeni nkhani imene ili pa tsamba 16 ndi 17.
Galamukani! Aug.
“Kodi mukuganiza kuti mabomawa angathetse vuto la kutentha kwa dziko? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Yeremiya 10:23.] Nkhani iyi musangalala nayo kwambiri. Ikufotokoza mmene Mulungu adzathetsere mavuto amene akuchititsa mantha pa dzikoli.”
Nsanja ya Olonda Sept. 1
“Anthu ambiri amadziwa bwino mawu a Yesu opezeka pa Mateyo 6:9. [Werengani.] Ngakhale zili choncho, ambiri amaona kuti sizingatheke kuyandikira Mulungu n’kumamuona ngati atate wathu. Kodi inu mukuganiza kuti tingayandikire bwanji Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza makhalidwe osiyanasiyana a Atate wathu wa kumwamba komanso zimene tingachite kuti timudziwe bwino kwambiri.”
Galamukani! Sept.
“Anthu akhala akutsutsana kwanthawi yaitali pankhani ya zimene zimachitika munthu akafa. Nanga inuyo mukuganiza bwanji pankhaniyi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yobu ankakhulupirira. [Werengani Yobu 14:14, 15.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira.”