LUKA
ZIMENE ZILI MʼBUKULI
1
Kalata yopita kwa a Teofilo (1-4)
Gabrieli ananeneratu za kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi (5-25)
Gabrieli ananeneratu za kubadwa kwa Yesu (26-38)
Mariya anapita kwa Elizabeti (39-45)
Mariya analemekeza Yehova (46-56)
Kubadwa kwa Yohane komanso mmene anamupatsira dzina (57-66)
Ulosi wa Zekariya (67-80)
2
Kubadwa kwa Yesu (1-7)
Angelo anaonekera kwa abusa (8-20)
Mdulidwe komanso kuyeretsedwa (21-24)
Simiyoni anaona Khristu (25-35)
Anna analankhula zokhudza mwanayo (36-38)
Anabwerera ku Nazareti (39, 40)
Yesu anapita kukachisi ali ndi zaka 12 (41-52)
3
Chiyambi cha ntchito ya Yohane (1, 2)
Yohane ankalimbikitsa anthu kuti abatizidwe (3-20)
Kubatizidwa kwa Yesu (21, 22)
Mzere wa makolo a Yesu Khristu (23-38)
4
Mdyerekezi anayesa Yesu (1-13)
Yesu anayamba kulalikira ku Galileya (14, 15)
Yesu anakanidwa ku Nazareti (16-30)
Zimene zinachitika musunagoge ku Kaperenao (31-37)
Apongozi a Simoni ndi anthu ena anachiritsidwa (38-41)
Gulu la anthu linapeza Yesu ali kwayekha (42-44)
5
Anagwira nsomba mozizwitsa; ophunzira oyambirira (1-11)
Munthu wakhate anachiritsidwa (12-16)
Yesu anachiritsa munthu wakufa ziwalo (17-26)
Yesu anaitana Levi (27-32)
Funso lokhudza kusala kudya (33-39)
6
Yesu ndi “Mbuye wa Sabata” (1-5)
Munthu wolumala dzanja anachiritsidwa (6-11)
Atumwi 12 (12-16)
Yesu ankaphunzitsa komanso kuchiritsa anthu (17-19)
Anthu osangalala komanso amene ali ndi tsoka (20-26)
Kukonda adani (27-36)
Siyani kuweruza (37-42)
Umadziwika ndi zipatso zake (43-45)
Nyumba yomangidwa bwino; nyumba yopanda maziko olimba (46-49)
7
Chikhulupiriro cha mtsogoleri wa asilikali (1-10)
Yesu anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye ku Naini (11-17)
Yohane Mʼbatizi anatamandidwa (18-30)
Anadzudzula mʼbadwo wosamvera (31-35)
Mkazi wochimwa anakhululukidwa (36-50)
8
Azimayi ankayenda ndi Yesu (1-3)
Fanizo la wofesa mbewu (4-8)
Chifukwa chake Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo (9, 10)
Anafotokoza tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (11-15)
Munthu akayatsa nyale saivundikira (16-18)
Amayi ake a Yesu komanso azichimwene ake (19-21)
Yesu analetsa mphepo yamphamvu (22-25)
Yesu anatumiza ziwanda munkhumba (26-39)
Mwana wamkazi wa Yairo; mzimayi anagwira chovala cha Yesu (40-56)
9
Atumwi 12 anapatsidwa malangizo okhudza utumiki (1-6)
Herode anathedwa nzeru ndi zimene Yesu ankachita (7-9)
Yesu anadyetsa anthu 5,000 (10-17)
Petulo anazindikira kuti Yesu ndi Khristu (18-20)
Yesu ananeneratu za imfa yake (21, 22)
Wophunzira weniweni wa Yesu (23-27)
Yesu anasintha maonekedwe ake (28-36)
Mnyamata wogwidwa ndi chiwanda anachiritsidwa (37-43a)
Yesu ananeneratu za imfa yake kachiwiri (43b-45)
Ophunzira anakangana kuti wamkulu ndi ndani (46-48)
Amene sakutsutsana nafe ali kumbali yathu (49, 50)
Mudzi wa Asamariya unakana Yesu (51-56)
Zimene munthu angachite kuti akhale wotsatira wa Yesu (57-62)
10
Yesu anatumiza ophunzira 70 (1-12)
Tsoka mizinda yosalapa (13-16)
Ophunzira 70 aja anabwerera (17-20)
Yesu anatamanda Atate wake chifukwa chokomera mtima anthu odzichepetsa (21-24)
Fanizo la Msamariya wachifundo (25-37)
Yesu anapita kwa Marita ndi Mariya (38-42)
11
Mmene tingapempherere (1-13)
Ankatulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu (14-23)
Mizimu yonyansa inabwerera (24-26)
Kusangalala kwenikweni (27, 28)
Chizindikiro cha Yona (29-32)
Nyale ya thupi (33-36)
Tsoka kwa atsogoleri achipembedzo achinyengo (37-54)
12
Zofufumitsa za Afarisi (1-3)
Muziopa Mulungu, osati anthu (4-7)
Kuvomereza kuti ndife ophunzira a Khristu (8-12)
Fanizo la munthu wolemera koma wopusa (13-21)
Siyani kuda nkhawa (22-34)
Kukhala maso (35-40)
Mtumiki woyangʼanira nyumba wokhulupirika komanso wosakhulupirika (41-48)
Sanabweretse mtendere, koma kudzagawanitsa (49-53)
Kufunika kozindikira tanthauzo la zimene zikuchitika (54-56)
Kuthetsa mikangano (57-59)
13
Lapani apo ayi mudzawonongedwa (1-5)
Fanizo la mtengo wa mkuyu wosabereka (6-9)
Mzimayi wopindika msana anachiritsidwa tsiku la Sabata (10-17)
Fanizo la kanjere ka mpiru komanso la zofufumitsa (18-21)
Pakufunika khama kuti tilowe pakhomo lalingʼono (22-30)
Herode ananenedwa kuti “nkhandwe” (31-33)
Yesu analirira Yerusalemu (34, 35)
14
Munthu amene anali ndi manja komanso miyendo yotupa anachiritsidwa tsiku la Sabata (1-6)
Mukakhala mlendo muzidzichepetsa (7-11)
Muziitana anthu amene sangathe kukubwezerani (12-14)
Fanizo la anthu amene anakana kupita kuphwando (15-24)
Zimene zimafunika kuti munthu akhale wophunzira (25-33)
Mchere umene watha mphamvu (34, 35)
15
Fanizo la nkhosa yotayika (1-7)
Fanizo la khobidi lotayika (8-10)
Fanizo la mwana wolowerera (11-32)
16
Fanizo la mtumiki woyangʼanira nyumba wosalungama (1-13)
Chilamulo komanso Ufumu wa Mulungu (14-18)
Fanizo la munthu wolemera ndi Lazaro (19-31)
17
Kupunthwa, kukhululuka ndi chikhulupiriro (1-6)
Akapolo opanda pake (7-10)
Anthu 10 akhate anachiritsidwa (11-19)
Kubwera kwa Ufumu wa Mulungu (20-37)
18
Fanizo la mkazi wamasiye amene anachita khama kupempha (1-8)
Mfarisi komanso wokhometsa msonkho (9-14)
Yesu ndi ana (15-17)
Funso la wolamulira wolemera (18-30)
Yesu ananeneratu za imfa yake kachitatu (31-34)
Wopemphapempha amene anali wosaona anayamba kuona (35-43)
19
Yesu anakacheza kwa Zakeyu (1-10)
Fanizo la ndalama zokwana ma mina 10 (11-27)
Yesu analowa mumzinda mwaulemerero (28-40)
Yesu analirira Yerusalemu (41-44)
Yesu anayeretsa kachisi (45-48)
20
Anthu anakayikira ulamuliro wa Yesu (1-8)
Fanizo la alimi opha anthu (9-19)
Mulungu komanso Kaisara (20-26)
Funso lokhudza kuuka kwa akufa (27-40)
Kodi Khristu ndi mwana wa Davide? (41-44)
Anachenjeza anthu kuti asamale ndi alembi (45-47)
21
Timakobidi tiwiri ta mkazi wamasiye (1-4)
CHIZINDIKIRO CHA ZINTHU ZAMʼTSOGOLO (5-36)
Nkhondo, zivomerezi zamphamvu, miliri, kusowa kwa chakudya (10, 11)
Yerusalemu adzazunguliridwa ndi magulu ankhondo (20)
Nthawi yoikidwiratu ya anthu amitundu ina (24)
Kubwera kwa Mwana wa munthu (27)
Fanizo la mtengo wa mkuyu (29-33)
Khalani maso (34-36)
Yesu anaphunzitsa mʼkachisi (37, 38)
22
Ansembe anakonza chiwembu kuti aphe Yesu (1-6)
Kukonzekera Pasika womaliza (7-13)
Kuyambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (14-20)
“Wondipereka ndili naye limodzi patebulo pompano” (21-23)
Anakangana kwambiri za amene anali wamkulu (24-27)
Pangano la Yesu la ufumu (28-30)
Ananeneratu kuti Petulo adzamukana (31-34)
Kufunika kokhala okonzeka; malupanga awiri (35-38)
Pemphero la Yesu paphiri la Maolivi (39-46)
Yesu anagwidwa (47-53)
Petulo anakana Yesu (54-62)
Yesu anachitiridwa zachipongwe (63-65)
Anamupititsa ku Khoti Lalikulu la Ayuda (66-71)
23
Yesu anaonekera pamaso pa Pilato ndi Herode (1-25)
Yesu anapachikidwa pamtengo limodzi ndi zigawenga ziwiri (26-43)
Imfa ya Yesu (44-49)
Kuikidwa mʼmanda kwa Yesu (50-56)
24
Yesu anaukitsidwa (1-12)
Pamsewu wopita ku Emau (13-35)
Yesu anaonekera kwa ophunzira (36-49)
Yesu anakwera kumwamba (50-53)