M’tsogolo mwa Mtundu wa Anthu—Kodi ndi Mosungika?
Ngati mukufuna moyo m’mikhalidwe yosungika, mudzapeza zimene zalongosoledwa m’kabukhu’ka kukhala zolimbikitsa kwambiri. Komabe, kuphatikiza pa kuliwerenga kwanu, tikukhulupirira kuti mudzafuna kukambitsirana za m’kati mwake ndi munthu wina amene amazindikira bwino Baibulo, chifukwa chakuti zinthu zimene’zi zimakhudza kwambiri miyoyo ya ife tonse. Aka kadzakukhozetsani kuona m’mene Baibulo leni-leni’lo limayankhira mafunso anu. Mboni za Yehova zidzakondwa kusonyeza, kwaulere, m’mene makambitsirano otero’wo angakhalire opindulitsa.