Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 1/8 tsamba 3-4
  • “Kusakaza Chilengedwe”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kusakaza Chilengedwe”
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuipitsa Pulaneti
  • “Tadzidzetsera Mliri”
  • Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino
    Galamukani!—2023
  • Mawu Oyamba
    Galamukani!—2023
  • Pulaneti Lathu Lokhala Pangozi—Bwanji za Mtsogolo?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Nkhalango Ziri ndi Mtsogolo?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 1/8 tsamba 3-4

“Kusakaza Chilengedwe”

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU IRELAND

UMBOMBO ukusokoneza mudzi wanu. Ukuwononga mphamvu ya dziko lapansi ya kutipatsa chakudya ndi malo okhala omwe ife tonse timafunikira kuti tikhale ndi moyo. Mosakayikira mwadziŵa kale mmene umbombo ukuwonongera dziko lapansi, koma nazi zikumbutso zingapo.

Kuipitsa Pulaneti

Kalelo mu 1962, Rachel Carson, m’buku lake lakuti Silent Spring, anachenjeza za kuipitsa pulaneti ndi mankhwala ophera tizilombo ndi zinyalala zapoizoni. Buku lakuti The Naked Savage likuti: “Anthu anali kuipitsa malo awo okhala ndi mudzi wawo womwe, chizindikiro chakuti mtunduwo udzasoloka.” Anthu mwaumbombo akali kuliipitsa pulaneti limeneli. “Pofuna kupeza mapindu aakulu koposa panthaŵi yaifupi kwambiri,” ikutero World Hunger: Twelve Myths, “achikumbe ali okonzeka kulima nthaka mopambanitsa, kugwiritsira ntchito madzi ndi mankhwala mopambanitsa, osaganizako za kukokolola nthaka, kuphwetsa madzi, ndi kuipitsa malo okhala.”

M’malo moteteza nkhalango za mvula zamtengo wapatali kwambiri za dziko—zofunika kwambiri kuti dziko lapansi lipitirize—anthu akuziwononga mofulumira kuposa ndi kale lonse. “Nkhalango zonse zabwino za kumadera otentha,” akutero olemba Far From Paradise—The Story of Man’s Impact on the Environment (1986), “zidzakhala pafupi kuzimirira pazaka makumi asanu ngati kawonongedwe kamene kalipoka kapitiriza osasintha.”

Asodzi opanda mwambo amagwiritsira ntchito madobi (dynamite) ndi mankhwala apoizoni kuphera nsomba pafupi ndi mitandadza ya makorali—imene yatchedwa “za m’madzi zolingana ndi nkhalango za mvula za kumadera otentha” chifukwa cha zamoyo zochuluka zamitundumitundu zimene zimakhalamo. Njira zosodzera zimenezi zowononga kwambiri ndiponso kuipitsa ndi mankhwala kopanda nzeru “zawononga kwadzaoneni” makorali ochuluka amoyo.—The Toronto Star.

“Tadzidzetsera Mliri”

Bwana Shridath Ramphal, yemwe anali pulezidenti wa World Conservation Union kuyambira 1991 mpaka 1993, akufotokoza kuti mtundu umenewu wa kusasamala chuma cha dziko lapansi ndiwo “kusakaza chilengedwe.” Kodi kuipa kwake kwafika poti? Ramphal akutchula chitsanzo mwa kulemba kuti: “Mitsinje yochuluka ya ku India yakhala moyenda chabe zam’chimbudzi zosaika mankhwala zochokera m’matauni ndi m’midzi kupita ku nyanja.” Kodi iye anafika ponena kuti chiyani? “Tadzidzetsera mliri.”

Umbombo wadzaza mbiri ya munthu zaka mazana ambiri, koma kupulumuka kwa pulaneti lerolino nkokayikitsa kwambiri. Chifukwa ninji? Chifukwa mphamvu yowononga ya munthu njaikulu kwambiri tsopano. “Ndi pazaka makumi asanu zokha zapitazo,” ikutero Far From Paradise, “pamene takhala ndi mankhwala ndi makina owonongeratu mitundu ina ya zamoyo papulaneti lathuli. . . . Homo sapiens [Chilatini, munthu wanzeru], dzina limene munthu mwini modzikuza amadzitcha, ali pafupifupi ndi mphamvu zonse ndipo wataya kudziletsa konse.” Posachedwa, bungwe la malo okhala la Greenpeace linalemba chikalata champhamvu choimba munthu mlandu, kuti: “Munthu wamakono wasandutsa Paradaiso [dziko lapansi] dzala . . . ndipo tsopano waima monga khanda lopulukira . . . ali pafupi . . . kuwonongeratu kasupe wa moyo ameneyu.”

Koma umbombo umawononga zambiri osati chabe mkhalidwe wamtsogolo kwambiri wa pulanetili. Umasokoneza mtendere ndi chisungiko chanu ndi cha banja lanu chalero. Motani? Ŵerengani nkhani yotsatira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena