Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb20 December tsamba 8
  • Tizigwiritsabe Ntchito Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tizigwiritsabe Ntchito Magazini
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Sankhani Nkhani Zokopa Chidwi cha Anthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20 December tsamba 8
Mlongo akukambirana ndi mzimayi wina za nkhani ya m’magazini ya ‘Galamukani!’

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tizigwiritsabe Ntchito Magazini

Kuyambira mu 2018, magazini iliyonse yogawira ikumangofotokoza nkhani imodzi yokha. Magazini onsewa ali mu gulu la Zinthu Zophunzitsira. Choncho tikhoza kuwagwiritsa ntchito mu utumiki. Tikhoza kunyamula magaziniwa tikakhala pa ulendo kapena tikamapita kumsika. Ngakhale kuti magaziniwa sanakonzedwe kuti tizigwiritsa ntchito pophunzira Baibulo ndi anthu, angathandize munthu kuti ayambe kukhala ndi chidwi pa zinthu zauzimu.

Mukayamba kukambirana ndi munthu, musonyezeni lemba kenako tchulani nkhani ina yam’magazini imene munthuyo angachite nayo chidwi. Mwachitsanzo, ngati munthuyo ali ndi banja, ali pa chisoni kapena ali ndi nkhawa, munganene kuti: “Posachedwapa ndawerenga nkhani yabwino yokhudza zimene mukukumana nazozi. Kodi mungakonde kuiona?” Ngati ali ndi chidwi, ngakhale pa ulendo woyambawo, mukhoza kumupatsa magaziniyo kapena kumutumizira pachipangizo chamakono. Ngakhale kuti cholinga chathu chachikulu si kugawira magazini kapena mabuku, magazini angatithandize kupeza anthu amene akufuna kugwiritsa ntchito zimene aphunzira.​—Mac 13:48.

2018

Zithunzi zosonyeza mitu ya magazini a ‘Nsanja ya Olonda’ ndi ‘Galamukani!’ a 2018. 1. ‘Kodi Baibulo Ndi Lothandizabe Masiku Ano?’ 2. ‘Kodi M’tsogolomu Muli Zotani?’ 3. ‘Kodi Mulungu Zimam’khudza Mukamavutika?’ 4. ‘Mungatani Kuti Muzikhala Wosangalala.’ 5. ‘Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino.’ 6. ‘Mfundo Zothandiza Amene Aferedwa.’

2019

Zithunzi zosonyeza mitu ya magazini a ‘Nsanja ya Olonda’ ndi ‘Galamukani!’ a 2019. 1. ‘Kodi Mulungu Ndi Ndani?’ 2. ‘Kodi Mukuona Kuti Palibenso Chifukwa Chokhalira ndi Moyo?’ 3. ‘Kodi Mulungu Ankafuna Kuti Tizikhala Ndi Moyo Waufupi Chonchi?’ 4. ‘Kodi Tingadzakhaledi Otetezeka Padzikoli?’ 5. ‘Makhalidwe 6 Amene Muyenera Kuphunzitsa Ana Anu.’ 6. ‘Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala Ndi Moyo Wabwino Kwambiri.’

2020

Zithunzi zosonyeza mitu ya magazini a ‘Nsanja ya Olonda’ ndi ‘Galamukani!’ a 2020. 1. ‘Kufufuza Choonadi.’ 2. ‘Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?’ 3. ‘Mulungu Wachikondi Adzatipatsa Madalitso Osatha.’ 4. ‘Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?’ 5. ‘Mayankho a Mafunso 5 Okhudza Kuvutika.’ 6. ‘Kodi Tsankho Lidzatha?’

Kodi ndi nkhani ziti zimene anthu a m’gawo lanu amachita nazo chidwi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena