UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NDI MALIKO
1 Chiyambi cha uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu: 2 Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mneneri Yesaya kuti: “(Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole* kukakukonzera njira.)*+ 3 Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.’”+ 4 Yohane Mʼbatizi anali mʼchipululu ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ 5 Choncho anthu onse amene ankakhala mʼdera la Yudeya komanso onse amene ankakhala mu Yerusalemu ankapita kwa iye. Yohane ankawabatiza* mumtsinje wa Yorodano ndipo anthuwo ankaulula machimo awo poyera.+ 6 Yohane ankavala chovala chaubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa mʼchiuno mwake+ ndipo ankadya dzombe ndi uchi.+ 7 Iye ankalalikira kuti: “Pambuyo pangapa pakubwera winawake wamphamvu kuposa ine amene sindili woyenera kuwerama nʼkumasula zingwe za nsapato zake.+ 8 Ine ndakubatizani ndi madzi, koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.”+
9 Mʼmasiku amenewo, Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu Yorodano.+ 10 Atangovuuka mʼmadzimo, iye anaona kumwamba kukutseguka ndiponso mzimu ukutsika ngati nkhunda kudzamutera.+ 11 Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”+
12 Nthawi yomweyo mzimuwo unamulimbikitsa kuti apite kuchipululu. 13 Choncho iye anakhala mʼchipululumo masiku 40, akuyesedwa ndi Satana.+ Mʼchipululumo munalinso nyama zakutchire ndipo angelo ankamutumikira.+
14 Yohane atamangidwa, Yesu anapita ku Galileya+ kukalalikira uthenga wabwino wa Mulungu.+ 15 Iye ankanena kuti: “Nthawi yoikidwiratu yakwana ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira. Lapani+ ndipo mukhulupirire uthenga wabwino!”
16 Pamene ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona Simoni ndi Andireya+ mchimwene wake wa Simoniyo, akuponya maukonde awo mʼnyanjamo+ chifukwa anali asodzi.+ 17 Choncho Yesu anawauza kuti: “Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 18 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.+ 19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane, ali mungalawa yawo ndipo ankasoka maukonde awo.+ 20 Nthawi yomweyo anawaitana. Choncho iwo anasiya bambo awo a Zebedayo mʼngalawamo limodzi ndi anthu aganyu ndipo anamutsatira. 21 Onsewo anachoka nʼkupita ku Kaperenao.
Sabata litangoyamba, anakalowa musunagoge nʼkuyamba kuphunzitsa.+ 22 Mmenemo anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu wokhala ndi ulamuliro, osati ngati alembi.+ 23 Pa nthawiyo, mʼsunagoge mwawomo munali munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa, ndipo munthuyo anafuula kuti: 24 “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu!”+ 25 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye!” 26 Choncho mzimu wonyansawo unamuchititsa kuti aphuphe ndipo unafuula mokweza. Kenako unatuluka mwa munthuyo. 27 Ataona zimenezi, anthu onse anadabwa kwambiri moti anayamba kukambirana kuti: “Kodi chimenechi nʼchiyani? Nʼchiphunzitso chatsopano! Ngakhale mizimu yonyansa akuilamula mwamphamvu ndipo ikumumvera.” 28 Choncho mbiri yake inawanda mofulumira kwambiri mʼchigawo chonse cha Galileya.
29 Zitatero iwo anachoka kusunagogeko nʼkupita kunyumba kwa Simoni ndi Andireya. Yakobo ndi Yohane nawonso anapita nawo.+ 30 Koma apongozi aakazi a Simoni+ anali chigonere, akudwala malungo.* Mwamsanga iwo anamuuza za mayiwo. 31 Choncho iye anapita kumene kunali mayiwo ndipo anawagwira dzanja nʼkuwadzutsa. Atatero malungowo anatheratu moti mayiwo anayamba kuwatumikira.
32 Chakumadzulo dzuwa litalowa, anthu anayamba kumubweretsera anthu onse amene ankadwala komanso ogwidwa ndi ziwanda.+ 33 Ndipo anthu onse amumzindawo anasonkhana pakhomopo. 34 Choncho Yesu anachiritsa anthu ambiri amene ankadwala matenda osiyanasiyana+ ndipo anatulutsa ziwanda zambiri. Koma sanalole kuti ziwandazo zilankhule, chifukwa zinkamudziwa kuti ndi Khristu.*
35 Mʼmawa kwambiri kudakali mdima, Yesu anadzuka nʼkutuluka panja ndipo anapita kumalo kopanda anthu. Kumeneko anayamba kupemphera.+ 36 Koma Simoni ndi ena amene anali naye anamufunafuna 37 ndipo anamupeza nʼkumuuza kuti: “Anthu onse akukufunafunani.” 38 Koma iye anawayankha kuti: “Tiyeni tipite kwina. Tipite kumidzi yapafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko, chifukwa ndinabwera kudzachita zimenezi.”+ 39 Iye anapitadi ndipo ankalalikira mʼmasunagoge mwawo mu Galileya monse ndiponso kutulutsa ziwanda.+
40 Kumenekonso munthu wina wakhate anafika kwa iye ndipo anagwada pansi nʼkumuchonderera kuti: “Ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 41 Yesu atamva zimenezo, anagwidwa chifundo moti anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo anamuuza kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.”+ 42 Nthawi yomweyo khate lakelo linatha, ndipo anakhala woyera. 43 Kenako anamupatsa malangizo amphamvu ndipo nthawi yomweyo anamuuza kuti azipita. 44 Anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi, koma upite ukadzionetse kwa wansembe ndipo chifukwa chakuti wayeretsedwa, ukapereke zinthu zimene Mose analamula,+ kuti ukhale umboni kwa iwo.”+ 45 Koma atachoka, munthu uja anayamba kulengeza zimenezo paliponse ndi kufalitsa nkhaniyo mʼmadera ena. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu asathenso kulowa mumzinda uliwonse moonekera moti ankakhala kunja kopanda anthu. Koma anthu ankabwerabe kwa iye kuchokera kumbali zonse.+
2 Koma patapita masiku angapo, Yesu analowanso mu Kaperenao ndipo anthu anamva kuti ali panyumba.+ 2 Choncho anthu ambiri anasonkhana kumeneko moti panalibenso malo okhala, chifukwa anthu anadzaza mpaka pakhomo ndipo anayamba kuwauza uthenga wabwino.+ 3 Ndiyeno kunafika anthu amene anamubweretsera munthu wakufa ziwalo ndipo ananyamulidwa ndi anthu 4.+ 4 Koma sakanatha kumufikitsa kwa Yesu chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho anasasula denga pamene Yesu anali, ndipo ataboola padengapo, anatsitsirapo machira a munthu wakufa ziwalo uja. 5 Yesu ataona chikhulupiriro chawo,+ anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ 6 Tsopano alembi ena anali pomwepo ndipo anayamba kuganiza mʼmitima mwawo+ kuti: 7 “Nʼchifukwa chiyani munthu ameneyu akulankhula chonchi? Akunyozatu Mulungu ameneyu. Ndi ndaninso wina amene angakhululukire machimo, si Mulungu yekha basi?”+ 8 Koma nthawi yomweyo Yesu anazindikira mumtima mwake kuti iwo ankaganiza zimenezo, ndipo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuganiza zinthu zimenezi mʼmitima mwanu?+ 9 Chosavuta nʼchiti, kuuza wakufa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo nyamula machira ako uyendeʼ? 10 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu+ ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo—”+ kenako anauza wakufa ziwalo uja kuti: 11 “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa ndipo uzipita kwanu.” 12 Zitatero munthuyo ananyamuka ndipo nthawi yomweyo ananyamula machira akewo nʼkuyenda yekha pamaso pa anthu onse. Choncho onsewo anadabwa kwambiri ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Zoterezi sitinazionepo.”+
13 Kenako iye anapitanso mʼmbali mwa nyanja. Gulu lonse la anthu linapitiriza kupita kwa iye ndipo anayamba kuwaphunzitsa. 14 Akudutsa anaona Levi mwana wa Alifeyo atakhala mu ofesi yokhomeramo msonkho ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Nthawi yomweyo ananyamuka nʼkumutsatira.+ 15 Nthawi inayake, ankadya chakudya* mʼnyumba mwa Levi ndipo anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ankadya limodzi ndi Yesu ndiponso ophunzira ake. Kumeneko kunali anthu ambiri amene ankamutsatira.+ 16 Koma alembi a Afarisi, ataona kuti Yesu akudya limodzi ndi anthu ochimwa ndi okhometsa msonkho, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Bwanji akudya limodzi ndi okhometsa msonkho komanso anthu ochimwa?” 17 Yesu atamva zimenezi anawayankha kuti: “Anthu amphamvu safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”+
18 Ophunzira a Yohane ndi Afarisi ankasala kudya. Choncho iwo anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 19 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati+ safunika kusala kudya ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, si choncho kodi? Ngati mkwatiyo ali nawo limodzi sangasale kudya. 20 Koma masiku akubwera pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo+ ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya. 21 Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimakoka nʼkungʼamba malaya akalewo ndipo kungʼambikako kumawonjezereka kwambiri.+ 22 Ndiponso, palibe munthu amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa akale. Akachita zimenezo, vinyoyo amaphulitsa matumbawo. Kenako vinyoyo amatayika ndipo matumbawo amawonongeka. Koma anthu amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa atsopano.”
23 Yesu akudutsa mʼminda ya tirigu pa tsiku la Sabata, ophunzira ake anayamba kubudula ngala za tirigu nʼkumadya.+ 24 Choncho Afarisi anamuuza kuti: “Taona! Nʼchifukwa chiyani akuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata?” 25 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala ndipo analibiretu chilichonse?+ 26 Nkhani yonena za Abiyatara+ wansembe wamkulu imanena kuti, Davide analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* umene aliyense sankayenera kudya malinga ndi malamulo koma ansembe okha.+ Iye anatenga mitanda ina ya mkatewo nʼkupatsa amuna amene anali naye limodzi. Kodi inu simunawerenge nkhani imeneyi?” 27 Kenako anawauza kuti: “Sabata linakhalako chifukwa cha munthu,+ osati munthu chifukwa cha Sabata. 28 Choncho Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+
3 Kachiwirinso Yesu analowa musunagoge. Mmenemo munali munthu wolumala dzanja.+ 2 Ndiyeno Afarisi ankamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa Sabata nʼcholinga choti amuimbe mlandu. 3 Ndipo iye anauza munthu wolumala dzanjayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.” 4 Kenako anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiyani pa Sabata, chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ Koma iwo anangokhala chete. 5 Yesu anawayangʼana mokwiya ndipo anamva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.+ Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhala labwinobwino. 6 Ataona zimenezi Afarisiwo anatuluka ndipo nthawi yomweyo anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi anthu amene ankatsatira Herode+ kuti amuphe.
7 Koma Yesu ndi ophunzira ake anachoka nʼkupita kunyanja ndipo chigulu cha anthu ochokera ku Galileya ndi ku Yudeya chinamutsatira.+ 8 Ngakhalenso anthu ambiri ochokera ku Yerusalemu, ku Idumeya, kutsidya la Yorodano komanso ochokera mʼmadera a ku Turo ndi Sidoni, anamva zonse zimene iye ankachita ndipo anapita kwa iye. 9 Ndipo iye anauza ophunzira ake kuti amubweretsere ngalawa yaingʼono yoti akweremo kuti gulu la anthulo lisamupanikize. 10 Popeza anali atachiritsa anthu ambiri, onse amene anali ndi matenda aakulu anamuunjirira kuti angomukhudza.+ 11 Ngakhalenso mizimu yonyansa,+ inkati ikamuona, inkadzigwetsa pansi pamaso pake nʼkufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”+ 12 Koma mobwerezabwereza iye anailamula mwamphamvu kuti isamuulule.+
13 Kenako anakwera phiri nʼkuitana anthu amene ankawafuna+ ndipo iwo anapita kwa iye.+ 14 Ndiyeno anasankha gulu la anthu 12, amenenso anawapatsa dzina lakuti atumwi, kuti aziyenda naye nthawi zonse komanso kuti aziwatuma kukalalikira 15 nʼkuwapatsa mphamvu zoti azitulutsa ziwanda.+
16 Mʼgulu la anthu 12+ amene anasankha aja munali Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo,+ 17 Yakobo mwana wa Zebedayo ndi Yohane mchimwene wake wa Yakobo (awiriwa anawapatsanso dzina lakuti Boanege, limene limatanthauza “Ana a Bingu”),+ 18 Andireya, Filipo, Batolomeyo, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19 ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anadzamʼpereka.
Kenako Yesu analowa mʼnyumba. 20 Kumeneko gulu la anthu linasonkhananso, moti sanathe nʼkomwe kudya chakudya. 21 Koma achibale ake atamva zimenezo, anapita kukamugwira chifukwa iwo ankanena kuti: “Wachita misala.”+ 22 Komanso alembi amene anachokera ku Yerusalemu ankanena kuti: “Ali ndi Belezebule,* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 23 Choncho atawaitana, anayankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu wagawanika, ufumu umenewo sungakhalitse.+ 25 Ndiponso ngati nyumba yagawanika, nyumba yoteroyo singakhalitse. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukira yekha ndipo wagawanika, sangakhalitse koma akupita kokatha. 27 Kunena zoona, palibe amene angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkuba katundu wake ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo. Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo. 28 Ndithu ndikukuuzani, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya anachita machimo otani kapena analankhula mawu onyoza bwanji. 29 Koma aliyense amene wanyoza mzimu woyera sadzakhululukidwa kwamuyaya,+ koma adzakhala ndi mlandu wa tchimo losatha.”+ 30 Ananena zimenezi chifukwa iwo ankamunena kuti: “Ali ndi mzimu wonyansa.”+
31 Tsopano panafika mayi ake ndi azichimwene ake+ ndipo anaima panja nʼkutuma munthu kuti akamuitane.+ 32 Gulu la anthu linakhala momuzungulira ndipo anthuwo anamuuza kuti: “Mayi anu ndi azichimwene anu ali panjapa akukufunani.”+ 33 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi mayi anga ndi azichimwene anga ndi ndani?” 34 Kenako anayangʼana onse amene anakhala pansi momuzungulira aja nʼkunena kuti: “Onani! Mayi anga ndi azichimwene anga ndi awa.+ 35 Aliyense amene amachita zimene Mulungu amafuna, ameneyo ndi mchimwene wanga, mchemwali wanga ndi mayi anga.”+
4 Yesu anayambanso kuphunzitsa mʼmphepete mwa nyanja ndipo chigulu cha anthu chinasonkhana pafupi ndi iye. Choncho iye anakwera ngalawa nʼkukhala mʼngalawamo chapatali pangʼono ndi anthuwo, koma gulu lonse la anthulo linakhala mʼmphepete mwa nyanjayo.+ 2 Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri pogwiritsa ntchito mafanizo.+ Powaphunzitsapo ankawauza kuti:+ 3 “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+ 4 Pamene ankafesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa msewu ndipo kunabwera mbalame nʼkuzidya. 5 Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+ 6 Koma dzuwa litawala kwambiri zinawauka ndipo zinafota chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinakula nʼkulepheretsa mbewuzo kukula moti sizinabereke chipatso chilichonse.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinamera nʼkukula, moti zinayamba kubereka zipatso. Mbewu ina inabereka zipatso 30, ina 60 ndipo ina 100.”+ 9 Kenako anawonjezera mawu akuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+
10 Tsopano pamene anali payekha, ena amene anali naye chapafupi limodzi ndi atumwi 12 aja, anayamba kumufunsa zokhudza mafanizo aja.+ 11 Iye anawauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse chinsinsi chopatulika+ cha Ufumu wa Mulungu. Koma amene ali kunja amauzidwa zonse pogwiritsa ntchito mafanizo+ 12 kuti kuyangʼana, aziyangʼana ndithu koma asamaone. Kumva, azimva ndithu koma asamazindikire tanthauzo lake. Komanso kuti asatembenuke nʼkukhululukidwa.”+ 13 Iye anawauzanso kuti: “Ngati simukumvetsa fanizo ili, ndiye mungamvetse bwanji mafanizo ena onse?
14 Wofesayo amafesa mawu.+ 15 Choncho mbewu zimene zimagwera mʼmbali mwa msewu ndi mawu amene afesedwa mwa anthu amene amati akangomva mawuwo, Satana amabwera+ nʼkudzachotsa mawu amene afesedwa mwa iwo.+ 16 Mofanana ndi zimenezi, mbewu zimene zafesedwa pamiyala ndi mawu amene afesedwa mwa anthu omwe amati akangomva mawuwo, amawalandira mosangalala.+ 17 Koma iwo amakhala opanda mizu ndipo amapitirizabe kwakanthawi. Ndiyeno akangoyamba kuvutitsidwa kapena kuzunzidwa chifukwa cha mawuwo, amapunthwa. 18 Ndiye palinso mbewu zina zimene zimafesedwa paminga. Amenewa ndi anthu amene amamva mawu,+ 19 koma nkhawa za moyo+ wamʼnthawi* ino, chinyengo champhamvu cha chuma+ komanso kulakalaka zinthu+ zina zonse, zimalowa mʼmitima yawo nʼkulepheretsa mawuwo kukula ndipo sabereka zipatso. 20 Pomaliza, mbewu zimene zinafesedwa panthaka yabwino ndi anthu amene amamvetsera mawu ndipo amawalandira bwino nʼkubereka zipatso wina 30, wina 60 ndipo wina 100.”+
21 Iye anawauzanso kuti: “Nyale saivindikira ndi dengu* kapena kuiika pansi pa bedi, amatero ngati? Koma amaiika pachoikapo nyale,+ si choncho kodi? 22 Chifukwa palibe chobisika chimene sichidzaululika ndipo palibe chimene chimasungidwa mwachinsinsi kwambiri chimene sichidzaululika.+ 23 Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+
24 Anapitiriza kuwauza kuti: “Mvetserani mosamala zimene ndikunenazi.+ Muyezo umene mukuyezera ena, nanunso adzakuyezerani womwewo. Inde, adzakuwonjezerani zochuluka. 25 Chifukwa amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka,+ koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.”+
26 Iye anapitiriza kulankhula kuti: “Ufumu wa Mulungu uli ngati mmene munthu amamwazira mbewu panthaka. 27 Munthuyo amagona usiku nʼkumadzuka kukacha ndipo mbewuzo zimamera nʼkukula. Koma mmene zimenezi zimachitikira, mwiniwakeyo sadziwa. 28 Pangʼonopangʼono, payokha nthaka ija imabereka zipatso. Choyamba tirigu amakula, kenako amatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tirigu amaonekera mʼngalamo. 29 Koma mbewuzo zikacha, iye amazimweta ndi chikwakwa chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
30 Iye anapitiriza kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyerekeze ndi chiyani kapena tingaufotokoze ndi fanizo lotani? 31 Uli ngati kanjere ka mpiru,* kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakangʼono kwambiri kuposa njere zonse zapadziko lapansi.+ 32 Koma akakafesa, kamamera nʼkukula kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo kamapanga nthambi zikuluzikulu, moti mbalame zamumlengalenga zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.”
33 Iye anawauza mawu pogwiritsa ntchito mafanizo ambiri+ ofanana ndi amenewa, malinga ndi zimene akanakwanitsa kumva. 34 Ndithudi, nthawi zonse iye ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo, koma kumbali ankafotokoza zinthu zonse kwa ophunzira ake.+
35 Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya linalo.”+ 36 Choncho atauza gulu la anthulo kuti lizipita, ophunzirawo anachoka naye pangalawa imene anakwera ija, koma analinso ndi ngalawa zina.+ 37 Kenako kunayamba chimphepo champhamvu chamkuntho, ndipo mafunde ankawomba ngalawayo moti inangotsala pangʼono kumira.+ 38 Koma Yesu anali kumbuyo kwa ngalawayo akugona, atatsamira pilo. Choncho anamudzutsa nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?” 39 Atamva zimenezi anadzuka nʼkudzudzula mphepoyo komanso kuuza nyanjayo kuti: “Leka! Khala bata!”+ Atatero mphepoyo inaleka ndipo kenako panachita bata lalikulu. 40 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi? Kodi mudakali opandiratu chikhulupiriro?” 41 Koma iwo anagwidwa ndi mantha aakulu ndipo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.”+
5 Kenako iwo anafika kutsidya lina la nyanja, mʼdera la Agerasa.+ 2 Ndipo Yesu atangotsika mʼngalawa, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa akuchokera mʼmanda.* 3 Iye ankakonda kukhala mʼmandamo, ndipo kuyambira kalekale panalibe munthu aliyense amene anakwanitsa kumumanga ngakhale ndi unyolo koma iye osadula. 4 Iye anamangidwapo ndi matangadza ndiponso maunyolo mobwerezabwereza, koma ankadula maunyolowo ndiponso kuthyola matangadzawo moti panalibe amene anatha kumugonjetsa. 5 Ndipo nthawi zonse, usiku ndi masana, ankafuula mʼmanda ndi mʼmapiri komanso ankadzitematema ndi miyala. 6 Koma ataona Yesu chapatali ndithu, anamuthamangira nʼkumugwadira.+ 7 Kenako anafuula ndi mawu amphamvu kuti: “Kodi mukufuna chiyani kwa ine, Yesu, Mwana wa Mulungu Wamʼmwambamwamba? Ndikukulumbiritsani pali Mulungu kuti musandizunze.”+ 8 Chifukwa Yesu ankauza mzimuwo kuti: “Tuluka mwa munthuyu, mzimu wonyansa iwe.”+ 9 Ndiyeno Yesu anafunsa munthuyo kuti: “Dzina lako ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Dzina langa ndi Khamu, chifukwa tilipo ambiri.” 10 Ndipo anapitiriza kuchonderera Yesu kuti asatumize mizimuyo kutali ndi deralo.+
11 Ndiyeno chigulu cha nkhumba+ chinkadya mʼmbali mwa phiri.+ 12 Choncho mizimuyo inamuchonderera kuti: “Titumizeni munkhumbazo kuti tikalowe mmenemo.” 13 Choncho iye anailola. Atatero mizimu yonyansayo inatuluka nʼkukalowa munkhumbazo ndipo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi* nʼkulumphira mʼnyanja. Nkhumbazo zinalipo pafupifupi 2,000 ndipo zinamira mʼnyanjamo. 14 Koma abusa a ziwetozo anathawa nʼkukanena zimenezi mumzinda ndi mʼmidzi, ndipo anthu anabwera kudzaona zimene zinachitikazo.+ 15 Choncho anafika kwa Yesu ndipo anaona munthu amene anagwidwa ndi chiwanda uja, amene poyamba anali ndi gulu la mizimu yonyansa. Anamuona atakhala pansi, atavala bwinobwino komanso maganizo ake ali bwinobwino ndipo iwo anachita mantha. 16 Komanso amene anaona zimene zinachitikazo, anafotokozera anthuwo zimene zinachitikira munthu wogwidwa ndi ziwanda uja ndiponso nkhumba zija. 17 Choncho anthuwo anayamba kuchonderera Yesu kuti achoke mʼdera lakwawoko.+
18 Ndiyeno Yesu akukwera ngalawa, munthu amene anali ndi ziwanda uja anamuchonderera kuti apite nawo.+ 19 Yesu sanamulole koma anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwa achibale ako ndipo ukawauze zonse zimene Yehova* wakuchitira ndi chifundo chimene wakusonyeza.” 20 Choncho munthu uja anachoka ndipo anayamba kufalitsa mu Dekapoli* zonse zimene Yesu anamuchitira, moti anthu onse anadabwa kwambiri.
21 Yesu atawolokanso pangalawa kubwerera kutsidya lina, gulu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye, pa nthawiyi iye anali mʼmphepete mwa nyanja.+ 22 Kenako mmodzi wa atsogoleri a sunagoge, dzina lake Yairo, anafika. Atamuona anagwada pamapazi ake.+ 23 Iye anamuchonderera mobwerezabwereza kuti: “Mwana wanga wamkazi akudwala mwakayakaya.* Chonde tiyeni mukamuike manja+ kuti achire nʼkukhala ndi moyo.” 24 Zitatero Yesu ananyamuka naye limodzi, ndipo gulu lalikulu la anthu linkamutsatira nʼkumamupanikiza.
25 Tsopano panali mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi+ kwa zaka 12.+ 26 Madokotala ambiri anamuchititsa kuti avutike kwambiri.* Iye anawononga chuma chake chonse koma sanachire, mʼmalomwake matendawo ankangokulirakulira. 27 Atamva zokhudza Yesu, anakalowa mʼgulu la anthulo nʼkumudzera kumbuyo kwake, kenako anagwira malaya ake akunja.+ 28 Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.”+ 29 Nthawi yomweyo anasiya kutaya magazi ndipo mʼthupi mwake anamva kuti wachira matenda ake aakuluwo.
30 Nthawi yomweyo, Yesu anazindikira kuti mphamvu+ yatuluka mʼthupi mwake ndipo anatembenuka mʼgulu la anthulo nʼkufunsa kuti: “Ndi ndani wagwira malaya anga akunjawa?”+ 31 Koma ophunzira ake anamuuza kuti: “Inunso mukuona kuti anthu onsewa akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndi ndani wandigwira?’” 32 Komabe iye ankayangʼanayangʼana kuti aone amene wachita zimenezi. 33 Mayi uja anachita mantha nʼkuyamba kunjenjemera atadziwa zimene zamuchitikira ndipo anafika pafupi nʼkugwada pamaso pake nʼkumuuza zoona zonse. 34 Iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere+ ndipo matenda ako aakuluwo atheretu.”+
35 Ali mkati molankhula, panafika amuna ena ochokera kunyumba kwa mtsogoleri wa sunagoge uja ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira! Musiyeni Mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 36 Koma Yesu anamva zimene ankanenazo ndipo anauza mtsogoleri wa sunagogeyo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi.”+ 37 Pa nthawiyo sanalolenso aliyense kuti amutsatire kupatulapo Petulo, Yakobo ndi Yohane, amene ndi mchimwene wake wa Yakobo.+
38 Choncho anafika kunyumba ya mtsogoleri wa sunagoge ndipo anamva chiphokoso cha anthu akulira komanso kubuma kwambiri.+ 39 Atalowa mkati, anafunsa anthuwo kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukupanga phokoso komanso kulira chonchi? Mwanayu sanamwalire, koma akugona.”+ 40 Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyoza. Koma atawatulutsa onsewo, anatenga bambo ndi mayi a mwanayo komanso anthu amene anali naye aja, ndipo analowa kumene kunali mwanayo. 41 Ndiyeno anagwira dzanja la mwanayo nʼkunena kuti: “Talʹi·tha cuʹmi,” mawu amene akamasuliridwa amatanthauza kuti: “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, dzuka!”+ 42 Nthawi yomweyo mtsikanayo anadzuka nʼkuyamba kuyenda. (Mtsikanayo anali ndi zaka 12.) Ndipo anthuwo anasangalala kwambiri. 43 Koma iye anawalamula mobwerezabwereza* kuti asauze aliyense zimenezi.+ Kenako anawauza kuti apatse mtsikanayo chakudya.
6 Kenako anachoka kumeneko nʼkufika mʼdera lakwawo+ ndipo ophunzira ake anamʼtsatira. 2 Sabata litakwana, iye anayamba kuphunzitsa musunagoge. Anthu ambiri amene anamumvetsera anadabwa ndipo ananena kuti: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti zinthu zimenezi?+ Ndipo nʼchifukwa chiyani nzeru zimenezi zinaperekedwa kwa iyeyu, komanso kuti azitha kuchita ntchito zamphamvu zoterezi?+ 3 Kodi iyeyu si kalipentala,+ mwana wa Mariya,+ komanso mchimwene wake wa Yakobo,+ Yosefe, Yudasi ndi Simoni?+ Ndipo azichemwali ake si awa tili nawo pompano?” Choncho anayamba kukhumudwa naye. 4 Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo, ngakhale ndi achibale ake, ngakhale mʼnyumba mwake momwe, koma kwina.”+ 5 Choncho sanathe kuchita ntchito zamphamvu zilizonse kumeneko, koma anangoika manja pa odwala owerengeka nʼkuwachiritsa. 6 Ndithudi, iye anadabwa kuona kuti anthuwo analibe chikhulupiriro. Choncho anazungulira mʼmidzi yapafupi nʼkumaphunzitsa anthu.+
7 Kenako anaitana ophunzira ake 12 aja nʼkuyamba kuwatumiza awiriawiri+ ndipo anawapatsa mphamvu kuti azitha kutulutsa mizimu yonyansa.+ 8 Komanso anawalamula kuti asatenge kanthu pa ulendowo koma ndodo yokha basi. Anawalamula kuti asatenge mkate, thumba la chakudya kapena ndalama* mʼzikwama zawo,+ 9 koma kuti avale nsapato ndiponso kuti asavale malaya awiri.* 10 Komanso anawauza kuti: “Mukafika panyumba iliyonse, muzikhala mʼnyumbayo mpaka nthawi yochoka kumeneko itakwana.+ 11 Kulikonse kumene sakakulandirani kapena kukumvetserani, mukamachoka kumeneko sansani fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni kwa iwo.”+ 12 Choncho anapita nʼkukalalikira kuti anthu alape,+ 13 ndipo anatulutsa ziwanda zambiri,+ komanso kudzoza mafuta anthu ambiri odwala nʼkuwachiritsa.
14 Ndiyeno Mfumu Herode inamva zimenezi chifukwa dzina la Yesu linatchuka kwambiri ndipo anthu ankanena kuti: “Yohane Mʼbatizi wauka kwa akufa nʼchifukwa chake akuchita ntchito zamphamvu.”+ 15 Koma ena ankanena kuti: “Ndi Eliya.” Ndipo ena ankanena kuti: “Ndi mneneri ngati mmene analili aneneri akale.”+ 16 Koma Herode atamva za Yesu ananena kuti: “Ndithu Yohane amene ndinamudula mutu uja waukitsidwadi.” 17 Ananena zimenezi chifukwa Herodeyo anatumiza anthu kuti akagwire Yohane nʼkumumanga ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa mchimwene wake Filipo amene Herodeyo anakwatira.+ 18 Anachita zimenezi chifukwa Yohane ankauza Herode kuti: “Nʼzosaloleka kuti mutenge mkazi wa mchimwene wanu.”+ 19 Choncho Herodiya anamusungira chidani mumtima ndipo ankafuna kumupha, koma sanakwanitse kuchita zimenezo. 20 Herode ankaopa Yohane chifukwa ankadziwa kuti ndi munthu wolungama komanso woyera,+ choncho ankamuteteza. Atamva zimene ankanena anathedwa nzeru, komabe anapitiriza kumumvetsera mosangalala.
21 Ndiyeno tsiku loti Herodiya akwaniritse zolinga zake linafika. Limeneli linali tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode+ ndipo anakonzera chakudya chamadzulo nduna zake, akuluakulu a asilikali ndi anthu otchuka kwambiri a mu Galileya.+ 22 Ndiye mwana wamkazi wa Herodiya analowa nʼkuyamba kuvina, moti anasangalatsa Herode ndi ena amene ankadya naye limodzi. Tsopano mfumu inauza mtsikanayo kuti: “Undipemphe chilichonse chimene ukufuna ndipo ndikupatsa.” 23 Ndithu, anachita kumulumbirira kuti: “Chilichonse chimene ungandipemphe ndikupatsa, ngakhale hafu ya ufumu wangawu.” 24 Choncho anatuluka nʼkukafunsa mayi ake kuti: “Ndikapemphe chiyani?” Mayi akewo anamuuza kuti: “Kapemphe mutu wa Yohane Mʼbatizi.” 25 Nthawi yomweyo anapita kwa mfumuyo mofulumira nʼkupempha kuti: “Ndikufuna mundipatse mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale pompano.”+ 26 Ngakhale kuti mfumu inamva chisoni kwambiri, sinafune kumukanira poganizira lumbiro lake lija komanso alendo ake aja.* 27 Choncho, nthawi yomweyo mfumu inatumiza msilikali amene ankamulondera nʼkumulamula kuti abweretse mutu wa Yohane. Iye anapita nʼkukamudula mutu mundendemo 28 ndipo anaubweretsa mʼmbale. Ndiyeno anaupereka kwa mtsikana uja ndipo mtsikanayo anakaupereka kwa mayi ake. 29 Ophunzira ake atamva zimenezo anabwera kudzatenga mtembo wake nʼkukauika mʼmanda.*
30 Atumwi anasonkhana kwa Yesu nʼkumuuza zonse zimene iwo anachita komanso kuphunzitsa.+ 31 Iye anawauza kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mukapume pangʼono.”+ Chifukwa anthu ambiri ankabwera komanso kupita ndipo analibe nthawi yoti apume ngakhalenso yoti adye chakudya. 32 Ndiyeno anakwera ngalawa nʼkupita kwaokhaokha kumalo opanda anthu.+ 33 Koma anthu anawaona akuchoka ndipo ambiri anadziwa zimenezo. Choncho kuchokera mʼmizinda yonse anthu anathamangira kumeneko wapansi ndipo anthuwo ndi amene anayamba kukafika kumaloko. 34 Koma atatsika anaona gulu lalikulu la anthu ndipo anawamvera chisoni,+ chifukwa anali ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa.+ Ndiye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.+
35 Tsopano kunja kunayamba kuda ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha.+ 36 Auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzi yapafupi ndi mʼmadera ozungulira kuti akagule chakudya choti adye.”+ 37 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.” Yesu atanena zimenezi iwo anamufunsa kuti: “Kodi tipite kukagula mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari* 200 nʼkuipereka kwa anthuwa kuti adye?”+ 38 Iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate? Pitani mukaone!” Ataiona ananena kuti: “Ilipo 5 ndi nsomba ziwiri.”+ 39 Kenako anauza anthuwo kuti akhale mʼmagulu pa udzu wobiriwira.+ 40 Ndipo anakhaladi mʼmagulu, ena anthu 100, ena anthu 50. 41 Ndiyeno anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndipo anapemphera.+ Kenako ananyemanyema mitanda ya mkateyo nʼkuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo ndiponso anaduladula nsomba ziwirizo nʼkugawira anthu onsewo. 42 Choncho onse anadya nʼkukhuta 43 ndipo anatolera madengu 12 odzaza mkate umene unatsala, osawerengera nsomba.+ 44 Anthu amene anadya mkatewo analipo amuna okwana 5,000.
45 Kenako mwamsanga, Yesu anauza ophunzira ake kuti akwere ngalawa nʼkutsogola kupita kutsidya lina loyangʼanizana nalo cha ku Betsaida. Koma iye anatsalira nʼcholinga choti auze anthuwo kuti azipita kwawo.+ 46 Atatsazikana ndi anthuwo, iye anachoka nʼkupita kuphiri kukapemphera.+ 47 Kunja kutada, ngalawa ija inali ili pakati pa nyanja, koma iye anali yekha kumtunda.+ 48 Ataona ophunzirawo akupalasa movutika chifukwa cholimbana ndi mphepo yamphamvu, iye anawalondola akuyenda panyanja. Uwu unali mʼbandakucha pafupifupi pa ulonda wa 4.* Koma ophunzirawo ankaona ngati akufuna kuwapitirira. 49 Atamuona akuyenda panyanjapo ophunzirawo anaganiza kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mokweza. 50 Anachita zimenezi chifukwa onsewo anamuona ndipo anachita mantha. Koma nthawi yomweyo iye anawauza kuti: “Mtima mʼmalo, ndine. Musachite mantha.”+ 51 Ndiyeno Yesu anakwera nawo mʼngalawamo ndipo mphepoyo inaleka. Ataona zimenezi anadabwa kwambiri. 52 Chifukwa choti sanamvetse tanthauzo la mitanda ya mkate ija, iwo ankavutikabe kuti amvetse zinthu zonse.
53 Atawoloka nʼkufika kumtunda, anafika ku Genesareti nʼkuimika ngalawayo chapafupi.+ 54 Koma atangotsika mʼngalawamo, anthu anamuzindikira. 55 Choncho anthu anathamanga uku ndi uku mʼdera lonselo nʼkuyamba kunyamula pamachira anthu onse amene ankadwala, kupita nawo kumene anamva kuti iye ali kumeneko. 56 Ndipo akangolowa mʼmidzi kapena mʼmizinda komanso mʼmadera ozungulira, anthu ankakhazika odwala mʼmisika. Iwo ankamuchonderera kuti angogwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo anthu onse amene anaugwira anachira.
7 Tsopano Afarisi ndi alembi ena amene anachokera ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu.+ 2 Ndiyeno iwo anaona ena mwa ophunzira ake akudya chakudya ndi manja oipitsidwa, kapena kuti mʼmanja mosasamba.* 3 (Afarisi ndi Ayuda onse sadya asanasambe mʼmanja mpaka mʼzigongono, potsatira mwambo wa makolo. 4 Ndipo akabwera kuchokera kumsika, sadya mpaka atasamba. Pali miyambo inanso yambiri imene anailandira ndipo akuitsatira, monga kuviika mʼmadzi makapu, mitsuko ndi ziwiya zakopa.*)+ 5 Choncho Afarisi ndi alembi amenewa anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira miyambo ya makolo, koma amadya chakudya ndi manja oipitsidwa?”+ 6 Iye anawayankha kuti: “Yesaya analosera zolondola zokhuza anthu achinyengo inu, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti, ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo aiika kutali ndi ine.+ 7 Chilichonse chomwe amachita pondilambira ndi chopanda pake, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati kuti ndi malamulo a Mulungu.’+ 8 Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu nʼkumaumirira miyambo ya anthu.”+
9 Komanso anawauza kuti: “Mochenjera, mumanyalanyaza malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu.+ 10 Mwachitsanzo, Mose ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu,’+ komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+ 11 Koma inu mumanena kuti, ‘Munthu akauza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ndili nacho, chimene ndikanakuthandizani nacho ndi khobani (kutanthauza, mphatso yoti ndipereke kwa Mulungu),”’ 12 inu simulolanso kuti munthuyo achitire bambo ake kapena mayi ake chinthu chilichonse.+ 13 Mukamachita zimenezi, mumapangitsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu imene munaipereka kwa anthu.+ Ndipo mumachita zinthu zambiri ngati zimenezi.”+ 14 Atatero, anaitana gulu la anthuwo kuti abwerenso kwa iye ndipo anawauza kuti: “Mvetserani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.+ 15 Palibe chilichonse chochokera kunja kwa munthu nʼkulowa mʼthupi mwake chimene chingaipitse munthu. Koma zinthu zimene zimatuluka mwa munthu ndi zimene zimaipitsa munthu.”+ 16*——
17 Tsopano atalowa mʼnyumba ina kutali ndi gulu la anthulo, ophunzira ake anayamba kumufunsa za fanizo lija.+ 18 Choncho iye anawafunsa kuti: “Kodi nanunso ndinu osazindikira ngati iwo aja? Kodi simukudziwa kuti palibe chochokera kunja kwa thupi nʼkulowa mʼthupi mwa munthu chimene chingamuipitse? 19 Zili choncho chifukwa sichidutsa mumtima mwake koma mʼmatumbo mwake, ndipo chimakatuluka kuchimbudzi.” Ndi mawu amenewa Yesu anagamula kuti zakudya zonse nʼzoyera. 20 Iye ananenanso kuti: “Chotuluka mʼthupi la munthu nʼchimene chimaipitsa munthu.+ 21 Chifukwa mumtima mwa anthu+ mumatuluka maganizo oipa ngati: zachiwerewere,* zakuba, zopha anthu, 22 zachigololo, dyera, kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lopanda manyazi,* diso la kaduka, mawu onyoza, kudzikweza ndiponso kuchita zinthu mopanda nzeru. 23 Zoipa zonsezi zimatuluka mumtima mwa munthu ndipo zimamuipitsa.”
24 Atachoka kumeneko anapita mʼchigawo cha Turo ndi Sidoni.+ Kumeneko anakalowa mʼnyumba ina ndipo sanafune kuti aliyense adziwe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziwabe. 25 Nthawi yomweyo, mayi wina amene mwana wake wamkazi anagwidwa ndi mzimu wonyansa anamva za iye ndipo anabwera nʼkudzagwada pamapazi ake.+ 26 Mayiyu anali Mgiriki, wa Chisurofoinike. Iye anapempha Yesu mobwerezabwereza kuti atulutse chiwanda mwa mwana wakeyo. 27 Koma Yesu anauza mayiyo kuti: “Choyamba, zimafunika kuti ana akhute kaye, chifukwa si bwino kutenga chakudya cha ana nʼkuponyera tiagalu.”+ 28 Koma mayiyo anamuyankha kuti: “Inde mbuyanga, komatu tiagalu timadya nyenyeswa za anawo pansi pa tebulo.” 29 Yesu atamva zimenezo anauza mayiyo kuti: “Chifukwa chakuti wanena zimenezi, pita, chiwandacho chatuluka mwa mwana wakoyo.”+ 30 Choncho anapita kunyumba kwake ndipo anakapeza mwanayo atagona pabedi chiwandacho chitatuluka.+
31 Pamene Yesu ankachoka mʼchigawo cha Turo kupita kunyanja ya Galileya, anadutsa ku Sidoni komanso mʼchigawo cha Dekapoli.*+ 32 Kumeneko anthu anamubweretsera munthu wa vuto losamva komanso wovutika kulankhula.+ Iwo anamupempha kuti aike dzanja lake pa munthuyo. 33 Koma iye anatenga munthuyo nʼkuchoka naye pagulu la anthulo kupita naye pambali. Kenako anapisa zala zake mʼmakutu a munthuyo, ndipo atalavulira pazala zake anakhudza lilime la munthuyo.+ 34 Atatero anayangʼana kumwamba nʼkuusa moyo mwamphamvu, kenako anauza munthuyo kuti: “Efata,” kutanthauza kuti, “Tseguka.” 35 Atatero, makutu ake anatseguka+ ndipo vuto lake losalankhulalo linatheratu, moti anayamba kulankhula bwinobwino. 36 Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimene zinachitikazo.+ Koma ankati akawaletsa mwamphamvu kuti asauze aliyense, mʼpamenenso iwo ankazifalitsa kwambiri.+ 37 Inde, iwo anadabwa kwambiri+ ndipo ananena kuti: “Wachita zinthu zonse bwinobwino ndithu. Ngakhale anthu amene anali ndi vuto losamva akumva komanso amene anali ndi vuto losalankhula akulankhula.”+
8 Mʼmasiku amenewo, gulu la anthu linasonkhananso koma linalibe chakudya. Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: 2 “Gulu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine kwa masiku atatu ndipo alibe chakudya.+ 3 Ndikawauza kuti azipita kwawo ali ndi njala,* alenguka panjira. Ndipo ena a iwo achokera kutali kwambiri.” 4 Koma ophunzira ake anamuyankha kuti: “Munthu angaipeze kuti mitanda ya mkate yokwanira kudyetsa anthu onsewa, kumalo kopanda anthu ngati kuno?” 5 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7.”+ 6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako, anatenga mitanda 7 ya mkate ija nʼkuyamika. Atatero anainyemanyema nʼkuyamba kupereka kwa ophunzira ake kuti agawe, ndipo iwo anagawira gulu la anthulo.+ 7 Ophunzirawo analinso ndi tinsomba towerengeka ndipo atadalitsa tinsombato, anawauza kuti agawirenso anthuwo. 8 Choncho anthu onsewo anadya nʼkukhuta, moti zotsala zimene anatolera zinadzaza madengu akuluakulu 7.+ 9 Komatu panali amuna pafupifupi 4,000. Kenako anawauza kuti azipita.
10 Nthawi yomweyo iye anakwera ngalawa limodzi ndi ophunzira ake nʼkufika mʼchigawo cha Dalamanuta.+ 11 Kumeneku kunafika Afarisi ndipo anayamba kutsutsana naye. Ankafuna kuti iye awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba, pofuna kumuyesa.+ 12 Choncho anausa moyo mwamphamvu nʼkunena kuti: “Nʼchifukwa chiyani mʼbadwo umenewu ukufunitsitsa chizindikiro?+ Ndithu ndikukuuzani, mʼbadwo umenewu sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse.”+ 13 Atanena zimenezi anawasiya nʼkukakweranso ngalawa kupita kutsidya lina.
14 Komano iwo anaiwala kutenga mikate, choncho analibe chilichonse mʼngalawamo kupatulapo mtanda wa mkate umodzi wokha basi.+ 15 Ndipo anawachenjeza mwamphamvu kuti: “Khalani maso! Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.”+ 16 Choncho ophunzirawo anayamba kukangana pa nkhani yosowa mkate. 17 Yesu ataona zimenezo, anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukukangana pa nkhani yosowa mkate? Kodi simukuzindikira ndi kumvetsa tanthauzo lake mpaka pano? Kodi mitima yanu ikadali yosazindikira? 18 ‘Ngakhale kuti muli ndi maso, simukuona. Ndipo ngakhale kuti muli ndi makutu, simukumva.’ Kodi simukukumbukira 19 zimene zinachitika nditanyemanyema mitanda 5 ya mkate+ nʼkudyetsa amuna 5,000? Kodi munatolera madengu angati a zotsala?” Iwo anayankha kuti: “Anali madengu 12.”+ 20 “Nditanyemanyema mitanda 7 ya mkate nʼkudyetsa amuna 4,000, kodi munatolera madengu akuluakulu angati a zotsala?” Iwo anamuyankha kuti: “Analipo 7.”+ 21 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi simukumvetsabe tanthauzo lake?”
22 Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneku anthu anamubweretsera munthu amene anali ndi vuto losaona. Anthuwo anamuchonderera kuti akhudze munthuyo.+ 23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo nʼkupita naye kunja kwa mudzi. Kumeneko iye anaika malovu mʼmaso mwa munthuyo+ nʼkuika manja ake pa munthuyo ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukuona chilichonse?” 24 Munthuyo anayangʼana mʼmwamba nʼkunena kuti: “Ndikuona anthu, koma akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.” 25 Iye anagwiranso mʼmaso mwa munthuyo ndipo anayamba kuona bwinobwino. Munthuyo anachiriratu moti anayamba kuona chilichonse bwinobwino. 26 Kenako anamuuza kuti azipita kwawo nʼkunena kuti: “Koma usalowe mʼmudzimu.”
27 Ndiyeno Yesu ndi ophunzira ake anachoka nʼkupita kumidzi ya Kaisareya wa Filipi. Ali mʼnjira, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 28 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti mmodzi wa aneneri.” 29 Ndiyeno anafunsa ophunzirawo kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu.”+ 30 Atanena zimenezo, anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye.+ 31 Komanso anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndipo adzaphedwa+ nʼkuukitsidwa patapita masiku atatu.+ 32 Ndithudi, iye analankhula mawu amenewa mosapita mʼmbali. Koma Petulo anatengera Yesu pambali nʼkuyamba kumudzudzula.+ 33 Atamva zimenezi, Yesu anatembenuka nʼkuyangʼana ophunzira ake, kenako anadzudzula Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”+
34 Kenako iye anaitana gulu la anthu limodzi ndi ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira.+ 35 Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.+ 36 Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake?+ 37 Kapena kodi munthu angapereke chiyani choti asinthanitse ndi moyo wake?+ 38 Chifukwa aliyense wochita manyazi ndi ine komanso mawu anga mu mʼbadwo wachigololo* ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi+ akadzabwera mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.”+
9 Ndiye anawauzanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa mʼpangʼono pomwe mpaka choyamba ataona Ufumu wa Mulungu utabwera ndi mphamvu zake.”+ 2 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane nʼkukwera nawo mʼphiri lalitali kwaokhaokha. Ndiyeno iye anasintha maonekedwe ake iwo akuona.+ 3 Malaya ake akunja anayamba kunyezimira nʼkuyera kwambiri kuposa mmene wochapa zovala aliyense padziko lapansi angayeretsere zovala. 4 Komanso Eliya ndi Mose anaonekera kwa iwo ndipo ankakambirana ndi Yesu. 5 Ndiye Petulo anauza Yesu kuti: “Rabi, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Choncho timange matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.” 6 Petulo sanadziwe choti anene, chifukwa ophunzirawo anachita mantha kwambiri. 7 Ndiyeno kunachita mtambo umene unawaphimba. Kenako panamveka mawu+ kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.+ Muzimumvera.”+ 8 Kenako iwo anayangʼana uku ndi uku ndipo anangoona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha basi.
9 Pamene ankatsika mʼphirimo, Yesu anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense zimene anaonazo,+ mpaka Mwana wa munthu atauka kwa akufa.+ 10 Iwo anasungadi zimenezo mumtima,* koma anayamba kukambirana zimene kuuka kwa akufa kumeneku kukutanthauza. 11 Ndiyeno anayamba kumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya+ ayenera kubwera choyamba?”+ 12 Iye anawayankha kuti: “Eliya adzabweradi choyamba nʼkubwezeretsa zinthu zonse.+ Koma nʼchifukwa chiyani malemba amanena kuti Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri+ komanso kumuchitira zinthu zachipongwe?+ 13 Koma ine ndikukuuzani kuti Eliya+ anabwera kale ndipo anamuchitira zilizonse zimene iwo anafuna, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena zokhudza iye.”+
14 Atayandikira kumene kunali ophunzira ena aja, iwo anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndipo panali alembi amene ankakangana nawo.+ 15 Koma gulu lonselo litangomuona linadabwa ndipo linamuthamangira kuti likamupatse moni. 16 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Mukukangana nawo chiyani?” 17 Munthu wina amene anali mʼgululo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, ine ndabweretsa mwana wanga wamwamuna kwa inu chifukwa ali ndi mzimu umene umamulepheretsa kulankhula.+ 18 Mzimuwo umati ukamugwira, umamugwetsera pansi. Akatero amachita thovu mʼkamwa komanso kukukuta mano ndipo amafooka. Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse koma alephera.” 19 Iye anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.”+ 20 Choncho iwo anapita naye kwa Yesu. Koma mzimuwo utamuona, nthawi yomweyo unachititsa kuti mwanayo aphuphe. Anagwa pansi nʼkumagubudukagubuduka ndipo ankachita thovu kukamwa. 21 Ndiyeno Yesu anafunsa bambo ake kuti: “Izi zakhala zikumuchitikira kwa nthawi yaitali bwanji?” Bambo a mwanayo ananena kuti: “Kuyambira ali wamngʼono 22 ndipo nthawi zambiri umamugwetsera pamoto komanso mʼmadzi kuti umuwononge. Koma ngati mungathe kuchitapo kanthu, tichitireni chifundo nʼkutithandiza.” 23 Yesu anafunsa bambowo kuti: “Mukuti ‘Ngati mungatheʼ? Chilichonsetu nʼchotheka kwa munthu amene ali ndi chikhulupiriro.”+ 24 Nthawi yomweyo bambo a mwanayo anafuula nʼkunena kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!”+
25 Tsopano Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kwa iwo, anakalipira mzimu wonyansawo kuti: “Iwe mzimu wolepheretsa munthu kulankhula komanso kumva, ndikukulamula, tuluka ndipo usadzalowenso mwa iye.”+ 26 Mwanayo atafuula ndi kuphupha kwambiri, mzimuwo unatuluka ndipo ankaoneka ngati wafa, moti anthu ambiri ankanena kuti: “Wamwalira!” 27 Koma Yesu anamugwira dzanja nʼkumudzutsa ndipo mwanayo anaimirira. 28 Ndiyeno atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali kwaokha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?”+ 29 Iye anawayankha kuti: “Mzimu wa mtundu umenewu sungathe kutuluka ndi chilichonse, koma pemphero basi.”
30 Atachoka kumeneko anapitiriza ulendo wawo kudutsa mu Galileya, koma iye sanafune kuti aliyense adziwe zoti ali kumeneko. 31 Chifukwa iye ankaphunzitsa ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu ndipo adzamupha.+ Koma ngakhale adzamuphe, adzauka patatha masiku atatu.”+ 32 Komabe ophunzirawo sanamvetse mawu akewo ndipo ankaopa kuti amufunse.
33 Kenako anafika ku Kaperenao. Ndiyeno pamene anali mʼnyumba anawafunsa kuti: “Mʼnjira muja mumakangana chiyani?”+ 34 Iwo anangokhala chete, chifukwa mʼnjira amakangana kuti wamkulu ndi ndani pakati pawo. 35 Choncho anakhala pansi nʼkuitana ophunzira 12 aja nʼkuwauza kuti: “Ngati aliyense akufuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza pa onse ndiponso mtumiki wa onse.”+ 36 Kenako anatenga mwana wamngʼono nʼkumuimika pakati pawo ndipo anamukumbatira nʼkuwauza kuti: 37 “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono+ ngati ameneyu mʼdzina langa, walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine, sanalandire ine ndekha, koma walandiranso Mulungu amene anandituma.”+
38 Kenako Yohane anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndiye tinamuletsa, chifukwa sakuyenda ndi ife.”+ 39 Koma Yesu ananena kuti: “Musamuletse, chifukwa palibe amene angachite ntchito zamphamvu mʼdzina langa, nthawi yomweyo nʼkundinenera zachipongwe. 40 Chifukwa amene sakutsutsana ndi ife ali kumbali yathu.+ 41 Komanso aliyense amene wakupatsani kapu ya madzi akumwa chifukwa chakuti ndinu ophunzira a Khristu,+ ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika.+ 42 Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana iti timene tili ndi chikhulupiriro, zingamukhalire bwino kwambiri ngati atamumangirira chimwala champhero mʼkhosi mwake chimene bulu amayendetsa nʼkumuponya munyanja.+
43 Ngati dzanja lako limakuphunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi, kusiyana nʼkupita ku Gehena,* kumoto umene sungazimitsidwe, uli ndi manja onse awiri.+ 44*—— 45 Ndipo ngati phazi lako limakupunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli wolumala, kusiyana nʼkuti uponyedwe mʼGehena* uli ndi mapazi onse awiri.+ 46*—— 47 Ngati diso lako limakuchimwitsa,* ulitaye.+ Ndi bwino kuti ukalowe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi, kusiyana nʼkuti uponyedwe mu Gehena* uli ndi maso onse awiri,+ 48 kumene mphutsi za mitembo sizifa ndipo moto wake suzima.+
49 Chifukwa aliyense akuyenera kuwazidwa mchere umene ukuimira moto.+ 50 Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvuyo mungaibwezeretse bwanji?+ Khalani ndi mchere mwa inu nokha+ ndipo sungani mtendere pakati panu.”+
10 Atachoka kumeneko anapita kumalire a Yudeya kutsidya lina la Yorodano. Kumenekonso gulu la anthu linasonkhana kwa iye. Mwachizolowezi chake Yesu anayambanso kuwaphunzitsa.+ 2 Ndiyeno Afarisi anabwera kwa iye nʼcholinga chodzamuyesa. Iwo anamufunsa ngati mwamuna ali ndi ufulu wothetsa banja ndi mkazi wake.+ 3 Iye anawafunsa kuti: “Kodi Mose anakulamulani chiyani?” 4 Iwo anati: “Mose analola kuti mwamuna azilemba kalata yothetsera ukwati nʼkusiya mkaziyo.”+ 5 Koma Yesu anawauza kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu+ iye anakulemberani lamulo limeneli.+ 6 Koma kuyambira pachiyambi pa chilengedwe, ‘Mulungu anawalenga mwamuna ndi mkazi.+ 7 Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake,+ 8 ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi,’+ moti sakhalanso kuti ndi awiri koma thupi limodzi. 9 Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi,* munthu asachilekanitse.”+ 10 Atalowanso mʼnyumba, ophunzira anayamba kumufunsa za nkhani imeneyi. 11 Iye anawauza kuti: “Aliyense amene wasiya mkazi wake nʼkukwatira wina, wachita chigololo+ ndipo walakwira mkaziyo. 12 Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake nʼkukwatiwa ndi wina, wachita chigololo.”+
13 Tsopano anthu anayamba kumubweretsera ana aangʼono kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14 Yesu ataona zimenezi anakwiya ndipo anawauza kuti: “Asiyeni anawo abwere kwa ine, musawaletse. Chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu ngati amenewa.+ 15 Ndithu ndikukuuzani, aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono sadzalowa nʼkomwe mu Ufumuwo.”+ 16 Ndiyeno anatenga anawo mʼmanja mwake ndipo anaika manja ake pa iwo nʼkuyamba kuwadalitsa.+
17 Pamene ankachoka kumeneko, mwamuna wina anamuthamangira nʼkugwada pamaso pake. Kenako anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 18 Yesu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 19 Iwe umadziwa malamulo akuti: ‘Musaphe munthu,*+ musachite chigololo,+ musabe,+ musapereke umboni wabodza,+ musabere munthu mwachinyengo+ ndiponso lakuti muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’”+ 20 Munthuyo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamngʼono.” 21 Yesu anamuyangʼana ndipo anamukonda. Kenako anamuuza kuti, “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita ukagulitse zinthu zimene uli nazo ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22 Koma iye atamva mawu amenewo anakhumudwa ndipo anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+
23 Yesu atayangʼana uku ndi uku, anauza ophunzira akewo kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu andalama adzalowe mu Ufumu wa Mulungu!”+ 24 Koma ophunzirawo anadabwa ndi mawu akewa. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ana inu, kulowa mu Ufumu wa Mulungu nʼkovuta kwambiri! 25 Nʼzosavuta kuti ngamila ilowe pakabowo ka singano kusiyana nʼkuti munthu wolemera alowe mu Ufumu wa Mulungu.”+ 26 Iwo anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa* kuti: “Ndiye angapulumuke ndi ndani?”+ 27 Yesu anawayangʼanitsitsa nʼkuwauza kuti: “Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma sizili choncho kwa Mulungu chifukwa zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”+ 28 Petulo anayamba kumuuza kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse nʼkukutsatirani.”+ 29 Yesu ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe amene wasiya nyumba, azichimwene, azichemwali, amayi, abambo, ana kapena minda chifukwa cha ine komanso chifukwa cha uthenga wabwino,+ 30 amene panopa sadzapeza zochuluka kuwirikiza maulendo 100 mʼnthawi* ino. Iye adzapeza nyumba, azichimwene, azichemwali, amayi, ana ndi minda, komanso adzazunzidwa,+ ndipo mʼnthawi imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha. 31 Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza ndipo omaliza adzakhala oyamba.”+
32 Tsopano anapitiriza ulendo wawo wopita ku Yerusalemu ndipo Yesu anali patsogolo pawo. Ophunzirawo anadabwa kwambiri ndipo anthu amene ankamutsatirawo anayamba kuchita mantha. Kachiwirinso anatengera pambali ophunzira 12 aja nʼkuyamba kuwauza zinthu izi zimene zinali zitatsala pangʼono kuti zimuchitikire:+ 33 “Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe ndipo akamupereka kwa anthu amitundu ina. 34 Iwo akamuchitira chipongwe, kumulavulira, kumukwapula ndi kumupha, koma pakadzapita masiku atatu, adzauka.”+
35 Ndiyeno Yakobo ndi Yohane, ana aamuna a Zebedayo,+ anapita kwa iye nʼkumuuza kuti: “Mphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire chilichonse chimene tingakupempheni.”+ 36 Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?” 37 Iwo anamuyankha kuti: “Mutilole kuti mmodzi wa ife adzakhale kudzanja lanu lamanja ndipo wina adzakhale kumanzere kwanu mu ulemerero wanu.”+ 38 Koma Yesu anawauza kuti: “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwe zimene ine ndikumwa kapena kubatizidwa ubatizo umene ine ndikubatizidwa?”+ 39 Iwo anayankha kuti: “Inde tingatero.” Atatero Yesu anawauza kuti: “Zimene ine ndikumwa mudzamwadi ndipo mudzabatizidwadi ubatizo umene ine ndikubatizidwa.+ 40 Koma si ine woyenera kusankha amene adzakhale kudzanja langa lamanja kapena lamanzere. Atate wanga adzapereka mwayi umenewo kwa anthu amene anawakonzera.”
41 Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndi Yakobo komanso Yohane.+ 42 Koma Yesu anawaitana nʼkuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti amene amaoneka ngati* akulamulira anthu a mitundu ina, amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu awo amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 43 Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu. Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 44 ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wa onse. 45 Chifukwa ngakhale Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa koma kudzatumikira+ ndi kudzapereka moyo wake dipo* kuti awombole anthu ambiri.”+
46 Kenako anafika ku Yeriko. Koma pamene iye ndi ophunzira ake komanso gulu lalikulu ndithu ankatuluka mu Yeriko, Batimeyu (mwana wa Timeyu) wopemphapempha amene anali ndi vuto losaona, anakhala pansi mʼmphepete mwa msewu.+ 47 Atamva kuti Yesu Mnazareti akudutsa, Batimeyu anayamba kufuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide,+ ndichitireni chifundo!”+ 48 Atatero anthu ambiri anayamba kumudzudzula nʼkumamuuza kuti akhale chete. Koma akatero mʼpamenenso iye ankafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!” 49 Choncho Yesu anaima nʼkunena kuti: “Muuzeni abwere kuno.” Iwo anaitana munthu wosaonayo nʼkumuuza kuti: “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.” 50 Choncho iye anaponya uko malaya ake akunja ndipo anaimirira mofulumira nʼkupita kwa Yesu. 51 Ndiyeno Yesu anamufunsa kuti: “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Munthu amene anali ndi vuto losaonayo anayankha kuti: “Rab·boʹni,* ndithandizeni kuti ndiyambe kuona.” 52 Yesu anamuuza kuti: “Pita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Nthawi yomweyo anayamba kuona,+ ndipo anayamba kutsatira Yesu mumsewu.
11 Iwo atayandikira ku Yerusalemu, ku Betefage ndi ku Betaniya+ paphiri la Maolivi, Yesu anatumiza ophunzira ake awiri.+ 2 Iye anawauza kuti: “Pitani mʼmudzi umene mukuuonawo ndipo mukakangolowa mmenemo, mukapeza bulu wamngʼono wamphongo atamumangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukamumasule nʼkubwera naye kuno. 3 Wina akakakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumasula buluyu?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akangotha kumugwiritsa ntchito adzamubweza nthawi yomweyo.’” 4 Choncho iwo ananyamuka ndipo anapezadi bulu wamphongo atamumangirira pakhomo, mʼmphepete mwa msewu waungʼono. Ndipo iwo anamasula buluyo.+ 5 Koma ena mwa anthu amene anali ataimirira chapomwepo anawafunsa kuti: “Cholinga chanu nʼchiyani pomasula buluyu?” 6 Iwo anawauza zimene Yesu ananena ndipo anawalola kuti apite.
7 Anthuwo anabweretsa bulu uja+ kwa Yesu. Kenako anayala malaya awo akunja pabuluyo ndipo iye anakwerapo.+ 8 Komanso anthu ambiri anayala malaya awo akunja mumsewu ndipo ena anadula masamba mʼminda.+ 9 Ndiyeno amene anali patsogolo komanso amene ankabwera mʼmbuyo ankafuula kuti: “Mʼpulumutseni!+ Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!*+ 10 Wodalitsidwa ndi Ufumu wa atate wathu Davide+ umene ukubwerawo! Mʼpulumutseni kumwambamwambako!” 11 Iye analowa mu Yerusalemu nʼkufika mʼkachisi. Ndiyeno anayangʼanayangʼana zinthu zonse, koma popeza nthawi inali itatha kale, anapita ku Betaniya limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+
12 Tsiku lotsatira, pamene ankachoka ku Betaniya, anamva njala.+ 13 Ndiye ali chapatali ndithu, anaona mtengo wamkuyu umene unali ndi masamba. Iye anapita pomwepo kuti akaone ngati angapezemo kanthu. Koma atafika pamtengowo, sanapezemo chilichonse koma masamba okha basi, chifukwa sinali nyengo ya nkhuyu. 14 Choncho iye anauza mtengowo kuti: “Munthu sadzadyanso zipatso zako mpaka kalekale.”+ Ndipo ophunzira ake ankamvetsera.
15 Tsopano iwo anafika ku Yerusalemu. Kumeneko analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuthamangitsa anthu amene ankagulitsa ndi kugula zinthu mʼkachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a anthu amene ankasintha ndalama komanso mabenchi a anthu amene ankagulitsa nkhunda.+ 16 Iye sanalole aliyense kuti adutse mʼkachisimo atanyamula katundu. 17 Iye ankaphunzitsa ndipo ankauza anthuwo kuti: “Kodi Malemba sanena kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonseʼ?+ Koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+ 18 Ansembe aakulu ndi alembi anamva zimenezo, ndipo anayamba kufunafuna njira yoti amuphere+ chifukwa ankamuopa popeza gulu lonse la anthu linkadabwa ndi zimene ankaphunzitsa.+
19 Chakumadzulo kwa tsikulo, iwo anatuluka mumzindawo. 20 Koma mʼmamawa pamene ankadutsa, anaona kuti mtengo wamkuyu uja wafota kale ndi mizu yomwe.+ 21 Choncho Petulo, anaukumbukira ndipo ananena kuti: “Rabi, taonani! Mtengo wamkuyu umene munautemberera uja wafota.”+ 22 Yesu anawayankha kuti: “Muzikhulupirira Mulungu. 23 Ndithu ndikukuuzani kuti aliyense wouza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye mʼnyanja,’ ndipo sakukayikira mumtima mwake koma ali ndi chikhulupiriro kuti zimene wanena zichitikadi, zidzaterodi.+ 24 Nʼchifukwa chake ndikukuuzani kuti, zinthu zonse zimene mukupempha ndi kuzipempherera, muzikhulupirira kuti mwazilandira kale ndipo mudzazilandiradi.+ 25 Ndipo mukaimirira nʼkumapemphera, muzikhululuka chilichonse chimene wina anakulakwirani kuti Atate wanu wakumwamba akukhululukireninso machimo anu.”+ 26*——
27 Kenako anafikanso ku Yerusalemu. Ndipo pamene ankayenda mʼkachisi, ansembe aakulu, alembi ndi akulu anabwera 28 nʼkumufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 29 Yesu anawayankha kuti: “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo inenso ndikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi. 30 Kodi ubatizo umene Yohane ankachita+ unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu? Ndiyankheni.”+ 31 Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 32 Koma tinganene kuti ‘Unachokera kwa anthuʼ ngati?” Iwo ankaopa gulu la anthu, chifukwa anthu onsewo ankakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri.+ 33 Choncho iwo anayankha Yesu kuti: “Sitikudziwa.” Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”
12 Kenako anayamba kulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ nʼkumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa nʼkumanga nsanja.+ Atatero anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina.+ 2 Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo. 3 Koma iwo anamugwira nʼkumumenya ndipo anamubweza chimanjamanja. 4 Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema mʼmutu komanso kumuchitira zachipongwe.+ 5 Anatumizanso wina koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha. 6 Iye anatsala ndi mmodzi yekha woti amutumize, mwana wake wokondedwa.+ Choncho anamutumizadi nʼkunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 7 Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa! uyu ndi amene adzalandire cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ 8 Choncho anamugwira nʼkumupha ndipo anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo.+ 9 Kodi mwiniwake wa mundawo adzachita chiyani? Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.+ 10 Kodi simunawerengepo zimene lemba limanena? Paja limanena kuti: ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.*+ 11 Umenewu wachokera kwa Yehova* ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.’”+
12 Atamva zimenezo ankafuna kumugwira,* koma anaopa gulu la anthu, chifukwa iwo anadziwa kuti iye ananena fanizolo akuganiza za iwowo. Choncho anangomusiya nʼkuchokapo.+
13 Pambuyo pake anamutumizira ena mwa Afarisi ndi anthu amene ankatsatira Herode kuti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule.+ 14 Atafika, iwo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo simuchita zinthu pongofuna kusangalatsa munthu, chifukwa simuyangʼana maonekedwe a anthu, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi nʼzololeka* kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi tizipereka kapena tisamapereke?” Yesu anazindikira chinyengo chawo ndipo anawafunsa kuti: “Bwanji mukundiyesa? Bweretsani khobidi la dinari* kuno ndilione.” 16 Iwo anamubweretsera ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi komanso mawu akewa nʼzandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 17 Choncho Yesu ananena kuti: “Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ Ndipo iwo anadabwa naye kwambiri.
18 Kenako Asaduki amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma osasiya mwana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.+ 20 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira alibe ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkaziyo, koma nayenso anamwalira osasiya mwana. Zinachitikanso chimodzimodzi kwa wachitatu. 22 Ndipo onse 7 aja sanasiye mwana. Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 23 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.” 24 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu?+ 25 Chifukwa akufa akadzaukitsidwa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 26 Koma pa mfundo yakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge mʼbuku la Mose munkhani yokhudza chitsamba chaminga, kuti Mulungu anamuuza kuti: ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakoboʼ?+ 27 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.”+
28 Mmodzi wa alembi amene anafika nʼkuwamva akutsutsana, anadziwa kuti anawayankha bwino. Choncho anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo loyamba* ndi liti pa malamulo onse?”+ 29 Yesu anayankha kuti: “Loyamba ndi lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova* Mulungu wathu ndi Yehova* mmodzi. 30 Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.’+ 31 Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ Palibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.” 32 Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi ndipo palibenso Mulungu wina kupatulapo iyeyo.’+ 33 Ndipo kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, nʼzofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.”+ 34 Yesu atazindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru, anamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Koma panalibe amene analimba mtima kuti amufunsenso.+
35 Komabe, pamene Yesu ankaphunzitsa mʼkachisi, ananena kuti: “Nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 36 Kudzera mwa mzimu woyera,+ Davideyo ananena kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako.”’+ 37 Davideyo anamutchula kuti Ambuye, ndiye zingatheke bwanji kuti akhale mwana wake?”+
Ndipo gulu lalikulu la anthu linkamumvetsera mosangalala. 38 Pophunzitsapo Yesu ananenanso kuti: “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika.+ 39 Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+ 40 Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*
41 Ndiyeno anakhala pansi pamalo amene ankatha kuona moponyeramo zopereka*+ ndipo anayamba kuona mmene gulu la anthu linkaponyera ndalama moponyera zoperekamo. Anaona anthu ambiri olemera akuponyamo makobidi ambiri.+ 42 Kenako panafika mkazi wamasiye wosauka ndipo anaponyamo timakobidi tiwiri tatingʼono, tochepa mphamvu kwambiri.*+ 43 Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama moponyera zoperekamo.+ 44 Zili choncho chifukwa onsewo aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene anali nazo, inde zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+
13 Yesu akutuluka mʼkachisi, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikukongolera!”+ 2 Koma Yesu anamuuza kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi? Pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+
3 Atakhala pansi mʼphiri la Maolivi, kachisi akuonekera bwino, Petulo, Yakobo, Yohane ndi Andireya anamufunsa ali paokha kuti: 4 “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zikufika kumapeto nʼchiyani?”+ 5 Choncho Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni.+ 6 Ambiri adzabwera mʼdzina langa nʼkunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri. 7 Komanso mukadzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi zikuyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+
8 Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha mavuto aakulu.*+
9 Koma inu khalani ochenjera. Anthu adzakutengerani kumakhoti aangʼono+ ndipo adzakukwapulani mumasunagoge+ nʼkukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo aphunzire za ine.+ 10 Komanso choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.+ 11 Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani. Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zomwezo chifukwa wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+ 12 Komanso munthu adzapereka mʼbale wake kuti aphedwe ndipo bambo adzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo awo ndipo adzachititsa kuti aphedwe.+ 13 Ndipo anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ Koma amene adzapirire* mpaka mapeto+ ndi amene adzapulumuke.+
14 Koma mukadzaona chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko+ chitaima pamalo amene sichikuyenera kuima (wowerenga adzazindikire), pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.+ 15 Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kapena kulowa mkati kukatenga chilichonse mʼnyumba mwakemo. 16 Ndipo munthu amene ali mʼmunda asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya mʼmbuyo kukatenga malaya ake akunja. 17 Tsoka kwa akazi oyembekezera komanso oyamwitsa ana mʼmasiku amenewo!+ 18 Pitirizani kupemphera kuti zisadzachitike mu nyengo yachisanu. 19 Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso+ chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo ndipo sichidzachitikanso.+ 20 Kunena zoona, Yehova* akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwa amene iye anawasankha, wafupikitsa masikuwo.+
21 Komanso pa nthawiyo, munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena, ‘Onani! Ali uko,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 22 Chifukwa kudzabwera anthu onamizira kuti ndi Khristu ndiponso aneneri abodza+ ndipo adzachita zizindikiro komanso zodabwitsa kuti ngati nʼkotheka, adzasocheretse osankhidwawo. 23 Choncho inuyo musamale.+ Ine ndakuuziranitu zinthu zonse.
24 Koma mʼmasiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake.+ 25 Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka. 26 Kenako anthu adzaona Mwana wa munthu+ akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.+ 27 Ndiyeno iye adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo 4, kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kukafika kumalekezero amumlengalenga.+
28 Tsopano phunzirani zokhudza mtengo wa mkuyu kuchokera pa fanizo ili: Nthambi yake yanthete ikaphuka nʼkuchita masamba, mumadziwa kuti chilimwe chili pafupi.+ 29 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.+ 30 Ndithu ndikukuuzani kuti mʼbadwo uwu sudzatha wonse kufa, mpaka zinthu zonsezi zitachitika.+ 31 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka,+ koma mawu anga adzakhalapo mpaka kalekale.+
32 Kunena za tsiku limenelo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, kupatulapo Atate wokha.+ 33 Khalani maso, khalani tcheru,+ chifukwa simukudziwa kuti nthawi yoikidwiratu idzafika liti.+ 34 Ndi zofanana ndi munthu amene akupita kudziko lina, amene wasiya nyumba mʼmanja mwa akapolo ake,+ aliyense pantchito yake, nʼkulamula mlonda wapageti kuti azikhala tcheru.+ 35 Choncho khalanibe maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwininyumba adzabwere.+ Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, mʼmbandakucha* kapena mʼmamawa,+ 36 kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona.+ 37 Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse: Khalani maso.”+
14 Tsopano kunangotsala masiku awiri kuti Pasika+ ndi Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa+ zichitike. Ndipo ansembe aakulu ndi alembi ankafunafuna njira yoti agwiritse ntchito pogwira* Yesu mochenjera nʼkumupha.+ 2 Iwo ankanena kuti: “Tisadzamugwire pachikondwerero, kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”
3 Pa nthawi imene Yesu anali ku Betaniya mʼnyumba mwa Simoni wakhate, kunafika mayi wina ali ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala la mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado weniweni ndipo anali okwera mtengo kwambiri. Iye anatsegula botolo la alabasitala lija mochita kuswa, nʼkuyamba kuthira mafutawo mʼmutu mwa Yesu.+ 4 Anthu ena ataona zimenezi, anayamba kuuzana mokwiya kuti: “Nʼchifukwa chiyani akuwononga chonchi mafuta onunkhirawa? 5 Mafuta onunkhirawatu akanatha kugulitsidwa ndalama zoposa madinari* 300 ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka!” Choncho iwo anakhumudwa kwambiri ndi mayiyo.* 6 Koma Yesu anawauza kuti: “Musiyeni, nʼchifukwa chiyani mukumuvutitsa? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+ 7 Chifukwa osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ ndipo mungathe kuwachitira zabwino nthawi iliyonse imene mwafuna. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+ 8 Mayiyu wachita zimene akanatha. Iye wathiriratu mafuta onunkhira pathupi langa pokonzekera kuikidwa mʼmanda kwanga.+ 9 Ndithu ndikukuuzani, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe padziko lonse,+ anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzamukumbukira.”+
10 Kenako Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anachoka nʼkupita kwa ansembe aakulu kuti akapereke Yesu kwa iwo.+ 11 Atamva zimenezo, iwo anasangalala ndipo anamulonjeza kuti amupatsa ndalama zasiliva.+ Choncho iye anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke.
12 Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ pamene mwamwambo ankapereka nsembe nyama ya Pasika,+ ophunzira ake anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako Pasika?”+ 13 Ndiyeno Yesu anatuma awiri mwa ophunzira akewo nʼkuwauza kuti: “Pitani mumzinda ndipo mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire,+ 14 ndipo mʼnyumba imene akalowe, mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 15 Iye akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukatikonzere Pasika mmenemo.” 16 Choncho ophunzirawo anapita nʼkulowa mumzinda ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo kumeneko anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
17 Chakumadzulo ndithu, Yesu anafika limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+ 18 Ndipo atakhala patebulo nʼkumadya chakudya, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu, amene akudya nane limodzi, andipereka.”+ 19 Iwo anamva chisoni ndipo anayamba kumufunsa mmodzimmodzi kuti: “Kodi ndine kapena?” 20 Iye anati: “Ndi mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane limodzi mʼmbalemu.+ 21 Mwana wa munthu achoka, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena za iye. Koma tsoka kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino kwa munthu ameneyu ngati akanapanda kubadwa.”+
22 Akupitiriza kudya, iye anatenga mkate nʼkuyamika Mulungu. Kenako anaunyemanyema nʼkuwapatsa ndipo anati: “Tengani, mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 23 Kenako anatenga kapu ya vinyo ndipo atayamika anaipereka kwa iwo moti onse anamwa.+ 24 Ndiyeno anawauza kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi anga+ a pangano,’+ amene adzakhetsedwe chifukwa cha anthu ambiri.+ 25 Ndithu ndikukuuzani, sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.” 26 Pamapeto pake, atamaliza kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,* anatuluka nʼkupita kuphiri la Maolivi.+
27 Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa nʼkundisiya ndekha, chifukwa Malemba amanena kuti: ‘Ndidzapha mʼbusa+ ndipo nkhosa zidzabalalika.’+ 28 Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+ 29 Koma Petulo anayankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa nʼkukusiyani, ine ndekha sindidzathawa.”+ 30 Atatero Yesu anamuyankha kuti: “Ndithu ndikukuuza iwe kuti lero, usiku womwe uno, tambala asanalire kawiri, undikana katatu.”+ 31 Koma iye anapitiriza kunena kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ndipo ena onse anayamba kunenanso chimodzimodzi.+
32 Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikukapemphera.”+ 33 Popita kumeneko anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane+ ndipo anayamba kumva chisoni komanso kuvutika kwambiri mumtima mwake. 34 Kenako anawauza kuti: “Ine ndikumva* chisoni+ chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso.”+ 35 Choncho atapita patsogolo pangʼono, anagwada mpaka nkhope yake pansi ndipo anayamba kupemphera kuti ngati zikanatheka, ola limeneli limupitirire. 36 Kenako anati: “Abba,* Atate,+ zinthu zonse nʼzotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+ 37 Atatero anabwerera ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Simoni, zoona ukugona? Kodi unalibe mphamvu kuti ukanakhalabe maso kwa ola limodzi?+ 38 Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 39 Atatero anachokanso kupita kukapemphera ndipo ananenanso mawu omwe aja.+ 40 Anabweranso nʼkuwapeza akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera, choncho iwo anasowa chomuyankha. 41 Anabweranso kachitatu nʼkuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula? Basi! Nthawi yakwana!+ Taonani! Mwana wa munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+
43 Nthawi yomweyo, mawu adakali mʼkamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi gulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu, alembi ndi akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+ 44 Apa nʼkuti womuperekayu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndikamukise* ndi yemweyo, mukamugwire nʼkupita naye ndipo muonetsetse kuti asathawe.” 45 Ndiyeno Yudasi anayenda molunjika nʼkufika kwa iye. Kenako anati: “Rabi!” Ndipo anamukisa. 46 Choncho iwo anamugwira nʼkumumanga. 47 Koma mmodzi mwa anthu amene anaimirira chapafupi anasolola lupanga lake nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 48 Koma Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba?+ 49 Tsiku ndi tsiku ndinali nanu mʼkachisi nʼkumaphunzitsa,+ koma simunandigwire. Komabe, izi zikuchitika kuti Malemba akwaniritsidwe.”+
50 Zitatero ophunzira ake onse anamuthawa nʼkumusiya yekha.+ 51 Koma mnyamata wina amene anangofunda nsalu yabwino popanda chovala china mkati, anayamba kumutsatira chapafupi ndipo anthuwo anayesa kuti amugwire. 52 Koma mnyamatayo anawasiyira mʼmanja nsalu yake ija nʼkuthawa ali maliseche.*
53 Tsopano iwo anatenga Yesu nʼkupita naye kwa mkulu wa ansembe+ ndipo ansembe aakulu komanso akulu ndi alembi onse anasonkhana kumeneko.+ 54 Koma Petulo ankamutsatira ali chapatali ndithu, mpaka anafika mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembeyo. Petuloyo anakhala pansi limodzi ndi antchito amʼnyumbamo nʼkumawotha moto walawilawi.+ 55 Ndiyeno ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni kuti anamizire Yesu mlandu nʼcholinga choti amuphe, koma sanaupeze.+ 56 Anthu ambiri ankapereka umboni wabodza kuti amunamizire mlandu,+ koma maumboni awowo ankatsutsana. 57 Komanso, anthu ena ankaimirira nʼkumapereka umboni womunamizira kuti: 58 “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja ndipo mʼmasiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’”+ 59 Komabe ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo sunali wogwirizana.
60 Kenako, mkulu wa ansembe anaimirira pakati pawo nʼkufunsa Yesu kuti: “Kodi suyankha? Kodi sukumva zimene anthuwa akukunenezazi?”+ 61 Koma iye anangokhala chete osayankha chilichonse.+ Apanso mkulu wa ansembe anayamba kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsidwayo?” 62 Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Inde ndinedi, ndipo mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera ndi mitambo yakumwamba.”+ 63 Mkulu wa ansembe atamva zimenezi anangʼamba zovala zake nʼkunena kuti: “Nanga tingafunenso mboni zina pamenepa?+ 64 Mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu. Mukuona bwanji pamenepa?”* Onse ananena kuti akuyenera kufa basi.+ 65 Ndipo ena anayamba kumulavulira,+ kumuphimba nkhope nʼkumamukhoma nkhonya. Iwo ankamuuza kuti: “Losera!” Atamuwomba mbama, asilikali apakhoti anamutenga.+
66 Tsopano pamene Petulo anali mʼmunsi, mʼbwalo, kunabwera mmodzi wa atsikana antchito a mkulu wa ansembe.+ 67 Ataona Petulo akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu, Mnazareti uja.” 68 Koma iye anakana kuti: “Sindikumudziwa ngakhale pangʼono ameneyo ndipo sindikumvetsa zimene ukunena.” Atatero anatuluka panja nʼkupita pageti.* 69 Kumenekonso mtsikana wantchito anamuona ndipo anayambanso kuuza anthu amene anali ataimirira chapafupi kuti: “Bambo awanso ali mʼgulu la ophunzira ake.” 70 Apanso Petulo anakana. Patapita kanthawi pangʼono, amene anali ataimirira chapafupi anayambanso kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli mʼgulu la ophunzira ake. Ndipo ndiwenso Mgalileya.” 71 Koma iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu amene mukunenayu ine sindikumudziwa ayi.” 72 Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri+ ndipo Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja akuti: “Tambala asanalire kawiri, udzandikana katatu.”+ Ndipo anamva chisoni nʼkuyamba kulira.
15 Mwamsanga mʼbandakucha, ansembe aakulu limodzi ndi akulu komanso alembi, kutanthauza Khoti lonse Lalikulu la Ayuda,* anasonkhana pamodzi kuti agwirizane zoti amuchite Yesu. Kenako anamumanga nʼkupita naye kukamupereka kwa Pilato.+ 2 Choncho Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?”+ Iye anayankha kuti: “Zili choncho, monga mmene mwanenera.”+ 3 Koma ansembe aakulu ankamuneneza zinthu zambiri. 4 Tsopano Pilato anamufunsanso kuti: “Kodi ukusowa choyankha?+ Taona kuchuluka kwa milandu imene akukuneneza.”+ 5 Koma Yesu sanayankhenso chilichonse, moti Pilato anadabwa kwambiri.+
6 Pa chikondwerero chilichonse, Pilato ankamasula mkaidi mmodzi amene anthu apempha.+ 7 Pa nthawiyo munthu wina dzina lake Baraba anali mundende limodzi ndi anthu oukira boma. Iwo anapha munthu pa nthawi imene ankaukira boma. 8 Choncho gulu la anthu linafika nʼkuyamba kupempha mogwirizana ndi zimene Pilato ankawachitira nthawi zonse. 9 Iye anawafunsa kuti: “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?”+ 10 Chifukwa Pilato ankadziwa kuti ansembe aakulu anamupereka chifukwa cha kaduka.+ 11 Komabe ansembe aakulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba.+ 12 Poyankha, Pilato anawafunsa kuti: “Nanga uyu amene mumati ndi Mfumu ya Ayuda, ndichite naye chiyani?”+ 13 Iwo anafuulanso kuti: “Apachikidwe ameneyo!”*+ 14 Koma Pilato anapitiriza kuwafunsa kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma anthuwo anapitiriza kufuula mwamphamvu kuti: “Ameneyo apachikidwe basi!”*+ 15 Atatero, pofuna kukwaniritsa zofuna za anthuwo, Pilato anawamasulira Baraba. Ndiyeno analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akamuphe pomupachika pamtengo.+
16 Asilikali anamutenga nʼkupita naye mʼbwalo lapanyumba ya bwanamkubwa. Kumeneko anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali.+ 17 Ndiyeno anamuveka chovala chapepo ndipo analuka chisoti chachifumu chaminga nʼkumuveka. 18 Tsopano anayamba kumufuulira kuti: “Moni, inu Mfumu ya Ayuda!”+ 19 Komanso ankamumenya mʼmutu ndi bango nʼkumamulavulira ndipo ankagwada nʼkumamuweramira. 20 Atamaliza kumunyozako, anamuvula chovala chapepo chija nʼkumuveka malaya ake akunja ndipo anatuluka naye kupita kukamukhomerera pamtengo.+ 21 Komanso iwo anakakamiza munthu wina amene ankangodutsa dzina lake Simoni wa ku Kurene kuti asenze mtengo wake wozunzikirapo.* Iyeyu ankachokera kudera lakumidzi ndipo anali bambo wa Alekizanda ndi Rufu.+
22 Choncho anafika naye pamalo otchedwa Gologota. Liwuli akalimasulira limatanthauza, “Malo a Chibade.”+ 23 Kumeneko anayesa kumupatsa vinyo wosakaniza ndi mule,+ koma iye anakana. 24 Ndipo anamukhomerera pamtengo nʼkugawana malaya ake akunja pochita maere pa malayawo, kuti aone chimene munthu aliyense angatenge.+ 25 Ndiyeno nthawi ili cha mʼma 9 koloko mʼmawa,* iwo anamukhomerera pamtengo. 26 Mawu osonyeza mlandu umene anamuphera anawalemba kuti: “Mfumu ya Ayuda.”+ 27 Komanso iwo anapachika pamtengo achifwamba awiri limodzi ndi iye. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+ 28*—— 29 Anthu amene ankadutsa pafupi ankanena mawu onyoza Yesu ndipo ankapukusa mitu yawo+ nʼkumanena kuti: “Iwe amene unkanena kuti ungathe kugwetsa kachisi nʼkumumanga mʼmasiku atatu,+ 30 dzipulumutse potsika pamtengo wozunzikirapowo!”* 31 Chimodzimodzinso ansembe aakulu limodzi ndi alembi nawonso ankamunyoza. Iwo ankanena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika!+ 32 Tsopanotu Khristu, Mfumu ya Isiraeli, itsike pamtengo wozunzikirapowo,* kuti ife tione ndi kukhulupirira.”+ Nawonso achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi aja ankamunyoza.+
33 Nthawi itakwana cha mʼma 12 koloko masana* kunagwa mdima mʼdziko lonselo, mpaka 3 koloko masana.*+ 34 Cha mʼma 3 kolokomo, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” Mawu amenewa akawamasulira amatanthauza kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 35 Ena mwa anthu amene anaimirira chapafupi atamva zimenezo anayamba kunena kuti: “Tamverani! Akuitana Eliya.” 36 Kenako wina anathamanga kukaviika siponji muvinyo wowawasa ndipo anaiika kubango nʼkumupatsa kuti amwe.+ Iye ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.” 37 Koma Yesu anafuula mokweza mawu ndipo anatsirizika.+ 38 Ndiyeno nsalu yotchinga yamʼnyumba yopatulika+ inangʼambika pakati kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 39 Tsopano, mtsogoleri wa asilikali amene anaimirira chapafupi moyangʼanizana ndi Yesu, ataona zimene zinachitika pa nthawi imene anatsirizika, ananena kuti: “Ndithudi munthu uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+
40 Panalinso azimayi amene ankaonerera chapatali ndithu. Ena mwa iwo anali Mariya wa ku Magadala, Mariya mayi a Yakobo Wamngʼono ndi Yose komanso panali Salome,+ 41 amene ankayenda naye limodzi nʼkumamutumikira+ pa nthawi imene anali ku Galileya. Panalinso azimayi ena ambiri amene anabwera naye limodzi kuchokera ku Yerusalemu.
42 Tsopano popeza anali madzulo kwambiri komanso linali Tsiku Lokonzekera, kapena kuti tsiku loti mawa lake ndi Sabata, 43 kunabwera Yosefe wa ku Arimateya, munthu wodziwika wa mʼKhoti Lalikulu la Ayuda, amenenso ankayembekezera Ufumu wa Mulungu. Iye anapita molimba mtima kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu.+ 44 Koma Pilato ankakayikira ngati anali atamwalira kale. Choncho anaitanitsa mtsogoleri wa asilikali nʼkumufunsa ngatidi Yesu anali atamwalira kale. 45 Atatsimikizira kuchokera kwa mtsogoleri wa asilikaliyo, analola kuti Yosefe akatenge mtembowo. 46 Ndiyeno Yosefe atagula nsalu yabwino kwambiri nʼkumutsitsa, anamukulunga ndi nsaluyo nʼkumuika mʼmanda*+ amene anawasema mʼthanthwe. Kenako anagubuduza chimwala nʼkutseka pakhomo la mandawo.+ 47 Koma Mariya wa ku Magadala ndi Mariya mayi wa Yose, anapitiriza kuyangʼanitsitsa pamene anaikidwapo.+
16 Tsiku la Sabata+ litatha, Mariya wa ku Magadala, Mariya+ mayi wa Yakobo ndi Salome anagula zonunkhiritsa kuti akapake thupi la Yesu.+ 2 Mʼmawa kwambiri tsiku loyamba la mlunguwo, iwo anafika kumandawo* dzuwa litatuluka.+ 3 Iwo ankafunsana kuti: “Ndi ndani amene akatigubuduzire chimwala chija pakhomo la mandawo?” 4 Koma atayangʼanitsitsa, anaona kuti mwalawo wagubuduzidwa kale ngakhale kuti unali waukulu kwambiri.+ 5 Atalowa mʼmandamo, anaona mnyamata atakhala pansi mbali yakumanja, atavala mkanjo woyera ndipo iwo anadabwa kwambiri. 6 Iye anawauza kuti: “Musadabwe choncho.+ Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, amene anaphedwa popachikidwa pamtengo. Iyetu waukitsidwa kwa akufa,+ muno mulibe. Taonani, pamene anamugoneka paja si apa!+ 7 Inuyo pitani mukauze ophunzira ake komanso Petulo kuti, ‘Watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona, mogwirizana ndi zimene anakuuzani.’”+ 8 Iwo atatuluka mʼmandawo anayamba kuthawa akunjenjemera komanso kunthunthumira kwambiri. Ndipo sanauze munthu aliyense zimene zinachitikazo chifukwa anali ndi mantha.*+
Mʼchilankhulo choyambirira, “pamaso pako.”
Maliko anatenga mawu amene ali mumkutiramawuwa pa Mki 3:1.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “ankawaviika; ankawamiza.”
MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesareti komanso nyanja ya Tiberiyo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atatentha thupi.”
Mabaibulo ena amati, “zinkamudziwa kuti ndi ndani.”
Kapena kuti, “atakhala patebulo.”
Kapena kuti, “mkate wachionetsero.”
Kapena kuti, “wakhama.”
Dzina limene Satana, yemwe ndi kalonga kapena kuti wolamulira ziwanda amadziwika nalo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “dengu loyezera.”
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakangʼono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita 4 ndipo kamakhala ndi nthambi.
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “kuphompho.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “Chigawo cha Mizinda 10.”
Kapena kuti, “watsala pangʼono kufa.”
Kapena kuti, “anamuchititsa kuti amve zopweteka zambiri.”
Kapena kuti, “anawalamula mwamphamvu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kopa.”
Kapena kuti, “chovala chowonjezera.”
Kapena kuti, “komanso amene ankadya nawo chakudya patebulo aja.”
Kepana kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Onani Zakumapeto B14.
Nthawi imeneyi inkayamba 3 koloko mpaka dzuwa litatuluka cha mma 6 koloko mʼmawa.
Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Onani Zakumapeto A3.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Chigawo cha Mizinda 10.”
Kapena kuti, “asanadye.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “wosakhulupirika.”
Mabaibulo ena amati, “Iwo sanauzedi aliyense zimenezo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A3.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A3.
Kapena kuti, “limakupunthwitsa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachimanga mugoli limodzi.”
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Mabaibulo ena amati, “anafunsana.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “amene amadziwika kuti.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza, “Mphunzitsi.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A3.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “kumumanga.”
Kapena kuti, “nʼzoyenera.”
Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “lofunika kwambiri.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “mʼmipando yabwino kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo amadya nyumba za akazi.”
Kapena kuti, “mwachiphamaso.”
Kapena kuti, “champhamvu.”
Kapena kuti, “bokosi la zopereka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malepitoni awiri amene anali okwana kwadiransi imodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “chiyambi cha mavuto aakulu ngati ululu umene mzimayi amamva akatsala pangʼono kubereka.”
Kapena kuti, “amene wapirira.”
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atambala akulira.”
Kapena kuti, “amangire.”
Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “anamulankhula mokwiya mayiyo; anakalipira mayiyo.”
Kapena kuti, “kuimba masalimo.”
Kapena kuti, “Moyo wanga ukumva.”
Mawu a Chiheberi kapena Chiaramu otanthauza “Ababa,” kapena, “Bambo anga!”
Kapena kuti, “ndikamupsompsone.”
Kapena kuti, “asanavale mokwanira; atavala zovala zamkati zokha.”
Kapena kuti, “Mukuganiza bwanji pamenepa?”
Kapena kuti, “nʼkupita pakanyumba kapageti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”
Kapena kuti, “Aphedwe popachikidwa pamtengo!”
Kapena kuti, “Aphedwe popachikidwa pamtengo basi!”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Onani Zakumapeto A3.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsowo.”
Mogwirizana ndi mipukutu yodalirika yakale, Uthenga Wabwino wa Maliko ukuthera muvesi 8. Onani Zakumapeto A3.