Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 5/8 tsamba 3-4
  • Mikhole Kapena Ophedwera Chikhulupiriro Kodi Pali Kusiyana Kotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mikhole Kapena Ophedwera Chikhulupiriro Kodi Pali Kusiyana Kotani?
  • Galamukani!—1993
  • Nkhani Yofanana
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
  • Okhulupirika Olimba Mtima Anapambana Chizunzo cha Nazi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Nkhondo Zikupha Ana
    Galamukani!—1997
  • Anthu Amakono Ofera Chikhulupiriro Akuchitira Umboni ku Sweden
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 5/8 tsamba 3-4

Mikhole Kapena Ophedwera Chikhulupiriro Kodi Pali Kusiyana Kotani?

MKATI mwa mbiri, nkhanza zimene anthu achitira amuna, akazi, ndi ana zachititsa kuvutika kosalekeza ndipo zachititsa mikhole mamiliyoni ambiri. Kaya kukhale pazifukwa za ndale zadziko, utundu, fuko, kapena zachipembedzo, mwazi wosachimwa wakhetsedwa ndipo ukukhetsedwabe. Chidani chimapambana chikondi ndi kumvana. Kutengeka maganizo kumathetsa kulekererana. Ndipo kuphako kukupitirizabe.

M’zaka mazana apitawo, nkhondo zinali kumenyedwa pakati pa magulu ankhondo okha, ndipo kuloŵetsedwamo kwa anthu wamba kunali kwa apa ndi apo. M’zaka zathu za zana la 20, limodzi ndi kupangidwa kwa njira zoponyera mabomba kuchokera m’mlengalenga, zida zopita patali ndi mamisayelo, chiŵerengero cha anthu wamba ovulala ndi ophedwa chakwera kwambiri kotero kuti kufufuza kwina kunavumbula kuti: “Tsopano anthu wamba ndiwo akukhala mikhole yaikulu m’nkhondo. M’zaka za zana lino anthu wamba ambiri opanda zida aphedwa m’nkhondo kuposa asilikali.” Anthu opanda liŵongo ndiwo akhala chandamale cha nkhondo zoyambitsidwa ndi atsogoleri a ndale zadziko. M’zaka za zana lathu lokha, chiŵerengero cha mikhole yankhondo chakwera, oposa mamiliyoni zana limodzi akumaphedwa ndi mazana mamiliyoni ambiri akusautsidwa chifukwa cha kuvulala ndi kuphedwa kwa okondedwa awo.

Kuwonjezera pa mikhole ya mikangano yamakono, palinso ophedwera chikhulupiriro.a Kodi pali kusiyana kotani? Mamiliyoni ambiri—Ayuda, Aslav, Agypsy, ogonana ofanana ziŵalo, ndi anthu ena—anafa monga mikhole ya Jeremani Wachinazi kokha chifukwa cha amene iwo anali. Iwo analibe wowathandiza, sakanachitira mwina. Mu dongosolo loipa limenelo, imfa yawo inali yosapeŵeka. Kumbali ina, ena sanafunikire kufa. Anali ndi pothaŵira, koma, chifukwa cha zikhulupiriro zawo, iwo anasankha kusatero.

Chitsanzo chimodzi chotchuka chinali chija cha wansembe Wachikatolika Maximilian Kolbe, amene anathandiza Ayuda othaŵa kwawo mkati mwa Nkhondo Yadziko II. Mu 1941 iye “anatumizidwa ku [msasa wachibalo Wachinazi ku] Auschwitz, kumene anapereka modzifunira moyo wake m’malo mwa mkaidi woweruzidwa kufa Franciszek Gajowniczek. Poyamba anamanidwa chakudya, ndipo pomalizira pake anabaidwa jekeseni ndi mankhwala a phenol ndiyeno mtembo wake unawotchedwa.” (Encyclopædia Britannica) Iye anakhala wophedwera chikhulupiriro wodzipereka yekha—wosiyana kwambiri ndi ena onse m’zipembedzo za Chiprotesitanti ndi Chikatolika.

M’nyengo ya Chinazi m’Jeremani (1933-45), Mboni za Yehova zinazunzidwa kowopsa chifukwa chokhala zauchete ndi kukana kutumikira m’magulu ankhondo a Hitler. Zikwi zambiri zinatumizidwa kumisasa yachibalo yoopsayo, kumene ambiri anaphedwa ndipo ena anafa chifukwa cha kuchitiridwa nkhanza. Komabe, izo sizinafunikire kuvutika ndi kufa. Izo zinayenera kusankha. Zinapatsidwa populumukira. Ngati zikanangosaina chipepala chokana chikhulupiriro chawo, zikanamasulidwa. Unyinji waukulu unasankha kusasaina ndipo sanangokhala mikhole ya nkhalwe Yachinazi komanso ophedwera chikhulupiriro. Chotero, pamene kuli kwakuti ophedwera chikhulupiriro onse ali mikhole, mikhole yoŵerengeka yokha ingakhoze ndipo ndiyo inasankha kukhala ophedwera chikhulupiriro. Iyo inalakika poyang’anizana ndi imfa.

Umboni wopanda tsankho wochokera kwa anthu ambiri omwe sali Mboni umatsimikizira mfundo imeneyi. “Pastor Bruppacher wa ku Switzerland ananena mu 1939 kuti ‘Pamene kuli kwakuti anthu amene amadzitcha Akristu alephera poyang’anizana ndi ziyeso zowopsa, mboni zosadziŵika za Yehova zimenezi, monga Akristu ophedwera chikhulupiriro, zikusunga umphumphu wosagwedera motsutsana ndi kutsendereza chikumbumtima ndi kulambira mafano achikunja . . . Izo zikuvutika ndi kufa chifukwa chakuti, monga mboni za Yehova ndi nzika za Ufumu wa Kristu, zimakana kulambira Hitler ndi mbendera ya Swastika.’”

Komabe, sikuli ku Jeremani Wachinazi kokha kumene Mboni za Yehova zasunga umphumphu wawo poyang’anizana ndi imfa. Izo zinasonyeza kulimba mtima kwawo poyang’anizana ndi Chikomyunizimu, Chifashizimu, ndi mitundu ina yankhalwe yandale zadziko, limodzi ndi chitsutso chachipembedzo. Ngakhale m’maiko otchedwa a demokrase a Kumadzulo, Mbonizo zakumana ndi chiwawa. Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza mwatsatanetsatane zina za nkhani zokhudza Mboni zimene zinalakika poyang’anizana ndi imfa.

[Mawu a M’munsi]

a Mkhole wamasuliridwa kukhala “munthu amene amavulazidwa kapena kuphedwa ndi wina . . . Amene amavulazidwa kapena kuvutitsidwa ndi chochitika, ngozi, nthumwi, kapena mkhalidwe.” Kumbali ina, wophedwera chikhulupiriro ali “amene amasankha kufa m’malo mokana zikhulupiriro zachipembedzo. . . . Amene amadzimana kwakukulu kapena kuvutika kwambiri kotero kuti achilikize chikhulupiriro, cholinga, kapena lamulo lamkhalidwe.”—The American Heritage Dictionary of the English Language, Kope Lachitatu.

[Chithunzi patsamba 3]

Pamapeto pa Nkhondo Yadziko II, mabwalo amilandu a ku Jeremani Wakum’maŵa anaweruza molakwa Mboni za Yehova kukhala azondi a Amereka

[Mawu a Chithunzi]

Neue Berliner Illustrierte

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena