Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • hdu nkhani 30
  • Kusamalira Nyumba za Ufumu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusamalira Nyumba za Ufumu
  • Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ntchito Yosamalira Nyumba za Ufumu Imakonzedwa Bwanji?
  • Kulipira Ndiponso Kugula Zinthu Zofunika
  • Ntchito Zikuluzikulu
  • Kusamalira Nyumba ya Ufumu Kumachititsa Kuti Yehova Alemekezedwe
  • Kodi Mungathandize Bwanji?
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Malo Olambirira Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Onani Zambiri
Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
hdu nkhani 30
M’bale amene ali pakatawala akuchotsa masamba padenga.

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Kusamalira Nyumba za Ufumu

APRIL 1, 2024

Mlongo wina wachitsikana wa ku Colombia, dzina lake Nicole ananena kuti: “Nyumba ya Ufumu yathu ndimaikonda kwambiri. Ndi malo amene ndingakonde kumakhalako ndi abale ndi alongo anga.” Kodi inunso mumamva choncho?

Padziko lonse, a Mboni za Yehova amasonkhana m’Nyumba za Ufumu zomwe zilipo pafupifupi 63,000. Nyumba zimenezi ndi malo abwino kwambiri omwe timalambiriramo Mulungu. Koma nyumbazi zimagwira ntchito zinanso zambiri. Mpainiya wina wa ku Colombia dzina lake David ananena kuti: “Nyumba ya Ufumu yathu imakometsera zimene timaphunzitsa. Alendo ambiri amadabwa akaona mmene timasamalira nyumbayi kuti izionekabe bwino.” Timachita khama pogwira ntchito yoyeretsa komanso kusamalira Nyumba za Ufumu. Kodi ntchito imeneyi imachitika bwanji?

Kodi Ntchito Yosamalira Nyumba za Ufumu Imakonzedwa Bwanji?

Mipingo imene imasonkhana pa Nyumba ya Ufumu ndi imene imakhala ndi udindo woisamalira. Abale ndi alongo amayeretsa Nyumba ya Ufumuyo pafupipafupi. Iwo amakonzanso zinthu zomwe zingayambitse ngozi kapena zinthu zing’onozing’ono zimene zawonongeka.

Pofuna kuthandiza mipingo, Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga (LDC), imasankha abale oti aziphunzitsa abale ndi alongo m’mipingo, mmene angasamalirire Nyumba za Ufumu. M’bale mmodzi amathandiza ofalitsa a Nyumba za Ufumu 6 kapena 10. Iye amayendera komanso kuphunzitsa ofalitsa mmene angasamalirire Nyumba ya Ufumu yawo. Pakatha zaka zitatu zilizonse, iye amayendera Nyumba ya Ufumu iliyonse n’kuona ngati pali zinthu zomwe zingayambitse ngozi kapena zimene zikufunika kukonza.

M’bale akuphunzitsa abale ndi alongo mmene angasamalire Nyumba ya Ufumu.

Abale amene amaphunzitsa kusamalira Nyumba za Ufumu amathandiza kuti nyumbazi zizioneka bwino

Abale ndi alongo amayamikira kwambiri maphunziro amene amalandira kwa abale ophunzitsa kusamalira Nyumba za Ufumu. Mlongo wina wa ku India dzina lake Indhumathi, anati: “Maphunzirowa anali abwino. Ndipo zinali zosangalatsa kuphunzira mmene tingasamalirire Nyumba ya Ufumu yathu kuti izioneka bwino.” M’bale wina wa ku Kenya dzina lake Evans, ananena kuti: “Tinaphunzira mmene tingapewere kuwononga ndalama zambiri, pokonza mavuto ang’onoang’ono asanafike pokhala mavuto aakulu.”

Kulipira Ndiponso Kugula Zinthu Zofunika

Ndalamaa zimene zimagwiritsidwa ntchito pachaka pokonza ndi kusamalira Nyumba ya Ufumu, zingakhale zambiri kapena zochepa potengera kumene Nyumba ya Ufumuyo ili, zaka zake komanso kuchuluka kwa mipingo yomwe imagwiritsa ntchito nyumbayo. Ndiye kodi ndalamazi zimapezeka bwanji?

Ndalama zimene zimagwiritsidwa ntchito posamalira Nyumba ya Ufumu, ndi zimene anthu amapereka mwakufuna kwawo. M’bale wina wa ku Kazakhstan dzina lake Alexander, anafotokoza kuti: “Ndalamazi zimagwiritsidwa ntchito polipira madzi, magetsi komanso intaneti. Ndipo ndalama zina zimagwiritsidwa ntchito kugula zinthu monga matishu, magulovesi, zinthu zoyeretsera komanso penti.” Ndipo ndalama zina zimatumizidwa kuti zikathandize pantchito yapadziko lonse, monga pantchito zikuluzikulu zomanga kapena kukonza malo olambirira, zomwe zimafuna ndalama zambiri.

Ntchito Zikuluzikulu

Ngati pakufunika kukonza kapena kusamalira Nyumba ya Ufumu, ndipo ndalama zimene zigwiritsidwe ntchito ndi zoposa zimene zimagwiritsidwa ntchito posamalira nyumbayo kwa miyezi iwiri kapena itatu, akulu amadziwitsa m’bale wa LDC wophunzitsa kusamalira Nyumba za Ufumu. Abale a LDC akavomereza, ndalama yogwirira ntchitoyo imachoka kuthumba la ntchito yapadziko lonse. M’chaka cha utumiki cha 2023, panachitika ntchito ngati zimenezi zokwana 8,793, ndipo ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito zinali zokwana madola 76.6 miliyoni. Tiyeni tione ziwiri mwa ntchitozi.

Ku Angola, Nyumba ya Ufumu ina yomwe inatha zaka 15 inali ndi mavuto ena. Mawaya amagetsi m’nyumbayi ankafunika kusinthidwa, khoma lake linali ndi ming’alu ndipo anthu oyandikana ndi nyumbayi ankadandaula za madzi a mvula omwe ankayenderera kupita kunyumba zawo. Abale a LDC anavomereza kuti pakhale ntchito yokonza mavuto amenewo. Ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchito zinali madola 9,285. Anthu oyandikana ndi Nyumba ya Ufumuyi anayamikira ndipo anachita chidwi ndi mmene ntchitoyi inayendera.

Nyumba ya Ufumu yokonzedwanso ku Angola

Ku Poland, Nyumba ya Ufumu ina inkadontha, ndipo kalapeti inawonongeka kwambiri. Abale a LDC anavomereza ntchito yokonza denga komanso kuika kalapeti ina. Ntchitoyi inali ya ndalama zokwana madola 9,757. Pachifukwa chimenechi, pa Nyumba ya Ufumuyi sipadzafunikanso ntchito yaikulu yokonza kwa zaka zingapo.

Zithunzi: 1. Abale awiri akutsuka denga la Nyumba ya Ufumu. 2. M’Nyumba ya Ufumu yomweyo, abale akuchotsa kalapeti.

Ntchito yokonzanso Nyumba ya Ufumu ku Poland

Kusamalira Nyumba ya Ufumu Kumachititsa Kuti Yehova Alemekezedwe

Sikuti ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu imangothandiza kuti ndalama zimene abale amapereka zisamawonongeke koma imathandizanso kuti Yehova azitamandidwa. M’bale wina wa ku Tonga dzina lake Shaun, ananena kuti: “Chifukwa cha ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu, timasonkhana m’malo abwino komanso aukhondo ndipo zimenezi zimathandiza kuti anthu a m’deralo aziganizira za Yehova. Timasangalalanso kuitanira anthu ku Nyumba ya Ufumu yathu.”

Kodi Mungathandize Bwanji?

Tonsefe tingathandize poyeretsa komanso kusamalira malo athu olambirira. Marino, yemwe amaphunzitsa kusamalira Nyumba za Ufumu ku Australia, anati: “Aliyense ali ndi mwayi wothandiza nawo posamalira Nyumba za Ufumu. Tikatero, timakhala tikuthandiza kuti ndalama zimene abale amapereka zisamawonongeke komanso kuti zizigwira ntchito pa zinthu zofunika.”

M’bale wina wa ku India dzina lake Joel, amasangalala kugwira nawo ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu yawo. Iye anati: “Kugwira ntchito limodzi ndi abale kumandithandiza kuona mmene zidzakhalire m’dziko latsopano.” Nicole, yemwe tinamutchula kale uja, ananena kuti: “Chaposachedwapa ndinathandiza kukolopa pamene abale amakonza paipi mutoileti. Ngakhale kuti sindinakonze nawo vutolo, ndinaona kuti ndathandiza kuti pasachitike ngozi.”

Ngati mukufuna kumathandiza nawo pa ntchito yokonza Nyumba ya Ufumu yanu, mungauze akulu amumpingo wanu. Kuwonjezera pamenepo, zopereka zanu zimathandiza pokonza Nyumba ya Ufumu yanu komanso Nyumba za Ufumu zina padziko lonse. Mungapereke ndalama poponya m’mabokosi a zopereka omwe ali m’Nyumba ya Ufumu yanu kapenanso kudzera pa donate.jw.org. Timayamikira kwambiri mtima wanu wopereka mowolowa manja.

Abale ndi alongo akuyeretsa m’Nyumba ya Ufumu pomwe m’bale wina akukonza mpando womwe wawonongeka.

Tonsefe tingathandize kusamalira Nyumba za Ufumu

a Ndalama zonse zotchulidwa munkhaniyi ndi madola a ku America.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena