Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Luke 1:1-24:53
  • Luka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Luka
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Luka

UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NDI LUKA

1 Anthu ambiri ayesetsa kulemba nkhani yofotokoza zochitika zenizeni zimene ife tonse timazikhulupirira.*+ 2 Iwo analemba ndendende mmene anatiuzira anthu amene kuchokera pachiyambi, anali mboni zoona ndi maso+ komanso atumiki a uthengawo.+ 3 Inenso, popeza kuti ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pachiyambi, ndatsimikiza kuti ndikulembereni mwatsatanetsatane, inu wolemekezeka kwambiri, a Teofilo.+ 4 Ndachita zimenezi kuti mudziwe bwinobwino kuti zinthu zimene anakuphunzitsani ndi mawu apakamwa nʼzodalirika.+

5 Mʼmasiku a Herode,*+ mfumu ya Yudeya, kunali wansembe wina dzina lake Zekariya wa mʼgulu la ansembe la Abiya.+ Mkazi wake anali wochokera mwa ana aakazi a Aroni ndipo dzina lake anali Elizabeti. 6 Awiri onsewo anali olungama pamaso pa Mulungu chifukwa ankayenda mokhulupirika, mogwirizana ndi malamulo onse komanso zimene chilamulo cha Yehova* chimafuna. 7 Koma iwo analibe mwana chifukwa Elizabeti anali wosabereka ndipo onse awiri anali okalamba.

8 Tsopano pamene Zekariya ankagwira ntchito monga wansembe pamaso pa Mulungu, kuimira gulu lake la ansembe,+ 9 mogwirizana ndi zimene ansembe ankachita nthawi zonse,* inali nthawi yake yakuti akalowa mʼnyumba yopatulika ya Yehova,*+ akapereke nsembe zofukiza.+ 10 Gulu lonse la anthu linkapemphera panja, pa ola lopereka nsembe zofukizalo. 11 Mngelo wa Yehova* anaonekera kwa iye, ataimirira mbali yakumanja ya guwa lansembe zofukiza. 12 Koma Zekariya ataona zimenezo anavutika mumtima ndipo anachita mantha kwambiri. 13 Ndiye mngeloyo anamuuza kuti: “Usachite mantha Zekariya chifukwa pemphero lako lopembedzera lamveka ndithu. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yohane.+ 14 Udzasangalala komanso kukondwera kwambiri ndipo anthu ambiri adzasangalala ndi kubadwa kwake+ 15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova.*+ Koma asadzamwe vinyo ngakhale pangʼono kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa+ ndipo adzadzazidwa ndi mzimu woyera asanabadwe nʼkomwe.*+ 16 Iye adzathandiza Aisiraeli ambiri kuti alape nʼkuyambiranso kumvera Yehova* Mulungu wawo.+ 17 Komanso adzatsogola monga kalambulabwalo wa Mulungu ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.+ Iye adzatembenuza mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana+ ndipo anthu osamvera adzawatembenuzira ku nzeru yeniyeni ya anthu olungama. Adzachita zimenezi kuti asonkhanitse anthu amene akonzekera kutumikira Yehova.”*+

18 Ndiyeno Zekariya anafunsa mngeloyo kuti: “Nditsimikiza bwanji zimenezi? Inetu ndine wokalamba ndipo mkazi wanganso ali ndi zaka zambiri.” 19 Mngeloyo anamuyankha kuti: “Ine ndine Gabirieli+ amene ndimaima pamaso pa Mulungu+ ndipo wandituma kudzalankhula nawe komanso kudzalengeza uthenga wabwinowu kwa iwe. 20 Ndiye tamvera! Udzakhala chete osatha kulankhula, mpaka tsiku limene zinthu zimenezi zidzachitike chifukwa sunakhulupirire mawu anga amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake imene inaikidwiratu.” 21 Pa nthawiyi nʼkuti anthu akuyembekezerabe Zekariya ndipo anadabwa chifukwa chakuti anachedwa kwambiri mʼnyumba yopatulikayo. 22 Atatuluka sanathenso kulankhula nawo ndipo iwo anazindikira kuti waona zinthu zodabwitsa* mʼnyumba yopatulikayo. Iye ankalankhula nawo ndi manja, sankathanso kutulutsa mawu. 23 Masiku ake ochita utumiki wopatulika* atatha, anapita kwawo.

24 Patapita masiku angapo, mkazi wake Elizabeti anakhala woyembekezera ndipo anakhala kwayekha miyezi 5. Iye ananena kuti: 25 “Izitu nʼzimene Yehova* wandichitira masiku ano. Iye wandikumbukira kuti achotse kunyozeka kwanga pamaso pa anthu.”+

26 Elizabeti ali woyembekezera kwa miyezi 6, Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli+ kumzinda wina wa ku Galileya, wotchedwa Nazareti. 27 Anamutumiza kwa namwali+ amene mwamuna wina dzina lake Yosefe, wa mʼnyumba ya Davide, anamulonjeza* kuti adzamukwatira. Namwali ameneyu dzina lake anali Mariya.+ 28 Mngelo uja atafika kwa namwaliyu ananena kuti: “Moni, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova* ali nawe.” 29 Koma mawu amenewa anamudabwitsa kwambiri moti anayamba kuganizira za moni wamtundu umenewu. 30 Choncho mngeloyo anamuuza kuti: “Usaope Mariya, chifukwa Mulungu wakukomera mtima. 31 Tsopano mvetsera! Udzakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna+ ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu.+ 32 Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wamʼmwambamwamba.+ Yehova* Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.+ 33 Iye adzalamulira monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya ndipo Ufumu wake sudzatha.”+

34 Koma Mariya anafunsa mngeloyo kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, chifukwa sindinagonepo ndi mwamuna?”+ 35 Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe+ ndipo mphamvu ya Wamʼmwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechi amene adzabadweyo adzatchedwa woyera,+ Mwana wa Mulungu.+ 36 Ndipotu mʼbale wako Elizabeti, amene anthu amamunena kuti mkazi wosabereka, nayenso ndi woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna mu ukalamba wake, moti uno ndi mwezi wake wa 6. 37 Izi zachitika chifukwa zimene Mulungu wanena sizilephereka.”*+ 38 Ndiyeno Mariya ananena kuti: “Ndine kapolo wa Yehova!* Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” Atatero mngeloyo anamusiya.

39 Choncho mʼmasiku amenewo Mariya ananyamuka mofulumira nʼkupita kudera lamapiri, kumzinda wina mʼdziko la fuko la Yuda. 40 Kumeneko analowa mʼnyumba ya Zekariya nʼkupereka moni kwa Elizabeti. 41 Ndiyeno Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali mʼmimba mwakemo linadumpha ndipo Elizabetiyo anadzazidwa ndi mzimu woyera. 42 Choncho anafuula mwamphamvu kuti: “Ndiwe wodalitsidwa mwa akazi onse ndipo chipatso cha mimba yako nʼchodalitsidwanso! 43 Koma zatheka bwanji kuti ndipeze mwayi umenewu, kuti mayi wa Mbuye wanga abwere kwa ine? 44 Mawu a moni wako atalowa mʼmakutu mwangamu, khanda ladumpha mosangalala mʼmimba mwangamu. 45 Ndipotu ndiwe wosangalala chifukwa unakhulupirira, moti zonse zimene unauzidwa zochokera kwa Yehova* zidzakwaniritsidwa.”

46 Ndiyeno Mariya ananena kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova,*+ 47 ndipo mzimu wanga sungalephere kusefukira ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,+ 48 chifukwa waona malo otsika a kapolo wake wamkazi.+ Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wosangalala.+ 49 Chifukwa Wamphamvuyo wandichitira zazikulu ndipo dzina lake ndi loyera.+ 50 Kumibadwomibadwo iye amachitira chifundo anthu amene amamuopa.+ 51 Wachita zamphamvu ndi dzanja lake, wabalalitsira kutali amene zolinga zamʼmitima yawo zikusonyeza kuti ndi odzikuza.+ 52 Watsitsa anthu amphamvu pamipando yachifumu+ ndipo wakweza anthu onyozeka.+ 53 Wakhutitsa anthu anjala ndi zinthu zabwino+ koma amene anali ndi chuma wawathamangitsa chimanjamanja. 54 Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli pokumbukira lonjezo lake lakuti adzasonyeza chifundo+ 55 kwamuyaya, mogwirizana ndi zimene anauza makolo athu akale, Abulahamu ndi mbadwa* zake.”+ 56 Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu kenako anabwerera kwawo.

57 Tsopano nthawi yoti Elizabeti abereke inakwana ndipo anabereka mwana wamwamuna. 58 Anthu oyandikana naye komanso achibale ake anamva kuti Yehova* anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anasangalala naye limodzi.+ 59 Pa tsiku la 8, iwo anabwera kudzachita mdulidwe wa mwanayo+ komanso ankafuna kumupatsa dzina la bambo ake, lakuti Zekariya. 60 Koma mayi ake anayankha kuti: “Limenelo ayi! Dzina lake akhala Yohane.” 61 Atanena zimenezi, iwo anamuuza kuti: “Palibe wachibale wako aliyense amene amadziwika ndi dzina limenelo.” 62 Kenako anafunsa bambo ake, polankhula ndi manja, dzina limene akufuna kuti amupatse mwanayo. 63 Choncho iye anapempha poti alembepo ndipo analemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.”+ Ataona zimenezi onse anadabwa. 64 Nthawi yomweyo pakamwa pake panatseguka ndipo lilime lake linamasuka moti anayamba kulankhula+ ndi kutamanda Mulungu. 65 Anthu onse amene ankakhala mʼdera limenelo anagwidwa ndi mantha ndipo nkhani imeneyi inali mʼkamwamʼkamwa mʼdera lonse lamapiri ku Yudeya. 66 Onse amene anamva zimenezi anazisunga mʼmitima yawo ndipo ankanena kuti: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani?” Chifukwa dzanja la Yehova* linalidi pa iye.

67 Ndiyeno Zekariya, bambo a mwanayo, anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo ananenera kuti: 68 “Atamandike Yehova* Mulungu wa Isiraeli,+ chifukwa wakumbukira anthu ake nʼkuwabweretsera chipulumutso.+ 69 Iye watikwezera nyanga yachipulumutso*+ mʼnyumba ya mtumiki wake Davide,+ 70 mogwirizana ndi zimene ananena kudzera pakamwa pa aneneri ake oyera akale,+ 71 zoti adzatipulumutsa kwa adani athu ndiponso mʼmanja mwa onse amene amadana nafe.+ 72 Adzakwaniritsa zimene analonjeza makolo athu akale ndipo adzawasonyeza chifundo. Iye adzakumbukira pangano lake loyera,+ 73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abulahamu,+ 74 kuti pambuyo poti tapulumutsidwa mʼmanja mwa adani, atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye mopanda mantha, 75 mokhulupirika komanso mwachilungamo pamaso pake masiku athu onse. 76 Koma kunena za mwana wamngʼonowe, udzatchedwa mneneri wa Wamʼmwambamwamba, chifukwa udzatsogola pamaso pa Yehova* kuti ukakonze njira zake.+ 77 Kuti ukathandize anthu ake kudziwa za chipulumutso chimene chidzatheke machimo awo akadzakhululukidwa,+ 78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu. Ndi chifundo chimenechi, kuwala kwamʼmawa kudzatifikira kuchokera kumwamba, 79 ndipo kudzaunikira amene akukhala mumdima komanso mumthunzi wa imfa+ ndi kutsogolera mapazi athu panjira yamtendere.”

80 Choncho mwana uja anakula ndipo analimba mwauzimu. Iye anapitiriza kukhala mʼchipululu mpaka tsiku limene anadzionetsera poyera kwa Isiraeli.

2 Tsopano mʼmasiku amenewo, Kaisara Augusito analamula kuti anthu onse mʼdzikolo akalembetse mʼkaundula. 2 (Kalembera ameneyu anali woyamba ndipo anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya.) 3 Anthu onse anapita kukalembetsa ndipo aliyense anapita kumzinda wakwawo. 4 Yosefe+ nayenso anachoka ku Galileya, mumzinda wa Nazareti nʼkupita ku Yudeya, kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu,+ chifukwa anali wa mʼbanja komanso fuko la Davide. 5 Anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya amene anamanga naye banja malinga ndi pangano.+ Pa nthawiyi nʼkuti Mariya atatsala pangʼono kubereka.+ 6 Ali kumeneko, nthawi yoti abereke inakwana. 7 Iye anabereka mwana wake woyamba wamwamuna+ ndipo anamukulunga ndi nsalu nʼkumugoneka modyeramo ziweto,+ chifukwa sanapeze malo mʼnyumba ya alendo.

8 Mʼdera limeneli munalinso abusa amene ankagonera kumalo odyetsera ziweto nʼkumayangʼanira nkhosa zawo usiku wonse. 9 Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova* anaima chapafupi ndi iwo, ndipo ulemerero wa Yehova* unawala pamalo onsewo moti anachita mantha kwambiri. 10 Koma mngeloyo anawauza kuti: “Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhale nacho. 11 Chifukwa lero, mumzinda wa Davide+ mwabadwa mpulumutsi wanu,+ amene ndi Khristu Ambuye.+ 12 Ndikukupatsani chizindikiro ichi: Kumeneko mukapeza mwana wakhanda atamukulunga ndi nsalu nʼkumugoneka modyeramo ziweto.” 13 Mwadzidzidzi, panaoneka gulu lalikulu lakumwamba lili limodzi ndi mngeloyo+ ndipo linkatamanda Mulungu kuti: 14 “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo padziko lapansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amasangalala nawo.”

15 Choncho angelowo atachoka nʼkubwerera kumwamba, abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu kuti tikaone zimene zachitikazo, zimene Yehova* watidziwitsa.” 16 Iwo anapita mwamsanga ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe komanso mwana wakhandayo, atamugoneka modyeramo ziweto. 17 Ataona zimenezi, anafotokoza uthenga umene anauzidwa wokhudza mwana ameneyu. 18 Onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anawauza. 19 Koma Mariya anasunga mawu onsewa ndipo anayamba kuganizira tanthauzo la zimenezi mumtima mwake.+ 20 Kenako abusa aja anabwerera, akulemekeza komanso kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anamva ndi kuziona, mogwirizana ndi zimene anauzidwa.

21 Patatha masiku 8, nthawi yoti achite mdulidwe wa mwanayo itakwana,+ anamupatsa dzina lakuti Yesu. Limeneli ndi dzina limene mngelo uja anatchula Mariya asanakhale woyembekezera.+

22 Komanso nthawi yoti iwo ayeretsedwe mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose itakwana,+ anapita ndi mwanayo ku Yerusalemu kukamupereka kwa Yehova.* 23 Izi zinali zogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Yehova* kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* adzakhala woyera kwa Yehova.”*+ 24 Kumeneko iwo anapereka nsembe mogwirizana ndi zimene Chilamulo cha Yehova* chimanena kuti: “njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.”+

25 Ndiyeno mu Yerusalemu munali munthu wina dzina lake Simiyoni. Mwamuna ameneyu anali wolungama komanso wodzipereka kwa Mulungu. Iye ankayembekezera nthawi imene Mulungu adzatonthoze Isiraeli+ ndipo mzimu woyera unali pa iye. 26 Komanso Mulungu anamuululira kudzera mwa mzimu woyera kuti sadzafa asanaone Khristu wa Yehova.* 27 Ndiye motsogoleredwa ndi mzimu, anabwera kukachisi. Ndipo pamene makolo a mwanayo, Yesu, anamubweretsa kudzamuchitira zimene Chilamulo chinkafuna,+ 28 iye ananyamula mwanayo mʼmanja mwake nʼkutamanda Mulungu kuti: 29 “Tsopano, Ambuye Wamkulu Koposa, mukulola kapolo wanu kupita mu mtendere+ mogwirizana ndi zimene inu munanena, 30 chifukwa maso anga aona njira yanu yopulumutsira anthu+ 31 imene mwakonza pamaso pa anthu a mitundu yonse.+ 32 Maso anga aona kuwala+ kochotsa nsalu yophimba imene ikulepheretsa mitundu ya anthu kuti isamaone,+ komanso ndaona ulemerero wa anthu anu Aisiraeli.” 33 Bambo ake a mwanayo ndiponso mayi ake ankangodabwa ndi zimene Simiyoni ankanena zokhudza mwanayo. 34 Komanso Simiyoni anadalitsa makolowo ndipo anauza Mariya, mayi a mwanayo kuti: “Tamvera! Mwanayu waikidwa kuti ambiri agwe+ ndiponso kuti ambiri adzukenso mu Isiraeli.+ Komanso kuti akhale chizindikiro chimene anthu adzachitsutse+ 35 (inde, lupanga lalitali lidzakubaya)+ kuti zimene anthu ambiri akuganiza mumtima mwawo zionekere poyera.”

36 Kunalinso mneneri wamkazi, dzina lake Anna mwana wa Fanueli, wa fuko la Aseri. Mayi ameneyu anali wachikulire kwambiri ndipo anakhala ndi mwamuna wake zaka 7 zokha kuchokera pamene anakwatirana.* 37 Tsopano anali mkazi wamasiye ndipo anali ndi zaka 84 koma sankasowa pakachisi. Ankachita utumiki wopatulika masana ndi usiku ndipo ankasala kudya komanso kupemphera mopembedzera. 38 Mu ola limenelo iye anafika pafupi nʼkuyamba kuyamika Mulungu komanso kulankhula zokhudza mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.+

39 Choncho atachita zonse mogwirizana ndi Chilamulo cha Yehova,*+ anabwerera ku Galileya, kumzinda wawo wa Nazareti.+ 40 Mwanayo anapitiriza kukula ndiponso kukhala wamphamvu. Nzeru zake zinkachuluka ndipo Mulungu anapitiriza kusangalala naye.+

41 Chaka ndi chaka makolo ake ankakonda kupita ku Yerusalemu, kuchikondwerero cha Pasika.+ 42 Ndiye ali ndi zaka 12, iwo anapita naye kumeneko mogwirizana ndi mwambo wa chikondwererocho.+ 43 Chikondwererocho chitatha, iwo ananyamuka kubwerera kwawo. Koma mnyamatayo Yesu anatsalira ku Yerusalemu ndipo makolo ake sanadziwe zimenezo. 44 Iwo ankaganiza kuti iye anali nawo mʼgulu la anthu a pa ulendowo, moti anayenda ulendo wa tsiku lathunthu. Kenako anayamba kumufunafuna mwa achibale ndi anzawo. 45 Koma atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anamufufuza pena paliponse. 46 Ndiyeno patatha masiku atatu, anamupeza ali mʼkachisi, atakhala pakati pa aphunzitsi ndipo ankawamvetsera nʼkumawafunsa mafunso. 47 Koma onse amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.+ 48 Makolo akewo atamuona anadabwa kwambiri, ndipo mayi ake anamufunsa kuti: “Mwanawe, nʼchifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinali ndi nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.” 49 Koma iye anawayankha kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka mʼnyumba ya Atate wanga?”+ 50 Koma iwo sanamvetse zimene ankawauzazo.

51 Kenako ananyamuka nawo limodzi nʼkubwerera ku Nazareti ndipo anapitiriza kuwamvera.+ Apanso mayi akewo anasunga mosamala kwambiri mawu onsewa mumtima mwawo.+ 52 Koma Yesu anapitiriza kukula mu nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kusangalala naye.

3 Mʼchaka cha 15 cha ulamuliro wa Kaisara Tiberiyo, Pontiyo Pilato anali bwanamkubwa wa Yudeya. Herode*+ anali wolamulira chigawo cha Galileya.* Filipo mʼbale wake anali wolamulira chigawo cha madera a Itureya ndi Tirakoniti. Ndipo Lusaniyo anali wolamulira chigawo cha Abilene. 2 Mʼmasiku amenewo Anasi anali wansembe wamkulu ndipo Kayafa+ anali mkulu wa ansembe. Pa nthawiyo mawu a Mulungu anafika kwa Yohane+ mwana wa Zekariya mʼchipululu.+

3 Choncho iye anapita mʼmidzi yonse yapafupi ndi Yorodano ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+ 4 Ankachita zimenezi mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mawu a Mneneri Yesaya kuti: “Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.+ 5 Chigwa chilichonse chikwiriridwe, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zisalazidwe. Njira zokhotakhota zikhale zowongoka ndipo malo okumbikakumbika akhale osalaza bwino. 6 Anthu onse adzaona njira ya Mulungu yopulumutsira anthu.’”+

7 Choncho anayamba kuuza gulu la anthu amene ankabwera kwa iye kudzabatizidwa kuti: “Ana a njoka inu, ndi ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+ 8 Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kuti mwalapa. Ndipo musamadzinamize kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’ Chifukwa ndikukuuzani kuti Mulungu akhoza kupangira Abulahamu ana kuchokera kumiyala iyi. 9 Ndithudi, nkhwangwa yaikidwa kale pamizu ya mitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabereka zipatso zabwino udulidwa nʼkuponyedwa pamoto.”+

10 Ndiyeno gulu la anthu linkamufunsa kuti: “Nanga tichite chiyani?” 11 Iye anawayankha kuti: “Munthu amene ali ndi zovala ziwiri agawireko munthu amene alibiretu ndipo amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”+ 12 Okhometsa msonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa+ ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tichite chiyani?” 13 Iye anawauza kuti: “Musamalipiritse anthu* zambiri kuposa mtengo weniweni wa msonkho.”+ 14 Asilikali nawonso ankamufunsa kuti: “Kodi tichite chiyani?” Ndipo iye ankawauza kuti: “Musamavutitse anthu* kapena kuimba aliyense mlandu wabodza,+ koma muzikhutira ndi zimene mumalandira.”*

15 Tsopano anthu ankayembekezera Khristu ndipo onse ankaganiza mʼmitima yawo za Yohane kuti, “Kodi Khristu uja si ameneyu?”+ 16 Yohane anayankha onsewo kuti: “Ine ndikukubatizani ndi madzi. Koma wina wamphamvu kuposa ine akubwera, amene ine sindili woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.+ Iyeyu adzakubatizani ndi mzimu woyera komanso moto.+ 17 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili mʼmanja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira munkhokwe, koma mankhusu adzawawotcha ndi moto umene sungazimitsidwe.”

18 Iye anaperekanso malangizo ena ambiri ndipo anapitiriza kulengeza uthenga wabwino kwa anthu. 19 Ndiyeno popeza kuti Yohane anadzudzula Herode wolamulira chigawo pa nkhani yokhudza Herodiya, mkazi wa mʼbale wake, komanso chifukwa cha zoipa zonse zimene Herode anachita, 20 Herode anawonjezera choipa china pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.+

21 Pamene anthu onse anali kubatizidwa, Yesu nayenso anabatizidwa.+ Ndiye pamene ankapemphera, kumwamba kunatseguka,+ 22 ndipo mzimu woyera wooneka ngati nkhunda unatsika kudzamutera. Ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: “Iwe ndi Mwana wanga wokondedwa, umandisangalatsa kwambiri.”+

23 Pamene Yesu+ anayamba ntchito yake anali ndi zaka pafupifupi 30.+ Anthu ankadziwa kuti Yesu anali mwana

wa Yosefe,+

mwana wa Heli,

24 mwana wa Matati,

mwana wa Levi,

mwana wa Meliki,

mwana wa Yananai,

mwana wa Yosefe,

25 mwana wa Matatiyo,

mwana wa Amosi,

mwana wa Nahumu,

mwana wa Esili,

mwana wa Nagai,

26 mwana wa Maati,

mwana wa Matatiyo,

mwana wa Semeini,

mwana wa Yoseki,

mwana wa Yoda,

27 mwana wa Yoanani,

mwana wa Resa,

mwana wa Zerubabele,+

mwana wa Salatiyeli,+

mwana wa Neri,

28 mwana wa Meliki,

mwana wa Adi,

mwana wa Kosamu,

mwana wa Elimadama,

mwana wa Ere,

29 mwana wa Yesu,

mwana wa Eliezere,

mwana wa Yorimu,

mwana wa Matati,

mwana wa Levi,

30 mwana wa Sumiyoni,

mwana wa Yudasi,

mwana wa Yosefe,

mwana wa Yonamu,

mwana wa Eliyakimu,

31 mwana wa Meleya,

mwana wa Mena,

mwana wa Matata,

mwana wa Natani,+

mwana wa Davide,+

32 mwana wa Jese,+

mwana wa Obedi,+

mwana wa Boazi,+

mwana wa Salimoni,+

mwana wa Naasoni,+

33 mwana wa Aminadabu,

mwana wa Arini,

mwana wa Hezironi,

mwana wa Perezi,+

mwana wa Yuda,+

34 mwana wa Yakobo,+

mwana wa Isaki,+

mwana wa Abulahamu,+

mwana wa Tera,+

mwana wa Nahori,+

35 mwana wa Serugi,+

mwana wa Reu,+

mwana wa Pelegi,+

mwana wa Ebere,+

mwana wa Shela,+

36 mwana wa Kainani,

mwana wa Aripakisadi,+

mwana wa Semu,+

mwana wa Nowa,+

mwana wa Lameki,+

37 mwana wa Metusela,+

mwana wa Inoki,

mwana wa Yaredi,+

mwana wa Mahalaliyeli,+

mwana wa Kainani,+

38 mwana wa Enosi,+

mwana wa Seti,+

mwana wa Adamu,+

mwana wa Mulungu.

4 Kenako Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo mzimuwo unamutenga nʼkumuyendetsa malo osiyanasiyana mʼchipululu+ 2 kwa masiku 40, kumene ankayesedwa ndi Mdyerekezi.+ Pa masiku amenewo sanadye chilichonse ndipo masikuwo atatha, anamva njala. 3 Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.” 4 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”+

5 Choncho anapita naye pamalo okwera ndipo anamuonetsa maufumu onse apadziko lapansi mʼkanthawi kochepa.+ 6 Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine+ ndipo ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndingakonde kumupatsa. 7 Ndiye ngati inuyo mungandilambire kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.” 8 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+

9 Kenako anapita naye ku Yerusalemu ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi* nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+ 10 Paja Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu, kuti akutetezeni,’ 11 ndipo ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+ 12 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+ 13 Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo, anamusiya mpaka nthawi ina yabwino.+

14 Tsopano Yesu anabwerera ku Galileya+ atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu. Ndipo mbiri yake yabwino inamveka paliponse mʼmadera onse ozungulira. 15 Komanso anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo anthu onse ankamulemekeza.

16 Kenako anapita ku Nazareti+ kumene anakulira. Mogwirizana ndi chizolowezi chake pa tsiku la Sabata, analowa mʼsunagoge+ nʼkuimirira kuti awerenge Malemba. 17 Ndiyeno anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anatambasula mpukutuwo nʼkupeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18 “Mzimu wa Yehova* uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu osauka. Anandituma kudzalengeza za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina komanso zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale pa ufulu,+ 19 ndi kudzalalikira za chaka chovomerezeka kwa Yehova.”*+ 20 Atatero anapinda mpukutuwo nʼkuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndipo anakhala pansi. Maso a anthu onse amene anali mʼsunagogemo anali pa iye nʼkumamuyangʼanitsitsa. 21 Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+

22 Zitatero onse anayamba kumutamanda komanso anadabwa ndi mawu ogwira mtima amene anatuluka pakamwa pake,+ moti ankanena kuti: “Kodi si mwana wa Yosefe ameneyu?”+ 23 Atamva zimenezi iye anawauza kuti: “Mosakayikira mudzagwiritsa ntchito pa ine mawu akuti, ‘Wochiritsa iwe, dzichiritse wekha. Zinthu zambiri zimene tinamva kuti unachita ku Kaperenao,+ uzichitenso kwanu kuno.’” 24 Iye ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneri amene amalandiridwa kwawo.+ 25 Mwachitsanzo, ndithu ndikukuuzani kuti: Munali akazi ambiri amasiye mu Isiraeli mʼmasiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekedwa kwa zaka zitatu ndi miyezi 6 ndipo mʼdziko lonse munali njala yaikulu.+ 26 Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akazi amenewo. Mʼmalomwake anatumizidwa kwa mkazi wamasiye ku Zarefati mʼdziko la Sidoni.+ 27 Ndiponso munali akhate ambiri mu Isiraeli mʼnthawi ya mneneri Elisa. Komabe palibe aliyense wa iwo amene anayeretsedwa,* koma Namani wa ku Siriya.”+ 28 Tsopano anthu onse amene ankamvetsera zinthu zimenezi mʼsunagogemo anakwiya kwambiri.+ 29 Iwo ananyamuka ndipo mwamsangamsanga anamutulutsira kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phiri pamene panali mzinda wawo, kuti akamuponye kuphedi. 30 Koma iye anangodutsa pakati pawo nʼkumapita.+

31 Kenako anapita ku Kaperenao, mzinda wa ku Galileya. Ndipo ankawaphunzitsa pa tsiku la Sabata.+ 32 Kumeneko anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa ankalankhula mosonyeza kuti ali ndi ulamuliro. 33 Ndiyeno mʼsunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu, chiwanda chonyansa, ndipo anafuula mwamphamvu kuti:+ 34 “Aa! Kodi mukufuna chiyani kwa ife, inu Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu!”+ 35 Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza. 36 Ataona zimenezi anthu onse anadabwa kwambiri ndipo anayamba kukambirana kuti: “Taonani, mawu ake ndi amphamvu kwambiri! Chifukwa akutha kudzudzula mizimu yonyansa mwa ulamuliro ndi mphamvu ndipo mizimuyo ikutulukadi.” 37 Choncho mbiri yake inapitiriza kufalikira paliponse mʼmidzi yonse yozungulira.

38 Atatuluka mʼsunagogemo, anakalowa mʼnyumba ya Simoni. Pa nthawiyo apongozi aakazi a Simoni ankadwala malungo aakulu,* choncho anamupempha kuti awathandize.+ 39 Ndiyeno anaima pamene mayiwo anagona nʼkuwachiritsa ndipo malungowo anatheratu. Nthawi yomweyo mayiwo anadzuka nʼkuyamba kuwatumikira.

40 Koma pamene dzuwa linkalowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa poika manja ake pa iwo.+ 41 Ziwanda nazonso zinatuluka mwa anthu ambiri zikufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”+ Koma iye anadzudzula ziwandazo ndipo sanazilole kuti zilankhule+ chifukwa zinkamudziwa kuti ndi Khristu.+

42 Kutacha, anachoka nʼkupita kumalo kopanda anthu.+ Koma gulu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anamupempha kuti asachoke. 43 Koma iye anawauza kuti: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.”+ 44 Choncho anapita kukalalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.

5 Nthawi inayake, gulu la anthu linkamvetsera pamene Yesu ankaphunzitsa mawu a Mulungu mʼmphepete mwa nyanja ya Genesarete*+ ndipo anthuwo ankamupanikiza. 2 Ndiyeno iye anaona ngalawa ziwiri ataziimika mʼmphepete mwa nyanjayo, koma asodzi anali atatsikamo ndipo ankachapa maukonde awo.+ 3 Choncho iye analowa mʼngalawa imodzi, imene inali ya Simoni ndipo anamupempha kuti aisunthire mʼmadzi pangʼono. Kenako anakhala pansi mʼngalawamo nʼkuyamba kuphunzitsa gulu la anthulo. 4 Atamaliza kulankhula, anauza Simoni kuti: “Palasira kwakuya, ndipo muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.” 5 Koma poyankha Simoni anati: “Mlangizi, ife tagwira ntchito usiku wonse koma osapha kalikonse.+ Koma popeza mwanena ndinu, ndiponya maukondewa.” 6 Atachita zimenezo, anagwira nsomba zochuluka kwambiri. Ndipo maukonde awo anayamba kungʼambika.+ 7 Choncho anakodola anzawo amene anali mʼngalawa ina kuti adzawathandize. Iwo anabweradi, ndipo nsombazo zinadzaza ngalawa zonse ziwiri, moti ngalawazo zinayamba kumira. 8 Ataona zimenezi, Simoni Petulo anagwada pamaso pa Yesu ndipo anamuuza kuti: “Ambuye, chokani pali ine pano chifukwa ndine munthu wochimwa.” 9 Simoni komanso amene anali naye limodzi anadabwa kwambiri ndi nsomba zimene anaphazo. 10 Komanso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo,+ amene ankapha nsomba limodzi ndi Simoni anadabwa kwambiri. Koma Yesu anauza Simoni kuti: “Usachite mantha. Kuyambira lero uzisodza anthu amoyo.”+ 11 Choncho ngalawazo anafika nazo kumtunda, ndipo iwo anasiya chilichonse nʼkumutsatira.+

12 Nthawi inanso pamene anali mumzinda wina, anakumana ndi munthu wakhate thupi lonse. Munthuyo ataona Yesu, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo anamupempha kuti: “Ambuye, ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 13 Choncho Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo ananena kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+ 14 Kenako analamula munthuyo kuti asauze aliyense. Ndiyeno anamuuza kuti: “Koma upite ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe ya kuyeretsedwa kwako, monga mmene Mose analamulira,+ kuti ikhale umboni kwa iwo.”+ 15 Koma mbiri yake inafalikira kwambiri ndipo magulu a anthu ankasonkhana pamodzi kudzamumvetsera komanso kudzachiritsidwa matenda awo.+ 16 Komabe nthawi zambiri iye ankapita kumalo kwayekha kukapemphera.

17 Tsiku lina iye akuphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi a Chilamulo amene anachokera mʼmidzi yonse ya Galileya, ku Yudeya ndi ku Yerusalemu anakhala pansi pamalo omwewo. Ndipo mphamvu ya Yehova* inali pa iye kuti athe kuchiritsa.+ 18 Kenako panafika anthu atanyamula munthu wakufa ziwalo pamachira. Iwo ankafunafuna njira yoti amulowetsere mʼnyumbamo nʼkukamuika pafupi ndi Yesu.+ 19 Koma atalephera kudutsa naye chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, anakwera padenga. Ndipo kudzera pabowo limene anapanga padengapo, anamutsitsa limodzi ndi machirawo nʼkumufikitsa pakati pa anthu amene anali pamaso pa Yesu. 20 Ataona chikhulupiriro chawo anati: “Bwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ 21 Kenako alembi ndi Afarisi anayamba kudzifunsa kuti: “Kodi ameneyu ndi ndani kuti azinyoza Mulungu chonchi? Winanso ndi ndani amene angakhululukire machimo kupatulapo Mulungu?”+ 22 Koma Yesu atazindikira zimene ankaganiza anawafunsa kuti: “Kodi mukuganiza chiyani mʼmitima mwanu? 23 Chosavuta nʼchiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka uyendeʼ? 24 Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo—” kenako anauza wakufa ziwalo uja kuti: “Ndikunena ndi iwe, Nyamuka, tenga machira akowa ndipo uzipita kwanu.”+ 25 Nthawi yomweyo anaimirira onse akuona, ndipo ananyamula machira ake aja nʼkumapita kwawo, akutamanda Mulungu. 26 Ndiyeno anthu onsewo anadabwa kwambiri ndipo anayamba kutamanda Mulungu, moti anagwidwa ndi mantha. Iwo ankanena kuti: “Komatu lero ndiye taona zodabwitsa!”

27 Zimenezi zitachitika, Yesu anachokako. Kenako anaona munthu wina wokhometsa msonkho dzina lake Levi atakhala mu ofesi yokhomeramo msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ 28 Leviyo anasiya chilichonse ndipo ananyamuka nʼkuyamba kumutsatira. 29 Kenako Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu kunyumba kwake. Kumeneko kunabwera anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ndipo ankadya* limodzi ndi Yesu komanso ophunzira ake.+ 30 Afarisi ndi alembi awo ataona izi, anayamba kungʼungʼudza nʼkufunsa ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho komanso anthu ochimwa?”+ 31 Yesu anawayankha kuti: “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.+ 32 Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.”+

33 Iwo anamuuza kuti: “Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri ndipo amapemphera mopembedzera. Ophunzira a Afarisi amachitanso chimodzimodzi, koma anuwa amangodya ndi kumwa.”+ 34 Yesu anawayankha kuti: “Inu simungauze anzake a mkwati kuti asale kudya pamene mkwatiyo ali nawo limodzi, mungatero ngati? 35 Koma masiku adzafika pamene mkwati+ adzachotsedwa pakati pawo. Zikadzatero, iwo adzasala kudya masiku amenewo.”+

36 Komanso anawapatsa fanizo lakuti: “Palibe amene amadula chigamba pamalaya akunja atsopano nʼkuchisokerera pamalaya akunja akale. Munthu akachita zimenezo, chigamba chatsopanocho chimachoka pansalu yakaleyo. Ndiponso chigamba cha nsalu yatsopanocho sichigwirizana ndi malaya akalewo.+ 37 Komanso palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa akale. Munthu akachita zimenezo, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba achikopawo ndipo amatayika. Ndiponso matumba achikopawo amawonongeka. 38 Koma vinyo watsopano akuyenera kuikidwa mʼmatumba achikopa atsopano. 39 Munthu akamwa vinyo wakale safunanso watsopano, chifukwa amanena kuti, ‘Wakaleyu ali bwino kwambiri.’”

6 Tsiku lina pa tsiku la sabata, Yesu ankadutsa mʼmunda wa tirigu ndipo ophunzira ake ankabudula ngala za tirigu+ nʼkumazitikita mʼmanja mwawo kenako nʼkudya.+ 2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata?”+ 3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala?+ 4 Kodi simunawerenge kuti analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* imene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sankayenera kudya malinga ndi malamulo, koma ansembe okha?”+ 5 Kenako anapitiriza kuwauza kuti: “Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+

6 Tsiku linanso la sabata,+ iye analowa musunagoge nʼkuyamba kuphunzitsa. Mmenemo munali munthu amene dzanja lake lamanja linali lolumala.+ 7 Alembi ndi Afarisi ankamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa Sabata nʼcholinga choti amuimbe mlandu. 8 Koma iye anadziwa zimene iwo ankaganiza.+ Choncho anauza munthu wolumala dzanjayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.” Munthuyo ananyamuka nʼkuima pamenepo. 9 Kenako Yesu anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiyani pa Sabata, chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ 10 Atayangʼana uku ndi uku, anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhalanso labwinobwino. 11 Koma iwo anakwiya kwambiri ndipo anayamba kukambirana zoti amuchite Yesu.

12 Mʼmasiku amenewo, Yesu anapita kuphiri kukapemphera+ ndipo anachezera usiku wonse kupemphera kwa Mulungu.+ 13 Kutacha, anaitana ophunzira ake nʼkusankhapo 12, amenenso anawapatsa dzina lakuti atumwi.+ 14 Iye anasankha Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo, ndi Andireya mchimwene wake. Anasankhanso Yakobo, Yohane, Filipo,+ Batolomeyo, 15 Mateyu, Tomasi,+ Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa “wakhama.” 16 Komanso anasankha Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anamupereka.

17 Kenako anatsika nawo nʼkukaima pamalo afulati. Pamenepo panali gulu lalikulu la ophunzira ake. Panalinso chigulu cha anthu ochokera ku Yudeya konse ndi ku Yerusalemu konse, komanso kumadera amʼmphepete mwa nyanja a ku Turo ndi ku Sidoni. Onsewo anabwera kuti adzamumvetsere komanso kuti adzawachiritse. 18 Ngakhalenso amene ankavutitsidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa. 19 Gulu lonse la anthulo linkayesetsa kuti limugwire, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa iye+ nʼkuchiritsa anthu onsewo.

20 Kenako anayangʼana ophunzira ake nʼkuyamba kuwauza kuti:

“Osaukanu ndinu osangalala, chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wanu.+

21 Osangalala ndinu amene mukumva njala, chifukwa mudzakhuta.+

Osangalala ndinu amene mukulira, chifukwa mudzaseka.+

22 Ndinu osangalala anthu akamadana nanu,+ kukusalani,+ kukunyozani komanso kukana* dzina lanu nʼkumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu. 23 Sangalalani pa tsiku limenelo ndipo mudumphedumphe mokondwera, chifukwa mphoto imene Mulungu adzakupatseni ndi yaikulu,* popeza zinthu zimenezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri.+

24 Koma tsoka kwa inu amene muli achuma,+ chifukwa mukulandiriratu zonse zokusangalatsani.+

25 Tsoka inu amene mukukhuta panopa, chifukwa mudzamva njala.

Tsoka inu amene mukuseka panopa, chifukwa mudzamva chisoni komanso kulira.+

26 Muli ndi tsoka anthu onse akamanena zabwino za inu,+ popeza zinthu zimenezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri abodza.

27 Koma inu amene mukumvetseranu, ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kuchitira zabwino amene akudana nanu.+ 28 Pitirizani kudalitsa anthu amene akukutembererani komanso kupempherera amene akukunyozani.+ 29 Amene wakumenya mbama patsaya ili, umupatsenso linalo. Amene wakulanda malaya ako akunja, usamuletse kutenga malaya ako amkati.+ 30 Aliyense amene wakupempha kanthu mupatse,+ ndipo amene wakulanda zinthu usamuumirize kuti abweze.

31 Komanso, zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.+

32 Kodi mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzapindula chiyani? Chifukwa ngakhale ochimwa amakonda anthu okhawo amene amawakonda.+ 33 Ngati mumachitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mudzapindula chiyani? Chifukwa ngakhale ochimwa amachita zomwezo. 34 Komanso, ngati mumakongoza popanda chiwongoladzanja kwa okhawo amene mukuyembekezera kuti adzabweza ngongoleyo, mudzapindula chiyani?+ Ochimwanso amakongoza ochimwa anzawo popanda chiwongoladzanja, kuti adzawabwezere zomwezo. 35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino ndi kukongoza popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse.+ Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wamʼmwambamwamba, chifukwa iye ndi wokoma mtima kwa osayamika ndi kwa oipa.+ 36 Pitirizani kukhala achifundo, mofanana ndi Atate wanu amenenso ndi wachifundo.+

37 Komanso, siyani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa.+ Siyani kutsutsa ena ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa.+ 38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira mʼmatumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwa muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”

39 Kenako anawauzanso fanizo lakuti: “Munthu wosaona sangatsogolere wosaona mnzake, angatero ngati? Ngati angatero onse awiri angagwere mʼdzenje, si choncho?+ 40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake. 41 Nanga nʼchifukwa chiyani umayangʼana kachitsotso mʼdiso la mʼbale wako, koma osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako?+ 42 Ungauze bwanji mʼbale wako kuti, ‘Mʼbale taima ndikuchotse kachitsotso kamene kali mʼdiso lako,’ pamene iwe ukulephera kuona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako? Wachinyengo iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lakowo. Ukatero udzatha kuona bwino, moti udzakwanitsa kuchotsa kachitsotso kamene kali mʼdiso la mʼbale wako.

43 Mtengo wabwino sungabereke chipatso chowola ndipo mtengo wowola sungabereke chipatso chabwino.+ 44 Chifukwa mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake.+ Mwachitsanzo, anthu sathyola nkhuyu mumtengo waminga, kapena kudula mphesa pachitsamba chaminga. 45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino mʼchuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa mʼchuma choipa chamumtima mwake, chifukwa pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+

46 Nanga nʼchifukwa chiyani mumandiitana kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osachita zimene ndimanena?+ 47 Aliyense amene amabwera kwa ine kudzamva mawu anga, nʼkuchita zimene wamvazo, ndikuuzani amene amafanana naye:+ 48 Iyeyo ali ngati munthu amene pomanga nyumba, anakumba mozama kwambiri nʼkuyala maziko pathanthwe. Ndiye mtsinje utasefukira, madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza chifukwa anaimanga bwino.+ 49 Pamene munthu amene wamva koma osachita chilichonse,+ ali ngati munthu amene wamanga nyumba yopanda maziko padothi. Apanso mtsinje unasefukira nʼkuwomba nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo inagwa, moti kugwa kwake kunali kwakukulu.”

7 Yesu atamaliza kunena zonse zimene ankafuna kuuza anthu, analowa mumzinda wa Kaperenao. 2 Kumeneko kapolo wa mtsogoleri wina wa asilikali, amene mtsogoleriyo ankamukonda kwambiri, ankadwala ndipo anali atatsala pangʼono kumwalira.+ 3 Mtsogoleriyo atamva za Yesu, anatumiza akulu ena a Ayuda kwa iye kukamupempha kuti abwere kudzachiritsa kapolo wakeyo. 4 Anthuwo atafika kwa Yesu anayamba kumuchonderera ndi mtima wonse kuti: “Ameneyu ndi woyenereradi kuti mumuthandize, 5 chifukwa amakonda anthu amtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge.” 6 Choncho Yesu ananyamuka nawo limodzi. Koma atatsala pangʼono kufika kunyumbako, anakumana ndi anzake a mtsogoleri wa asilikali uja, amene anawatuma kuti adzamuuze kuti: “Ambuye musavutike ndi kubwera, sindine munthu woyenera kuti mulowe mʼnyumba mwanga.+ 7 Nʼchifukwa chake inenso sindinadzione kuti ndine woyenera kubwera kwa inu. Koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira. 8 Chifukwa inenso ndili ndi akuluakulu amene anaikidwa kuti azindiyangʼanira komanso ndili ndi asilikali amene ndimawayangʼanira. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti, ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.” 9 Yesu atamva zimenezi anadabwa ndi munthu ameneyu. Kenako anatembenukira gulu la anthu omwe ankamutsatira nʼkuwauza kuti: “Kunena zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.”+ 10 Koma anthu amene anatumidwa aja atabwerera kunyumba, anakapeza kapolo uja ali bwinobwino.+

11 Patangopita kanthawi pangʼono, ananyamuka kupita kumzinda wina wotchedwa Naini. Ophunzira ake ndiponso gulu lalikulu la anthu linkayenda naye limodzi. 12 Atayandikira pageti la mzindawo, anakumana ndi anthu atanyamula maliro. Munthu amene anamwalirayo anali mwana wamwamuna yekhayo kwa mayi ake.+ Komanso mayi akewo anali mkazi wamasiye. Gulu lalikulu ndithu la anthu ochokera mumzindawo linali limodzi ndi mayiwo. 13 Ambuye ataona mayiwo anawamvera chisoni,+ ndipo anawauza kuti: “Tontholani mayi.”+ 14 Atatero anayandikira nʼkugwira chithathacho ndipo amene ananyamulawo anangoima. Kenako iye ananena kuti: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, dzuka!”+ 15 Zitatero mnyamata amene anamwalirayo anadzuka nʼkuyamba kulankhula ndipo Yesu anamupereka kwa mayi ake.+ 16 Ataona zimenezi anthu onse anachita mantha ndipo anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu.”+ Ananenanso kuti, “Mulungu wakumbukira anthu ake.”+ 17 Nkhani imeneyi, yonena za Yesu, inafala paliponse mu Yudeya monse ndi mʼmadera onse ozungulira.

18 Ndiyeno ophunzira a Yohane anamuuza zinthu zonsezi.+ 19 Choncho Yohane anaitanitsa ophunzira ake awiri nʼkuwatuma kwa Ambuye kukafunsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja* ndinu+ kapena tiyembekezere wina?” 20 Atafika kwa iye amunawo ananena kuti: “Yohane Mʼbatizi watituma kudzakufunsani kuti: ‘Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndi inu kapena tiyembekezere wina?’” 21 Mu ola limenelo iye anachiritsa anthu ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana+ komanso amene ankadwala mwakayakaya ndi kutulutsa mizimu yoipa. Anathandizanso anthu ambiri amene anali ndi vuto losaona kuti ayambe kuona. 22 Choncho poyankha anauza amuna awiri aja kuti: “Pitani mukauze Yohane zimene mwaona ndi kumva: Amene anali ndi vuto losaona akuona,+ olumala akuyenda, akhate akuyeretsedwa ndipo amene anali ndi vuto losamva akumva.+ Akufa akuukitsidwa ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino.+ 23 Wosangalala ndi amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”+

24 Anthu amene Yohane anawatuma aja atachoka, Yesu anayamba kuuza gulu la anthu za Yohane kuti: “Kodi munapita mʼchipululu kukaona chiyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 25 Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena?+ Ayi, paja amene amavala zovala zapamwamba ndiponso anthu amene amakhala moyo wamwanaalirenji amapezeka mʼnyumba zachifumu. 26 Nangano munapita kukaona chiyani makamaka? Mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, Yohane ndi mneneri komanso ndi wofunika kwambiri kuposa aneneri.+ 27 Malemba amanena za iyeyu kuti: ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole kukakukonzera njira.’+ 28 Ndithudi ndikukuuzani, pa anthu onse,* palibe wamkulu kuposa Yohane. Koma munthu amene ali wocheperapo mu Ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iyeyu.”+ 29 (Anthu onse komanso okhometsa msonkho atamva zimenezi, analengeza kuti Mulungu ndi wolungama, chifukwa iwo anali atabatizidwa ndi Yohane.+ 30 Koma Afarisi ndi anthu odziwa Chilamulo ananyalanyaza malangizo amene Mulungu anawapatsa.+ Choncho Yohane sanawabatize.)

31 “Kodi anthu a mʼbadwo uwu ndiwayerekeze ndi ndani ndipo kodi akufanana ndi ndani?+ 32 Iwo ali ngati ana aangʼono amene akhala pansi mumsika nʼkumafuulirana kuti: ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunalire.’ 33 Mofanana ndi zimenezi, Yohane Mʼbatizi anabwera ndipo sakudya chakudya kapena kumwa vinyo,+ koma inu mukunena kuti: ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa munthu wabwera ndipo iye akudya ndi kumwa, koma inu mukunena kuti: ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa!’+ 35 Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha zotsatira zake.”+

36 Ndiyeno Mfarisi wina anaumiriza Yesu kuti akadye naye. Choncho anapita kunyumba ya Mfarisiyo ndipo anamupatsa chakudya. 37 Koma mayi wina amene anali wodziwika mumzindawo kuti ndi wochimwa, anamva kuti Yesu akudya chakudya mʼnyumba ya Mfarisiyo. Choncho anapita komweko ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala, muli mafuta onunkhira.+ 38 Atafika anagwada kumapazi ake nʼkuyamba kulira, moti anayamba kunyowetsa mapaziwo ndi misozi, kwinaku akupukuta mapaziwo ndi tsitsi lamʼmutu mwake. Komanso anakisa mapazi akewo mwachikondi nʼkuwapaka mafuta onunkhirawo. 39 Mfarisi amene anamuitana uja ataona zimenezi, mumtima mwake ananena kuti: “Munthuyu akanakhala kuti ndi mneneridi, akanadziwa kuti mkazi amene akumugwirayu ndi ndani, ndiponso kuti ndi wotani. Akanadziwa kuti ndi wochimwa.”+ 40 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Simoni, ndikufuna ndikuuze kanthu kena.” Iye anati: “Ndiuzeni Mphunzitsi!”

41 “Amuna awiri anatenga ngongole kwa munthu wina wokongoza ndalama. Mmodzi anatenga ngongole ya madinari* 500, koma winayo anatenga ngongole ya madinari 50. 42 Atalephera kubweza ngongolezo, mwiniwake uja anawakhululukira ndi mtima wonse. Kodi ndi ndani mwa awiriwo amene angakonde kwambiri wokongozayo?” 43 Poyankha Simoni anati: “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira zambiriyo.” Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola.” 44 Atatero anacheukira mayi uja nʼkuuza Simoni kuti: “Wamuona mayiyu? Ngakhale kuti ndalowa mʼnyumba yako, sunandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma mayiyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake nʼkuwapukuta ndi tsitsi lake. 45 Iwe sunandikise, koma chilowereni muno, mayiyu sanasiye kukisa mapazi anga mwachikondi. 46 Iwe sunathire mafuta mʼmutu mwanga, koma mayiyu wapaka mapazi anga mafuta onunkhira. 47 Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuza kuti, machimo ake akhululukidwa, ngakhale kuti ndi ochuluka.+ Nʼchifukwa chake akusonyeza chikondi chochuluka. Koma amene wakhululukidwa machimo ochepa amasonyezanso chikondi chochepa.” 48 Kenako anauza mayiyo kuti: “Machimo ako akhululukidwa.”+ 49 Anthu onse amene anakhala naye patebulopo anayamba kudzifunsa mumtima mwawo kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani amene amathanso ngakhale kukhululukira machimo?”+ 50 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa.+ Pita mu mtendere.”

8 Pasanapite nthawi yaitali, Yesu anayamba kuyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi nʼkumalalikira komanso kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.+ Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi. 2 Analinso ndi azimayi ena amene anawatulutsa mizimu yoipa komanso kuwachiritsa matenda awo. Ena mwa iwo anali Mariya amene ankatchulidwanso kuti Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7. 3 Jowana+ mkazi wa Kuza amene anali kapitawo wa Herode, Suzana ndi azimayi ena ambiri, amene ankatumikira Yesu ndi atumwiwo pogwiritsa ntchito chuma chawo.+

4 Ndiyeno gulu lalikulu la anthu litasonkhana, limodzi ndi ena amene ankamulondola kuchokera mʼmizinda yosiyanasiyana, Yesu anafotokoza fanizo lakuti:+ 5 “Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu zake. Pamene ankafesa, zina zinagwera mʼmbali mwa msewu nʼkupondedwapondedwa ndipo zinadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga.+ 6 Zina zinagwera pathanthwe. Koma zitamera, zinauma chifukwa panalibe chinyezi.+ 7 Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinkakulira limodzi ndi mbewuzo ndipo zinalepheretsa mbewuzo kukula.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino, ndipo zitakula, zinabereka zipatso kuwirikiza maulendo 100.”+ Atanena zimenezi, analankhula mokweza mawu kuti: “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

9 Koma ophunzira ake anamufunsa tanthauzo la fanizo limeneli.+ 10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse zinsinsi zopatulika za Ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuyangʼana aziyangʼana ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asamamvetse zimene zikunenedwa.+ 11 Tsopano fanizoli tanthauzo lake ndi ili: Mbewuzo ndi mawu a Mulungu.+ 12 Zogwera mʼmbali mwa msewuzo ndi anthu amene amamva mawuwo. Kenako Mdyerekezi amabwera nʼkudzachotsa mawuwo mʼmitima yawo kuti asakhulupirire ndiponso kupulumuka.+ 13 Zogwera pathanthwe ndi anthu amene amati akangomva mawuwo, amawalandira mosangalala, koma oterewa alibe mizu. Amakhulupirira kwa kanthawi, koma nthawi yoyesedwa ikafika amagwa.+ 14 Zimene zinagwera paminga, ndi anthu amene amva mawu a Mulungu koma chifukwa chotengeka ndi nkhawa, chuma+ ndi zosangalatsa za moyo uno,+ amalephera kukula bwino ndipo zipatso zawo sizikhwima.+ 15 Koma zogwera panthaka yabwino, ndi anthu amene pambuyo pomva mawuwo ndi mtima wabwino kwambiri,+ amawagwiritsitsa nʼkubereka zipatso mopirira.+

16 Palibe amene amati akayatsa nyale, amaivindikira ndi chiwiya kapena kuiika pansi pa bedi. Koma amaiika pachoikapo nyale kuti amene akulowa aone kuwala.+ 17 Chifukwa palibe chobisika chimene sichidzaululika. Ndipo zinthu zonse zosungidwa mwachinsinsi kwambiri zidzadziwika, sizidzabisika mpaka kalekale.+ 18 Choncho muzimvetsera mwatcheru kwambiri. Chifukwa amene ali nazo, adzapatsidwa zochuluka,+ koma amene alibe, adzalandidwa ngakhalenso zimene akuganizira kuti ali nazo.”+

19 Ndiyeno mayi ake ndi azichimwene ake+ anabwera kumeneko, koma chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, analephera kufika kumene iyeyo anali.+ 20 Koma ena anamuuza kuti: “Mayi anu ndi azichimwene anu aima panjapo akufuna kuonana nanu.” 21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Mayi anga ndi azichimwene anga ndi awa amene amamvetsera mawu a Mulungu nʼkumawachita.”+

22 Tsiku lina Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalawa ndipo anawauza kuti: “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Choncho iwo anayamba kupalasa.+ 23 Koma ulendowo uli mkati, Yesu anagona tulo. Kenako panyanjapo panayamba kuwomba mphepo yamkuntho, ndipo madzi anayamba kudzaza mʼngalawamo moti akanatha kumira.+ 24 Kenako anapita kukamudzutsa ndipo anamuuza kuti: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!” Atamva zimenezi anadzuka nʼkudzudzula mphepo ndi mafunde amphamvuwo, moti zinasiya, ndipo panyanjapo panakhala bata.+ 25 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo anagwidwa ndi mantha ndipo anathedwa nzeru, moti anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi ndani kwenikweni? Nanga taonani, akutha kulamula mphepo ndi madzi ndipo zikumumvera.”+

26 Ndiyeno anaimika ngalawa ija mʼdera la Agerasa,+ tsidya linalo, moyangʼanizana ndi Galileya. 27 Yesu atangotsika nʼkufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina wogwidwa ndi chiwanda wochokera mumzindawo. Kwa nthawi yaitali ndithu, munthuyo ankangokhala wosavala, komanso sankakhala mʼnyumba, koma kumanda.*+ 28 Munthuyo ataona Yesu, anafuula kwambiri nʼkudzigwetsa pansi pamaso pake. Kenako anafuula mwamphamvu kuti: “Kodi mukufuna chiyani kwa ine, Yesu, Mwana wa Mulungu Wamʼmwambamwamba? Chonde ndikukupemphani, musandizunze.”+ 29 (Chifukwa Yesu ankauza mzimu wonyansawo kuti utuluke mwa munthuyo. Mzimu umenewu unamugwira mwamphamvu maulendo ambiri.*+ Mobwerezabwereza ankamumanga ndi maunyolo komanso matangadza nʼkumamuyangʼanira. Koma chifukwa cha mphamvu ya chiwandacho, ankadula maunyolowo nʼkuthawira kumalo opanda anthu.) 30 Yesu anamufunsa kuti: “Dzina lako ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Khamu,” chifukwa mwa iye munalowa ziwanda zambiri. 31 Ziwandazo zinkamuchonderera mobwerezabwereza kuti asazilamule kuti zipite kuphompho.+ 32 Ndiyeno gulu lalikulu la nkhumba+ linkadya paphiri kumeneko. Choncho ziwandazo zinamuchonderera kuti azilole kukalowa munkhumbazo ndipo iye anazilola.+ 33 Zitatero ziwandazo zinatuluka mwa munthuyo nʼkukalowa munkhumbazo. Nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi nʼkulumphira mʼnyanja ndipo zinamira. 34 Koma abusa a ziwetozo ataona zimene zinachitikazo, anathawa nʼkukanena zimenezi mumzinda ndi mʼmidzi.

35 Kenako anthu anapita kukaona zomwe zinachitikazo. Iwo atafika kwa Yesu anapeza munthu amene anamutulutsa ziwanda uja atakhala pansi pafupi ndi Yesu. Munthuyo anali atavala bwino komanso maganizo ake ali bwinobwino ndipo iwo anachita mantha. 36 Amene anaona zimene zinachitikazo anawafotokozera mmene munthu wogwidwa ziwandayo anamuchiritsira. 37 Kenako gulu lonse lochokera mʼmidzi yapafupi ya Agerasa linamupempha kuti achoke kwawoko, chifukwa linagwidwa ndi mantha aakulu. Zitatero iye anakwera ngalawa kuti azipita. 38 Ndiyeno munthu amene anamutulutsa ziwanda uja anamupempha mobwerezabwereza kuti aziyenda naye. Koma Yesu anauza munthuyo kuti apite kwawo. Iye anati:+ 39 “Pita kunyumba ndipo ukafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Choncho munthu uja anapitadi ndipo ankafalitsa mumzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira.

40 Yesu atabwerera ku Galileya, gulu la anthu linamulandira ndi manja awiri, chifukwa onse ankamuyembekezera.+ 41 Kenako panafika munthu wina dzina lake Yairo. Munthu ameneyu anali mtsogoleri wa sunagoge. Ndiyeno anadzigwetsa pamapazi a Yesu nʼkuyamba kumuchonderera kuti apite kunyumba kwake.+ 42 Yairo anachita zimenezi chifukwa mwana wake wamkazi amene anali ndi zaka pafupifupi 12, mwana yekhayo amene anali naye, anali atatsala pangʼono kumwalira.

Pamene Yesu ankapita, anthu ambiri anamutsatira ndipo ankamupanikiza. 43 Ndiyeno panali mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi+ kwa zaka 12, ndipo palibe aliyense amene anatha kumuchiritsa.+ 44 Mayiyu anatsatira Yesu kumbuyo nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja.+ Nthawi yomweyo magazi ake anasiya kutuluka. 45 Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: “Ndi ndani amene wandigwira?” Onse atakana, Petulo anati: “Mlangizi, simukuona kuti anthu onsewa akuzungulirani ndipo akukupanikizani?”+ 46 Koma Yesu anati: “Ndithu wina wandigwira, chifukwa ndamva mphamvu+ ikutuluka mwa ine.” 47 Mayiyo ataona kuti zimene wachitazo zadziwika, anapita kwa Yesu akunjenjemera ndipo anagwada nʼkuulula pamaso pa anthu onse chimene chinamuchititsa kuti amugwire, komanso mmene wachirira nthawi yomweyo. 48 Koma iye anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”+

49 Ali mkati molankhula, panafika nthumwi ya mtsogoleri wa sunagoge uja, ndipo anamuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira. Musiyeni Mphunzitsiyu musamuvutitse.”+ 50 Yesu atamva zimenezi, anamuuza kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi, ndipo mwana wakoyo akhalanso ndi moyo.”*+ 51 Atafika kunyumbako sanalole kuti aliyense alowe naye limodzi mʼnyumba kupatulapo Petulo, Yohane ndi Yakobo komanso bambo ndi mayi a mtsikanayo. 52 Koma anthu onse ankalira komanso kudziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni. Choncho Yesu anawauza kuti: “Tontholani,+ chifukwa mwanayu sanamwalire, koma akugona.”+ 53 Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyoza, chifukwa ankadziwa kuti mwanayo wamwalira. 54 Koma iye anamugwira dzanja nʼkumuitana kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!”+ 55 Zitatero mzimu* wake+ unabwerera ndipo nthawi yomweyo anadzuka.+ Ndiyeno Yesu anawauza kuti amupatse chakudya mtsikanayo. 56 Pamenepo, makolo akewo anasangalala kwambiri, koma Yesu anawalangiza kuti asauze aliyense zimene zachitikazo.+

9 Kenako Yesu anasonkhanitsa atumwi 12 aja nʼkuwapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse+ komanso kuti azitha kuchiritsa matenda.+ 2 Ndiyeno anawatumiza kuti azikalalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuchiritsa anthu. 3 Iye anawauza kuti: “Musatenge kanthu pa ulendowu, kaya ndodo, thumba la chakudya, mkate, ndalama kapena malaya awiri.*+ 4 Mukafika panyumba iliyonse, muzikhala mʼnyumbayo mpaka nthawi yochoka kumeneko itakwana.+ 5 Kulikonse kumene munthu sakakulandirani, mukamatuluka mumzinda umenewo muzisansa fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni wowatsutsa.”+ 6 Pamenepo ananyamuka nʼkulowa mʼderalo mudzi ndi mudzi nʼkumalengeza uthenga wabwino komanso kuchiritsa anthu kwina kulikonse.+

7 Tsopano Herode,* wolamulira chigawo,* anamva zonse zimene zinkachitika. Iye anathedwa nzeru chifukwa ena ankanena kuti Yohane waukitsidwa.+ 8 Koma ena ankanena kuti Eliya waonekera. Enanso ankanena kuti mmodzi wa aneneri akale wauka.+ 9 Ndiyeno Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu.+ Nanga amene akuchita zomwe ndikumvazi ndi ndani?” Choncho ankafunitsitsa atamuona.+

10 Atumwi aja atabwerako anafotokozera Yesu zimene anachita.+ Atatero anawatenga nʼkupita nawo kwaokha mumzinda wotchedwa Betsaida.+ 11 Koma gulu la anthu linadziwa zimenezi moti linamutsatira. Yesu anawalandira bwino nʼkuyamba kuwauza za Ufumu wa Mulungu, ndipo anachiritsa amene ankafunika kuchiritsidwa.+ 12 Komano nthawi inali chakumadzulo. Choncho atumwi 12 aja anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzi ndi mʼmadera ozungulira kuti akapeze malo ogona komanso chakudya choti adye.”+ 13 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.”+ Iwo anati: “Tilibe chilichonse kupatulapo mitanda ya mkate isanu ndi nsomba ziwiri zokha basi. Kapenatu tipite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa.” 14 Panali amuna pafupifupi 5,000 ndipo Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Uzani anthuwa kuti akhale mʼmagulu a anthu 50.” 15 Ophunzirawo anachitadi zimenezo, moti anthu onsewo anakhala pansi. 16 Kenako anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndipo anadalitsa chakudyacho. Atatero ananyemanyema mitanda ya mkateyo nʼkuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo. 17 Choncho onse anadya nʼkukhuta, ndipo anatolera zotsala zodzaza madengu 12.+

18 Kenako akupemphera payekha, ophunzira ake anafika kwa iye. Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 19 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane Mʼbatizi, ena akumati Eliya, koma ena akumanena kuti mmodzi wa aneneri akale.”+ 20 Pamenepo anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu wa Mulungu.”+ 21 Ndiyeno anawalangiza mwamphamvu kuti asauze aliyense zimenezo.+ 22 Kenako anati: “Mwana wa munthu akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndipo adzaphedwa+ nʼkuukitsidwa patapita masiku atatu.”+

23 Kenako anauza onse kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha+ ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira tsiku ndi tsiku.+ 24 Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense amene wataya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+ 25 Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake kapena kudzivulaza?+ 26 Chifukwa aliyense wochita manyazi ndi ine komanso mawu anga, Mwana wa munthu adzachita nayenso manyazi akadzabwera mu ulemerero wake, wa Atate wake ndi wa angelo oyera.+ 27 Koma ndithu ndikukuuzani, pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa mʼpangʼono pomwe mpaka choyamba ataona Ufumu wa Mulungu.”+

28 Patapita masiku pafupifupi 8 atanena mawu amenewa, iye anatenga Petulo, Yohane ndi Yakobo nʼkukwera nawo phiri kukapemphera.+ 29 Pamene ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake anasintha ndipo chovala chake chinaoneka choyera kwambiri ndi chonyezimira. 30 Ndiyeno panaoneka anthu awiri akukambirana naye. Anthu amenewa anali Mose ndi Eliya. 31 Iwo anaonekera ndi ulemerero ndipo anayamba kukambirana za mmene Yesu adzachokere mʼdzikoli, ku Yerusalemu.+ 32 Apa nʼkuti Petulo ndi ena amene anali naye atatheratu ndi tulo. Koma tulo titawathera, anaona ulemerero wake+ ndiponso amuna awiri ataima naye. 33 Ndiyeno pamene amunawa ankasiyana naye, Petulo anauza Yesu kuti: “Mlangizi, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Choncho timange matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.” Koma iye sankazindikira zimene ankanena. 34 Pamene ankanena zimenezi, kunachita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Mtambowo utawaphimba, anachita mantha. 35 Ndiyeno panamveka mawu+ kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga, amene ndinamusankha.+ Muzimumvera.”+ 36 Pamene mawuwo ankamveka, anaona kuti Yesu ali yekha. Koma iwo anakhala chete ndipo sanauze aliyense mʼmasiku amenewo chilichonse pa zimene anaonazo.+

37 Tsiku lotsatira, atatsika mʼphirimo, chigulu cha anthu chinamuchingamira.+ 38 Munthu wina amene anali mʼgululo anafuula kuti: “Mphunzitsi, ndikukupemphani kuti mukaone mwana wanga wamwamuna, chifukwa ndi mmodzi yekhayo.+ 39 Mzimu umamugwira, ndipo mwadzidzidzi amafuula, kenako umamuchititsa kuti aphuphe kwinaku akuchita thovu. Mzimu umenewu umamuvulaza kwambiri ndipo zimavuta kuti umusiye. 40 Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse koma alephera.” 41 Yesu anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera naye kuno mwana wakoyo.”+ 42 Koma ngakhale pamene ankamupititsa kwa iye, chiwandacho chinamugwetsa pansi nʼkumuchititsa kuti aphuphe mwamphamvu. Yesu anakalipira mzimu wonyansawo nʼkuchiritsa mnyamatayo ndipo anamupereka kwa bambo ake. 43 Anthu onse anadabwa ndi mphamvu zodabwitsa za Mulungu.

Anthuwo adakali odabwa ndi zonse zimene iye ankachita, Yesu anauza ophunzira ake kuti: 44 “Mvetserani mosamala ndipo muzikumbukira mawu awa, chifukwa Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu.”+ 45 Koma ophunzirawo sanamvetse zimene anawauzazo. Tanthauzo lake linali lobisika kwa iwo kuti asazindikire ndipo ankaopa kumufunsa za mawu amenewa.

46 Kenako iwo anayamba kukangana zokhudza amene anali wamkulu pakati pawo.+ 47 Yesu atazindikira zimene ankaganiza mumtima mwawo, anatenga mwana wamngʼono nʼkumuimika pambali pake. 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati uyu mʼdzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ Chifukwa aliyense amene amachita zinthu ngati mwana wamngʼono pakati panu ndi amene ali wamkulu.”+

49 Kenako Yohane ananena kuti: “Mlangizi, ife tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndiye tinamuletsa, chifukwa sakuyenda ndi ife.”+ 50 Koma Yesu anamuuza kuti: “Musamuletse chifukwa amene sakutsutsana nanu, ali kumbali yanu.”

51 Pamene masiku oti atengedwe kupita kumwamba ankayandikira,*+ anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu. 52 Choncho anatuma anthu kuti atsogole. Anthuwo anakalowa mʼmudzi wa Asamariya kuti akakonzekere kufika kwake. 53 Koma anthu amʼmudziwo sanamulandire bwino+ chifukwa anatsimikiza mumtima mwake kuti apite ku Yerusalemu. 54 Ophunzira ake, Yakobo ndi Yohane+ ataona zimenezi, ananena kuti: “Ambuye, kodi mukufuna tiwaitanire moto kuchokera kumwamba kuti uwanyeketse?”+ 55 Koma iye anatembenuka nʼkuwadzudzula. 56 Choncho Yesu ndi ophunzira ake anapita kumudzi wina.

57 Ndiyeno ali pa ulendowo, winawake anauza Yesu kuti: “Ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.” 58 Koma Yesu anamuuza kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zamumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti nʼkutsamiritsa mutu wake.”+ 59 Kenako anauza munthu wina kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Koma munthuyo anati: “Ambuye, ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.”+ 60 Yesu anamuuza kuti: “Asiye akufa+ aike akufa awo, koma iwe pita ukalengeze zokhudza Ufumu wa Mulungu kulikonse.”+ 61 Winanso ananena kuti: “Ine ndikutsatirani Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzika amʼbanja langa.” 62 Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wogwira pulawo nʼkumayangʼana zinthu zakumbuyo+ sakuyenera Ufumu wa Mulungu.”+

10 Pambuyo pa zimenezi, Ambuye anasankha anthu ena 70 nʼkuwatumiza awiriawiri+ kuti atsogole kupita mumzinda ndi malo alionse kumene iye ankafunika kudzapitako. 2 Kenako anawauza kuti: “Inde, pali zinthu zambiri zofunika kukolola, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize antchito kukakolola.+ 3 Pitani! Inetu ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.+ 4 Musatenge chikwama cha ndalama, thumba la chakudya, kapena nsapato,+ ndipo musamapereke moni kwa wina aliyense* panjira. 5 Mukafika panyumba, choyamba muzinena kuti: ‘Mtendere ukhale panyumba pano.’+ 6 Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye. Koma ngati palibe, udzabwerera kwa inu. 7 Choncho muzikhala mʼnyumba imeneyo+ ndipo muzidya ndi kumwa zimene angakupatseni,+ chifukwa wantchito ayenera kulandira malipiro ake.+ Musamachoke kumene mwafikirako nʼkupita kunyumba zina.

8 Komanso mukalowa mumzinda ndipo iwo nʼkukulandirani, muzidya zimene akukonzerani, 9 muzichiritsanso odwala amene ali mmenemo komanso muziwauza kuti: ‘Ufumu wa Mulungu wakuyandikirani.’+ 10 Koma mukalowa mumzinda umene sanakulandireni bwino, muzichokamo nʼkupita mʼmisewu yawo nʼkunena kuti: 11 ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi lamumzinda wanu uno,+ limene lamatirira kumapazi kwathu. Komabe dziwani kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12 Ndikukuuzani, chilango cha mzinda umenewo chidzakhala chopweteka kwambiri pa tsiku limenelo kuposa cha Sodomu.+

13 Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanakhala kuti zinachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli nʼkukhala paphulusa.+ 14 Choncho chilango chanu pachiweruzo chidzakhala chopweteka kwambiri kuposa cha Turo ndi Sidoni. 15 Iwenso Kaperenao, kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi, koma udzatsikira ku Manda.*

16 Amene akukumverani, akumveranso ine.+ Amene akunyalanyaza inu, akunyalanyazanso ine ndipo amene akunyalanyaza ine, akunyalanyazanso Mulungu amene anandituma.”+

17 Kenako anthu okwana 70 aja anabwerera akusangalala ndipo anauza Yesu kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zimatigonjera tikagwiritsa ntchito dzina lanu.”+ 18 Atamva zimenezo iye anawauza kuti: “Ndayamba kuona Satana atagwa kale+ ngati mmene mphezi imachitira kuchokera kumwamba. 19 Taonani! Inetu ndakupatsani ulamuliro kuti muzitha kupondaponda njoka ndi zinkhanira. Komanso ndakupatsani ulamuliro kuti mugonjetse mphamvu zonse za mdani,+ ndipo palibe chimene chidzakuvulazeni. 20 Komano musasangalale chifukwa choti mizimu yakugonjerani, koma sangalalani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.”+ 21 Pa nthawi imeneyo Yesu anasangalala kwambiri mwa mzimu woyera nʼkunena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa anthu anzeru ndi ozindikira mwawabisira mosamala zinthu zimenezi+ ndipo mwaziulula kwa ana aangʼono. Inde Atate, chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike.+ 22 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha+ ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.”+

23 Ndiyeno Yesu ndi ophunzira akewo ali kwaokha, anawauza kuti: “Osangalala ndi anthu amene akuona zimene inu mukuonazi.+ 24 Chifukwa ndithu ndikukuuzani, aneneri ambiri komanso mafumu ankalakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione,+ komanso kuti amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve.”

25 Kenako munthu wina wodziwa Chilamulo anaimirira kuti amuyese ndipo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, ndizichita chiyani kuti ndidzapeze moyo wosatha?”+ 26 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi mʼChilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” 27 Iye anayankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, mphamvu zanu zonse ndi maganizo anu onse.’+ Komanso ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’”+ 28 Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola. Uzichita zimenezo ndipo udzapeza moyo.”+

29 Koma pofuna kudzionetsera kuti ndi wolungama,+ munthuyo anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndi ndani kwenikweni?” 30 Poyankha Yesu ananena kuti: “Munthu wina ankayenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko ndipo anakumana ndi achifwamba amene anamuvula nʼkumumenya koopsa. Kenako anachoka, nʼkumusiya atatsala pangʼono kufa. 31 Ndiye zinangochitika kuti wansembe wina ankadutsa mumsewu womwewo, koma atamuona, anangomulambalala. 32 Chimodzimodzinso Mlevi, atafika pamalowo nʼkumuona, anangomulambalala. 33 Koma panafika Msamariya wina+ amene ankadutsanso mumsewu womwewo. Ndipo atamuona, anamva chisoni. 34 Choncho anafika pamene panali munthuyo ndipo anathira mafuta komanso vinyo mʼmabala ake nʼkuwamanga. Kenako anamukweza pabulu wake nʼkupita naye kunyumba ya alendo kumene anamusamalira. 35 Tsiku lotsatira anatulutsa madinari* awiri nʼkupereka kwa mwini nyumba ya alendoyo ndipo anamuuza kuti: ‘Musamalireni bwino, mukawononga ndalama zina zowonjezera, ndidzakubwezerani ndikadzabwera.’ 36 Ndi ndani pa anthu atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda+ munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” 37 Iye anayankha kuti: “Ndi amene anamuchitira chifundoyo.”+ Ndiye Yesu anamuuza kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.”+

38 Ndiyeno iwo anapitiriza ulendo wawo ndipo analowa mʼmudzi wina. Kumeneko mayi wina dzina lake Marita+ anamulandira mʼnyumba mwake monga mlendo. 39 Iye anali ndi mchemwali wake dzina lake Mariya, amene anakhala pansi pafupi ndi Ambuye nʼkumamvetsera zimene ankanena.* 40 Koma Marita anatanganidwa ndi ntchito zambiri. Choncho anafika kwa Yesu nʼkunena kuti: “Ambuye, kodi sizikukukhudzani kuti mchemwali wangayu wandisiyira ndekha ntchito? Tamuuzeni kuti abwere adzandithandize.” 41 Poyankha Ambuye anamuuza kuti: “Marita, Marita, ukuda nkhawa ndiponso kutanganidwa ndi zinthu zambiri. 42 Komatu zinthu zofunika kwenikweni ndi zochepa, mwinanso nʼchimodzi chokha basi. Kumbali yake, Mariya wasankha chinthu chabwino kwambiri+ ndipo sadzalandidwa chinthu chimenechi.”

11 Tsopano Yesu ankapemphera pamalo enaake. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera ngati mmene Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”

2 Ndiyeno iye anawauza kuti: “Mukamapemphera muzinena kuti, ‘Atate, dzina lanu liyeretsedwe.*+ Ufumu wanu ubwere.+ 3 Mutipatse chakudya chalero mogwirizana ndi chakudya chofunika pa tsikuli.+ 4 Ndipo mutikhululukire machimo athu,+ chifukwa nafenso timakhululukira aliyense amene amatilakwira.*+ Komanso tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa.’”*+

5 Kenako anawauza kuti: “Tiyerekeze kuti mmodzi wa inu ali ndi mnzake ndipo wapita kwa mnzakeyo pakati pa usiku kukamupempha kuti, ‘Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate, 6 chifukwa mnzanga winawake wangofika kumene kuchokera ku ulendo ndipo ndilibe choti ndimupatse.’ 7 Koma mnzake ali mʼnyumbayo nʼkuyankha kuti: ‘Usandivutitse ine. Takhoma kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona kale. Sindingathe kudzuka kuti ndikupatse kanthu.’ 8 Ndithu ndikukuuzani, adzadzuka nʼkumupatsa chilichonse chimene akufuna, osati chifukwa chakuti ndi mnzake, koma chifukwa chakuti wakakamira kwambiri.+ 9 Choncho ndikukuuzani, pitirizani kupempha+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.+ 10 Chifukwa aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira. 11 Kodi pakati panu pali bambo amene mwana wake atamupempha nsomba, angamupatse njoka mʼmalo mwa nsomba?+ 12 Kapenanso atamupempha dzira, kodi angamupatse chinkhanira? 13 Choncho ngati inuyo mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, ngakhale kuti ndinu oipa, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.”+

14 Kenako anatulutsa chiwanda mwa munthu chimene chinkamulepheretsa kulankhula.+ Chiwandacho chitatuluka, munthu wosalankhulayo analankhula ndipo gulu la anthu linadabwa kwambiri.+ 15 Koma ena mwa iwo ananena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule,* wolamulira ziwanda.”+ 16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumukakamiza kuti awasonyeze chizindikiro+ chochokera kumwamba. 17 Atadziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo nyumba yogawanika imagwa. 18 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana nayenso wagawanika, kodi ufumu wake ungakhalepo bwanji? Chifukwa inu mukunena kuti ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule. 19 Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Nʼchifukwa chake otsatira anuwo adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. 20 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu,+ ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikirani modzidzimutsa.+ 21 Munthu wamphamvu amene ali ndi zida zokwanira, akamalondera nyumba yake, chuma chake chimatetezeka. 22 Koma wina wamphamvu kuposa iyeyu akabwera nʼkumugonjetsa, amamulanda zida zake zonse zimene amadalira ndipo katundu amene wamulanda, amamugawa kwa ena. 23 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine ndipo amene sagwira ntchito yosonkhanitsa anthu limodzi ndi ine amawabalalitsa.+

24 Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa mʼmalo opanda madzi kufunafuna malo okhala, koma akapanda kupezeka, umanena kuti, ‘Ndibwerera kunyumba yanga imene ndinatulukamo ija.’+ 25 Ndiye ukafika umapeza kuti ndi mosesedwa bwino komanso mokongoletsedwa. 26 Ukatero umapita kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambiri kuposa umenewo ndipo ikalowa mkatimo imakhala mmenemo. Choncho zotsatira zake nʼzakuti zochita za munthuyo zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba.”

27 Ali mkati molankhula zimenezi, mayi wina mʼgulu la anthulo anafuula nʼkumuuza kuti: “Wosangalala ndi mayi amene mimba yake inanyamula inu ndiponso amene munayamwa mabere ake!”+ 28 Koma iye ananena kuti: “Ayi, mʼmalomwake, osangalala ndi anthu amene akumva mawu a Mulungu nʼkuwasunga!”+

29 Pamene gulu la anthulo linkachulukirachulukira, iye anayamba kunena kuti: “Mʼbadwo uwu ndi mʼbadwo woipa, ukufuna chizindikiro. Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.+ 30 Mofanana ndi Yona+ amene anakhala chizindikiro kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu adzakhalanso chizindikiro ku mʼbadwo uwu. 31 Mfumukazi yakumʼmwera+ adzaiukitsa kwa akufa pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi anthu a mʼbadwo uwu ndipo idzawatsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo. Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+ 32 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi mʼbadwo uwu ndipo adzautsutsa, chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano. 33 Munthu akayatsa nyale saiika pamalo obisika kapena kuivindikira ndi dengu,* koma amaiika pachoikapo nyale,+ kuti amene akulowa aone kuwala. 34 Nyale ya thupi ndi diso lako. Ngati diso lako likuyangʼana* pachinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhalanso lowala kwambiri. Koma ngati lili ladyera,* thupi lako lonse lidzachitanso mdima.+ 35 Choncho khala tcheru kuti kuwala kumene kuli mwa iwe kusakhale mdima. 36 Ndiye ngati thupi lako lonse ndi lowala kwambiri, popanda mbali ina yamdima, thupi lonse lidzawala kwambiri ngati mmene nyale imachitira pokuunikira ndi kuwala kwake.”

37 Atalankhula zimenezi, Mfarisi wina anamupempha kuti akadye naye. Choncho iye anapita ndipo anakadya chakudya. 38 Koma Mfarisiyo anadabwa ataona kuti akudya chakudyacho asanasambe.*+ 39 Choncho Ambuye anamuuza kuti: “Inu Afarisi muli ngati kapu ndi mbale zimene zatsukidwa kunja kokha koma mkati mwake muli mwakuda. Mkati mwa mitima yanu mwadzaza dyera ndi zinthu zoipa.+ 40 Anthu opanda nzeru inu! Kodi amene anapanga kunja si amenenso anapanga mkati? 41 Koma inu mukamapereka mphatso zachifundo,* muzipereka zinthuzo kuchokera pansi pamtima, mukatero zina zonse zokhudza inuyo zidzakhala zoyera. 42 Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti ndi ta luwe komanso cha mbewu zakudimba zamtundu uliwonse.+ Koma mumanyalanyaza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu! Unali udindo wanu kuchita zinthu zimenezi, koma simumayenera kunyalanyaza zinthu zinazo.+ 43 Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso kupatsidwa moni mʼmisika!+ 44 Tsoka kwa inu, chifukwa muli ngati manda* amene sakuoneka bwinobwino*+ moti anthu amayenda pamwamba pake koma osadziwa!”

45 Poyankha mmodzi wa anthu odziwa Chilamulo anamuuza kuti: “Mphunzitsi, zimene mukunenazi mukunyoza ndi ife tomwe.” 46 Ndiyeno iye anati: “Tsoka kwa inunso odziwa Chilamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simukhudza katunduyo ngakhale ndi chala chanu!+

47 Tsoka kwa inu, chifukwa mumamanga manda* a aneneri, komatu makolo anu ndi amene anawapha!+ 48 Mosakayikira, ndinu mboni pa zimene makolo anu anachita. Ndipo mukugwirizana ndi zimene anachitazo, chifukwa iwo anapha aneneri,+ pamene inu mukumanga manda awo. 49 Nʼchifukwa chake nzeru ya Mulungu inanenanso kuti: ‘Ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, koma iwo adzapha komanso kuzunza ena mwa iwo. 50 Choncho mʼbadwo uwu udzaimbidwa mlandu wa magazi a aneneri, amene anakhetsedwa kuyambira pamene dziko linakhazikika.+ 51 Kuyambira magazi a Abele+ mpaka magazi a Zekariya, amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi nyumba yopatulika.’*+ Inde ndikukuuzani, mʼbadwo uwu udzayankha mlandu wa magazi amenewo.

52 Tsoka kwa inu odziwa Chilamulo, chifukwa munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu. Inuyo simunalowemo,* ndipo anthu amene akufuna kulowamo mukuwatsekereza!”+

53 Choncho atachoka kumeneko, alembi ndi Afarisi anayamba kumupanikiza koopsa nʼkumamufunsa mafunso ambiri, 54 ndipo ankayembekezera kuti anene mawu oti amupezerepo chifukwa.+

12 Pa nthawiyi, chigulu cha anthu masauzande ambirimbiri chinasonkhana, moti ankapondanapondana. Ndiyeno Yesu anayamba kulankhula ndi ophunzira ake choyamba kuti: “Samalani ndi zofufumitsa za Afarisi, zimene ndi chinyengo.+ 2 Komatu palibe chimene chabisidwa mwachinsinsi kwambiri chimene sichidzaululika komanso palibe chinsinsi chimene sichidzadziwika.+ 3 Choncho chilichonse chimene mumanena mumdima chidzamveka poyera ndipo zimene mumanongʼona kwanokha mʼzipinda zanu zidzalalikidwa padenga. 4 Komanso ndikukuuzani mabwenzi anga,+ musamaope amene amapha thupi lokha, omwe sangathe kuchita zoposa pamenepa.+ 5 Koma ndikuuzani woti muzimuopa: Muziopa Iye amene amati akapha, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthu mʼGehena.*+ Ndithu ndikukuuzani, muziopa Ameneyu.+ 6 Mpheta 5 amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu,* si choncho? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa mbalame zimenezi imene Mulungu amaiiwala.*+ 7 Ndipotu ngakhale tsitsi lonse lamʼmutu mwanu amaliwerenga.+ Musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.+

8 Ndikukuuzani kuti, aliyense amene akuvomereza pamaso pa anthu kuti ndi wophunzira wanga,+ Mwana wa munthunso adzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu kuti ndi wophunzira wake.+ 9 Koma aliyense amene adzandikane pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.+ 10 Ndipo aliyense amene wanena mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa. Koma aliyense amene wanyoza mzimu woyera, sadzakhululukidwa.+ 11 Akapita nanu kumabwalo amilandu,* kwa akuluakulu aboma komanso kwa olamulira, musade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukanena chiyani,+ 12 chifukwa mzimu woyera udzakuphunzitsani mu ola lomwelo zimene mukuyenera kunena.”+

13 Kenako munthu wina mʼgululo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mumuuze mchimwene wanga kuti andigawireko cholowa.” 14 Iye anamuuza kuti: “Munthu iwe, ndi ndani amene anandisankha kuti ndikhale woweruza wanu kapena wogawa chuma chanu?” 15 Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi dyera* lamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”+ 16 Atatero anawauza fanizo lakuti: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino. 17 Choncho anayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi?’ 18 Ndiyeno anati, ‘Ndichita izi:+ Ndigwetsa nyumba zanga zosungiramo zinthu nʼkumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse ndidzazitutira mmenemo, 19 ndiye ndidzadziuza kuti: “Uli ndi zinthu zambiri zabwino ndipo zisungika kwa zaka zambiri. Mtima mʼmalo, udye, umwe ndi kusangalala.”’ 20 Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako aufuna. Nanga zinthu zimene wasungazi zidzakhala za ndani?’+ 21 Umu ndi mmene zimakhalira ndi munthu amene wadziunjikira chuma, koma si wolemera kwa Mulungu.”+

22 Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chake ndikukuuzani kuti, siyani kudera nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ 23 Chifukwa moyo ndi wofunika kwambiri kuposa chakudya ndipo thupi ndi lofunika kwambiri kuposa chovala. 24 Ganizirani za akhwangwala: Iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nkhokwe kapena nyumba yosungiramo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa.+ Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame?+ 25 Ndi ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pangʼono pokha* chifukwa cha kuda nkhawa? 26 Choncho ngati inu simungathe kuchita zimenezi, nʼchifukwa chiyani mukuda nkhawa ndi zinthu zinazo?+ 27 Ganizirani za mmene maluwa amakulira: Iwo sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Koma ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.+ 28 Ndiye ngati Mulungu amaveka chonchi zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha mawa nʼkuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo. 29 Choncho siyani kudera nkhawa kuti mudzadya chiyani komanso kuti mudzamwa chiyani ndipo siyani kuvutika mumtima.+ 30 Chifukwa zonsezi ndi zinthu zimene anthu a mitundu ina mʼdzikoli amazifunafuna mwakhama, koma Atate wanu amadziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.+ 31 Mʼmalomwake nthawi zonse muziika Ufumu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.+

32 Musaope, kagulu ka nkhosa inu,+ chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.+ 33 Gulitsani zinthu zanu nʼkupereka mphatso zachifundo.*+ Pangani zikwama za ndalama zomwe sizingathe, kutanthauza chuma chosatha kumwamba,+ kumene akuba sangafikeko komanso njenjete* sizingawononge. 34 Chifukwa kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko.

35 Valani epuloni ndipo mukhale okonzeka.*+ Nyale zanu zikhale zikuyaka+ 36 ndipo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kuti mbuye wawo abwere+ kuchokera ku ukwati,+ kuti akafika nʼkugogoda amutsegulire mwamsanga. 37 Osangalala ndi akapolo amene mbuye wawo pobwera adzawapeza akudikira! Ndithu ndikukuuzani, iye adzavala epuloni kuti agwire ntchito ndipo adzawakhazika patebulo kuti adye chakudya nʼkumawatumikira. 38 Iwo adzakhala osangalala ngati atawapeza akudikirabe ngakhale atafika pa ulonda wachiwiri* kapenanso wachitatu.* 39 Koma dziwani izi, ngati mwininyumba atadziwa nthawi imene wakuba angabwere, sangalole kuti wakuba athyole nʼkulowa mʼnyumba mwake.+ 40 Inunso khalani okonzeka, chifukwa Mwana wa munthu adzafika pa ola limene simukuliganizira.”+

41 Kenako Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi fanizoli mukutiuza ife tokha kapena mukuuzanso aliyense?” 42 Ndiye Ambuye ananena kuti: “Ndi ndani kwenikweni amene ndi mtumiki woyangʼanira nyumba wokhulupirika komanso wanzeru, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyangʼanira gulu la atumiki ake,* kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yoyenera?+ 43 Kapolo ameneyo adzakhala wosangalala, ngati mbuye wake pobwera adzamupeze akuchita zimenezo! 44 Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyangʼanira zinthu zake zonse. 45 Koma ngati kapolo ameneyu anganene mumtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiyeno nʼkuyamba kumenya antchito anzake aamuna ndi aakazi komanso kudya, kumwa ndi kuledzera,+ 46 mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera ndi pa ola limene sakulidziwa, ndipo adzamupatsa chilango choopsa nʼkumupatsa gawo, limodzi ndi anthu osakhulupirika. 47 Ndiyeno kapolo ameneyo, amene anadziwa zimene mbuye wake ankafuna koma osakonzekera kubwera kwake kapena kuchita zimene anamuuza,* adzakwapulidwa zikoti zambiri.+ 48 Koma amene sanadziwe ndipo wachita zinthu zofunika kumʼkwapula, adzamukwapula zikoti zochepa. Inde, aliyense amene anapatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunika kwa iye. Ndipo aliyense amene anaikidwa kuti aziyangʼanira zinthu zochuluka, anthu adzafunanso zochuluka kwa iye.+

49 Ndinabwera kudzakoleza moto padziko lapansi, ndiye ngati motowo wayaka kale, ndingafunenso chiyani? 50 Ndithudi pali ubatizo umene ndikuyenera kubatizidwa, ndipotu ndikuvutika kwambiri mumtima mpaka utatha!+ 51 Kodi mukuganiza kuti ndinabwera padziko lapansi kudzakhazikitsa mtendere? Ayi ndithu, koma ndinabwera kudzagawanitsa anthu.+ 52 Chifukwa kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, mʼnyumba imodzi mudzakhala anthu 5 osemphana maganizo, atatu kutsutsana ndi awiri, awiri kutsutsana ndi atatu. 53 Iwo adzagawanika, bambo kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna ndipo mwana wamwamuna kutsutsana ndi bambo ake. Mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi ndipo mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake. Mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake ndipo mkazi wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.”+

54 Kenako anauzanso gulu la anthulo kuti: “Mukaona mtambo ukukwera chakumadzulo, nthawi yomweyo mumanena kuti, ‘Kukubwera chimvula,’ ndipo chimabweradi. 55 Ndipo mukaona mphepo yakumʼmwera ikuwomba, mumanena kuti, ‘Lero kutentha kwambiri,’ ndipo zimachitikadi. 56 Anthu achinyengo inu! Mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi kuthambo. Nanga zimakukanikani bwanji kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika pa nthawi ino?+ 57 Nʼchifukwa chiyani panokha simutha kuzindikiranso zinthu zimene ndi zolungama? 58 Mwachitsanzo, ukamapita ndi munthu amene akukuimba mlandu kwa wolamulira, muli mʼnjira udziyesetsa kuchitapo kanthu kuti uthetse mlanduwo. Uzichita zimenezi kuti asakutengere kwa woweruza, woweruzayo nʼkukupereka kwa msilikali wapakhoti, msilikaliyo nʼkukuponya mʼndende.+ 59 Ndithu ndikukuuza, sudzatulukamo mpaka utalipira kakhobidi kotsiriza kochepa mphamvu kwambiri.”*

13 Pa nthawiyo, ena mwa anthu amene anali pamenepo anamufotokozera za Agalileya amene magazi awo, Pilato anawasakaniza ndi nsembe zawo. 2 Iye anawayankha kuti: “Kodi mukuganiza kuti Agalileya amenewo anali ochimwa kwambiri kuposa Agalileya ena onse chifukwa chakuti zimenezo zinawachitikira? 3 Ayi ndithu. Choncho ndikukuuzani kuti ngati simulapa, nonsenu mudzawonongedwa mofanana ndi iwowo.+ 4 Nanga bwanji za anthu 18 aja, amene nsanja inawagwera ku Siloamu nʼkuwapha? Kodi mukuganiza kuti anali ochimwa kwambiri kuposa anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu? 5 Ayi ndithu. Choncho ndikukuuzani kuti, ngati simulapa, nonsenu mudzawonongedwa ngati mmene iwo anawonongedwera.”

6 Kenako anayamba kufotokoza fanizo ili: “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu mʼmunda wake wa mpesa, ndipo anapita kukafuna chipatso mumtengowo, koma sanapezemo chilichonse.+ 7 Ndiyeno anauza munthu wosamalira munda wa mpesawo kuti, ‘Kwa zaka zitatu tsopano ndakhala ndikubwera kudzafuna nkhuyu mumtengowu, koma sindinapezemo ngakhale imodzi. Uduleni mtengo umenewu! Nʼchifukwa chiyani ukungowononga nthaka?’ 8 Wosamalira mundayo anayankha kuti, ‘Mbuyanga, bwanji muusiye chaka chino chokha. Ine ndikumba kuzungulira mtengowu nʼkuthirapo manyowa. 9 Ukadzabereka zipatso mʼtsogolo, zidzakhala bwino, koma ngati sudzabereka mudzaudule.’”+

10 Tsopano ankaphunzitsa mʼsunagoge winawake pa Sabata. 11 Mmenemo munali mayi wina amene mzimu woipa* unamudwalitsa kwa zaka 18. Iye anali wopindika msana moti sankatha kuweramuka. 12 Yesu atamuona, analankhula naye nʼkumuuza kuti: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.”+ 13 Ndiyeno anaika manja ake pamayiyo, ndipo nthawi yomweyo anaweramuka nʼkuyamba kutamanda Mulungu. 14 Koma mtsogoleri wa sunagoge ataona zimenezi, anakwiya chifukwa Yesu anachiritsa munthu pa Sabata. Choncho anauza gulu la anthu kuti: “Pali masiku 6 amene tikuyenera kugwira ntchito.+ Muzibwera masiku amenewo kudzachiritsidwa, osati tsiku la Sabata.”+ 15 Koma Ambuye anamuyankha kuti: “Achinyengo inu,+ kodi aliyense wa inu samasula ngʼombe yake kapena bulu wake mʼkhola pa Sabata nʼkupita naye kukamumwetsa madzi?+ 16 Kodi sikunali koyenera kuti mayi uyu, amenenso ndi mwana wa Abulahamu, amene Satana anamumanga kwa zaka 18, amasulidwe mʼmaunyolo amenewa tsiku la Sabata?” 17 Atanena zimenezi, onse amene ankamutsutsa anachita manyazi. Koma gulu lonse la anthu linayamba kusangalala chifukwa cha zodabwitsa zonse zimene iye anachita.+

18 Choncho anapitiriza kunena kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu uli ngati chiyani, nanga ndingauyerekezere ndi chiyani? 19 Uli ngati kanjere ka mpiru* kamene munthu anakatenga nʼkukadzala mʼmunda wake. Kenako kanamera nʼkukhala mtengo, moti mbalame zamumlengalenga zinamanga zisa munthambi zake.”+

20 Iye ananenanso kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu ndingauyerekezere ndi chiyani? 21 Uli ngati zofufumitsa zimene mayi wina anazitenga nʼkuzisakaniza ndi ufa wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezera,* moti mtanda wonsewo unafufuma.”+

22 Yesu anayenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Iye ankaphunzitsa nʼkumapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 23 Ndiyeno munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi nʼzoona kuti anthu amene adzapulumuke ndi ochepa?” Iye anawauza kuti: 24 “Yesetsani mwamphamvu kuti mulowe pakhomo lalingʼono.+ Chifukwa ndithu ndikukuuzani, ambiri adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha. 25 Mwininyumba akadzanyamuka nʼkukiya chitseko, inu mudzaima panja nʼkumagogoda chitsekocho, ndipo mudzanena kuti, ‘Ambuye titsegulireni.’+ Koma iye adzakuyankhani kuti: ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera.’ 26 Ndiyeno mudzayamba kunena kuti, ‘Tinkadya ndi kumwa pamaso panu ndipo inu munkaphunzitsa mʼmisewu yathu.’+ 27 Koma iye adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera. Chokani pamaso panga, inu nonse ochita zinthu zosalungama!’ 28 Kumeneko mudzalira ndi kukukuta mano mukadzaona Abulahamu, Isaki ndi Yakobo komanso aneneri onse ali mu Ufumu wa Mulungu, koma inuyo atakukankhirani kunja.+ 29 Komanso, anthu adzabwera kuchokera kumʼmawa, kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera ndipo adzakhala patebulo mu Ufumu wa Mulungu. 30 Ndithudi amene ali omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.”+

31 Mu ola lomwelo kunafika Afarisi ena nʼkumuuza kuti: “Nyamukani muchoke kuno, chifukwa Herode akufuna kukuphani.” 32 Iye anawayankha kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe imeneyo kuti, ‘Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchiritsa anthu lero ndi mawa, ndipo ndimaliza tsiku lachitatu.’ 33 Komabe ndiyenera kupitiriza ulendo wanga lero ndi mawa ndi tsiku linalo, chifukwa nʼkosayenera kuti mneneri amuphere kunja kwa Yerusalemu.+ 34 Yerusalemu, Yerusalemu, wopha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, ngati mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake mʼmapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 35 Tsopano tamverani! Mulungu wachoka nʼkukusiyirani nyumba yanuyi.+ Ndithu ndikukuuzani, simudzandionanso mpaka pamene mudzanene kuti: ‘Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!’”*+

14 Nthawi ina anapita kukadya chakudya mʼnyumba ya mmodzi wa atsogoleri a Afarisi pa Sabata ndipo anthu amene anali mʼnyumbamo ankamuyangʼanitsitsa. 2 Patsogolo pake panali munthu amene ankadwala matenda amene anachititsa kuti manja ndi miyendo yake itupe.* 3 Atamuona, Yesu anafunsa anthu odziwa Chilamulo komanso Afarisiwo kuti: “Kodi nʼzololeka kuchiritsa pa Sabata kapena ayi?”+ 4 Koma iwo anangokhala chete. Zitatero iye anagwira munthu uja nʼkumuchiritsa ndipo anamuuza kuti azipita kwawo. 5 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Ndi ndani wa inu amene mwana wake kapena ngʼombe yake itagwera mʼchitsime+ tsiku la Sabata, sangaitulutse nthawi yomweyo?”+ 6 Iwo sanathe kumuyankha funso limeneli.

7 Ataona kuti anthu amene anaitanidwawo akusankha malo olemekezeka kwambiri,+ anawauza fanizo kuti: 8 “Wina akakuitana kuphwando laukwati, usakhale pamalo olemekezeka kwambiri.+ Mwina nʼkutheka kuti waitananso wina wolemekezeka kuposa iwe. 9 Ndiye amene anakuitanani uja angabwere nʼkudzakuuza kuti, ‘Choka pamenepa pakhale bambo awa.’ Zikatero ungachokepo mwamanyazi nʼkukakhala kumapeto kwenikweni. 10 Koma ukaitanidwa, pita ndipo ukakhale kumapeto kwenikweni, kuti munthu amene anakuitana uja akafika adzakuuze kuti, ‘Bwanawe, khala pamalo aulemuwa.’ Zikadzatero udzalemekezeka pamaso pa alendo anzako onse.+ 11 Chifukwa aliyense amene amadzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.”+

12 Kenako anauzanso munthu amene anamuitana uja kuti: “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usaitane anzako, kapena azichimwene ako, kapena achibale ako, kapena anthu olemera omwe amakhala nawe pafupi. Mwina nthawi ina iwonso angadzakuitane ndipo adzakhala ngati akukubwezera. 13 Koma ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala ndi osaona.+ 14 Ukatero udzakhala wosangalala chifukwa alibe choti adzakubwezere. Mulungu adzakubwezera anthu olungama akamadzaukitsidwa.”+

15 Atamva zimenezi, mmodzi wa alendo anzake anamuuza kuti: “Wosangalala ndi munthu amene adzadye chakudya* mu Ufumu wa Mulungu.”

16 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la chakudya chamadzulo+ ndipo anaitana anthu ambiri. 17 Nthawi ya chakudya chamadzulocho itakwana, anatumiza kapolo wake kukauza anthu amene anawaitanawo kuti, ‘Tiyeni, chifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ 18 Koma onse anayamba kupereka zifukwa zokanira.+ Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda ndipo ndikuyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kubwera.’ 19 Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ngʼombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kubwera.’+ 20 Komanso wina ananena kuti, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sindingathe kubwera.’ 21 Ndiyeno kapolo uja anabwerera kukanena zimenezi kwa mbuye wake. Mwininyumbayo atamva zimenezi anakwiya ndipo anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita mwamsanga mʼmisewu ndi mʼnjira zamumzindawu, ukatenge anthu osauka, otsimphina, osaona komanso olumala nʼkubwera nawo kuno.’ 22 Patapita kanthawi kapolo uja anati, ‘Mbuyanga, zimene munalamula zachitika, komabe malo adakalipo.’ 23 Ndiyeno mbuye uja anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita mʼmisewu ina yakunja kwa mzinda ndipo ukalimbikitse anthu abwere kuno kuti nyumba yanga idzaze.+ 24 Chifukwa ndikukuuzani kuti, palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaitanidwa aja amene adzalaweko chakudya changa chamadzulo.’”+

25 Ndiyeno gulu lalikulu la anthu linkayenda limodzi ndi Yesu ndipo iye anacheuka nʼkuwauza kuti: 26 “Ngati wina akunditsatira koma osadana ndi* bambo ake, mayi ake, mkazi wake, ana ake, azichimwene ake komanso azichemwali ake, inde ngakhale moyo wake umene,+ sangakhale wophunzira wanga.+ 27 Aliyense wosanyamula mtengo wake wozunzikirapo* nʼkunditsatira sangakhale wophunzira wanga.+ 28 Mwachitsanzo, ndi ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi nʼkuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo? 29 Akapanda kutero, angayale maziko koma osatha kuimaliza ndipo onse oona angayambe kumuseka 30 nʼkumanena kuti: ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma zamukanika kumaliza.’ 31 Kapena ndi mfumu iti, imene popita kukakumana ndi mfumu inzake kunkhondo, siyamba yakhala pansi nʼkuganizira mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angathe kulimbana ndi asilikali 20,000 a mfumu imene ikubwera kudzalimbana naye? 32 Koma akaona kuti sangakwanitse, mwamsanga amatumiza akazembe kwa mfumu inayo isanafike pafupi, kukapempha mtendere. 33 Mofanana ndi zimenezi, ndithu palibe aliyense wa inu amene akulephera kusiya chuma chake chonse, amene angathe kukhala wophunzira wanga.+

34 Kunena zoona, mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvu yakeyo ingabwezeretsedwe bwanji?+ 35 Ndi wosayenera kuuthira munthaka kapena mʼmanyowa. Anthu amangoutaya kunja. Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

15 Tsopano okhometsa msonkho onse komanso anthu ochimwa, ankabwera kwa Yesu kuti adzamumvetsere.+ 2 Ndiye Afarisi ndi alembi ankangʼungʼudza kuti: “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa nʼkumadya nawo limodzi.” 3 Choncho iye anawauza fanizo ili: 4 “Ndi ndani pakati panu amene atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nʼkusowa, sangasiye nkhosa 99 zinazo mʼchipululu nʼkupita kukafunafuna imodzi imene yasowayo mpaka ataipeza?+ 5 Ndipo akaipeza amainyamula paphewa pake ndipo amasangalala. 6 Akafika kunyumba amasonkhanitsa anzake ndi anthu oyandikana naye nyumba nʼkuwauza kuti, ‘Sangalalani limodzi ndi ine, chifukwa ndapeza nkhosa yanga imene inasowa ija.’+ 7 Ndithu ndikukuuzani kuti, mofanana ndi zimenezi, kumwamba kudzakhala chisangalalo chochuluka chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa+ kuposa cha anthu 99 olungama amene sakufunika kulapa.

8 Kapena ndi mayi uti amene ali ndi ndalama zokwana madalakima 10,* ndiye imodzi itamutayika, sangayatse nyale ndi kusesa mʼnyumba nʼkuifufuza mosamala mpaka ataipeza? 9 Ndipo akaipeza amasonkhanitsa anzake* komanso anthu oyandikana nawo nyumba nʼkuwauza kuti, ‘Sangalalani limodzi ndi ine, chifukwa ndapeza khobidi la dalakima* limene linanditayika lija.’ 10 Choncho ndikukuuzani kuti, mofanana ndi zimenezi, angelo a Mulungu amasangalala kwambiri chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene walapa.”+

11 Kenako ananena kuti: “Munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. 12 Wamngʼono anapempha bambo ake kuti, ‘Bambo, mundipatsiretu cholowa changa pa chuma chanuchi.’ Choncho bambowo anagawa chuma chawocho kwa anawo. 13 Patangopita masiku owerengeka, mwana wamngʼono uja anasonkhanitsa zinthu zake zonse nʼkupita kudziko lina lakutali. Kumeneko anayamba kukhala moyo wotayilira ndipo anasakaza chuma chake chonse. 14 Atawononga chuma chake chonse, mʼdziko lonselo munagwa njala yaikulu ndipo iye anayamba kuvutika kwambiri. 15 Moti anapita kumakagwira ntchito kwa nzika ina yamʼdzikolo ndipo inamutumiza kubusa kwake kuti azikaweta nkhumba.+ 16 Iye anafika pomalakalaka chakudya chimene nkhumbazo zinkadya, koma palibe amene ankamupatsa kanthu.

17 Nzeru zitamubwerera ananena kuti, ‘Komatu aganyu ambiri a bambo anga ali ndi chakudya chochuluka, koma ine kuno ndikufa ndi njala! 18 Basi ndinyamuka ndizipita kwa bambo anga ndikawauze kuti: “Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu. 19 Si inenso woyenera kutchulidwa kuti mwana wanu. Munditenge ngati mmodzi wa aganyu anu.”’ 20 Choncho ananyamukadi nʼkupita kwa bambo ake. Ali chapatali ndithu, bambo akewo anamuona ndipo anagwidwa ndi chifundo. Kenako anamuthamangira nʼkumukumbatira ndipo anamukisa* mwachikondi. 21 Ndiyeno mwanayo anauza bambo akewo kuti, ‘Bambo, ndachimwira kumwamba komanso ndachimwira inu.+ Si inenso woyenera kutchulidwa kuti mwana wanu.’ 22 Koma bambowo anauza akapolo ake kuti, ‘Fulumirani, tengani mkanjo wabwino kwambiri uja mumuveke. Mumuvekenso mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi kwake. 23 Komanso mubweretse mwana wa ngʼombe wamphongo wonenepa, mumuphe ndipo tidye ndi kusangalala. 24 Chifukwa mwana wangayu anali wakufa koma tsopano wakhalanso ndi moyo,+ anatayika koma wapezeka.’ Choncho onse anayamba kusangalala.

25 Koma mwana wamkulu anali kumunda. Ndiyeno pamene ankabwerera nʼkuyandikira kunyumbako, anamva phokoso la nyimbo komanso anthu akuvina. 26 Choncho anaitana mmodzi wa antchito nʼkumufunsa chimene chinkachitika. 27 Iye anamuuza kuti, ‘Mngʼono wanu wabwera ndipo bambo anu amuphera mwana wa ngʼombe wonenepa, chifukwa amulandira ali bwinobwino.’* 28 Koma iye anakwiya kwambiri moti anakana kulowa mʼnyumbamo. Ndiyeno bambo akewo anatuluka nʼkuyamba kumuchonderera. 29 Poyankha iye anauza bambo akewo kuti, ‘Zaka zonsezi ine ndakhala ndikukugwirirani ntchito ngati kapolo ndipo sindinaphwanyepo malamulo anu nʼkamodzi komwe. Koma simunandipatseko ngakhale kamwana ka mbuzi kuti ndisangalale ndi anzanga. 30 Koma atangofika mwana wanuyu, amene anawononga* chuma chanu ndi mahule, mwamuphera mwana wa ngʼombe wamphongo wonenepa bwino.’ 31 Bambo akewo anamuuza kuti, ‘Mwana wanga, iwe wakhala nane nthawi zonse ndipo zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zako. 32 Komatu tinangoyenera kusangalala ndi kukondwera, chifukwa mʼbale wakoyu anali wakufa koma panopa ali ndi moyo, anatayika koma panopa wapezeka.’”

16 Kenako anauzanso ophunzira ake kuti: “Munthu wina wolemera anali ndi mtumiki woyangʼanira nyumba yake, amene anthu ena anamuneneza kuti akumusakazira chuma. 2 Choncho anamuitana nʼkumuuza kuti, ‘Ndamva zoipa zimene ukuchita. Pita ukalembe lipoti la mmene wakhala ukugwirira ntchito yoyangʼanira nyumba ino nʼkundipatsa, chifukwa supitiriza kuyendetsa ntchito zapanyumba pano.’ 3 Ndiyeno mtumikiyo mumtima mwake anati, ‘Nditani ine? Abwana anga akufuna kundichotsa ntchito. Sindingathe kulima chifukwa ndilibe mphamvu ndipo ndikuchita manyazi kuti ndikhale wopemphapempha. 4 Eya! Ndadziwa zoti ndichite kuti akandichotsa ntchito, anthu akandilandire bwino mʼnyumba zawo.’ 5 Ndiyeno anaitana amene anali ndi ngongole kwa bwana wake mmodzi ndi mmodzi, ndipo anafunsa woyamba kuti, ‘Uli ndi ngongole yochuluka bwanji kwa bwana wanga?’ 6 Iye anayankha kuti, ‘Mitsuko* 100 ya mafuta a maolivi.’ Iye anamuuza kuti, ‘Tenga kalata ya mgwirizano wa ngongole yako ndipo ukhale pansi nʼkulemba mitsuko 50 mwamsanga.’ 7 Kenako anafunsa wina kuti, ‘Nanga iwe, ngongole yako ndi yochuluka bwanji?’ Iye anayankha kuti, ‘Madengu 100 a tirigu.’* Iye anamuuza kuti, ‘Tenga kalata ya mgwirizano wa ngongole yako ndipo ulembepo madengu 80.’ 8 Bwana wake uja anayamikira mtumiki ameneyu, ngakhale kuti anali wosalungama, chifukwa anachita zinthu mwanzeru.* Chifukwa ana a mu nthawi ino* amachita mwanzeru akamachita zinthu ndi anthu a mʼbadwo wawo kuposa ana a kuwala.+

9 Inunso ndikukuuzani kuti: Pezani anzanu pogwiritsa ntchito chuma chosalungama,+ kuti chumacho chikatha, akakulandireni mʼmalo okhala amuyaya.+ 10 Munthu amene ndi wokhulupirika pa chinthu chachingʼono amakhalanso wokhulupirika pa chinthu chachikulu, ndipo munthu amene ndi wosakhulupirika pa chinthu chachingʼono amakhalanso wosakhulupirika pa chinthu chachikulu. 11 Choncho ngati simunasonyeze kuti ndinu wokhulupirika pa chuma chosalungama, ndi ndani amene angakupatseni ntchito yoyangʼanira chuma chenicheni? 12 Komanso ngati simunasonyeze kuti ndinu wokhulupirika pa zinthu za ena, ndi ndani angakupatseni mphoto imene anakusungirani?+ 13 Mtumiki sangakhale kapolo wa ambuye awiri, chifukwa akhoza kudana ndi mmodzi nʼkukonda winayo, kapena angakhale wokhulupirika kwa mmodzi nʼkunyoza winayo. Simungakhale akapolo a Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”+

14 Tsopano Afarisi amene ankakonda kwambiri ndalama, ankamvetsera zonsezi ndipo anayamba kumunyoza.+ 15 Choncho iye anawauza kuti: “Inu ndi amene mumanena pamaso pa anthu kuti ndinu olungama,+ koma Mulungu akudziwa mitima yanu.+ Chifukwa chimene anthu amachiona kuti ndi chapamwamba ndi chonyansa pamaso pa Mulungu.+

16 Anthu ankalalikira za Chilamulo ndi zimene aneneri analemba kudzafika mʼnthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, uthenga wabwino umene ukulengezedwa ndi wokhudza Ufumu wa Mulungu, ndipo anthu osiyanasiyana akuyesetsa mwakhama kuti akalowemo.+ 17 Ndithudi, nʼzosavuta kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kusiyana ndi kuti kachigawo kakangʼono ka chilembo cha mʼChilamulo kasakwaniritsidwe.+

18 Aliyense amene wasiya mkazi wake nʼkukwatira wina, wachita chigololo ndipo aliyense amene wakwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+

19 Panali munthu winawake wolemera amene ankakonda kuvala zovala zapepo ndi nsalu zabwino kwambiri. Iye ankasangalala komanso kudyerera tsiku ndi tsiku. 20 Komanso panali munthu wina wopemphapempha, amene anali ndi zilonda thupi lonse dzina lake Lazaro ndipo anthu ankamukhazika pageti la munthu wachumayo. 21 Iyeyo ankalakalaka kudya nyenyeswa zakugwa patebulo la wachuma uja. Agalu nawonso ankabwera kudzanyambita zilonda zakezo. 22 Patapita nthawi wopemphapempha uja anamwalira ndipo angelo anamutenga kukamuika pambali pa Abulahamu.*

Munthu wachuma ujanso anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda. 23 Ali mʼMandamo* komanso akuzunzika, anakweza maso ake nʼkuona Abulahamu ali chapatali ndipo Lazaro anali pambali pake.* 24 Choncho anaitana kuti, ‘Atate Abulahamu, ndichitireni chifundo. Mutume Lazaro kuti aviike nsonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikuzunzika mʼmoto wolilimawu.’ 25 Koma Abulahamu anati, ‘Mwanawe, kumbukira kuti unalandiriratu zabwino zako zonse pamene unali moyo, ndipo Lazaro analandira zinthu zoipa. Ndiye panopa akusangalala kuno koma iwe ukuzunzika. 26 Komanso pakati pa ife ndi inu paikidwa phompho lalikulu kwambiri, moti amene akufuna kubwera kumeneko kuchokera kuno sangathe. Komanso anthu sangaoloke kuchokera kumeneko kubwera kuno.’ 27 Ndiyeno munthu wachuma uja anati, ‘Popeza zili choncho, ndikukupemphani atate kuti mumutumize kunyumba ya bambo anga. 28 Chifukwa ndili ndi azichimwene anga 5 kumeneko, choncho apite akawapatse umboni wokwanira, kuti nawonso asadzabwere kumalo ozunzikira kuno.’ 29 Koma Abulahamu ananena kuti, ‘Kumeneko ali ndi zolemba za Mose komanso za aneneri, amvere zimenezo.’+ 30 Kenako iye anati, ‘Ayi chonde atate Abulahamu, koma ngati wina wochokera kwa akufa angapite kumeneko, iwo adzalapa ndithu.’ 31 Koma iye anamuuza kuti, ‘Ngati sakumvera zolemba za Mose+ komanso za aneneri, sangathekebe ngakhale wina atauka kwa akufa.’”

17 Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nʼzosatheka kuti pakhale popanda zopunthwitsa. Koma tsoka kwa munthu amene zopunthwitsazo zimadzera mwa iye! 2 Zingamukhalire bwino kwambiri atamumangirira chimwala cha mphero mʼkhosi mwake nʼkumuponya mʼnyanja, kusiyana ndi kuti akhumudwitse mmodzi wa tiana iti.+ 3 Samalani ndithu. Ngati mʼbale wako wachita tchimo umudzudzule+ ndipo akalapa umukhululukire.+ 4 Ngakhale atakuchimwira maulendo 7 pa tsiku, nʼkubwera kwa iwe maulendo 7 kudzanena kuti, ‘Ndalapa ine,’ umukhululukire ndithu.”+

5 Kenako atumwiwo anauza Ambuye kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.”+ 6 Ndiyeno Ambuye anawauza kuti: “Mukanakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mukanatha kuuza mtengo wa mabulosi uwu kuti, ‘Zuka pano, kadzidzale mʼnyanjamo!’ ndipo ukanakumverani.+

7 Ndi ndani wa inu amene angauze kapolo wake yemwe wangofika kumene kuchokera kumunda kapena koweta nkhosa kuti, ‘Bwera kutebulo kuno msanga udzadyeʼ? 8 Kodi sadzamuuza kuti, ‘Ndikonzere chakudya chamadzulo, uvale epuloni nʼkunditumikira mpaka nditamaliza kudya ndi kumwa, pambuyo pake iwenso udye ndi kumwaʼ? 9 Munthuyo sangamuyamikire kapoloyo chifukwa zimene wachitazo ndi ntchito yake, si choncho? 10 Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munapatsidwa pa ntchito yanu, muzinena kuti: ‘Ife ndi akapolo opanda pake. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’”+

11 Ndiyeno pamene ankapita ku Yerusalemu, anadutsa mʼmalire a Samariya ndi Galileya. 12 Pamene ankalowa mʼmudzi winawake, anakumana ndi amuna 10 akhate koma iwo anaima chapatali ndithu.+ 13 Kenako anafuula mokweza kuti: “Yesu, Mlangizi, tichitireni chifundo!” 14 Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.”+ Ndiyeno pamene ankapita anayeretsedwa.+ 15 Mmodzi wa iwo ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera akutamanda Mulungu mokweza mawu. 16 Atafika anagwada pamaso pa Yesu nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anamuthokoza. Munthu ameneyu anali Msamariya.+ 17 Yesu ananena kuti: “Kodi amene ayeretsedwa si anthu 10? Nanga anthu ena 9 aja ali kuti? 18 Kodi palibenso wina aliyense amene wabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatulapo munthu wa mtundu wina yekhayu?” 19 Ndiyeno Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+

20 Afarisi atamufunsa kuti Ufumu wa Mulungu udzabwera liti,+ iye anawayankha kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi. 21 Ndipo anthu sadzanena kuti, ‘Onani uli kuno!’ kapena, ‘Onani uli uko!’ Chifukwa Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”+

22 Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Masiku akubwera pamene mudzalakalaka kuona limodzi la masiku a Mwana wa munthu koma simudzaliona. 23 Anthu adzakuuzani kuti, ‘Onani ali uko!’ kapena ‘Onani ali kuno!’ Koma inu musadzapiteko kapena kuwatsatira.+ 24 Chifukwa mofanana ndi mphezi imene imangʼanima kuchokera mbali ina ya thambo kukafika mbali ina ya thambo, zidzakhalanso choncho ndi Mwana wa munthu+ mʼtsiku lake.+ 25 Koma choyamba akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri komanso kukanidwa ndi mʼbadwo uwu.+ 26 Komanso mofanana ndi zimene zinachitika mʼmasiku a Nowa,+ zidzachitikanso chimodzimodzi mʼmasiku a Mwana wa munthu.+ 27 Mʼmasiku amenewo anthu ankadya ndi kumwa. Amuna ankakwatira ndipo akazi ankakwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchingalawa,+ ndipo Chigumula chinabwera nʼkuwononga anthu onsewo.+ 28 Chimodzimodzinso ndi zimene zinachitika mʼmasiku a Loti.+ Anthu ankadya, kumwa, kugula, kugulitsa, kudzala komanso kumanga. 29 Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula nʼkuwononga anthu onse.+ 30 Zidzakhalanso chimodzimodzi pa tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekere.+

31 Pa tsiku limenelo, munthu amene adzakhale padenga la nyumba koma katundu wake ali mʼnyumba, asadzatsike kukatenga katundu wakeyo. Chimodzimodzinso munthu amene adzakhale ali mʼmunda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya mʼmbuyo. 32 Kumbukirani mkazi wa Loti.+ 33 Aliyense wofunitsitsa kuteteza moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake adzausunga.+ 34 Ndithu ndikukuuzani, usiku umenewo anthu awiri adzagona limodzi pabedi. Mmodzi adzatengedwa, koma wina adzasiyidwa.+ 35 Akazi awiri adzakhala akupera limodzi pamphero. Mmodzi adzatengedwa, koma winayo adzasiyidwa.” 36 *—— 37 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti Ambuye?” Iye anawauza kuti: “Kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga zidzasonkhananso komweko.”+

18 Ndiyeno Yesu anawauza fanizo pofuna kuwasonyeza kufunika koti azipemphera nthawi zonse komanso kuti asamataye mtima.+ 2 Iye anati: “Mumzinda winawake munali woweruza amene anali wosaopa Mulungu ndiponso wosasamala za munthu. 3 Mumzindawo munalinso mkazi wamasiye amene ankapitapita kwa woweruza uja kukamupempha kuti, ‘Ndiweruzireni mlandu wanga ndi munthu amene ndili naye pa mlandu, kuti pachitike chilungamo.’ 4 Kwa kanthawi ndithu woweruzayo sankafuna, koma pambuyo pake ananena mumtima mwake kuti, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kusamala za munthu aliyense, 5 ndionetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa mkazi wamasiyeyu chifukwa choti akundivutitsa. Ndichita zimenezi kuti asapitirize kubwera nʼkunditopetsa ndi zimene akupemphazo.’”+ 6 Kenako Ambuye anati: “Mwamvatu zimene woweruzayo ananena ngakhale kuti anali wosalungama! 7 Ndiye kodi Mulungu sadzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa osankhidwa ake, amene amafuulira kwa iye masana ndi usiku,+ pamene akuwalezera mtima?+ 8 Ndithu ndikukuuzani, iye adzaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa iwo mwamsanga. Kodi Mwana wa munthu akadzafika, adzapezadi chikhulupiriro ngati chimenechi* padziko lapansi?”

9 Yesu ananenanso fanizo lotsatirali kwa ena amene ankadziona ngati olungama, amenenso ankaona anthu ena ngati opanda pake. Iye anati: 10 “Anthu awiri anapita mʼkachisi kukapemphera. Mmodzi anali Mfarisi ndipo winayo anali wokhometsa msonkho. 11 Mfarisi uja anaimirira nʼkuyamba kupemphera mumtima mwake kuti, ‘Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ndine wosiyana ndi anthu ena onse. Iwo ndi achifwamba, osalungama komanso achigololo. Ndinenso wosiyana ndi wokhometsa msonkho uyu. 12 Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu ndipo ndimapereka chakhumi pa zinthu zonse zimene ndimapeza.’+ 13 Koma wokhometsa msonkho uja, ataima chapatali ndithu, sanafune ngakhale kukweza maso ake kumwamba. Iye ankangodziguguda pachifuwa nʼkumanena kuti, ‘Mulungu wanga, ndikomereni mtima* munthu wochimwa ine.’+ 14 Ndithu ndikukuuzani, munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kuti ndi wolungama kwambiri kuposa Mfarisi uja.+ Chifukwa aliyense wodzikweza adzachititsidwa manyazi, koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.”+

15 Ndiyeno anthu ankamubweretsera ana awo kuti awakhudze ndi manja ake, koma ophunzirawo ataona zimenezo anayamba kuwakalipira.+ 16 Komabe Yesu anaitana anawo. Iye anati: “Asiyeni anawo abwere kwa ine, musawaletse. Chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu ngati amenewa.+ 17 Ndithu ndikukuuzani, aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono sadzalowa nʼkomwe mu Ufumuwo.”+

18 Tsopano wolamulira wina anamufunsa kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndichite chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 19 Yesu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.+ 20 Iwe umadziwa malamulo akuti: ‘Musachite chigololo,+ musaphe munthu,*+ musabe,+ musapereke umboni wabodza+ ndiponso lakuti, muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’”+ 21 Ndiyeno iye anati: “Zonsezi ndakhala ndikuzitsatira kuyambira ndili wamngʼono.” 22 Yesu atamva zimenezo, anamuuza kuti: “Pali chinthu chimodzi chimene chikusowekabe mwa iwe: Ukagulitse zinthu zonse zimene uli nazo ndipo ndalamazo ukagawe kwa anthu osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 23 Atamva zimenezi, anamva chisoni kwambiri, chifukwa anali wolemera kwambiri.+

24 Yesu anamuyangʼana nʼkunena kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu a ndalama adzalowe mu Ufumu wa Mulungu!+ 25 Kunena zoona, nʼzosavuta kuti ngamila ilowe pakabowo ka singano kusiyana nʼkuti munthu wolemera alowe mu Ufumu wa Mulungu.”+ 26 Amene anamva zimenezi anafunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndi ndani?”+ 27 Iye anawauza kuti: “Zinthu zosatheka kwa anthu nʼzotheka kwa Mulungu.”+ 28 Koma Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu nʼkukutsatirani.”+ 29 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe amene wasiya nyumba, mkazi, azichimwene, makolo kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu+ 30 amene sadzapeza zochuluka kwambiri kuposa zimenezi mu nthawi ino, ndipo mu nthawi* imene ikubwerayo, adzapeza moyo wosatha.”+

31 Kenako anatengera pambali ophunzira 12 aja nʼkuwauza kuti: “Tamverani! Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo zonse zimene zinalembedwa ndi aneneri zokhudza Mwana wa munthu zikakwaniritsidwa.+ 32 Mwachitsanzo, akamupereka kwa anthu a mitundu ina+ ndipo akamuchitira chipongwe,+ kumunyoza komanso kumulavulira.+ 33 Akakamaliza kumukwapula akamupha,+ koma pa tsiku lachitatu iye adzauka.”+ 34 Koma iwo sanamvetse tanthauzo la chilichonse cha zimenezi chifukwa mawu amenewa anabisika kwa iwo ndipo sanamvetse zimene zinanenedwazo.

35 Tsopano pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona anakhala pansi mʼmphepete mwa msewu nʼkumapemphapempha.+ 36 Atamva gulu la anthu likudutsa chapomwepo, anafunsa chimene chinkachitika. 37 Iwo anamuuza kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!” 38 Atamva zimenezo anafuula kuti: “Yesu, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!” 39 Ndiyeno anthu amene anali patsogolo anayamba kumudzudzula nʼkumamuuza kuti akhale chete. Koma akatero mʼpamenenso iye ankafuula kwambiri kuti: “Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo!” 40 Choncho Yesu anaima nʼkulamula kuti munthuyo apite naye kwa iye. Atafika pafupi, Yesu anamufunsa kuti: 41 “Ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye anayankha kuti: “Ambuye, ndithandizeni kuti ndiyambe kuona.” 42 Choncho Yesu anamuuza kuti: “Yamba kuona, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ 43 Nthawi yomweyo anayamba kuona, ndipo anayamba kumutsatira+ akulemekeza Mulungu. Komanso anthu onse ataona zimenezi, anatamanda Mulungu.+

19 Ndiyeno Yesu analowa mu Yeriko, koma anangodutsamo. 2 Kumeneko kunali munthu wina dzina lake Zakeyu. Iyeyu anali mkulu wa okhometsa msonkho ndipo anali wolemera. 3 Zakeyu ankafunitsitsa ataona Yesu, koma sanathe kumuona chifukwa cha gulu la anthu popeza anali wamfupi. 4 Choncho anathamangira kutsogolo nʼkukwera mumtengo wamkuyu kuti athe kumuona, chifukwa ankadutsa njira imeneyo. 5 Yesu atafika pamalopo, anayangʼana mʼmwambamo nʼkumuuza kuti: “Zakeyu, fulumira tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala mʼnyumba mwako.” 6 Atamva zimenezo anatsika mofulumira ndipo anamulandira mʼnyumba mwake monga mlendo mosangalala. 7 Anthu ataona Yesu akulowa mʼnyumbamo, onse anayamba kungʼungʼudza kuti: “Wapita kukakhala mlendo mʼnyumba ya munthu wochimwa.”+ 8 Koma Zakeyu anaimirira nʼkuuza Ambuye kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense* ndibweza kuwirikiza ka 4.”+ 9 Atamva zimenezi, Yesu anamuuza kuti: “Lero chipulumutso chafika panyumba ino, chifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu. 10 Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndiponso kudzapulumutsa anthu osochera.”+

11 Pamene iwo ankamvetsera zimenezi, iye anawauza fanizo lina, chifukwa anali pafupi ndi Yerusalemu ndipo anthuwo ankaganiza kuti Ufumu wa Mulungu uonekera nthawi yomweyo.+ 12 Choncho iye ananena kuti: “Munthu wina wa mʼbanja lachifumu ankakonzekera kuti apite kudziko lakutali+ kuti akalandire ufumu nʼkubwerako. 13 Ndiyeno anaitana akapolo ake 10 nʼkuwapatsa ndalama zokwana ma mina* 10 ndipo anawauza kuti, ‘Muchite malonda ndi ndalamazi mpaka nditabwera.’+ 14 Koma anthu amʼdziko lakwawo anadana naye ndipo iye atapita anatumiza akazembe kuti akanene kuti, ‘Ife sitikufuna kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’

15 Atabwerera kwawo pambuyo polandira ufumuwo, anaitana akapolo amene anawapatsa ndalama* aja kuti abwere kwa iye, kuti awerengerane nʼkuona mmene apindulira pa malonda awo.+ 16 Woyamba anabwera ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija yapindula ndalama zina zokwana ma mina 10.’+ 17 Iye anamuuza kuti, ‘Wachita bwino, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kuti ndiwe wokhulupirika pa chinthu chachingʼono, ndikupatsa ulamuliro woyangʼanira mizinda 10.’+ 18 Kenako kunabwera wachiwiri ndipo anati, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija yapindula ndalama zina zokwana ma mina 5.’+ 19 Iye anauzanso ameneyu kuti, ‘Nawenso ukhala woyangʼanira mizinda 5.’ 20 Koma kunabwera wina ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija ndi iyi. Ndinaimanga pansalu nʼkuibisa. 21 Ndinachita zimenezi chifukwa ndimakuopani. Inutu ndinu munthu wouma mtima. Mumatenga zimene simunasungitse ndipo mumakolola zimene simunafese.’+ 22 Iye anamuuza kuti, ‘Ndikuweruza potengera zimene wanena, kapolo woipa iwe. Ukuti umadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wotenga zimene sindinasungitse ndi kukolola zimene sindinafese.+ 23 Ndiye nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yangayo* kubanki? Ukanatero, ine pobwera ndikanaitenga limodzi ndi chiwongoladzanja chake.’

24 Atatero anauza anthu amene anaima chapafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya minayo nʼkuipereka kwa amene ali ndi ndalama za mina 10.’+ 25 Koma iwo anamuuza kuti, ‘Mbuyathu, iyetu ali ndi ndalama za mina 10!’— 26 ‘Ndithu ndikukuuzani, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 27 Komanso adani angawa, amene sanafune kuti ine ndikhale mfumu yawo, bwerani nawo kuno muwaphe ine ndikuona.’”

28 Atamaliza kunena zimenezi, anapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 29 Ndiyeno atayandikira ku Betefage ndi Betaniya paphiri lotchedwa phiri la Maolivi,+ anatumiza ophunzira ake awiri.+ 30 Iye anawauza kuti: “Pitani mʼmudzi umene mukuuonawo, ndipo mukalowa mmenemo mukapeza bulu wamngʼono wamphongo atamumangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukamumasule nʼkubwera naye kuno. 31 Koma aliyense akakakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumasula buluyu?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna.’” 32 Choncho anthu amene anatumidwawo ananyamuka ndipo anakamupezadi mmene iye anawauzira.+ 33 Koma pamene ankamasula buluyo, eniake anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukumasula buluyu?” 34 Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.” 35 Pamenepo iwo anamutenga nʼkupita naye kwa Yesu. Kenako iwo anaponya malaya awo akunja pabuluyo ndipo Yesu anakwerapo.+

36 Pamene ankayenda, anthu ankayala malaya awo akunja mumsewu.+ 37 Atangofika pafupi ndi msewu wochokera mʼphiri la Maolivi, gulu lonse la ophunzirawo linayamba kusangalala ndi kutamanda Mulungu mokweza mawu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene anaona. 38 Iwo ankanena kuti: “Wodalitsidwa ndi amene akubwera monga Mfumu mʼdzina la Yehova!* Mtendere kumwamba ndi ulemerero kumwambamwambako!”+ 39 Koma Afarisi ena mʼgululo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anuwa.”+ 40 Poyankha iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, ngati awa atakhala chete, miyala ingathe kufuula.”

41 Tsopano Yesu atayandikira mzinda wa Yerusalemu, anaona mzindawo nʼkuyamba kuulirira.+ 42 Iye anati: “Ngati iwe lero ukanazindikira zinthu zamtendere—* koma tsopano zabisika kuti usathe kuziona.+ 43 Chifukwa masiku adzakufikira pamene adani ako adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulira. Adaniwo adzakutsekereza nʼkukuukira* kuchokera kumbali zonse.+ 44 Iwo adzakugwetsa pansi nʼkukuwononga limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe.+ Ndipo sadzasiya mwala pamwamba pa mwala unzake mwa iwe,+ chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.”

45 Ndiyeno analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuthamangitsa anthu amene ankagulitsamo zinthu+ 46 nʼkuwauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+

47 Ndipo tsiku ndi tsiku iye anapitiriza kuphunzitsa mʼkachisimo. Koma ansembe aakulu, alembi ndi akuluakulu a anthu ankafunitsitsa kumupha.+ 48 Koma sanathe kuchita zimenezi chifukwa anthu ambiri ankangomuunjirira kuti amumvetsere ndipo sankasiyana naye.+

20 Tsiku lina akuphunzitsa anthu mʼkachisi komanso kulengeza uthenga wabwino, kunabwera ansembe aakulu, alembi limodzi ndi akulu 2 nʼkudzamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 3 Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi ndipo mundiyankhe: 4 Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kumwamba kapena kwa anthu?” 5 Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 6 Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala, chifukwa iwo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane anali mneneri.”+ 7 Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera. 8 Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”

9 Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndipo anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+ 10 Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo. Koma alimiwo anamumenya nʼkumubweza chimanjamanja.+ 11 Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya nʼkumuchitira zachipongwe,* ndipo anamubweza chimanjamanja. 12 Anatumizanso wachitatu. Ameneyunso anamuvulaza nʼkumuponya kunja. 13 Zitatero mwiniwake wa munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mosakayikira mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 14 Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa, uyu ndi amene adzalandire cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’ 15 Choncho anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo nʼkumupha.+ Ndiye kodi mwiniwake wa munda wa mpesawo adzachita chiyani kwa alimiwo? 16 Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.”

Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!” 17 Koma iye anawayangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Paja malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’*+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? 18 Aliyense amene adzagwere pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, adzanyenyeka.”

19 Alembi ndi ansembe aakulu aja atazindikira kuti mufanizolo akunena za iwowo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma ankaopa anthu.+ 20 Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, nʼcholinga choti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule,+ kuti akamupereke kuboma ndi kwa bwanamkubwa. 21 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti zimene mumanena ndi kuphunzitsa ndi zolondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. 22 Kodi nʼzololeka* kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 23 Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti: 24 “Ndionetseni khobidi la dinari.* Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 25 Iye anawauza kuti: “Choncho perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 26 Iwo analephera kumutapa mʼkamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, koma anadabwa ndi yankho lake moti anangokhala chete kusowa chonena.

27 Koma Asaduki ena, amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 28 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma sanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 29 Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira asanabereke mwana. 30 Wachiwirinso chimodzimodzi. 31 Kenako wachitatu anamukwatira. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja, onse anamwalira osasiya ana. 32 Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 33 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.”

34 Yesu anawayankha kuti: “Ana a mʼnthawi* ino amakwatira ndi kukwatiwa. 35 Koma amene aonedwa kuti ndi oyenerera kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo nʼkudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.+ 36 Komanso iwo sadzafanso, chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa. 37 Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza munkhani ya chitsamba cha minga, pamene ananena kuti Yehova* ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+ 38 Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye* onsewa ndi amoyo.”+ 39 Poyankha, ena mwa alembiwo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino.” 40 Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi.

41 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 42 Chifukwa Davideyo ananena mʼbuku la Masalimo kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 44 Choncho Davide anamutchula kuti Ambuye. Ndiye zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?”

45 Kenako anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzira akewo kuti: 46 “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika. Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+ 47 Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*

21 Tsopano atakweza maso anaona anthu olemera akuponya zopereka zawo moponyera zopereka.*+ 2 Kenako anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiwiri tatingʼono, tochepa mphamvu kwambiri.*+ 3 Ndipo iye anati: “Ndithu ndikukuuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu, waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama zawo.+ 4 Chifukwa onsewa aponya zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo, koma mayiyu, mu umphawi wake, waponya zonse zimene zikanamuthandiza pa moyo wake.”+

5 Nthawi ina, pamene anthu ena ankalankhula za kachisi, mmene anamukongoletsera ndi miyala yabwino kwambiri komanso mphatso zoperekedwa kwa Mulungu,+ 6 iye ananena kuti: “Kunena za zinthu zimene mukuzionazi, masiku adzafika pamene sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+ 7 Ndiyeno anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti kwenikweni, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti nthawi yoti zinthu zimenezi zichitike yatsala pangʼono chidzakhala chiyani?”+ 8 Iye anayankha kuti: “Samalani kuti asadzakusocheretseni,+ chifukwa ambiri adzabwera mʼdzina langa nʼkumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ komanso adzanena kuti, ‘Nthawi ija yayandikira.’ Musadzawatsatire.+ 9 Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi zipolowe,* musadzachite mantha. Chifukwa zimenezi zikuyenera kuchitika choyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”+

10 Kenako anawauza kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina+ ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ 11 Kudzachitika zivomerezi zamphamvu ndipo kudzakhala miliri+ ndi njala mʼmalo osiyanasiyana. Kudzaoneka zinthu zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.

12 Koma zinthu zonsezi zisanachitike, anthu adzakugwirani nʼkukuzunzani+ ndipo adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.+ 13 Zimenezi zidzakupatsani mpata woti muchitire umboni. 14 Choncho tsimikizirani mʼmitima yanu kuti musachite kukonzekera zoti mukayankhe podziteteza,+ 15 chifukwa ine ndidzakuuzani mawu oti munene komanso ndidzakupatsani nzeru zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.+ 16 Komanso makolo anu enieniwo, azichimwene anu, achibale anu komanso anzanu, adzakuperekani ndipo adzapha ena a inu.+ 17 Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ 18 Komatu ngakhale tsitsi limodzi lokha lamʼmutu mwanu silidzawonongeka.+ 19 Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.+

20 Koma mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu,+ mudzadziwe kuti mzindawu watsala pangʼono kuwonongedwa.+ 21 Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri,+ ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali mʼmadera akumidzi asadzalowe mumzindawo, 22 chifukwa amenewa ndi masiku opereka chiweruzo* kuti zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe. 23 Tsoka kwa akazi oyembekezera komanso oyamwitsa ana mʼmasiku amenewo!+ Chifukwa mʼdzikoli mudzakhala mavuto aakulu komanso mkwiyo pa anthu awa. 24 Anthu adzaphedwa ndi lupanga ndiponso kutengedwa ukapolo kupita nawo ku mitundu ina yonse.+ Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu mpaka nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira.+

25 Komanso padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi.+ Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika chifukwa chothedwa nzeru poona kuti nyanja ikuchita mkokomo komanso kuwinduka. 26 Anthu adzakomoka chifukwa cha mantha komanso chifukwa choyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, popeza mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 27 Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera mumtambo ndi mphamvu ndiponso ulemerero waukulu.+ 28 Koma zinthu zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.”

29 Atanena zimenezi, anawauza fanizo kuti: “Onetsetsani mtengo wa mkuyu ndi mitengo ina yonse.+ 30 Mukaona mitengo ikuphukira, mumadziwa ndithu kuti tsopano chilimwe chili pafupi. 31 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira. 32 Ndithu ndikukuuzani kuti mʼbadwo uwu sudzatha wonse kufa, mpaka zinthu zonse zitachitika.+ 33 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga adzakhalapo mpaka kalekale.+

34 Koma samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri+ komanso nkhawa za moyo,+ kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa 35 ngati msampha.+ Chifukwa lidzafikira onse okhala padziko lonse lapansi. 36 Choncho khalani maso+ ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse,+ kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyenera kuchitika, komanso kuti mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.”+

37 Masana Yesu ankaphunzitsa mʼkachisi, koma usiku ankapita kukagona kuphiri la Maolivi. 38 Ndipo anthu onse ankalawirira mʼmawa kwambiri kupita kwa iye kukachisi kuti akamumvetsere.

22 Tsopano Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa, chimene chinkadziwikanso kuti Pasika,+ chinali chitayandikira.+ 2 Komanso ansembe aakulu ndi alembi ankafunafuna njira yabwino yoti aphere Yesu,+ chifukwa ankaopa anthu.+ 3 Koma Satana analowa mwa Yudasi, amene ankadziwika kuti Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja.+ 4 Iye anapita kukakambirana ndi ansembe aakulu ndi oyangʼanira kachisi za mmene angamuperekere kwa iwo.+ 5 Iwo anasangalala ndipo anagwirizana kuti amupatse ndalama zasiliva.+ 6 Choncho iye anavomereza, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke kwa iwo popanda gulu la anthu pafupi.

7 Tsopano tsiku la Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa linafika, tsiku limene nsembe ya Pasika inkayenera kuperekedwa.+ 8 Yesu anatumiza Petulo ndi Yohane nʼkuwauza kuti: “Pitani mukatikonzere Pasika kuti tidye.”+ 9 Iwo anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti?” 10 Iye anawayankha kuti: “Mukalowa mumzinda, mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire mʼnyumba imene akalowe.+ 11 Ndipo mukauze mwininyumba imeneyo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 12 Ndiyeno munthu ameneyo akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukakonzere mmenemo.” 13 Choncho ananyamuka ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.

14 Nthawi itakwana, anakhala patebulo la chakudya limodzi ndi atumwi ake.+ 15 Ndiyeno anawauza kuti: “Ndakhala ndikulakalaka kwambiri kuti ndidye Pasika uyu limodzi ndi inu ndisanayambe kuzunzika. 16 Chifukwa ndikukuuzani kuti sindidzadyanso Pasika mpaka zonse zimene Pasikayu akuimira zitakwaniritsidwa mu Ufumu wa Mulungu.” 17 Ndiyeno analandira kapu nʼkuyamika, kenako anati: “Landirani kapu iyi, ndipo nonse mumwe mopatsirana. 18 Ndithu ndikukuuzani, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka Ufumu wa Mulungu utabwera.”

19 Kenako anatenga mkate.+ Atayamika, anaunyemanyema nʼkuwapatsa ndipo anati: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu.+ Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 20 Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu atadya chakudya chamadzulocho. Iye anati: “Kapu iyi ikuimira pangano latsopano+ limene linakhazikitsidwa pogwiritsa ntchito magazi anga,+ amene adzakhetsedwe chifukwa cha inu.+

21 Koma taonani! Wondipereka ndili naye limodzi patebulo pompano.+ 22 Chifukwa Mwana wa munthu achoka mogwirizana ndi zimene zinanenedweratu.+ Koma tsoka kwa munthu amene akumupereka!”+ 23 Choncho anayamba kukambirana pakati pawo za amene anakonza chiwembu chimenecho.+

24 Kenako anayamba kukangana kwambiri za amene anali wamkulu kwambiri.+ 25 Koma Yesu anawauza kuti: “Mafumu a anthu a mitundu ina amachita ulamuliro pa anthu awo, ndipo amene ali ndi mphamvu pa anthuwo amadziwika kuti ndi anthu amene amachitira ena zabwino.+ 26 Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamngʼono+ kwambiri pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleri akhale ngati wotumikira. 27 Kodi wamkulu ndi ndani, amene akudya patebulo kapena amene akutumikira? Kodi si amene akudya patebulo? Koma ine ndili pakati panu ngati wotumikira.+

28 Komabe, inu ndi amene mwakhalabe ndi ine+ mʼmayesero anga.+ 29 Choncho ndikuchita nanu pangano, mofanana ndi mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine,+ 30 kuti mukadye ndi kumwa patebulo langa mu Ufumu wanga,+ komanso kuti mukakhale mʼmipando yachifumu+ kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.+

31 Simoni, Simoni! Ndithu Satana akufuna kuti nonsenu akupeteni ngati tirigu.+ 32 Koma ine ndakupempherera kuti chikhulupiriro chako chisathe.+ Choncho iwenso ukabwerera, ukalimbikitse abale ako.”+ 33 Kenako iye anauza Yesu kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu limodzi kundende kapena kufa nanu limodzi.”+ 34 Koma iye anati: “Ndikukuuza iwe Petulo, tambala asanalire lero, undikana katatu kuti sukundidziwa.”+

35 Yesu anauzanso ophunzirawo kuti: “Pamene ndinakutumizani opanda chikwama cha ndalama, thumba la chakudya kapena nsapato,+ kodi munasowa kanthu?” Iwo anati: “Ayi!” 36 Kenako anawauza kuti: “Koma tsopano amene ali ndi chikwama cha ndalama achitenge, chimodzimodzinso thumba la chakudya. Ndipo amene alibe lupanga agulitse malaya ake akunja nʼkugula lupanga. 37 Chifukwa ndikukuuzani kuti zimene zinalembedwa ziyenera kukwaniritsidwa mwa ine, zakuti, ‘Iye anaikidwa mʼgulu la anthu osamvera malamulo.’+ Zili choncho chifukwa zimene zinanenedwa zokhudza ine zikukwaniritsidwa.”+ 38 Ndiyeno iwo anati: “Ambuye, onani! Tili ndi malupanga awiri awa.” Iye anawauza kuti: “Amenewa ndi okwanira.”

39 Atachoka kumeneko anapita kuphiri la Maolivi ngati mmene ankachitira nthawi zonse ndipo ophunzira ake nawonso anamutsatira.+ 40 Atafika pamalowo anauza ophunzirawo kuti: “Pitirizani kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.”+ 41 Iye anachoka pamene panali ophunzirawo nʼkuyenda kamtunda, kutalika kwake ngati pamene pangagwere mwala munthu atauponya. Kumeneko anagwada nʼkuyamba kupemphera 42 kuti: “Atate, ngati mukufuna, ndichotsereni kapu iyi. Komatu zimene mukufuna zichitike, osati zofuna zanga.”+ 43 Atatero mngelo wochokera kumwamba anaonekera kwa iye nʼkumulimbikitsa.+ 44 Koma anazunzika koopsa mumtima mwake, moti anapitiriza kupemphera ndi mtima wonse+ ndipo thukuta lake linkaoneka ngati madontho amagazi amene akugwera pansi. 45 Atanyamuka pamene amapempherapo nʼkupita kwa ophunzira aja, anawapeza atagona chifukwa anali atafooka ndi chisoni.+ 46 Iye anawauza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukugona? Dzukani ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.”+

47 Mawu adakali mʼkamwa, panafika gulu la anthu limodzi ndi Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, akuwatsogolera. Ndiyeno Yudasi anapita pamene panali Yesu kuti akamukise.*+ 48 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Yudasi, kodi ukupereka Mwana wa munthu ndi kisi?” 49 Anthu amene anali naye pafupi ataona zimene zinkachitika anati: “Ambuye, kodi tiwateme ndi lupanga?” 50 Mmodzi wa iwo anatemadi kapolo wa mkulu wa ansembe nʼkuduliratu khutu lake lakumanja.+ 51 Koma Yesu anati: “Musachite zimenezi.” Ndipo anagwira khutu lija nʼkumuchiritsa. 52 Ndiyeno Yesu anafunsa ansembe aakulu, oyangʼanira kachisi ndi akulu amene anabwera kudzamugwira kuti: “Bwanji mwabwera ndi malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba?+ 53 Tsiku ndi tsiku ndinali nanu mʼkachisi+ koma simunandigwire.+ Koma ino tsopano ndi nthawi yanu komanso nthawi ya ulamuliro wamdima.”+

54 Zitatero anamugwira nʼkumutenga+ ndipo anakamulowetsa mʼnyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petulo ankawatsatira chapatali.+ 55 Atasonkha moto mkati mwa bwalo nʼkukhala pansi onse pamodzi, Petulo nayenso anakhala nawo pamenepo.+ 56 Koma mtsikana wina wantchito atamuona atakhala pafupi ndi moto wowala, anamuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Bambo awanso anali naye limodzi.” 57 Koma iye anakana kuti: “Mtsikana iwe, ameneyu ine sindikumudziwa.” 58 Patapita kanthawi pangʼono, munthu wina anamuona nʼkunena kuti: “Iwenso uli mʼgulu la ophunzira ake.” Koma Petulo anati: “Munthu iwe, ayi si ine.”+ 59 Patapita pafupifupi ola limodzi, munthu winanso anayamba kunena motsimikiza kuti: “Ndithu sindikukayika, munthu uyunso anali naye limodzi, komanso iyeyu ndi Mgalileya!” 60 Koma Petulo anati: “Munthu iwe, ine sindikudziwa zimene ukunena.” Nthawi yomweyo mawu ali mʼkamwa, tambala analira. 61 Zitatero Ambuye anacheuka nʼkuyangʼana Petulo, ndipo Petulo anakumbukira mawu amene Ambuye anamuuza aja akuti: “Tambala asanalire lero, undikana katatu.”+ 62 Kenako Petulo anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.

63 Tsopano amuna amene anagwira Yesu aja anayamba kumuchitira zachipongwe+ komanso kumumenya.+ 64 Iwo ankamuphimba kumaso nʼkumamufunsa kuti: “Losera. Wakumenya ndi ndani?” 65 Ndipo anapitiriza kunena zinthu zambiri zomunyoza.

66 Kenako kutacha, bungwe la akulu, kuphatikizapo ansembe aakulu komanso alembi, anasonkhana pamodzi,+ ndipo anamutengera kuholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda.* Kumeneko iwo anati: 67 “Tiuze ngati ndiwe Khristu.”+ Koma iye anawayankha kuti: “Ngakhale ndikuuzeni, simukhulupirira. 68 Komanso nditakufunsani, simungathe nʼkomwe kuyankha. 69 Koma kuyambira panopa mpaka mʼtsogolo, Mwana wa munthu+ adzakhala kudzanja lamanja lamphamvu la Mulungu.”+ 70 Atanena zimenezi onse anati: “Kodi ndiye kuti ndiwe Mwana wa Mulungu?” Iye anawayankha kuti: “Inunso mukunena nokha kuti ndine amene.” 71 Iwo anati: “Tifuniranjinso umboni wina? Apatu tadzimvera tokha kuchokera pakamwa pake.”+

23 Choncho gulu lonse linanyamuka pamodzi nʼkupita ndi Yesu kwa Pilato.+ 2 Ndiyeno anayamba kumuneneza kuti:+ “Ife tapeza munthu uyu akupandutsa mtundu wathu, akuletsa anthu kuti asamakhome msonkho kwa Kaisara+ komanso akunena kuti ndi Khristu mfumu.”+ 3 Tsopano Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Iye anayankha kuti: “Zili choncho, monga mmene mwanenera.”+ 4 Kenako Pilato anauza ansembe aakulu ndi gulu la anthulo kuti: “Sindikupeza mlandu uliwonse mwa munthu uyu.”+ 5 Koma iwo anaumirira nʼkunena kuti: “Iyeyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, kuyambira ku Galileya mpaka kudzafika kuno.” 6 Atamva zimenezo, Pilato anafunsa ngati munthuyu ndi Mgalileya. 7 Ndiyeno atadziwa kuti akuchokera mʼchigawo chimene amalamulira Herode,+ anamutumiza kwa Herode, amenenso mʼmasiku amenewo anali mu Yerusalemu.

8 Herode ataona Yesu anasangalala kwambiri. Kwa nthawi yaitali ndithu ankafunitsitsa kuti aone Yesu chifukwa anali atamva zambiri zokhudza iye.+ Komanso ankayembekezera kuti aone chizindikiro chimene iye angachite. 9 Choncho anayamba kumufunsa zinthu zambiri, koma iye sanamuyankhe.+ 10 Komabe ansembe aakulu ndi alembi ankangonyamukanyamuka nʼkumamuneneza mwaukali. 11 Ndiyeno Herode limodzi ndi asilikali ake anamuchitira zachipongwe.+ Anamunyoza+ pomuveka chovala chokongola kwambiri, kenako anamutumizanso kwa Pilato. 12 Tsiku lomwelo Herode anakhala mnzake wa Pilato, koma mʼmbuyo monsemo zimenezi zisanachitike ankadana kwambiri.

13 Ndiyeno Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulira ndi anthu ena 14 nʼkuwauza kuti: “Inu mwabweretsa munthu uyu kwa ine ndi mlandu wakuti akulimbikitsa anthu kuukira. Koma mwaona nokha! Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinamupeze ndi chifukwa chomuimbira milandu imene mukumunenezayi.+ 15 Ndipotu ngakhale Herode sanamupeze ndi mlandu, nʼchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ndithudi ameneyu sanachite chilichonse choyenera chilango cha imfa. 16 Choncho ndingomukwapula+ nʼkumumasula.” 17 *—— 18 Koma gulu lonse linafuula kuti: “Ameneyu muthane naye basi, koma ife mutimasulire Baraba!”+ 19 (Munthu ameneyu anaponyedwa mʼndende chifukwa cha kuukira boma kumene kunachitika mumzindawo komanso chifukwa chopha munthu.) 20 Pilato analankhula nawonso kachiwiri chifukwa ankafunitsitsa kuti amasule Yesu.+ 21 Ndiyeno anthuwo anayamba kufuula kuti: “Apachikidwe ameneyo! Apachikidwe ameneyo!”+ 22 Anawafunsa kachitatu kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani? Ine sindinamupeze ndi chifukwa chilichonse chomuphera. Choncho ndimukwapula nʼkumumasula.” 23 Atamva zimenezi anamuumiriza mokweza mawu kuti Yesu aphedwe basi. Anthuwo ankafuula mwamphamvu moti Pilato anangololera.+ 24 Choncho Pilato anapereka chiweruzo chogwirizana ndi zimene anthuwo ankafuna. 25 Iye anamasula munthu amene anthuwo ankafuna, amene anaikidwa mʼndende pa mlandu woukira boma komanso kupha munthu. Koma Yesu anamupereka mʼmanja mwawo kuti achite zimene ankafuna.

26 Pamene ankapita naye, iwo anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera kudera lakumidzi. Iwo anamusenzetsa mtengo wozunzikirapo* kuti aunyamule nʼkumatsatira pambuyo pa Yesu.+ 27 Gulu lalikulu la anthu linkamutsatira kuphatikizapo azimayi ambiri amene ankadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni komanso kumulirira. 28 Yesu anacheukira azimayiwo nʼkunena kuti: “Inu ana aakazi a Yerusalemu, siyani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu.+ 29 Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Osangalala ndi akazi amene alibe ana, akazi amene sanaberekepo komanso akazi amene sanayamwitsepo!’+ 30 Mʼmasiku amenewo iwo adzayamba kuuza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza mapiri angʼonoangʼono kuti, ‘Tikwirireni!’+ 31 Ngati akuchita zinthu zimenezi mtengo uli wauwisi, kuli bwanji mtengowo ukadzauma?”

32 Anthuwo anatenganso amuna ena awiri, amene anali zigawenga, kuti akawaphe limodzi ndi Yesu.+ 33 Ndiyeno atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamukhomerera pamtengo limodzi ndi zigawenga zija. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+ 34 Koma Yesu ananena kuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.” Iwo anagawana zovala zake pochita maere.+ 35 Anthu anangoima nʼkumaonerera zimene zinkachitikazo. Koma olamulira ankamunyogodola nʼkumanena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, musiyeni adzipulumutse yekha, ngati alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwa.”+ 36 Ngakhale asilikali nawonso ankamuchitira zachipongwe, ankabwera kudzamupatsa vinyo wowawasa+ 37 nʼkumanena kuti: “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” 38 Pamwamba pake analembapo mawu akuti: “Uyu ndi Mfumu ya Ayuda.”+

39 Ndiyeno mmodzi wa zigawenga zimene zinapachikidwa naye limodzi zija, anayamba kumulankhulira zachipongwe+ kuti: “Kodi si iwe Khristu? Dzipulumutse wekha, limodzi ndi ife.” 40 Poyankha mnzake uja anamudzudzula kuti: “Kodi iwe sukuopa Mulungu poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu? 41 Ifetu mpake kulangidwa chonchi, chifukwa tikulandira zimene timayenera kulandira mogwirizana ndi zimene tinachita. Koma munthu uyu sanalakwe chilichonse.” 42 Kenako ananena kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.”+ 43 Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine mʼParadaiso.”+

44 Apa nʼkuti nthawi ili cha mʼma 12 koloko masana,* koma kunagwa mdima mʼdziko lonselo mpaka 3 koloko masana,*+ 45 chifukwa dzuwa linachita mdima. Pa nthawi imeneyi nsalu yotchinga yamʼnyumba yopatulika+ inangʼambika pakati kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 46 Kenako Yesu anafuula mokweza mawu kuti: “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu!”+ Atanena zimenezi anatsirizika.+ 47 Ataona zimene zinachitikazo, mtsogoleri wa asilikali anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Ndithudi munthu uyu anali wolungama.”+ 48 Anthu onse amene anasonkhana kumeneko kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonse zimene zinachitika, anabwerera kwawo akudziguguda pachifuwa. 49 Anthu onse amene ankamudziwa anaimirira chapatali ndithu. Komanso azimayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya anali pomwepo ndipo anaona zinthu zimenezi.+

50 Ndiyeno panali mwamuna wina dzina lake Yosefe, amene anali wa mʼKhoti Lalikulu la Ayuda. Munthu ameneyu anali wabwino komanso wolungama.+ 51 (Iye sanavomereze chiwembu chawo komanso zimene anachita.) Yosefe anali wochokera ku Arimateya, mzinda wa Ayudeya ndipo ankayembekezera Ufumu wa Mulungu. 52 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 53 Choncho anautsitsa+ nʼkuukulunga munsalu yabwino kwambiri ndipo anakauika mʼmanda*+ amene anawagoba muthanthwe, mmene anali asanaikemo munthu chiyambire. 54 Tsopano linali Tsiku Lokonzekera,+ ndipo Sabata+ linali litatsala pangʼono kuyamba. 55 Koma azimayi amene anabwera limodzi ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anamutsatira ndipo anaona mandawo* komanso mmene mtembo wakewo anauikira.+ 56 Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira. Komabe pa tsiku la Sabata anapuma+ malinga ndi chilamulo.

24 Koma pa tsiku loyamba la mlungu, azimayi aja analawirira mʼmawa kwambiri kupita kumandako,* atatenga zonunkhira zimene anakonza zija.+ 2 Koma anapeza kuti mwala wagubuduzidwa pamandawo,*+ 3 ndipo atalowa mʼmandamo, mtembo wa Ambuye Yesu sanaupezemo.+ 4 Atathedwa nzeru ndi zimenezi, anangoona amuna awiri ovala zovala zonyezimira ataima pambali pawo. 5 Azimayiwo anagwidwa ndi mantha ndipo anaweramira pansi. Ndiyeno amunawo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukufunafuna munthu wamoyo pakati pa anthu akufa?+ 6 Iye kuno kulibe, waukitsidwa. Kumbukirani zimene anakuuzani pamene anali ku Galileya. 7 Paja ananena kuti Mwana wa munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa ndi kuphedwa pomupachika pamtengo nʼkuuka tsiku lachitatu.”+ 8 Choncho anakumbukira mawu akewo+ 9 ndipo anachoka kumandako* nʼkubwerera kukanena zonsezi kwa ophunzira 11 aja ndi kwa ena onse.+ 10 Azimayiwa anali Mariya wa ku Magadala, Jowana ndi Mariya amayi ake a Yakobo. Komanso azimayi ena onse amene anali nawo limodzi ankauza atumwi zinthu zimenezi. 11 Koma kwa iwo, zimene ankawauzazo zinkaoneka ngati zopanda pake ndipo sanawakhulupirire azimayiwo.

12 Koma Petulo ananyamuka nʼkuthamangira kumandako,* ndipo atasuzumira mkati, anangoona nsalu zokha. Choncho anachoka ali wodabwa kwambiri ndi zimene zinachitikazo.

13 Koma tsiku lomweli, awiri a iwo anali pa ulendo wopita kumudzi wina wotchedwa Emau, pamtunda wa pafupifupi makilomita 11* kuchokera ku Yerusalemu. 14 Iwo ankakambirana zokhudza zinthu zonse zimene zinachitikazo.

15 Ndiye ali mkati mokambirana zinthu zimenezi, Yesu anafika nʼkuyamba kuyenda nawo limodzi. 16 Koma sanathe kumuzindikira.+ 17 Iye anawafunsa kuti: “Kodi ndi nkhani zotani zimene mukukambirana mukuyenda pamsewu pano?” Iwo anangoima chilili akuoneka achisoni. 18 Poyankha, mmodzi wa iwo dzina lake Keleopa, anamufunsa kuti: “Kodi iwe ukukhala wekhawekha mʼYerusalemu monga mlendo,* moti sukudziwa zinthu zimene zachitika mmenemo mʼmasiku amenewa?” 19 Iye anawafunsa kuti: “Zinthu zake ziti?” Iwo anamuuza kuti: “Zinthu zokhudza Yesu Mnazareti,+ amene anali mneneri wamphamvu mʼzochita komanso mʼmawu pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.+ 20 Komanso zokhudza mmene ansembe athu aakulu ndi olamulira anamuperekera kwa anthu amene anamuweruza kuti aphedwe ndipo anamukhomerera pamtengo.+ 21 Koma ife tinkayembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.+ Kuwonjezera pamenepo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni zinthu zimenezi. 22 Komanso azimayi ena mʼgulu lathuli atidabwitsa kwambiri. Iwo analawirira mʼmawa kwambiri kumandako,*+ 23 koma ataona kuti mtembo wake sanaupeze, anabwerako nʼkumanena kuti aonanso masomphenya a angelo, amene awauza kuti iye ali ndi moyo. 24 Kenako enanso mʼgulu lathu lomweli anapita kumandako,*+ ndipo anapezadi kuti mʼmandamo mulibe aliyense, mogwirizana ndi zimene azimayiwo ananena, koma iyeyo sanamuone.”

25 Ndiyeno iye anawauza kuti: “Opanda nzeru inu komanso okayikakayika pa zinthu zonse zimene aneneri ananena! 26 Kodi sikunali koyenera kuti Khristu amve zowawa zonsezi+ nʼkulowa mu ulemerero wake?”+ 27 Atatero anayamba kuwatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo mʼMalemba onse, kuyambira ndi Zolemba za Mose komanso zonse zimene aneneri analemba.+

28 Kenako anayandikira mudzi umene ankapita, ndipo iye anachita ngati akupitirira ndi ulendo wake. 29 Koma iwo anamuumiriza kuti: “Tiyeni tikhalebe limodzi, chifukwa kunja kwayamba kuda ndipo tsiku latsala pangʼono kutha.” Atanena zimenezo analowa mʼnyumba ndipo anakhala nawo. 30 Pamene ankadya nawo chakudya,* anatenga mkate nʼkuudalitsa, kenako anaunyemanyema nʼkuyamba kuwagawira.+ 31 Ataona zimenezi, maso awo anatsegukiratu ndipo anamuzindikira, koma iye anazimiririka.+ 32 Iwo anayamba kuuzana kuti: “Kodi si paja tinakhudzidwa kwambiri mumtima pamene amalankhula nafe mumsewu muja ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?” 33 Pa ola lomwelo ananyamuka nʼkubwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anakapeza ophunzira 11 aja komanso anthu ena amene anasonkhana nawo pamodzi. 34 Iwo anawauza kuti: “Nʼzoonadi, Ambuye auka kwa akufa ndipo aonekera kwa Simoni!”+ 35 Nawonso anafotokoza zimene zinachitika pamsewu komanso mmene iwo anamuzindikirira pamene ananyemanyema mkate.+

36 Akulankhula choncho, Yesu anaimirira pakati pawo nʼkuwauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 37 Koma popeza iwo anadzidzimuka kwambiri ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzimu. 38 Choncho iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika maganizo komanso kukayikakayika mʼmitima yanu? 39 Onani manja ndi mapazi angawa, mutsimikize kuti ndine ndithu. Ndikhudzeni muone, chifukwa mzimu ulibe mnofu ndi mafupa ngati anga amene mukuwaonawa.” 40 Pamene ankanena zimenezi, anawaonetsa manja ndi mapazi ake. 41 Koma popeza iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, iye anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” 42 Choncho anamupatsa chidutswa cha nsomba yowotcha, 43 ndipo iye analandira nʼkudya onse akuona.

44 Ndiyeno anawauza kuti: “Pamene ndinali nanu limodzi ndinakuuzani mawu akuti,+ zonse zokhudza ine zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose, zimene aneneri analemba komanso zimene zinalembedwa mʼMasalimo ziyenera kukwaniritsidwa.”+ 45 Zitatero anatseguliratu maganizo awo kuti amvetse tanthauzo la Malemba+ 46 ndipo anawauza kuti, “Malemba amanena kuti: Khristu adzazunzika ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa,+ 47 ndipo mʼdzina lake, uthenga woti anthu alape machimo awo+ kuti akhululukidwe udzalalikidwa kwa anthu a mitundu yonse,+ kuyambira ku Yerusalemu.+ 48 Inu mudzakhala mboni za zinthu zimenezi.+ 49 Ndipo ine ndidzakutumizirani chimene Atate wanga anakulonjezani. Koma inu mukhalebe mumzindawu mpaka mutalandira mphamvu zochokera kumwamba.”+

50 Kenako anawatsogolera mpaka kukafika nawo ku Betaniya ndipo kumeneko anakweza manja ake nʼkuwadalitsa. 51 Pamene ankawadalitsa, analekana nawo ndipo Mulungu anamutenga kupita naye kumwamba.+ 52 Iwo anamugwadira* nʼkubwerera ku Yerusalemu akusangalala kwambiri.+ 53 Nthawi zonse iwo ankakhala mʼkachisi nʼkumatamanda Mulungu.+

Kapena kuti, “timaona kuti nʼzodalirika.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “mogwirizana ndi mwambo wa ansembe.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “kuyambira ali mʼmimba mwa mayi ake.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “waona masomphenya.”

Kapena kuti, “utumiki wotumikira anthu.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “anali pachibwenzi.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “chifukwa palibe chosatheka ndi Mulungu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “watikwezera mpulumutsi wamphamvu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Nyanga.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwamuna aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera pa unamwali wake.”

Onani Zakumapeto A5.

Ameneyu anali Herode Antipa. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anali bwanamkubwa wa chigawo cha 4 cha dera.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “Musamakakamize anthu kulipira.”

Kapena kuti, “Musamalande anthu zinthu zawo.”

Kapena kuti, “ndi malipiro anu.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “malo okwera kwambiri a kachisi.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “amene anachiritsidwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kutentha thupi.”

Imeneyi inali nyanja ya Galileya.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ndipo anakhala patebulo.”

Kapena kuti, “mkate wachionetsero.”

Kapena kuti, “kunyoza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi Wobwerayo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwa onse amene anabadwa kwa akazi.”

Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “kumanda achikumbutso.”

Mabaibulo ena amati, “unamugwira kwa nthawi yaitali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “apulumutsidwa.”

Kapena kuti, “mphamvu ya moyo.”

Kapena kuti, “chovala chowonjezera.”

Ameneyu ndi Herodi Antipa. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “bwanamkubwa wa chigawo cha 4 cha dera.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anakwana.”

Kapena kuti, “ndipo musamachedwe ndi kupereka moni.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu awo.”

Kapena kuti, “lizionedwa kuti ndi lopatulika; lizionedwa kuti ndi loyera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ali nafe ngongole.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musatilowetse mʼmayesero.”

Dzina limene Satana, yemwe ndi kalonga kapena kuti wolamulira ziwanda amadziwika nalo.

Kapena kuti, “dengu loyezera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “likulunjika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “loipa.”

Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.

Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mipando yabwino kwambiri.”

Kapena kuti, “manda achikumbutso.”

Kapena kuti, “manda opanda chizindikiro chilichonse.”

Kapena kuti, “manda achikumbutso.”

Kapena kuti, “kachisi.”

Kutanthauza mu Ufumu wakumwamba. Onani Mt 23:13.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “maasaliyoni awiri.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “amainyalanyaza.”

Mabaibulo ena amati, “Akapita nanu kumasunagoge.”

Kapena kuti, “kusirira kwa nsanje.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “nʼkupereka mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.

Kapena kuti, “Mangani lamba mʼchiuno mwanu.”

Nthawi imeneyi inkayamba cha mʼma 9 koloko usiku mpaka pakati pa usiku.

Nthawi imeneyi inkayamba pakati pa usiku mpaka cha mʼma 3 koloko mʼbandakucha.

Kapena kuti, “gulu la antchito ake apakhomo.”

Kapena kuti, “kuchita mogwirizana ndi zimene amafuna.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “lepitoni yomalizira.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “mzimu wolumalitsa.”

“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakangʼono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita 4 ndipo kamakhala ndi nthambi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “miyezo itatu ya seya.” Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.

Onani Zakumapeto A5.

Munthu amene ali ndi matenda amenewa amatupa chifukwa cha kuchuluka kwa madzi mʼthupi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate.”

Kapena kuti, “koma osachepetsa chikondi chake kwa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “azimayi ena omwe ndi anzake.”

Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “anamupsompsona.”

Kapena kuti, “ali wotetezeka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anadya.”

Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “miyezo 100 ya kori.” Muyezo umodzi wa kori unkakwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “mochenjera.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pachifuwa cha Abulahamu.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pachifuwa chake.”

Onani Zakumapeto A3.

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzapezadi chikhulupiriro.”

Kapena kuti, “ndichitireni chifundo.”

Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu.”

Mina yotchulidwa mʼMalemba a Chigiriki inkalemera magalamu 340 ndipo inali yofanana ndi madalakima 100. Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “siliva.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “siliva wanga.”

Onani Zakumapeto A5.

Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.

Kapena kuti, “kukusautsa.”

Kapena kuti, “anamumenya nʼkumunyoza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”

Kapena kuti, “nʼzoyenera.”

Onani Zakumapeto B14.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “chifukwa iye amaona kuti.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “mʼmipando yabwino kwambiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo amadya nyumba za akazi.”

Kapena kuti, “ataliatali mwachiphamaso.”

Kapena kuti, “chilango champhamvu.”

Kapena kuti, “mʼbokosi la zopereka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “malepitoni awiri.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “zipwirikiti.”

Kapena kuti, “masiku obwezera chilango.”

Kapena kuti, “akamupsompsone.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”

Onani Zakumapeto A3.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.

Kapena kuti, “manda achikumbutso.”

Kapena kuti, “manda achikumbutsowo.”

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”

Kapena kuti, “pamanda achikumbutsowo.”

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “masitadiya 60.” Sitadiya imodzi inkakwana mamita 185. Onani Zakumapeto B14.

Mabaibulo ena amati, “Kodi ndiwe mlendo yekhayo mu Yerusalemu amene sakudziwa?”

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”

Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”

Kapena kuti, “Atakhala patebulo.”

Kapena kuti, “anamuweramira.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena