-
Genesis 22:15-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiyeno mngelo wa Yehova anaitana Abulahamu kachiwiri kuchokera kumwamba, 16 nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndikulumbira pali dzina langa,+ kuti chifukwa cha zimene wachitazi, posakana kupereka mwana wako mmodzi yekhayo,+ 17 ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbadwa* zako ngati nyenyezi zakumwamba komanso ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.+ Ndipo mbadwa yako idzalanda mzinda* wa adani ake.+ 18 Kudzera mwa mbadwa* yako,+ mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.’”+
-