NKHANI YOPHUNZIRA 48
NYIMBO NA. 129 Tipitirizebe Kupirira
Buku la Yobu Lingakuthandizeni Mukamakumana ndi Mavuto
“Ndithudi, Mulungu sachita zoipa.”—YOBU 34:12.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Tiona zimene tingaphunzire m’buku la Yobu pa nkhani ya chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika komanso zimene tingachite kuti tipirire tikamakumana ndi mavuto.
1-2. N’chifukwa chiyani buku la Yobu ndi lofunika kuliwerenga?
KODI mwawerengapo buku la Yobu posachedwapa? Ngakhale kuti linalembedwa zaka 3,500 zapitazo, buku la Yobu ndi limodzi mwa mabuku othandiza kwambiri padzikoli. Pofotokoza mmene bukuli linalembedwera m’njira yosavuta kumva, mawu osangalatsa komanso amphamvu omwe anagwiritsidwa ntchito, buku lina linanena kuti amene analemba bukuli anali “wanzeru kwambiri.” Ngakhale kuti Mose ndi amene analemba bukuli, Yehova Mulungu ndi amene anamuuza zoti alembe.—2 Tim. 3:16.
2 Buku la Yobu ndi limodzi mwa mabuku ofunika kwambiri m’Baibulo. Tikutero chifukwa limatithandiza kumvetsa nkhani yaikulu imene imakhudza angelo komanso anthu onse, yomwe ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova. Limatiphunzitsanso za makhalidwe abwino a Yehova monga chikondi, chilungamo, nzeru komanso mphamvu. Mwachitsanzo, buku la Yobu limafotokoza kuti Yehova ndi “Wamphamvuyonse” maulendo 31, kuposa mabuku onse a m’Baibulo tikawaphatikiza pamodzi. Bukuli limayankhanso mafunso ambiri okhudza moyo kuphatikizapo limene likuvutitsa anthu ambiri, lakuti: N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti tizivutika?
3. Kodi kuphunzira buku la Yobu kungatithandize m’njira ziti?
3 Tikakwera pamwamba pa phiri timaona bwinobwino zinthu zimene zatizungulira. Mofanana ndi zimenezi, buku la Yobu limatithandiza kuona bwinobwino mavuto athu. Timawaona mmene Yehova amawaonera. Tiyeni tione mmene buku la Yobu lingatithandizire tikamavutika. Tionanso mmene nkhani ya Yobu inathandizira Aisiraeli, mmene ingatithandizire masiku ano komanso mmene tingagwiritsire ntchito nkhaniyi pothandiza ena.
MULUNGU ANALOLA KUTI YOBU AVUTIKE
4. Kodi Yobu ndi Aisiraeli amene ankakhala ku Iguputo ankasiyana bwanji?
4 Pa nthawi imene Aisiraeli ankavutika monga akapolo ku Iguputo, panali munthu wina dzina lake Yobu amene ankakhala ku Uzi. Zikuoneka kuti dzikoli linali kum’mawa kwa Dziko Lolonjezedwa komanso chakumpoto kwa Arabia. Mosiyana ndi Aisiraeli omwe anayamba kulambira mafano ku Iguputo, Yobu ankatumikira Yehova mokhulupirika. (Yos. 24:14; Ezek. 20:8) Yehova ananena za Yobu kuti: “Padziko lapansi palibe wina wofanana naye.”a (Yobu 1:8) Yobu anali wolemera kwambiri ndipo ankalemekezedwa kuposa anthu onse akum’mawa. (Yobu 1:3) Satana ayenera kuti anakwiya kwambiri kuona munthu wotchuka komanso wolemerayu akutumikira Mulungu mokhulupirika.
5. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti Yobu avutike? (Yobu 1:20-22; 2:9, 10)
5 Satana ankanena kuti Yobu akhoza kusiya kutumikira Yehova ngati atakumana ndi mavuto. (Yobu 1:7-11; 2:2-5) Ngakhale kuti Yehova ankakonda kwambiri Yobu, zimene Satana ananena zinayambitsa nkhani zofunika kwambiri. Ndiye Yehova analola kuti Satana asonyeze ngati zimene ananenazo zinali zoona. (Yobu 1:12-19; 2:6-8) Satana analanda ziweto za Yobu, anapha ana ake 10 komanso anapangitsa Yobu kuti adwale zilonda zowawa kwambiri zimene zinatuluka kuyambira kumutu mpaka kuphazi. Ngakhale zinali choncho, iye anapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. (Werengani Yobu 1:20-22; 2:9, 10.) Patapita nthawi, Yehova anachiritsa Yobu, anamupatsa chuma chambiri, anamupatsa ana ena 10 ndipo anthu anayambiranso kumulemekeza. Anamupatsanso moyo wautali pomuwonjezera zaka zina 140 ndipo anakwanitsa kuona mibadwo 4 ya ana ake. (Yobu 42:10-13, 16) Kodi nkhani ya Yobuyi ikanathandiza bwanji atumiki a Yehova m’mbuyomu, nanga ifeyo ingatithandize bwanji?
6. Kodi nkhani ya Yobu ikanathandiza bwanji Aisiraeli kudziwa chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika? (Onaninso chithunzi.)
6 Mmene nkhaniyi ikanathandizira Aisiraeli. Aisiraeli ankavutika kwambiri ku Iguputo. Mwachitsanzo, Yoswa ndi Kalebe anakula ali akapolo. Kenako kwa zaka 40 ankangoyendayenda m’chipululu chifukwa choti Aisiraeli ena sanamvere Yehova. Ngati Aisiraeli ankadziwa mavuto amene Yobu anakumana nawo komanso mmene zinthu zinayendera pa moyo wake, n’zosakayikitsa kuti zinawathandiza iwowo komanso m’badwo wam’tsogolo kudziwa amene amapangitsa kuti tizivutika. Akanamvetsanso chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika komanso amaona kuti anthu amene amakhalabe okhulupirika ndi amtengo wapatali.
Aisiraeli, omwe anakhala nthawi yaitali ku ukapolo ku Iguputo, akanatha kuphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira Yobu (Onani ndime 6)
7-8. Kodi buku la Yobu lingathandize bwanji anthu amene akukumana ndi mavuto? Perekani chitsanzo.
7 Mmene nkhaniyi ingatithandizire. N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ambiri asiya kukhulupirira Mulungu chifukwa samvetsa chifukwa chake anthu abwino amavutika. Chitsanzo ndi Mlongo Hazelb wa ku Rwanda. Ali mwana ankakhulupirira Mulungu. Koma kenako zinthu zinasintha. Banja la makolo ake linatha, zomwe zinapangitsa kuti aleredwe ndi bambo ake omupeza amene ankamuchitira nkhanza. Ali wachinyamata, munthu wina anamugwiririra. Hazel anapita kutchalitchi kwawo kuti akalimbikitsidwe koma sanamuthandize. Kenako Hazel analembera Mulungu kalata. Iye analemba kuti: “Mulungu, ndakhala ndikupemphera kwa inu ndipo ndayesetsa kuchita zinthu zabwino, koma mwandibwezera zoipa m’malo mwa zabwino. Panopa ndikukusiyani ndipo ndizichita zimene zingandisangalatse.” Timamvera chisoni anthu ngati Hazel amene anauzidwa zabodza zokhudza Mulungu ndipo amakhulupirira kuti iye ndi amene amachititsa mavuto awo.
8 Komabe, taphunzira kuchokera m’buku la Yobu kuti si Mulungu amene amapangitsa kuti tizivutika koma Satana. Taonanso kuti tisamaganize kuti anthu amene akukumana ndi mavuto, akukolola zimene anafesa. Malemba amatiuza kuti “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka” zikhoza kuchitikira aliyense, nthawi iliyonse. (Mlal. 9:11; Yobu 4:1, 8) Taphunziranso kuti tikamapirira mayesero mokhulupirika, Yehova amapeza chomuyankha Satana. Zimenezi zimathandiza kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. (Yobu 2:3; Miy. 27:11) Timayamikira kwambiri mwayi wodziwa mfundo zimenezi. Zimatithandiza kudziwa chifukwa chake anthufe timavutika. Patapita nthawi, Hazel anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anamvetsa kuti Mulungu si amene anapangitsa kuti iye azivutika. Iye anati: “Ndinapempheranso kwa Mulungu kuchokera pansi pa mtima. Ndinamuuza kuti pamene ndimanena kuti ndikumusiya, sindimanena zenizeni. Ndinalankhula zimenezi chifukwa chosamudziwa bwino. Panopa ndamvetsa kuti Yehova amandikonda. Ndimasangalala kwambiri ndipo ndine wokhutira.” Timayamikira kudziwa chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika. Tiyeni tione mmene nkhani ya Yobu ingathandizire aliyense wa ife akamakumana ndi mavuto.
MMENE NKHANI YA YOBU INGATITHANDIZIRE KUTI TIZIPIRIRA
9. Kodi Yobu anachita chiyani pamene ankavutika? (Yakobo 5:11)
9 Taganizirani kuti mukumuona Yobu atakhala yekhayekha paphulusa, thupi lonse lili zilonda zokhazokha ndipo akumva ululu woopsa. Khungu lake lawonongekeratu ndi matendawo ndipo wawonda kwambiri. Chifukwa chotopa ndi ululu, Yobu ayenera kuti anangokhala n’kumadzikanda ndi kaphale, uku akudandaula za mavuto ake. Sikuti Yobu anangopitiriza kukhala ndi moyo, koma ankapirira. (Werengani Yakobo 5:11.) N’chiyani chinathandiza Yobu kuti apirire?
10. Kodi Yobu anali pa ubwenzi wotani ndi Yehova? Fotokozani.
10 Yobu anauza Yehova mmene ankamvera. (Yobu 10:1, 2; 16:20) Mwachitsanzo, chaputala 3 chimatiuza kuti Yobu anadandaula mowawidwa mtima za mavuto ake, poganiza kuti ndi Yehova amene akuchititsa. Kenako mobwerezabwereza, anzake atatu aja ankanena kuti Mulungu akumulanga chifukwa cha zoipa zimene anachita. Koma Yobuyo ankanena kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova ndipo zina zimene ananena zimasonyeza kuti pa nthawi ina ankadziona kuti anali wolungama kuposa Mulungu. (Yobu 10:1-3; 32:1, 2; 35:1, 2) Komabe, iye anavomereza kuti zimene ankanena posonyeza kuti ndi wolungama kunali ‘kulankhula mosaganiza bwino.’ (Yobu 6:3, 26) Ndipo muchaputala 31, Yobu ananena kuti ankafuna kuti Mulungu amuyankhe. (Yobu 31:35) Komabe, iye sankafunika kukakamiza Mulungu kuti amuuze chifukwa chake ankavutika.
11. Kodi Yehova anatani pamene Yobu ananena kuti ndi wolungama kuposa Mulungu?
11 Mmene Yobu ankalankhulira ndi Yehova zikungosonyeza kuti anali naye pa ubwenzi wolimba ndipo ankadziwa kuti akuona kukhulupirika kwake. Pamene Yehova anamuyankha kudzera muchimphepo, sanamufotokozere zifukwa zonse zimene zinkapangitsa kuti azivutika. Iye sanaimbe mlandu Yobu chifukwa chodandaula komanso chifukwa chonena kuti sanalakwe. M’malomwake, anamulangiza ngati mmene bambo amachitira ndi mwana wake ndipo imeneyi inali njira yabwino kwambiri. Zotsatira zake, Yobu anavomereza modzichepetsa kuti sakudziwa zambiri komanso analapa chifukwa cholankhula mosaganiza bwino. (Yobu 31:6; 40:4, 5; 42:1-6) Kodi nkhaniyi ikanathandiza bwanji anthu akale, nanga ingatithandize bwanji masiku ano?
12. Kodi nkhani ya Yobu ikanathandiza bwanji Aisiraeli?
12 Mmene nkhaniyi ikanathandizira Aisiraeli. Aisiraeli akanatha kuphunzirapo kanthu pa zimene zinachitikira Yobu. Taganizirani chitsanzo cha Mose. Sizinali zophweka kuti Mose atsogolere Aisiraeli. Nthawi zambiri iwo sankamvera Yehova komanso ankakhumudwitsa Mose. Mosiyana ndi Aisiraeli opanduka amene ankadandaula zokhudza Yehova akakumana ndi mavuto, Mose ankapemphera kwa Yehova kuti amuthandize akakumana ndi mavuto. (Eks. 16:6-8; Num. 11:10-14; 14:1-4, 11; 16:41, 49; 17:5) Mose nayenso ankafunika kudzichepetsa Yehova atamudzudzula. Mwachitsanzo, Aisiraeli ali ku Kadesi, mwina m’chaka cha 40 ali m’chipululu, iye “analankhula mosaganiza bwino” ndipo analephera kulemekeza Yehova. (Sal. 106:32, 33) Zotsatira zake, Yehova sanamulole kuti akalowe m’Dziko Lolonjezedwa. (Deut. 32:50-52) Chilango chimenechi chiyenera kuti chinali chowawa kwa Mose koma anavomereza modzichepetsa. Nkhani ya Yobu ikanathandiza m’badwo wa kutsogolo wa Isiraeli kuti uzipirira ukakumana ndi mavuto. Kuganizira nkhaniyi kukanathandiza atumiki okhulupirika kudziwa mmene angauzire Yehova mmene akumvera, kupewa kudzionetsa kuti ndi olungama pamaso pake komanso kuvomereza chilango chochokera kwa Yehova modzichepetsa.
13. Kodi nkhani ya Yobu ingatithandize bwanji kuti tizipirira? (Aheberi 10:36)
13 Mmene nkhaniyi ingatithandizire. Akhristufe timafunikanso kukhala opirira. (Werengani Aheberi 10:36.) Mwachitsanzo, enafe tikudwala kapena tikulimbana ndi nkhawa, mavuto a m’banja, tili ndi chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene timamukonda kapena mavuto ena aakulu. Ndipotu nthawi zina zimene anthu angalankhule kapena kuchita, zingapangitse kuti zikhale zovuta kuti tipirire. (Miy. 12:18) Ngakhale zili choncho, buku la Yobu limatiphunzitsa kuti tingathe kumuuza Yehova mmene tikumvera n’kumakhulupirira kuti atimvetsera. (1 Yoh. 5:14) Iye sangatiimbe mlandu ngati popemphera ‘tingalankhule mosaganiza bwino’ ngati mmene anachitira Yobu. M’malomwake, Mulungu adzatipatsa mphamvu komanso nzeru kuti tithe kupirira. (2 Mbiri 16:9; Yak. 1:5) Iye angatidzudzule ngati mmene anachitira ndi Yobu. Bukuli lingatithandizenso kupirira tikalandira malangizo kuchokera m’Mawu a Mulungu, gulu lake kapena kwa anzathu olimba mwauzimu. (Aheb. 12:5-7) Mofanana ndi Yobu, ifenso tingapindule ngati timavomereza modzichepetsa malangizo amene timapatsidwa. (2 Akor. 13:11) Zimenezitu ndi mfundo zothandiza kwambiri zimene taphunzira m’buku la Yobu. Tsopano tikambirana mmene tingagwiritsire ntchito nkhani ya Yobu pothandiza ena.
MUZIGWIRITSA NTCHITO BUKU LA YOBU POTHANDIZA ENA
14. Kodi tingafotokozere bwanji anthu mu utumiki chifukwa chake padzikoli pali mavuto?
14 Kodi munthu anakufunsanipo chifukwa chake timavutika? Ndiye munamuyankha bwanji? Mwina munamuyankha pomufotokozera zimene zinachitika m’munda wa Edeni. N’kutheka kuti munayamba ndi kumufotokozera kuti Satana, yemwe ndi mngelo woipa, anauza anthu oyambirira bodza, zomwe zinachititsa kuti apandukire Mulungu. (Gen. 3:1-6) Kenako munamufotokozera kuti chifukwa chakuti Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, anthu padzikoli anayamba kuvutika komanso kumwalira. (Aroma 5:12) Pomaliza, munamufotokozera kuti Mulungu walola kuti padutse nthawi yokwanira pofuna kuthandiza aliyense kudziwa kuti zimene Satana ananena ndi zabodza komanso kuti anthu amve uthenga wabwino wakuti adzakhalanso angwiro. (Chiv. 21:3, 4) Imeneyi ndi njira yabwino yoyankhira funsoli ndipo ingathandize anthu ambiri kudziwa chifukwa chake timavutika.
15. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji buku la Yobu pothandiza munthu yemwe watifunsa chifukwa chake timavutika? (Onaninso zithunzi.)
15 Njira ina imene tingagwiritsire ntchito pofotokozera anthu chifukwa chake timavutika ndi kuwauza zokhudza Yobu. Mwina tingayambe ndi kuyamikira munthuyo chifukwa chofunsa funso labwino limeneli. Kenako tingamuuze kuti munthu winanso wokhulupirika dzina lake Yobu, amene anakumana ndi mavuto aakulu, anafunsanso funso ngati limeneli. Iye ankaganiza zoti Mulungu ndi amene ankachititsa mavuto amene ankakumana nawo. (Yobu 7:17-21) Zimenezi zingathandize munthuyo kudziwa kuti kuyambira kalekale anthu akhala akufuna atadziwa chifukwa chake timavutika. Kenako mwaluso tingamufotokozere kuti si Mulungu amene ankachititsa kuti Yobu azivutika koma ndi Satana. Iye anachita zimenezi pofuna kusonyeza kuti anthu amatumikira Mulungu chifukwa cha zolinga zadyera. Mwina tingawonjezerenso kuti Mulungu si amene ankachititsa kuti Yobu azivutika koma anangolola kuti avutike. Pochita zimenezi, anasonyeza kuti amakhulupirira kuti atumiki ake okhulupirika akhoza kusonyeza kuti Satana ndi wabodza. Pomaliza, tingamufotokozere kuti Mulungu anadalitsa Yobu chifukwa anakhalabe wokhulupirika. Choncho tikhoza kuwalimbikitsa powatsimikizira kuti si Yehova amene akuchititsa mavuto awowo.
Kodi mungagwiritsire ntchito bwanji buku la Yobu potsimikizira anthu kuti “Mulungu sachita zoipa”? (Onani ndime 15)
16. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti buku la Yobu lingathandize munthu amene akukumana ndi mavuto.
16 Taganizirani mmene buku la Yobu linathandizira Mario. Tsiku lina mu 2021, mlongo wina ankachita ulaliki wapafoni. Pa ulendo woyamba, mlongoyo anawerengera Mario lemba n’kumufotokozera kuti si kuti Mulungu amangomvetsera mapemphero athu koma watilonjezanso tsogolo labwino komanso zinthu zabwino. Mlongoyo atamufunsa maganizo ake, Mario ananena kuti pa nthawi imene amamuimbirayo amalemba kapepala kotsanzika chifukwa amafuna kudzipha. Iye anati: “Ndimakhulupirira Mulungu, koma m’mawawu ndinayamba kuganiza kuti Mulungu anandinyanyala.” Atamuimbiranso foni, mlongoyo anakambirana naye za mavuto amene Yobu anakumana nawo. Mario anaganiza zoti awerenge buku lonse la Yobu. Ndiyeno mlongoyo anamutumizira linki ya Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Zotsatira zake, Mario anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndipo anasangalala kuphunzira zambiri zokhudza Mulungu wachikondi, yemwe anamusonyeza chidwi.
17. N’chifukwa chiyani timathokoza Yehova polola kuti buku la Yobu likhale mbali ya Mawu ake ouziridwa? (Yobu 34:12)
17 Kunena zoona, Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yothandiza anthu kuphatikizapo amene akukumana ndi mavuto. (Aheb. 4:12) Timathokoza kwambiri Yehova chifukwa anaika nkhani ya Yobu m’Mawu ake. (Yobu 19:23, 24) Buku la Yobu limatitsimikizira kuti “ndithudi, Mulungu sachita zoipa.” (Werengani Yobu 34:12.) Limatiphunzitsanso chifukwa chake Mulungu amalola kuti tizivutika, zimene tingachite kuti tizipirira komanso limatithandiza kuti tizilimbikitsa anthu amene akukumana ndi mavuto. Munkhani yotsatira, tidzakambirana mmene buku la Yobu lingatithandizire tikamapereka malangizo.
NYIMBO NA. 156 Ndi Maso a Chikhulupiro
a Zikuoneka kuti Yobu anakhala ndi moyo pa nthawi imene mtumiki wokhulupirika Yosefe anamwalira (mu 1657 B.C.E.) kudzafika nthawi imene Mose anaikidwa kukhala mtsogoleri wa Aisiraeli. (cha m’ma 1514 B.C.E.) N’kutheka kuti nthawi imeneyi ndi imene Yehova ankakambirana ndi Satana zokhudza Yobu komanso ndi nthawi imene Yobuyo anakumana ndi mayesero.
b Mayina ena asinthidwa.