NKHANI YOPHUNZIRA 50
NYIMBO NA. 48 Tiziyenda ndi Yehova Tsiku Lililonse
Muzitsanzira Yehova pa Nkhani Yodzichepetsa
“Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa.”—AEF. 5:1.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana njira 4 za mmene tingatsanzirire Yehova pa nkhani yodzichepetsa.
1. N’chifukwa chiyani kudzichepetsa kwa Yehova n’kochititsa chidwi?
MUKAMAONA anthu audindo masiku ano, kodi mumaona kuti ndi odzichepetsa? Osati kwenikweni. Koma Yehova yemwe ndi wamphamvuyonse ndi wodzichepetsa. (Sal. 113:5-8) Palibe munthu wodzichepetsa kuposa Yehova, iye si wodzikuza ngakhale pang’ono. Munkhaniyi, tikambirana njira 4 zimene Yehova amasonyezera kuti ndi wodzichepetsa kwambiri. Tionanso mmene Yesu anatsanzirira Atate wake pa nkhani yodzichepetsa. Zimenezi zitithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova komanso kuti tizikhala odzichepetsa kwambiri ngati iyeyo.
YEHOVA NDI WOFIKIRIKA
2. Kodi lemba la Salimo 62:8 limatiuza chiyani zokhudza Yehova? (Onaninso chapachikuto.)
2 Nthawi zambiri anthu onyada amakhala osafikirika. Iwo amachita zinthu mopanda chifundo chifukwa chodziona kuti ndi apamwamba ndipo zimenezi zimapangitsa kuti ena aziwapewa. Koma Yehova ndi wosiyana kwambiri ndi anthu amenewa. Iye ndi wodzichepetsa ndipo sitivutika kufika kwa iye n’kumuuza zamumtima mwathu. (Werengani Salimo 62:8.) Mofanana ndi bambo wachikondi amene amakhala wokonzeka kumvetsera nkhawa za ana ake, Yehovanso ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero athu. Ndipotu anachititsa kuti mapemphero ambiri a atumiki ake alembedwe m’Baibulo, kusonyeza kuti ndi wofikirika kwambiri. (Yos. 10:12-14; 1 Sam. 1:10-18) Koma kodi tingatani ngati nthawi zina timadziona kuti ndife osayenera kulankhula ndi Yehova?
Potsanzira Yehova, bambo akumvetsera modzichepetsa mwana wake amene waphwanya mphika wamaluwa pamene amasewera (Onani ndime 2)
3. N’chiyani chimatitsimikizira kuti Yehova amafuna kuti tizipemphera kwa iye nthawi zonse?
3 Tingapemphere kwa Yehova ngakhale pamene tikuona kuti ndife osayenera kuti azitikonda. N’chifukwa chiyani tikutero? Mufanizo la mwana wolowerera, Yesu anayerekezera Yehova ndi bambo wachifundo, amene mwana wake analakwitsa zinthu moti ankadzimva kuti ndi wosayenera ndipo bambo ake sangamulole kubwereranso panyumba. Ndiye kodi bambowo anatani mwanayo atabwerera kunyumba? Yesu ananena kuti bambowo atangoona mwanayo “anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa mwachikondi.” (Luka 15:17-20) Yehova ali ngati bambo ameneyu. Chifukwa choti ndi wodzichepetsa, akangomva anthu amene akudzimvera chisoni chifukwa cha zolakwa zimene anachita kapena nkhawa akupemphera, amawamvetsera mwatcheru. (Maliro 3:19, 20) Iye amawathamangira mwachifundo ngati mmene anachitira bambo uja, n’kukawalimbikitsa komanso kuwatsimikizira kuti amawakonda ndipo awachitira chifundo. (Yes. 57:15) Koma kodi Yehova ‘amatithamangira’ bwanji masiku ano? Iye amagwiritsa ntchito akulu, achibale athu amene ndi a Mboni komanso Akhristu anzathu. (Yak. 5:14, 15) Yehova amachita zonsezi chifukwa amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi.
4. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wofikirika?
4 Yesu amatsanzira Atate wake. Iye ndi wodzichepetsa ngati Atate wake. N’chifukwa chake ali padzikoli, anthu ankamufikira momasuka. Iwo sankaopa kumufunsa mafunso. (Maliko 4:10, 11) Akapempha anthu kuti afotokoze maganizo awo pa nkhani inayake, iwo ankafotokoza momasuka mmene ankamvera. (Mat. 16:13-16) Ndipo akalakwitsa zinthu sankachita mantha kuti awakalipira chifukwa ankadziwa kuti Yesu ndi wachifundo, wokoma mtima komanso woleza mtima. (Mat. 17:24-27) N’zosadabwitsa kuti otsatira ake anadziwa bwino Yehova chifukwa Yesu ankatsanzira kwambiri Atate wake. (Yoh. 14:9) Iwo anadziwa kuti Yehova sanali ngati atsogoleri awo achipembedzo omwe anali ankhanza, onyada komanso odzikweza. M’malomwake iye ndi wodzichepetsa komanso wofikirika.
5. Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kuti tikhale ofikirika?
5 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova? Tikamayesetsa kukhala odzichepetsa zimakhala zosavuta kuti tikhalenso ofikirika. Kudzichepetsa kungatithandize kuti tipewe makhalidwe amene amachititsa kuti tisakhale ofikirika monga nsanje, kunyada komanso kusakhululuka. Kungatithandizenso kuti tikhale achifundo, oleza mtima komanso okhululuka. Makhalidwe amenewa amapangitsa kuti anthu asamavutike kutifikira. (Akol. 3:12-14) Makamaka akulu ayenera kuyesetsa kuti akhale ofikirika. Kuti zimenezi zitheke, iwo ayenera kumapezeka pakati pa abale ndi alongo. Kutanthauza kuti ayenera kuyesetsa kumapezeka pamisonkhano ya pamasom’pamaso m’malo momvetsera pazipangizo zamakono popanda zifukwa zomveka. Ngati n’zotheka, ayenera kuyesetsa kumalowa nawo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Zimenezi zingapangitse kuti abale ndi alongo aziwadziwa bwino n’kumamasuka kuwapempha thandizo.
YEHOVA NDI WOLOLERA
6-7. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yehova ndi wokonzeka kusintha atumiki ake akamupempha zinazake.
6 Anthu ambiri onyada salolera akamachita zinthu ndi ena. Koma ngakhale kuti Yehova ndi wapamwamba kuposa aliyense, iye ndi wodzichepetsa, wololera komanso wokonzeka kusintha. Taganizirani mmene anachitira zinthu ndi Miriamu, yemwe anali mchemwali wake wa Mose. Iye limodzi ndi Aroni ankadandaula zokhudza Mose, yemwe ankaimira Yehova. Pamenepatu tingati Miriamu sanalemekeza Yehova. Zotsatira zake Yehova anamukwiyira ndipo anamudwalitsa khate. Koma pamene Aroni anachonderera m’malo mwa Miriamu, komanso Mose atapempha Yehova kuti achiritse mchemwali wawoyo, kodi Mulungu anatani? Chifukwa chakuti Yehova ndi wodzichepetsa anamvera zimene Aroni ndi Mose ananena ndipo anasintha chilango chimene anapatsa Miriamu n’kumuchiritsa.—Num. 12:1-15.
7 Yehova anasonyezanso kudzichepetsa mmene anachitira zinthu ndi Mfumu Hezekiya. Kudzera mwa mneneri, Yehova anauza Mfumu Hezekiya kuti afa. Hezekiya anapempha Yehova akulira kuti amuchiritse. Yehova anamuyankha ndipo anamuwonjezera zaka zina 15. (2 Maf. 20:1, 5, 6) Kudzichepetsa kunachititsa Yehova kuti achite zinthu mwachifundo komanso mololera.
8. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yesu ndi wololera? (Maliko 3:1-6)
8 Yesu amatsanzira Atate wake. Ali padzikoli, Yesu ankachitira ena zabwino akafunika thandizo. Mwachitsanzo, anachiritsa anthu pa tsiku la Sabata ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo omwe anali ouma mtima sankafuna kuti achite zimenezo. (Werengani Maliko 3:1-6.) Monga mutu wampingo wa Chikhristu, Yesu ndi wololera ndipo amachita zinthu mwachifundo. Mwachitsanzo, munthu wina mumpingo akachita tchimo lalikulu amamulezera mtima komanso kumupatsa nthawi yokwanira kuti alape.—Chiv. 2:2-5.
9. Kodi tingatani kuti tikhale ololera? (Onaninso zithunzi.)
9 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova? Tiyenera kuyesetsa kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu ngati Yehova pa nkhani yololera. (Yak. 3:17) Makolo amene amatsanzira Yehova sangayembekezere kuti ana awo azichita zinthu zimene sangakwanitse. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yakobo ndipo nkhani yake ili pa Genesis 33:12-14. Makolo odzichepetsa komanso ololera akuyenera kuyesetsa kuti azipewa kuyerekezera zimene mwana wawo amachita ndi zimene mwana wawo wina amachita. Nawonso akulu amafunika kukhala ololera. Njira imodzi imene angachitire zimenezi ndi kuvomereza zimene akulu ambiri asankha ngati kuchita zimenezi sikukuphwanya mfundo za m’Baibulo. (1 Tim. 3:2, 3) Ndipo tonsefe tiyenera kuyesetsa kumvetsera maganizo a ena ngakhale kuti timaona zinthu mosiyana. (Aroma 14:1) Tonse mumpingo tiyenera kuyesetsa kuti ‘anthu onse azidziwa kuti ndife ololera.’—Afil. 4:5.
Bambo akusonyeza kuti ndi wololera posayembekezera kuti ana ake achite zambiri mu utumiki (Onani ndime 9)
YEHOVA NDI WOLEZA MTIMA
10. Kodi Yehova amasonyeza kuti ndi woleza mtima m’njira ziti?
10 Mwina munaonapo kuti anthu onyada nthawi zambiri sasangalala akauzidwa kuti adikire. Kunyada kumapangitsa kuti asamaleze mtima. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi Yehova. Iye ndi woleza mtima kwambiri kuposa aliyense. Mwachitsanzo, m’nthawi ya Nowa Yehova ananena kuti adikira zaka 120 asanawononge anthu oipa. (Gen. 6:3) Zimenezi zinathandiza kuti Nowa akhale ndi nthawi yobereka, kulera ana komanso kumanga chingalawa limodzi ndi banja lake. Patapita nthawi mngelo wa Yehova anamvetsera Abulahamu moleza mtima pamene ankamufunsa zokhudza kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora. Akanakhala wonyada akananena kuti, ‘N’chifukwa chiyani ukundifunsa mafunso onsewa?’ Koma potsanzira Yehova, mngeloyu anamulezera mtima Abulahamu.—Gen. 18:20-33.
11. Mogwirizana ndi 2 Petulo 3:9, n’chifukwa chiyani Yehova akuchita zinthu moleza mtima masiku ano?
11 Masiku anonso Yehova akusonyeza kuleza mtima. Iye akudikira kuti nthawi imene anaisankha kuti abweretse mapeto ifike. N’chifukwa chiyani akuleza mtima? “Chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.” (Werengani 2 Petulo 3:9) Kodi kuleza mtima kwa Yehova kwangopita pachabe? Ayi. Pali anthu mamiliyoni ambiri a mtima wabwino amene asankha kukhala anzake ndipo tikuyembekezera kuti enanso ambiri achita chimodzimodzi. Komabe kuleza mtima kwa Yehova kuli ndi malire. Iye amakonda anthu koma si wolekerera ndipo sadzalola kuti anthu oipa apitirize kukhalapo mpaka kalekale.—Hab. 2:3.
12. Kodi Yesu amatsanzira bwanji kuleza mtima kwa Yehova?
12 Yesu amatsanzira Atate wake. Iye wakhala akutsanzira kuleza mtima kwa Yehova kwa zaka masauzande ambiri. Yesu wakhala akuona Satana akunena mabodza oipa kwambiri okhudza Yehova komanso atumiki ake okhulupirika. (Gen. 3:4, 5; Yobu 1:11; Chiv. 12:10) Iye wakhalanso akuona anthu ambiri akuvutika koopsa ndipo ayenera kuti akufunitsitsa “kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yoh. 3:8) N’chiyani chikuthandiza Yesu kudikira moleza mtima kuti Yehova amupatse chilolezo choti awononge ntchito za Mdyerekezi mpaka kalekale? Chifukwa chimodzi n’chakuti Yesu ndi wodzichepetsa. Iye akudziwa kuti Yehova yekha ndi amene ali ndi udindo wosankha nthawi yoti mapeto adzikoli afike.—Mac. 1:7.
13. Kodi Yesu anasonyeza kuleza mtima kwa atumwi ake m’njira ziti, nanga n’chifukwa chiyani?
13 Yesu ali padzikoli ankachitanso zinthu moleza mtima ndi atumwi ake. Mwachitsanzo, pamene ankakangana kuti wamkulu ndi ndani, Yesu sanawaone kuti ndi okanika, koma anapitiriza kuwalezera mtima. (Luka 9:46; 22:24-27) Iye ankakhulupirira kuti adzasintha n’kukhala odzichepetsa. Kodi inunso mwakhala mukulakwitsa zinazake mobwerezabwereza? Ngati ndi choncho, kodi mumayamikira kuti muli ndi Mfumu yodzichepetsa komanso yoleza mtima?
14. Kodi tingatani kuti tikhale oleza mtima?
14 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova? Tikamakhala ndi maganizo a Khristu zimakhala zosavuta kuti tiziganiza komanso kuchita zinthu ngati Yehova. (1 Akor. 2:16) N’chiyani chingatithandize kuti tiziganiza ngati Khristu? Palibe chidule pa nkhaniyi. Tiziwerenga mabuku a Uthenga Wabwino, tiziganizira zimene tawerengazo n’kuona mmene zikutithandizira kudziwa maganizo a Yesu pa nkhani zosiyanasiyana. Tizipempha Yehova kuti atithandize kukhala odzichepetsa komanso oleza mtima ngati Yesu. Tikakhala ndi maganizo a Khristu tidzayesetsa kutsanzira Yehova pa nkhani yodzilezera mtima ifeyo komanso anthu ena.—Mat. 18:26-30, 35.
YEHOVA AMALEMEKEZA ANTHU ODZICHEPETSA
15. Kodi Yehova wachita bwanji zinthu mogwirizana ndi mawu opezeka pa Salimo 138:6?
15 Werengani Salimo 138:6. Anthu odzichepetsa ali ndi mwayi waukulu chifukwa amadziwidwa ndi Wolamulira Wamkulu wachilengedwe chonse. Tiona zitsanzo zochepa za anthu odzichepetsa amene Yehova anawalemekeza m’mbuyomu. Ena mwa anthuwa sitikuwadziwa bwinobwino koma nkhani zawo zinalembedwa m’Baibulo. Yehova anauzira Mose kulemba nkhani ya kapolo wina wokhulupirika dzina lake Debora. Iye anagwira ntchito mokhulupirika kubanja la Isaki komanso Yakobo kwa zaka 125. Ngakhale kuti sitikudziwa zambiri zokhudza mayiyu, Yehova anaonetsetsa kuti Mose alembe m’Baibulo zinthu zokhudza mmene anthu ankamukondera. (Gen. 24:59; 35:8, mawu a m’munsi) Patadutsa zaka zambiri, Yehova anasankha m’busa wachinyamata dzina lake Davide kuti akhale mfumu ya mtundu wa Aisiraeli. (2 Sam. 22:1, 36) Yesu atangobadwa kumene, Yehova analemekeza abusa odzichepetsa powatumizira angelo kuti akawadziwitse zoti mumzinda wapafupi wa Betelehemu, mwabadwa mwana yemwe adzakhale Mesiya. (Luka 2:8-11) Komanso Yosefe ndi Mariya atapita ndi Yesu kukachisi, Yehova analemekeza Simiyoni ndi Anna omwe anali achikulire powaonetsa Mwana wake. (Luka 2:25-30, 36-38) Izitu zikusonyeza kuti “ngakhale kuti Yehova ali pamwamba amaona wodzichepetsa.”
16. Kodi Yesu anatsanzira bwanji mmene Atate wake amachitira zinthu ndi ena?
16 Yesu amatsanzira Atate wake. Mofanana ndi Atate wake, Yesu ankalemekeza anthu odzichepetsa. Iye ankaphunzitsa anthu “osaphunzira komanso anthu wamba” choonadi chokhudza Ufumu wa Mulungu. (Mac. 4:13; Mat. 11:25) Yesu ankachiritsa odwala ndipo akamawachiritsa, ankawalemekezanso. (Luka 5:13) Pa usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake, yomwe inali ntchito ya akapolo. (Yoh. 13:5.) Komanso asanapite kumwamba, analemekeza otsatira ake onse amene analipo pa nthawiyo komanso am’tsogolo powapatsa ntchito yofunika kwambiri kuposa iliyonse, yothandiza anthu kudzapeza moyo wosatha.—Mat. 28:19, 20.
17. Kodi tingatani kuti tizilemekeza ena? (Onaninso chithunzi.)
17 Kodi tingatsanzire bwanji Yehova? Timasonyeza kuti timalemekeza anthu powauza uthenga wabwino posatengera mtundu, chikhalidwe, kumene akuchokera komanso maphunziro awo. Timalemekezanso abale ndi alongo tikamaona kuti amatiposa posatengera maudindo kapena maluso amene tili nawo. (Afil. 2:3.) Yehova amasangalala akaona kuti modzichepetsa ‘tikuyamba ndi ifeyo’ kulemekeza ena m’njira zimenezi komanso m’njira zina.—Aroma 12:10; Zef. 3:12.
Timatsanzira Yehova pa nkhani yodzichepetsa tikamauza anthu amitundu yonse uthenga wabwino (Onani ndime 17)a
18. N’chifukwa chiyani tikufunikira kutsanzira Yehova pa nkhani yodzichepetsa?
18 Tikamayesetsa kutsanzira Atate wathu pa nkhani yodzichepetsa, tidzakhala ofikirika, ololera komanso oleza mtima kwambiri. Ndipo tidzayesetsa kulemekeza ena ngati mmene Yehova amachitira. Tikamachita zomwe tingathe kuti tikhale ngati Mulungu wathu yemwe ndi wodzichepetsa, timakhala amtengo wapatali kwambiri pamaso pake.—Yes. 43:4.
NYIMBO NA. 159 Mpatseni Yehova Ulemerero
a MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI : Alongo akutsanzira Yehova pa nkhani yodzichepetsa pamene akulalikira akaidi.