Miyambi ya Azulu Yodziŵira za Afirika
MTUNDU wa Azulu, umene amapezeka chakugombe kum’maŵa kwa South Africa, uli ndi miyambi yosangalatsa yokhalamo ndi maphunziro a moyo Wachiafirika. Popeza kuti ng’ombe nzofunika kwambiri m’moyo wa Azulu, mposadwabwita kuti zimenezi zimawonekera m’miyambi yawo yambiri.
Mwachitsanzo, talingalirani mmene Mzulu akafotokozera zotulukapo pamene atsogoleri aŵiri ayesa kutsogoza nyumba imodzi. Zimenezo zikakhala zaupandu mofanana ndi kuika ‘ng’ombe ziŵiri zamphongo m’khola limodzi.’ (Akukho zinkunzi zahlala ndawonye.)
Ndipo ponena za ng’ombe, fungo lamphamvu la nyanga yotenthedwa pamoto wapamudzi limanunkha moipa kwa onse okhala pafupi. Chifukwa chake, kunena munthu wandewu ndi wolongolola, wina angati: “Muwoneni, amka nawotchanso nyanga.” (Ushis’ uphondo.)
Kusenza mtolo wa munthuwe m’moyo kumawonedwa kukhala khalidwe labwino ndi anthu ambiri. Zirinso tero kwa Azulu. Choncho, mkulu wanzeru angathirire ndemanga kuti: “Uyenera kunyamula thayo lako lonse, popeza kuti ‘palibe njovu imene inalemedwa ndi chitamba chake.’” (Akundlovu yasindwa umboko wayo.)—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:5.
Ngati wina apezana ndi chipembere wamkali m’chipululu, kukwera kumtengo ndiko kungathandize koposa. Nchifukwa chake ali ndi mwambi wakuti: “Chipembere samtchula ngati palibe mtengo pafupi!” (Ungakhulumi ngobhejane kungekho sihlahla eduze.) Chenjezo la mwambiwu nlowonekeratu.
Mofananamo, kuyesa kuchita zinthu zambiri panthaŵi imodzi kungakhale kowonongetsa. “Sapitikitsa nswala ziŵiri panthaŵi imodzi,” amatero Azulu. (Ungexoshe mpalambili.) Amene anayesapo kuchita zimenezi amadziŵa kuti pamene ulimbikira panswala imodzi, inayo imathaŵa zolimba kuti usaipezenso. Phunziro? Chitani chinthu chimodzi panthaŵi imodzi.
Anthu ambiri samafuna munthu waliuma lopanda nzeru. Azulu ali ndi njira yabwino yachidule yofotokozera munthu wouma khosi motero pamene amati: “Pomphika, anaphikidwa pamodzi ndi mwala, ndipo mwala udayamba kupsa.” (Kwaphekwa yena kwaphekw’ itshe, kwavuthw’ itshe kuqala.)
Ngakhale kuti miyambiyi siyouziridwa monga ija ya m’Baibulo, mawu ake ambiri amasonyeza makhalidwe abwino amene amatithandiza kukhala anthu abwino.—Miyambo 1:5, 6.
[Chithunzi patsamba 32]
MTENGO WOTSATIRA 10 KM